“Tidzaonana M’Paradaiso”
“Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”—LUKA 23:43.
NYIMBO: 145, 139
1, 2. Kodi anthu ena amati paradaiso n’chiyani?
MSONKHANO wina utangotha mumzinda wa Seoul ku Korea, zinali zosangalatsa kuona abale ndi alongo akutsanzikana ndi alendo amene anabwera. Ambiri ankabayibitsana uku akunena kuti: “Tidzaonana m’paradaiso.” Kodi pamenepa ankanena za paradaiso uti?
2 Anthu ambiri amakhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya mawu oti “paradaiso.” Ena amati “paradaiso” ndi zimene anthu amangolakalaka koma kulibe. Enanso amati ndi malo amene angakhaleko mosangalala. Mwachitsanzo, munthu wanjala akapeza chakudya chambirimbiri akhoza kuganiza kuti ali m’paradaiso. Munthu wina wokaona malo ataona maluwa am’tchire okongola kwambiri anafuula kuti, “Eee, uyu ndiye paradaisotu.” Mpaka pano, malo amenewa amadziwika ndi dzina loti Paradaiso ngakhale kuti nthawi zina kumachita sinowo wambiri. Nanga kodi inuyo mumati paradaiso n’chiyani? Kodi mumayembekezera kudzakhala m’paradaiso?
3. Kodi Baibulo limafotokoza bwanji paradaiso?
3 Baibulo limanena za paradaiso wakale komanso amene akubwera. Nkhani ya paradaiso inayamba kufotokozedwa m’buku loyambirira la m’Baibulo. Lemba la Genesis 2:8 la m’Baibulo lina (Catholic Douay Version) limene linamasuliridwa kuchokera ku Chilatini limati: “Ambuye anadzala paradaiso wosangalatsa kuyambira pachiyambi ndipo anaikamo [Adamu] amene anamupanga.” Lembali m’Chiheberi limanena kuti ‘munda wa Edeni.’ Mawu oti Edeni amatanthauza “Chisangalalo” ndipo n’zoona kuti mundawo unali wosangalatsa. M’mundawo munali chakudya cha mwanaalirenji, malo okongola kwambiri komanso nyama zambiri zoti munthu akhoza kusangalala nazo.—Gen. 1:29-31.
4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti munda wa Edeni unali paradaiso?
4 Mawu achigiriki amene anagwiritsidwa ntchito pomasulira mawu achiheberi akuti munda ndi akuti pa·raʹdei·sos. Buku lina lofotokoza zinthu za m’Baibulo lolembedwa ndi M’Clintock komanso Strong limanena za mawu amenewa kuti: “Ndi malo aakulu otetezeka, okongola komanso osawonongedwa. Amakhala ndi mitengo yam’tchire ndipo mitengo yambiri imakhala ya zipatso. Mumakhala mitsinje yabwino ndipo m’mbali mwa mitsinjeyo mumapezeka agwape kapena nkhosa zambiri. Izi n’zimene munthu wachigiriki angaganize akamva za paradaiso.”—Yerekezerani ndi Genesis 2:15, 16.
5, 6. Kodi chinachitika n’chiyani kuti padzikoli pasakhalenso paradaiso, nanga tingadzifunse mafunso ati?
5 Mulungu anaika Adamu ndi Hava m’paradaiso koma sanakhalitsemo. Iwo anathamangitsidwamo chifukwa chosamvera Mulungu. Izi zinachititsa kuti iwo ndi ana awo onse asakhalenso m’paradaiso. (Gen. 3:23, 24) Ngakhale kuti mu Edeni simunkakhala anthu, mundawu unali ulipobe mpaka m’masiku a Nowa, pamene chigumula chinafika.
6 Choncho ena angadzifunse kuti: ‘Kodi zidzatheka kuti anthu ena adzakhale m’paradaiso padzikoli?’ Nanga pali zilizonse zosonyeza kuti kudzakhala paradaiso? Ngati mumayembekezera kudzakhala ndi anzanu m’paradaiso, kodi muli ndi zifukwa zomveka zokhulupirira zimenezi? Kodi mungafotokoze chifukwa chake simukayikira zoti kudzakhaladi paradaiso?
ZIMENE ZIMASONYEZA KUTI KUDZAKHALA PARADAISO
7, 8. (a) Kodi Yehova analonjeza chiyani kwa Abulahamu? (b) Kodi Abulahamu ayenera kuti ankaganizira za chiyani atamva lonjezolo?
7 Kuti tipeze mayankho a mafunso amenewa, tiyenera kufufuza m’buku louziridwa ndi amene anapanga paradaiso woyambirira. Taganizirani zimene Mulungu anauza Abulahamu. Anamuuza kuti adzachulukitsa mbadwa zake mpaka kufika pokhala ngati “mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.” Kenako anamulonjeza kuti: “Kudzera mwa mbewu yako, mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso ndithu chifukwa chakuti wamvera mawu anga.” (Gen. 22:17, 18) Yehova anabwerezanso lonjezoli kwa mwana wa Abulahamu komanso chidzukulu chake.—Werengani Genesis 26:4; 28:14.
8 Palibe umboni uliwonse wosonyeza kuti Abulahamu ankaganiza zoti anthu adzakakhala m’paradaiso wakumwamba. Choncho pamene Mulungu ananena kuti “mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso,” Abulahamu ayenera kuti ankaona kuti madalitsowo ndi a padzikoli. Apa tingati Mulungu analonjeza kuti anthu a “mitundu yonse ya padziko lapansi” zinthu zidzayamba kuwayendera bwino. Kodi pali umboni winanso wotsimikizira zimene tikunenazi?
9, 10. Kodi ndi malonjezo ena ati amene akusonyeza kuti Yehova adzadalitsa anthu m’tsogolomu?
9 Davide, yemwe anali mbadwa ya Abulahamu, ananena kuti idzafika nthawi pamene “anthu ochita zoipa” komanso “ochita zosalungama” adzaphedwa. Apa zikutanthauza kuti ‘oipa sadzakhalakonso.’ (Sal. 37:1, 2, 10) Koma “anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.” Mulungu anathandizanso Davide kulosera kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Sal. 37:11, 29; 2 Sam. 23:2) Kodi mukuganiza kuti malonjezo amenewa anakhudza bwanji anthu amene ankafuna kuchita zimene Mulungu amafuna? Ayenera kuti anaganiza kuti ngati padzikoli padzakhala anthu olungama okhaokha, ndiye kuti moyo udzakhala ngati wa m’munda wa Edeni.
10 Koma patapita zaka, Aisiraeli ambiri amene ankanena kuti amatumikira Yehova anakhala osakhulupirika. Choncho Mulungu analola kuti Ababulo abwere n’kudzawagonjetsa, kuwononga dziko lawo komanso kutenga anthu ambiri kupita nawo ku ukapolo. (2 Mbiri 36:15-21; Yer. 4:22-27) Komabe aneneri a Mulungu analosera kuti pakatha zaka 70, anthuwo adzabwerera kwawo. N’zoona kuti maulosiwa anakwaniritsidwa koma akutikhudzanso ifeyo. Tiyeni tikambirane ena mwa maulosiwa n’kuona kuti akugwirizana bwanji ndi nkhani ya paradaiso padziko lapansi.
11. Kodi lemba la Yesaya 11:6-9 linakwaniritsidwa bwanji, nanga tingafunse funso liti?
11 Werengani Yesaya 11:6-9. Mulungu anagwiritsa ntchito Yesaya polosera kuti anthu ake akadzabwerera kudziko lawo sadzavutika ndi nyengo zoipa, zilombo zolusa kapena anthu oopsa. Aliyense adzakhala wotetezeka, kaya wamkulu kapena wamng’ono. Zimenezitu zikutikumbutsa mmene moyo unalili m’munda wa Edeni. (Yes. 51:3) Ulosi womwewu unanenanso kuti dziko lonse, osati la Isiraeli lokha, “lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.” Kodi zimenezi zidzachitika liti?
12. (a) Kodi anthu ochoka ku Babulo anadalitsidwa bwanji? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti lemba la Yesaya 35:5-10 lidzakwaniritsidwanso m’tsogolo?
12 Werengani Yesaya 35:5-10. Yesaya analoseranso kuti anthu obwerera kwawo sadzaopa zilombo kapena anthu. Dziko lawo lidzabereka zipatso zambiri chifukwa choti mudzakhala madzi okwanira ngati mmene zinalili m’munda wa Edeni. (Gen. 2:10-14; Yer. 31:12) Kodi zonsezi zinakwaniritsidwa mu nthawi ya Aisiraeli? Palibe umboni wakuti anthu amene anachoka ku ukapolo anachiritsidwa mozizwitsa. Mwachitsanzo, akhungu sanayambe kuona. Choncho Mulungu ayenera kuti ankatanthauza kuti zoterezi zidzachitika m’tsogolo.
13, 14. Kodi ulosi wa pa Yesaya 65:21-23 unakwaniritsidwa bwanji, nanga ndi mbali iti imene sinakwaniritsidwebe? (Onani chithunzi choyambirira.)
13 Werengani Yesaya 65:21-23. Ayuda ochoka ku Babulo sanafikire m’nyumba zabwino ndipo sanapeze minda yolimalima ya mpesa ndi mbewu zina. Koma pamene Mulungu ankawadalitsa, zinthu zinkasintha. Iwo anasangalala kumanga nyumba n’kukhalamo komanso kulima minda n’kumadya zokolola zake.
14 Mu ulosi wa Yesayawu muli mfundo ina yofunika kuiganizira kwambiri. Kodi ndi liti pamene masiku a anthufe “adzakhala ngati masiku a mtengo?” Mitengo ina imakhala zaka masauzande angapo. Kuti anthu akhale ndi moyo zaka zonsezi afunika kukhala athanzi. Ndipo zinthu zabwino zonse zimene Yesaya analosera zitati zichitike ndiye kuti paradaiso wafika basi. Komatu ulosi umenewu udzakwaniritsidwa ndithu.
15. Kodi Yesaya anafotokoza madalitso ati?
15 Ganizirani mmene malonjezo amulemba limene tawerengali akusonyezera kuti kudzakhala paradaiso. Anthu padziko lonse adzadalitsidwa ndi Mulungu ndipo sadzaopanso zilombo zolusa kapena anthu oopsa. Anthu osaona, okhala ndi vuto la kumva komanso olumala adzachiritsidwa. Anthu adzamanga nyumba zawo komanso kulima mbewu zomwe zizidzabereka bwino. Azidzakhala ndi moyo masiku ambiri kuposa a mitengo. Baibulo limasonyeza kuti zonsezi zidzachitika m’tsogolomu. Koma ena akhoza kuganiza kuti maulosiwa satanthauza kuti paradaiso adzakhala padzikoli. Kodi inuyo mutamva wina akunena zimenezi mungamuyankhe bwanji? Kodi n’chiyani chimakutsimikizirani kuti paradaiso adzabweradi padzikoli? Yesu anapereka zifukwa zomveka zotichititsa kukhulupirira zimenezi.
UDZAKHALA M’PARADAISO
16, 17. Kodi chinachitika n’chiyani kuti Yesu anene za paradaiso?
16 Ngakhale kuti Yesu sanalakwe chilichonse, anapachikidwa limodzi ndi zigawenga ziwiri. Koma asanafe, chigawenga chimodzi chinavomereza zoti Yesu ndi mfumu ndipo chinapempha kuti: “Yesu, mukandikumbukire mukakalowa mu ufumu wanu.” (Luka 23:39-42) Koma zimene Yesu anayankha munthuyu pa Luka 23:43 zikukhudzanso tsogolo lanu. Akatswiri ena amamasulira lembali kuti: “Ndithu ndikukuuza, lero iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” Mawu amene tikufuna kukambirana kwambiri ndi oti “lero.” Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza chiyani? Anthu amakhala ndi maganizo osiyanasiyana pa mawu amenewa.
17 M’zilankhulo zambiri, anthu amaika chizindikiro chopumira pang’ono pothandiza anthu kuti amvetse tanthauzo la chiganizo. Koma m’mipukutu yoyambirira yachigiriki sankagwiritsa ntchito kwambiri zizindikiro za m’kalembedwe. Ndiye funso n’kumati: Kodi Yesu ananena kuti, “Ndithu ndikukuuza, lero iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso?” Kapena kodi ananena kuti, “Ndithu ndikukuuza lero, iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso?” Omasulira amaika chizindikiro chopumira pamene akufuna malinga ndi mmene akumvera chiganizo. Ndipo kalembedwe kawiri konseka kamapezeka m’Mabaibulo osiyanasiyana.
18, 19. Kodi mungafotokoze bwanji mawu amene Yesu anauza chigawenga chija?
18 Koma tisaiwale kuti izi zisanachitike, Yesu anauza otsatira ake kuti: “Mwana wa munthu adzakhala mumtima wa dziko lapansi masiku atatu, usana ndi usiku.” Anawauzanso kuti: “Mwana wa munthu adzaperekedwa m’manja mwa anthu, ndipo adzamupha. Koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.” (Mat. 12:40; 16:21; 17:22, 23; Maliko 10:34) Mtumwi Petulo anatsimikizira kuti zimenezi zinachitikadi. (Mac. 10:39, 40) Izi zikusonyeza kuti Yesu sanapite kuparadaiso aliyense pa tsiku limene anaphedwa limodzi ndi chigawenga chija. Iye anali m’manda kwa masiku angapo mpaka pamene Mulungu anamuukitsa.—Mac. 2:31, 32. *
19 Malinga ndi zimene takambiranazi, tingaone kuti Yesu anauza chigawenga chija kuti: “Ndithu ndikukuuza lero.” Kalankhulidwe kameneka kanali kofala ngakhale munthawi ya Mose. Paja nayenso ananena kuti: “Mawu awa amene ndikukulamula lero azikhala pamtima pako.”—Deut. 6:6; 7:11; 8:1, 19; 30:15.
20. Perekani maumboni ena otsimikizira kuti zimene tikudziwa pa mawu a Yesu n’zolondola.
20 Munthu wina womasulira Baibulo wa ku Middle East anapereka maganizo ake pa zimene Yesu ananenazi. Iye anati: “Pa lembali, mawu amene anatsindikidwa ndi akuti ‘lero’ ndipo ayenera kulembedwa kuti: ‘Ndithu ndikukuuza lero, iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.’ Lonjezoli linaperekedwa pa tsiku limene Yesu anapachikidwalo koma lidzakwaniritsidwa m’tsogolo. Umu ndi mmene anthu akuderalo ankalankhulira potanthauza kuti lonjezo laperekedwa pa tsiku linalake ndipo lidzakwaniritsidwa ndithu.” N’chifukwa chake Baibulo lina lakale lochokera kudera limene Yesu ankakhala linamasulira vesili kuti: “Ameni, ndikukuuza iwe lero kuti udzakhala nane m’Munda wa Edeni.” Kunena zoona, lonjezo limeneli ndi lolimbikitsa kwa tonsefe.
21. N’chifukwa chiyani tinganene kuti chigawenga chija sichinapite kuparadaiso wakumwamba?
21 Chigawenga chija sichinkadziwa kuti Yesu anachita pangano ndi atumwi ake okhulupirika loti akalamulire naye mu Ufumu wakumwamba. (Luka 22:29) Chigawengacho chinalinso chosabatizidwa n’komwe. (Yoh. 3:3-6, 12) Choncho tingati paradaiso amene Yesu analonjeza ndi wapadzikoli. Patapita zaka zingapo, mtumwi Paulo ananena za masomphenya a munthu amene “anakwatulidwa n’kukalowa m’paradaiso.” (2 Akor. 12:1-4) Mosiyana ndi chigawenga chija, Paulo ndi atumwi ena okhulupirika anasankhidwa kuti akalamulire limodzi ndi Yesu kumwamba. Ngakhale zinali choncho, Paulo ananena za “paradaiso” amene akubwera. * Kodi paradaiso ameneyo adzakhala padzikoli? Nanga inuyo mudzakhalamo?
KODI MUNGAYEMBEKEZERE CHIYANI?
22, 23. Kodi inuyo mungayembekezere chiyani?
22 Kumbukirani kuti Davide analosera kuti “olungama adzalandira dziko lapansi.” (Sal. 37:29; 2 Pet. 3:13) Apa Davide ankanena za nthawi imene anthu onse padzikoli azidzayendera mfundo za Mulungu zachilungamo. Ndipo ulosi wa pa Yesaya 65:22 umanena kuti: “Masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo.” Izi zikutanthauza kuti anthu azidzakhala zaka masauzande. Kodi inuyo mungayembekezeredi zimenezi? Inde, chifukwa malinga ndi lemba la Chivumbulutso 21:1-4, Mulungu adzadalitsa anthu ndipo lonjezo lina ndi lakuti “imfa sidzakhalaponso.”
23 Apa tsopano tingati mfundo yamveka. Adamu ndi Hava anataya mwayi wokhala m’paradaiso mu Edeni koma mwayiwu sunatheretu. Mulungu walonjeza kuti anthu adzadalitsidwanso padzikoli. Davide anauziridwa kulemba kuti ofatsa komanso olungama adzakhala padzikoli kwamuyaya. Ulosi wa Yesaya uyenera kutichititsa mtima dyokodyoko kuti tidzaone madalitso amene Yehova walonjeza. Zonsezi zidzachitika m’paradaiso amene Yesu analonjeza chigawenga chija. Ndipo inunso mukhoza kudzakhala m’paradaisoyu. Pa nthawi imeneyo, mawu oti, “Tidzaonana m’paradaiso,” amene anthu anauza alendo ku Korea aja adzakwaniritsidwa.
^ ndime 18 Pa nkhani imeneyi, pulofesa wina analemba kuti akatswiri ambiri amaganiza kuti pamene Yesu anati “lero” ankatanthauza kuti adzakhala m’paradaiso pa tsiku lomwelo la maola 24. Koma pulofesayu ananenanso kuti: “Kukhala ndi maganizo amenewa pa nkhaniyi kumavuta chifukwa Baibulo limasonyeza kuti Yesu ataphedwa ‘anatsikira’ kaye m’manda (Mat. 12:40; Mac. 2:31; Aroma 10:7) ndipo kenako anapita kumwamba.”
^ ndime 21 Onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” m’magazini yomweyi.
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA