Achinyamata, Mukhoza Kukhala ndi Moyo Wosangalala
“Mudzandidziwitsa njira ya moyo.”—SAL. 16:11.
NYIMBO: 133, 89
1, 2. Kodi chitsanzo cha Tony chikusonyeza bwanji kuti munthu akhoza kusintha?
MNYAMATA wina dzina lake Tony sankakonda sukulu ndipo anali atatsala pang’ono kuisiya. Iye analibe bambo ndipo Loweruka ndi Lamlungu ankangocheza ndi anzake kapena kupita kukaonera mafilimu. Sankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kapena kuchita zachiwawa, kungoti analibe cholinga pa moyo wake. Iye ankakayikiranso zoti kuli Mulungu. Koma kenako anakumana ndi banja lina la Mboni ndipo anakambirana ndi banjalo zimene zinkamuchititsa kukayikira zoti kuli Mulungu. Kenako anamupatsa kabuku kakuti, Mmene Moyo Unayambira—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri ndi kakuti, Kodi Zamoyo Zinachita Kulengedwa?
2 Banjali litabweranso kudzamuona, Tony anali atasintha maganizo ake. Iye anali atawerenga timabukuto kambirimbiri moti tinali titakwinyikakwinyika. Iye anati: “Ndaona kuti Mulungu alikodi.” Tony anavomera kuphunzira Baibulo ndipo pang’ono ndi pang’ono anayamba kusintha mmene ankaonera zinthu. Anayambanso kuchita bwino kwambiri kusukulu. Ngakhale ahedi ake, omwe ankadziwa kuti Tony wayamba kuphunzira ndi a Mboni, anadabwa naye kwambiri. Ahediwo anamuuza kuti: “Maganizo ako asintha kwambiri ndipo ukukhoza bwino. Kodi n’chifukwa choti ukuphunzira ndi a Mboni za Yehova?” Tony anavomera ndipo anawalalikira. Iye anakhoza bwino mayeso ndipo panopa ndi mpainiya wokhazikika komanso mtumiki wothandiza. Akusangalalanso kuti panopa ali ndi Bambo abwino kwambiri omwe ndi Yehova.—Sal. 68:5.
MUZIMVERA YEHOVA NDIPO ZINTHU ZIDZAKUYENDERANI BWINO
3. Kodi Yehova ananena kuti achinyamata azitani?
3 Nkhani ya Tony ikusonyeza kuti Yehova amaganizira kwambiri achinyamata. Iye amafuna kuti achinyamatanu muzikhala ndi moyo wosangalala. N’chifukwa chake ananena kuti: “Kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako.” (Mlal. 12:1) N’zoona kuti kuchita zimenezi masiku ano si kophweka koma n’zotheka. Mulungu akhoza kukuthandizani kuti muzisangalala panopa komanso kwa moyo wanu wonse. Kuti timvetse nkhaniyi, tiyeni tikambirane zimene tikuphunzira pa zimene zinachitika pamene Aisiraeli ankagonjetsa adani awo m’Dziko Lolonjezedwa komanso nkhani ya Davide ndi Goliyati.
4, 5. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhondo ya pakati pa Aisiraeli ndi Akanani ndi ya pakati pa Davide ndi Goliyati? (Onani zithunzi zoyambirira.)
4 Aisiraeli atayandikira Dziko Lolonjezedwa, Yehova sanawauze kuti ayambe kukonzekera nkhondo. (Deut. 28:1, 2) M’malomwake anangowauza kuti azitsatira malamulo ake komanso kumukhulupirira. (Yos. 1:7-9) Munthu akhoza kuona kuti malangizo amenewa anali osathandiza. Koma zoona zake n’zakuti anali othandiza kwambiri chifukwa Yehova anathandiza anthu ake kuti azigonjetsa asilikali a ku Kanani. (Yos. 24:11-13) Munthu amafunika kukhala ndi chikhulupiriro kuti amvere Yehova ndipo nthawi zonse chikhulupirirocho chimamuthandiza kuti zinthu zizimuyendera bwino. Mfundo imeneyi sinasinthe ndipo ndi yoona mpaka pano.
5 Goliyati anali msilikali wamphamvu. Iye anali wamtali pafupifupi mamita atatu ndipo anali ndi zida zamphamvu. (1 Sam. 17:4-7) Koma tingati Davide anali ndi zida ziwiri zokha. Anali ndi gulaye komanso ankadalira Yehova. Kwa anthu osakhulupirira Yehova, zimene Davide anachita zikanaoneka ngati zopusa. Koma si mmene zinalili chifukwa pa mapeto pake zinaoneka kuti wopusa anali Goliyati.—1 Sam. 17:48-51.
6. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
6 Munkhani yapita ija tinakambirana zinthu 4 zimene zimatithandiza kuti tizisangalala. Tinakambirana za kupeza zosowa zathu zauzimu, kuyamikira kuti tili ndi anzathu abwino, kukhala ndi zolinga zabwino komanso kuyamikira ufulu umene Mulungu watipatsa. Tsopano tiyeni tikambirane zinthu zimenezi ndipo tizigwirizanitse ndi mfundo za mu Salimo 16.
MUZIPEZA ZOSOWA ZANU ZAUZIMU
7. (a) Kodi munthu wokonda zinthu zauzimu amatani? (b) Kodi “gawo” la Davide linali chiyani, nanga ankamva bwanji akaganizira za gawoli?
7 Munthu wauzimu amakhulupirira Mulungu ndipo amaona zinthu mmene iye amazionera. Amadalira malangizo a Yehova ndipo amamumvera. (1 Akor. 2:12, 13) Davide ndi chitsanzo chabwino pa nkhani imeneyi. Iye anaimba kuti: “Yehova ndiye gawo langa, gawo limene ndinapatsidwa, komanso chikho changa.” (Sal. 16:5) Ponena mawu oti “gawo” Davide ankatanthauza zinthu monga ubwenzi wake ndi Mulungu amene iye ankamuona ngati pothawirapo pake. (Sal. 16:1) Kodi zotsatira zake zinali zotani? Iye analemba kuti: “Moyo wanga ukukondwera.” Mawu amenewa akusonyeza kuti palibe chimene chinkamusangalatsa kwambiri kuposa ubwenzi wake ndi Yehova.—Werengani Salimo 16:9, 11.
8. Kodi n’chiyani chimathandiza munthu kuti akhale wosangalala?
8 Anthu amene amangokhalira kufunafuna chuma ndi zosangalatsa sangakhale osangalala ngati mmene Davide ankachitira. (1 Tim. 6:9, 10) M’bale wina wa ku Canada ananena kuti: “Munthu sakhala wosangalala chifukwa cha zimene amapeza pa moyo wake, koma chifukwa cha zimene iyeyo amapereka kwa Yehova yemwe ndi wopereka mphatso iliyonse yabwino.” (Yak. 1:17) Kukhulupirira Yehova komanso kumutumikira kungakuthandizeni kuti muzikhala osangalala. Ndiye kodi mungatani kuti mukhale ndi chikhulupiriro cholimba? Muyenera kumapeza nthawi yoti mudziwe bwino Yehova. Mungachite zimenezi powerenga Mawu ake, kuona chilengedwe chake komanso kuganizira makhalidwe ake monga chikondi chimene amakusonyezani.—Aroma 1:20; 5:8.
9. Kodi mungatani kuti Mawu a Mulungu azikuthandizani ngati mmene anathandizira Davide?
9 Nthawi zina Mulungu amatisonyeza chikondi potipatsa malangizo ngati mmene bambo angachitire ndi mwana wake. Davide atapatsidwa malangizo anawalandira bwino ndipo anati: “Ndidzatamanda Yehova amene wandipatsa malangizo. Ndithudi, usiku impso zanga zandiwongolera.” (Sal. 16:7) Iye ankaganizira kwambiri mfundo za Yehova, kuzikonda komanso kulola kuti zisinthe maganizo ake. Inunso mukamachita zimenezi mudzayamba kukonda kwambiri Yehova komanso kukhala ndi mtima wofunitsitsa kumumvera. Mudzakhalanso Mkhristu wolimba mwauzimu. Mlongo wina dzina lake Christin anati: “Ndikamafufuza mfundo za m’Baibulo komanso kuziganizira kwambiri ndimamva ngati mfundozi Yehova analembera ineyo.”
10. Malinga ndi Yesaya 26:3, kodi kukhala munthu wauzimu n’kothandiza bwanji?
10 Kukhala munthu wauzimu kumathandizanso munthu kukhala wozindikira komanso wanzeru. Zili choncho chifukwa amatha kuona zinthu za m’dzikoli komanso zam’tsogolo ngati mmene Mulungu amazionera. Koma kodi n’chifukwa chiyani Yehova amakupatsani nzeru zimenezi komanso kuzindikira? Iye amafuna kuti muziika zinthu zofunika kwambiri pamalo oyamba, muzisankha zochita mwanzeru komanso musamaope zimene zichitike m’tsogolo. (Werengani Yesaya 26:3.) M’bale wina wa ku United States dzina lake Joshua anati: “Munthu akakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova amakhala ndi maganizo oyenera pa zinthu zonse.” Zimenezi ndi zoona ndipo zimathandiza kuti munthu azikhala wosangalala kwambiri.
MUZIPEZA ANZANU ABWINO
11. Kodi Davide anasonyeza kuti tingapeze bwanji anzathu abwino?
11 Werengani Salimo 16:3. Davide ankadziwa zimene zingathandize munthu kupeza anzake abwino. Iye ankasangalala kwambiri kukhala limodzi ndi anthu okonda Yehova. Iye anati anzakewo anali “oyera” kutanthauza kuti anali amakhalidwe abwino. Munthu winanso wolemba masalimo ankasankha bwino anthu ocheza nawo. Iye analemba kuti: “Ine ndine mnzawo wa anthu okuopani, ndiponso wa anthu osunga malamulo anu.” (Sal. 119:63) Nkhani yapita ija inasonyeza kuti m’gulu la Yehova tikhoza kupezamo anzathu abwino. Anzathuwo akhoza kukhala anthu amisinkhu yosiyanasiyana.
12. Kodi zinatheka bwanji kuti Davide ndi Yonatani azigwirizana?
12 Davide sankacheza ndi anthu amsinkhu wake okha. Kodi mukukumbukira mmodzi mwa “anthu aulemerero” amene anali mnzake wapamtima? Anali Yonatani. Baibulo limasonyeza kuti awiriwa anali pa ubwenzi wabwino kwambiri. Koma kodi mukudziwa kuti Yonatani anali wamkulu moti ankasiyana ndi Davide zaka 30? Ndiye kodi zinatheka bwanji kuti ayambe kugwirizana? Onse ankakhulupirira Mulungu, ankalemekezana komanso anali olimba mtima pomenyana ndi adani a Mulungu.—1 Sam. 13:3; 14:13; 17:48-50; 18:1.
13. Kodi mungatani kuti mukhale ndi anzanu ambiri? Perekani chitsanzo.
13 Ifenso tikhoza kukhala osangalala kwambiri tikamagwirizana ndi anthu amene amakonda Yehova komanso kumukhulupirira. Mlongo wina dzina lake Kiera, yemwe watumikira Mulungu kwa zaka zambiri, ananena kuti: “Ndili ndi anzanga a m’mayiko osiyanasiyana komanso azikhalidwe zosiyanasiyana.” Inunso mukamayesetsa kucheza ndi anthu osiyanasiyana mudzaona umboni wakuti Mawu a Mulungu komanso mzimu wake zimathandiza anthu kuti azigwirizana.
MUZIKHALA NDI ZOLINGA ZABWINO
14. (a) N’chiyani chingakuthandizeni kukhala ndi zolinga zabwino? (b) Kodi achinyamata ena amamva bwanji akaganizira zimene anasankha?
14 Werengani Salimo 16:8. Davide ankaona kuti kutumikira Yehova kunali kofunika kwambiri pa moyo wake. Inunso mukamaika kutumikira Yehova pamalo oyamba komanso kukhala ndi zolinga zogwirizana ndi chifuniro chake, mudzakhala osangalala. M’bale wina dzina lake Steven anati: “Ndikamayesetsa kuti ndikwaniritse cholinga changa kenako n’kuchikwaniritsa ndiye n’kumaganizira mmene zinthu zayendera bwino, ndimasangalala kwambiri.” M’bale winanso wa ku Germany amene anapita kukatumikira kudziko lina anati: “Sindikufuna kuti ndikadzakalamba ndizidzaona kuti pa moyo wanga wonse ndinkangochita zofuna zanga.” Kodi umu ndi mmene inunso mumaganizira? Ngati ndi choncho, muziyesetsa kugwiritsa ntchito luso komanso mphamvu zanu kuti mulemekeze Mulungu komanso muthandize anthu ena. (Agal. 6:10) Muzikhala ndi zolinga zauzimu, kenako n’kupempha Yehova kuti akuthandizeni kuzikwaniritsa. Yehova amasangalala kwambiri kuyankha mapemphero oterowo.—1 Yoh. 3:22; 5:14, 15.
15. Kodi mungakhale ndi zolinga zotani? (Onani bokosi lakuti “ Zolinga Zina Zothandiza.”)
15 Kodi ndi zolinga ziti zimene mungakhale nazo? Mwina mungakhale ndi cholinga choti muziyankha pamisonkhano m’mawu anuanu, kuchita upainiya kapena kukatumikira ku Beteli. Mwinanso mungafune kuphunzira chilankhulo china n’cholinga choti muzitha kulalikira anthu olankhula chilankhulocho. Mnyamata wina dzina lake Barak, yemwe ndi mpainiya, ananena kuti: “Tsiku lililonse ndikaganizira kuti ndikugwiritsa ntchito mphamvu zanga zonse potumikira Yehova ndimaona kuti ndinasankha ntchito yabwino kwambiri.”
MUZIYAMIKIRA UFULU UMENE MULUNGU WAKUPATSANI
16. Kodi Davide ankaona bwanji mfundo zachilungamo za Yehova? Perekani chifukwa.
16 Werengani Salimo 16:2, 4. Monga tinaonera munkhani yapita ija, malamulo ndi mfundo zachilungamo za Mulungu zimatimasula chifukwa zimatithandiza kukonda zabwino n’kumadana ndi zoipa. (Amosi 5:15) Davide anazindikira kuti ubwino umachokera kwa Yehova. Khalidwe la ubwino limatanthauza kukhala ndi makhalidwe abwino kwambiri. Davide ankayesetsa kutsanzira ubwino wa Mulungu komanso kuti azidana ndi zimene Mulungu amadana nazo. Mwachitsanzo, Mulungu amadana ndi kulambira mafano chifukwa kuchita zimenezi kumanyozetsa anthu komanso kumamulanda ulemerero umene ayenera kulandira.—Yes. 2:8, 9; Chiv. 4:11.
17, 18. (a) Kodi Davide ananena chiyani zokhudza zotsatira za kulambira konyenga? (b) N’chiyani chimachititsa kuti anthu akhale ndi ‘zopweteka zochuluka’?
17 Kale, anthu akamalambira milungu yonyenga, nthawi zambiri ankachitanso zachiwerewere. (Hos. 4:13, 14) Anthuwo ankakonda kulambira milungu yonyenga chifukwa ankakondanso zachiwerewere. Koma sizinathandize anthu kuti azikhaladi osangalala. Paja Davide ananena kuti “zopweteka zimachuluka kwa anthu” amene amalambira milungu ina. Anthuwo anafikanso pomapereka nsembe ana awo kwa milungu yonyenga. (Yes. 57:5) Yehova ankadana ndi nkhanza zimenezi. (Yer. 7:31) Mukanakhala mu nthawi imeneyo, mukanasangalala kwambiri ngati makolo anu akanakhala kuti amakhulupirira Yehova n’kumamumvera.
18 Masiku anonso, zipembedzo zonyenga zimalekerera anthu ochita chiwerewere komanso kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha. Anthu akamachita zimenezi amaganiza kuti ali pa ufulu. Koma zoona zake n’zakuti ‘amangochulukitsa zopweteka zawo.’ (1 Akor. 6:18, 19) Mwina inuyo panokha mwaonapo mavuto amene anthu oterewa amakumana nawo. Choncho achinyamatanu muzimvera Atate wanu wakumwamba. Musamakayikire ngakhale pang’ono kuti kumvera Mulungu n’kothandiza kwambiri. Muzikhulupiriranso kuti mavuto amene angabwere mukamachita zoipa ndi ochuluka kwambiri kuposa chisangalalo cha kanthawi chimene mungapeze. (Agal. 6:8) Joshua yemwe tamutchula kale uja ananena kuti: “Tikhoza kugwiritsa ntchito ufulu wathu mmene tikufunira koma tikapanda kuugwiritsa ntchito mwanzeru sitingakhale osangalala.”
19, 20. Kodi achinyamata amene amakhulupirira Mulungu komanso kumumvera adzadalitsidwa bwanji?
19 Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mukamasunga mawu anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yoh. 8:31, 32) Ophunzira a Yesu amamasulidwa ku chipembedzo chonyenga, zikhulupiriro zabodza komanso kuti asakhale osazindikira. Komanso pa mapeto pake adzapeza “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Ngakhale panopa, tikhoza kulawa ufuluwu ‘tikamasunga mawu a Khristu.’ Tikamachita zimenezi ‘tidzadziwa choonadi’ osati chifukwa chongochiphunzira koma chifukwa chochitsatira.
20 Achinyamatanu muyenera kuyamikira kwambiri ufulu umene Mulungu wakupatsani. Muzigwiritsa ntchito ufuluwo mwanzeru ndipo mukatero mudzakhala ndi tsogolo labwino. Mnyamata wina anati: “Mukamagwiritsa ntchito ufulu wanu mwanzeru muli wamng’ono zimakuthandizani kuti mudzasankhe bwino pa nkhani zikuluzikulu. Mwachitsanzo, mudzatha kusankha mwanzeru pa nkhani ya ntchito komanso yokhudza kulowa m’banja kapena kudikira kaye.”
21. Kodi mungatani kuti mukhalebe pa njira yopita ku ‘moyo weniweni’?
21 M’dziko lakaleli, moyo umene anthu ambiri amati ndi wabwino umakhala wosadalirika komanso wakanthawi. Paja sitidziwa zimene zingachitike mawa. (Yak. 4:13, 14) Choncho ndi nzeru kukhalabe pa njira yopita ku ‘moyo weniweni,’ womwe ndi moyo wosatha. (1 Tim. 6:19) Koma Mulungu satikakamiza kuyenda pa njirayo. Tiyenera kusankha tokha. Choncho muziyesetsa kuti Yehova akhale “gawo” lanu ndipo muziyamikira kwambiri “zinthu zabwino” zimene wakupatsani. (Sal. 103:5) Muzikhulupiriranso kuti iye angakuthandizeni kuti muzisangalala kwambiri komanso kuti mukhale ndi “chimwemwe mpaka muyaya.”—Sal. 16:11.
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA