Tizilemekeza “Chimene Mulungu Wachimanga Pamodzi”
“Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—MALIKO 10:9.
NYIMBO: 131, 132
1, 2. Kodi lemba la Aheberi 13:4 limatilimbikitsa kuchita chiyani?
N’ZOSACHITA kufunsa kuti inuyo mumafuna kulemekeza Yehova. Iye ndi woyenera kumulemekeza ndipo analonjeza kuti nayenso adzakulemekezani. (1 Sam. 2:30; Miy. 3:9; Chiv. 4:11) Mulungu amafuna kuti muziperekanso ulemu woyenerera kwa anthu monga akuluakulu a boma. (Aroma 12:10; 13:7) Koma iye amafunanso kuti muzilemekeza ukwati.
2 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posaipitsidwa.” (Aheb. 13:4) Apa sikuti Paulo ankangotchula mfundo basi. Lembali likulamula Akhristu kuti azilemekeza ukwati n’kumaona kuti ndi wamtengo wapatali. Kodi umu ndi mmene inuyo mumaonera ukwati? Ngati muli pa banja, kodi mumalemekeza ukwati wanu?
3. Kodi Yesu anapereka malangizo ofunika ati pa nkhani ya ukwati? (Onani chithunzi choyambirira.)
3 Yesu ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yolemekeza ukwati. Afarisi atamufunsa nkhani yothetsa banja, iye anafotokoza zimene Mulungu ananena zokhudza ukwati wa anthu oyambirira. Paja Mulungu anati: “Pa chifukwa chimenechi, mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.” Ndiyeno Yesu anapitiriza kuti: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Werengani Maliko 10:2-12; Gen. 2:24.
4. Kodi Yehova anali ndi cholinga chotani pa nkhani ya ukwati?
4 Yesu anasonyeza kuti Mulungu ndi amene anayambitsa ukwati ndipo anatsindika kuti suyenera kutha. Paja Mulungu sanauze Adamu ndi Hava kuti iwo akhoza kuthetsa banja lawo. Zimene zinachitika mu Edeni zimasonyeza kuti ukwati ndi mgwirizano wosatha wa pakati pa mwamuna mmodzi ndi mkazi mmodzi.
ZINTHU ZINASINTHA KWA KANTHAWI PA NKHANI YA BANJA
5. Kodi zinthu zinasintha bwanji pa nkhani ya ukwati chifukwa cha imfa?
5 Koma Adamu atachimwa, zinthu zinasintha. Anthu anayamba kufa ndipo zimenezi zinakhudza mabanja. Tingatsimikizire zimenezi tikaganizira zimene Paulo ananena posonyeza kuti Akhristu sayendera Chilamulo cha Mose. Iye ananena kuti imfa imathetsa banja ndipo wotsalayo akhoza kukwatira kapena kukwatiwanso.—Aroma 7:1-3.
6. Kodi Chilamulo cha Mose chimasonyeza bwanji kuti Mulungu amalemekeza ukwati?
6 M’Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli munalinso malamulo okhudza banja. Chilamulochi chinkalola mwamuna kukwatira mitala koma izi zinali zitayamba kale kuchitika Chilamulocho chisanaperekedwe. Komabe panali malamulo oyenera kutsatira pa nkhani ya mitala n’cholinga choti akazi ndi ana asamachitiridwe nkhanza. Mwachitsanzo, ngati mwamuna wakwatira mkazi wachiwiri, sankayenera kusintha zimene ankachita posamalira mkazi woyambayo pa nkhani ya chakudya, zovala komanso kugonana. Mulungu ankafuna kuti mwamunayo azisamalirabe mkazi woyambayo komanso kumuteteza. (Eks. 21:9, 10) N’zoona kuti masiku ano sitiyendera Chilamulo, koma mfundo zimene takambiranazi zikusonyeza kuti Yehova amaona kuti ukwati ndi wamtengo wapatali. Mfundo zimenezi ziyenera kulimbikitsanso ifeyo kuti tizilemekeza ukwati.
7, 8. (a) Malinga ndi Deuteronomo 24:1, kodi Chilamulo chinkati chiyani pa nkhani yothetsa banja? (b) Kodi Yehova amaona bwanji kuthetsa banja?
7 Kodi Chilamulo chinkati chiyani pa nkhani ya kutha kwa banja? Ngakhale kuti Mulungu amalemekeza kwambiri banja, mu Chilamulochi analolabe kuti anthu azithetsa mabanja. (Werengani Deuteronomo 24:1.) Mwamuna wachiisiraeli ankaloledwa kuthetsa banja ngati ‘wam’peza mkazi wake ndi vuto linalake.’ Chilamulocho sichinafotokoze kuti “vuto” lake lingakhale lotani. Koma liyenera kuti linkakhala lalikulu kapena lochititsa manyazi kwambiri. (Deut. 23:14) N’zomvetsa chisoni kuti pofika nthawi ya Yesu, Ayuda ankathetsa mabanja “pa chifukwa chilichonse.” (Mat. 19:3) Ifeyo sitingafune m’pang’ono pomwe kutengera maganizo amenewa.
8 Mneneri Malaki anafotokoza maganizo a Yehova pa nkhani yothetsa banja. Pa nthawiyo, amuna ankakonda kuthetsa mabanja ndi ‘akazi amene anawakwatira ali achinyamata’ mwina n’cholinga choti akwatire achitsikana, omwe n’kutheka kuti sankalambira Yehova. Ndiyeno pofotokoza maganizo a Yehova, Malaki analemba kuti: “Ndimadana ndi zakuti anthu azithetsa mabanja.” (Mal. 2:14-16) Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Mawu a Mulungu amanena pa nkhani ya banja loyambirira. Paja amati: ‘Mwamuna adzadziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.’ (Gen. 2:24) Yesu anatsindika maganizo a Atate akewa ponena kuti: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Mat. 19:6.
CHIFUKWA CHOVOMEREZEKA CHOTHETSERA BANJA
9. Kodi mawu a Yesu a pa Maliko 10:11, 12 amatanthauza chiyani?
9 Mwina tingadzifunse kuti, ‘Kodi pangakhale chifukwa choti Mkhristu athetsere banja n’kukwatira kapena kukwatiwanso?’ Yesu anafotokoza maganizo ake pa nkhaniyi. Iye anati: “Aliyense wosiya mkazi wake ndi kukwatira wina, wachita chigololo molakwira mkaziyo. Ndipo ngati mkazi wasiya mwamuna wake, ndiyeno n’kukwatiwa ndi wina, wachita chigololo.” (Maliko 10:11, 12; Luka 16:18) Apa zikuonekeratu kuti Yesu amalemekeza ukwati ndipo amafuna kuti ifenso tizichita zimenezi. Mwamuna akasiya mkazi wake wokhulupirika (kapena mkazi akasiya mwamuna wake wokhulupirika) pa zifukwa zina n’kukwatira wina ndiye kuti akuchita chigololo. Kwa Mulungu, anthu awiriwo amakhala adakali “thupi limodzi.” Yesu ananenanso kuti munthu akasiya mkazi wake wosalakwa amamuchititsa chigololo. Zili choncho chifukwa pa nthawiyo mkazi amene banja lake latha ankakakamizika kuti akwatiwenso n’cholinga choti azisamaliridwa. Koma akakwatiwanso ankakhala kuti wachita chigololo.
10. Kodi Mkhristu angathetse banja n’kukwatiwa kapena kukwatira wina pa chifukwa chiti?
10 Yesu anafotokoza chifukwa chovomerezeka chothetsera banja. Iye anati: “Ine ndikukuuzani kuti aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama [pa Chigiriki amati por·neiʹa].” (Mat. 19:9) Iye ananenanso mfundo yomweyi pa ulaliki wake wapaphiri. (Mat. 5:31, 32) Pa nthawi zonse ziwirizi, Yesu ananena za “dama.” Mawu amenewa amanena za zinthu monga chigololo, uhule, kugonana pakati pa anthu amene sali pa banja, kugonana amuna kapena akazi okhaokha komanso kugona nyama. Ngati mwamuna amene ali pa banja wachita dama, mkazi wake angasankhe kuthetsa banja kapena ayi. Akasankha kuthetsa banjalo ndiye kuti lathanso pamaso pa Mulungu.
11. N’chifukwa chiyani Mkhristu angasankhe kuti asathetse banja ngakhale kuti pali chifukwa chovomerezeka?
11 Koma Yesu sananene kuti munthu wina m’banja akachita dama ndiye kuti winayo amafunika kuthetsa banja basi. Mwachitsanzo, mkazi amene mwamuna wake wachita dama akhoza kusankha kuti akhalebe naye pa banja. Mwina amamukondabe ndipo akufuna kumukhululukira n’kumayesetsa kuti banja lawo liziyenda bwino. Komanso akathetsa banja n’kumakhala wosakwatiwa akhoza kukumana ndi mavuto osiyanasiyana. Mwachitsanzo, akhoza kuvutika kupeza zofunika pa moyo, angasowe wocheza naye komanso wogonana naye. Ngati ali ndi ana angamavutike kuwasamalira komanso kuwaphunzitsa choonadi. (1 Akor. 7:14) Choncho n’zoonekeratu kuti mwamuna kapena mkazi wosalakwa akasankha kuthetsa banja akhoza kukumana ndi mavuto ena.
12, 13. (a) N’chiyani chinachitika m’banja la Hoseya? (b) N’chifukwa chiyani Hoseya anatenganso Gomeri, nanga zimenezi zikutiphunzitsa chiyani?
12 Chitsanzo cha Hoseya ndi chothandiza pa nkhaniyi. Mulungu anauza Hoseya kuti akwatire mkazi wina dzina lake Gomeri yemwe ‘adzachite dama’ komanso kubereka ana ‘chifukwa cha dama lakelo.’ Gomeri ‘anamuberekera Hoseya mwana wamwamuna.’ (Hos. 1:2, 3) Kenako anabereka mwana wamkazi komanso wamwamuna mwina chifukwa choti anachita chigololo. Ngakhale kuti Gomeri ankachita chigololo mobwerezabwereza, Hoseya sanamusiye. Koma kenako Gomeri anamusiya Hoseya n’kukakhala kapolo. Ngakhale zinali choncho, Hoseya anakamutenga. (Hos. 3:1, 2) Yehova anagwiritsa ntchito Hoseya kuti asonyeze zimene iyeyo anachita pokhululukira Aisiraeli omwe ankamusiya mobwerezabwereza n’kumakalambira milungu yonyenga. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhaniyi?
13 Ngati mwamuna kapena mkazi wa Mkhristu angachite dama, Mkhristu wosalakwayo ayenera kusankha zochita. Yesu ananena kuti wosalakwayo ali ndi chifukwa chovomerezeka chothetsera banja n’kukwatira kapena kukwatiwanso. Komabe akhoza kusankha kukhululukira mwamuna kapena mkazi wakeyo. Kuchita zimenezi si kulakwa. Paja Hoseya anamutenganso Gomeri. Hoseya atamutenganso anamuuza kuti asachitenso dama ndi mwamuna wina. Hoseya sanagone ndi Gomeri kwa kanthawi. (Hos. 3:3) Koma kenako ayenera kuti anayambanso kugonana naye. Zimenezi zinasonyeza kuti Mulungu anali wokonzeka kukhululukira anthu ake n’kumachitanso nawo zinthu. (Hos. 1:11; 3:3-5) Kodi mfundo imeneyi ingatithandize bwanji masiku ano pa nkhani ya ukwati? Ngati Mkhristu wayambanso kugonana ndi mwamuna kapena mkazi wake yemwe wachita chigololo ndiye kuti akusonyeza kuti wamukhululukira. (1 Akor. 7:3, 5) Akatero sakhalanso ndi ufulu wothetsa banja ndipo ayenera kuthandizana ndi mnzakeyo kuti akhale ndi maganizo a Mulungu pa nkhani ya ukwati.
TIZILEMEKEZA BANJA LATHU NGAKHALE PAMENE SILIKUYENDA BWINO
14. Malinga ndi lemba la 1 Akorinto 7:10, 11, n’chiyani chingachitike m’banja?
14 Akhristu onse ayenera kuyesetsa kuti azilemekeza ukwati ngati mmene Yesu ndi Yehova amachitira. Komabe ena angalephere kuchita zimenezi chifukwa anthufe si angwiro. (Aroma 7:18-23) Choncho sitiyenera kudabwa kuti Akhristu ena akale ankakumana ndi mavuto m’mabanja awo. Nthawi zina ankapatukana ngakhale kuti Paulo analemba kuti “mkazi asasiye mwamuna wake.”—Werengani 1 Akorinto 7:10, 11.
15, 16. (a) Ngakhale kuti anthu akukumana ndi mavuto m’banja lawo, kodi ayenera kukhala ndi cholinga chotani? Perekani chifukwa. (b) Kodi mfundo imeneyi iyenera kugwiritsidwa ntchito bwanji m’banja loti wina si wa Mboni?
15 Paulo sanafotokoze chimene chinkachititsa kuti ena apatukane. Chomwe tikudziwa n’chakuti vuto silinali lakuti mwamuna anachita dama chifukwa zimenezi zikanapatsa mkaziyo chifukwa chomveka choti athetsere banja n’kukwatiwanso. Koma Paulo analemba kuti mkazi amene anapatukana ndi mwamuna wake “akhale choncho wosakwatiwa. Apo ayi, abwererane ndi mwamuna wakeyo.” Izi zikusonyeza kuti pamaso pa Mulungu anthu awiriwo anali adakali pa banja. Paulo anafotokoza kuti mwamuna ndi mkazi amene akumana ndi mavuto, koma wina sanachite chigololo, ayenera kukhala ndi cholinga choti akonze zinthu m’banja mwawo. Iwo akhoza kupempha akulu mumpingo kuti awathandize kuchita zimenezi. Akulu ayenera kuwapatsa malangizo a m’Malemba koma azipewa kukhala mbali ya wina aliyense.
16 Nanga bwanji ngati Mkhristu ali pa banja ndi munthu amene satumikira Yehova? Kodi akakumana ndi mavuto m’banja lawo, akhoza kungopatukana? Monga tanena kale, Malemba amanena kuti munthu akhoza kuthetsa banja ngati mnzake wachita dama, koma safotokoza zifukwa zochititsa kuti anthu apatukane. Paulo analemba kuti: “Mkazi amene mwamuna wake ndi wosakhulupirira, koma mwamunayo akulola kukhala naye, asamusiye mwamuna wakeyo.” (1 Akor. 7:12, 13) Masiku anonso tiyenera kutsatira malangizo amenewa.
17, 18. N’chifukwa chiyani Akhristu ena anasankha kukhalabe m’banja ngakhale kuti munali mavuto aakulu?
17 N’zoona kuti nthawi zina mwamuna “wosakhulupirira” amasonyeza kuti sakufuna kuti akhalebe ndi mkazi wake. Mwina amamuchitira nkhanza kwambiri moti mkaziyo amaona kuti moyo wake uli pa ngozi. Apo ayi mwina amakaniratu kusamalira iyeyo ndi ana ake. Kapenanso amamulepheretsa kulambira Yehova. Zimenezi zikachitika akazi ena angasankhe kupatukana ndi mwamunayo chifukwa choona kuti ‘sakulola kukhala naye’ ngakhale kuti sananene zimenezi. Koma Akhristu ena amene akumana ndi mavuto oterewa amasankha kungopirira n’kumayesetsa kuti banja lawo liziyenda bwino. N’chifukwa chiyani amachita zimenezi?
18 Anthu akapatukana amakhalabe kuti ali pa banja. Choncho akakhala kosiyana amakumana ndi mavuto amene tawatchula kale aja. Mtumwi Paulo anatchula chifukwa chinanso chimene chimachititsa kuti anthu ena azikhalabe m’banja lamavuto. Iye anati: “Mwamuna wosakhulupirira amayeretsedwa chifukwa cha mkazi wake, ndiponso mkazi wosakhulupirira amayeretsedwa chifukwa cha m’baleyo, apo ayi, ana anu akanakhala osayera, koma tsopano ndi oyera.” (1 Akor. 7:14) Akhristu ambiri okhulupirika anasankha kuti asapatukane ndi amuna kapena akazi awo ngakhale kuti m’banja mwawo munali mavuto aakulu. Iwo anasangalala kwambiri kuti anachita zimenezi chifukwa zinathandiza kuti mnzawoyo asinthe n’kukhala wa Mboni.—Werengani 1 Akorinto 7:16; 1 Pet. 3:1, 2.
19. N’chifukwa chiyani m’mipingo muli mabanja ambiri osangalala?
19 Yesu anafotokoza mfundo zina zokhudza kuthetsa banja ndipo Paulo anauziridwa kuti alembe malangizo okhudza kupatukana. Onse awiriwa ankafuna kuti atumiki a Mulungu azilemekeza ukwati. M’mipingo yapadziko lonse, muli mabanja ambiri amene akuyenda bwino. N’zosachita kufunsa kuti mumpingo wanunso muli mabanja ambiri osangalala. M’mabanja oterewa muli abale okhulupirika amene amakonda akazi awo komanso akazi achikondi amene amalemekeza amuna awo. Ndipo onsewa amasonyeza kuti amalemekeza ukwati. Timasangalala kwambiri kuti mabanjawa amapereka umboni wakuti zimene Mulungu ananena ndi zoona. Paja ananena kuti: “Pa chifukwa chimenechi, mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.”—Aef. 5:31, 33.
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA