“Ndani Ali Kumbali ya Yehova?”

“Ndani Ali Kumbali ya Yehova?”

‘Muziopa Yehova Mulungu wanu. Muzim’tumikira ndi kum’mamatira.’​—DEUT. 10:20.

NYIMBO: 28, 32

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti ndi nzeru kukhala kumbali ya Yehova? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

YEHOVA MULUNGU wathu ndi wamphamvu, wanzeru komanso wachikondi kuposa aliyense. Choncho n’zomveka kuti timafuna kukhala kumbali yake nthawi zonse. (Sal. 96:4-6) Koma atumiki a Yehova ena amasiya kukhala kumbali yake akapanikizika ndi mavuto enaake.

2 Munkhaniyi tikambirana za anthu ena amene ankanena kuti amalambira Mulungu koma kwinaku n’kumachita zinthu zina zomukhumudwitsa. Nkhani zimenezi zitithandiza kudziwa zoyenera kuchita kuti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova.

YEHOVA AMADZIWA ZIMENE ZILI MUMTIMA

3. N’chifukwa chiyani Yehova analankhula ndi Kaini, nanga anamuuza chiyani?

3 Tiyeni tiyambe ndi kukambirana za Kaini. Iye ankanena kuti amalambira Yehova osati milungu ina. Koma Yehova sankasangalala ndi zimene ankachita pomulambira. Zinali choncho chifukwa chakuti maganizo oipa anayamba kukula mumtima mwake. (1 Yoh. 3:12) Yehova analankhula ndi Kaini n’kumuuza kuti: “Ukasintha n’kuchita chabwino, sindikuyanja kodi? Koma ngati susintha kuti uchite chabwino, uchimo wamyata pakhomo kukudikirira, ndipo ukulakalaka kukudya. Kodi iweyo suugonjetsa?” (Gen. 4:6, 7) Apa tingati Yehova ankauza Kaini kuti: “Tangolapa n’kukhala kumbali yanga ndipo inenso ndikhala kumbali yako.”

4. Kodi Kaini anatani atapatsidwa mwayi woti akhale kumbali ya Yehova?

4 Yehova akanayamba kusangalala ndi Kaini ngati akanamvera n’kusintha maganizo ake. Koma Kaini sanamvere malangizo a Yehova. Maganizo oipa amene anali nawo anakula mpaka anachita zinthu zoipa kwambiri. (Yak. 1:14, 15) N’kutheka kuti kuyambira ali mwana, Kaini sanaganizepo zoti angachite zinthu motsutsana ndi Yehova. Koma patapita nthawi anachita zinthu zimene sankaziganizira n’komwe kuti angazichite. Iye anakana kumvera Yehova ndipo anapha m’bale wake.

5. Kodi ndi mtima wotani umene ungasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova?

5 Mofanana ndi Kaini, masiku anonso Mkhristu akhoza kumanena kuti amalambira Yehova koma kwinaku akuyenda panjira yolakwika. (Yuda 11) Mwachitsanzo, akhoza kukhala ndi mtima wadyera, wolakalaka chiwerewere kapena wokwiyira Mkhristu mnzake. (1 Yoh. 2:15-17; 3:15) Mtima umenewu ukhoza kuchititsa kuti tsiku lina adzachite tchimo. Zimenezi zikhoza kuchitika ngakhale kuti munthuyo amachita bwinobwino zinthu monga kulalikira ndi kupezeka pamisonkhano nthawi zonse. N’zoona kuti anthu ena sangadziwe zimene zili mumtima mwathu koma Yehova amadziwa zonse ndipo sangalephere kudziwa ngati sitili kumbali yake ndi mtima wonse.​—Werengani Yeremiya 17:9, 10.

6. Kodi Yehova amatithandiza bwanji kuti tigonjetse maganizo olakwika?

6 Chosangalatsa n’chakuti Yehova safulumira kutiona kuti ndife okanika. Anthu akayamba kuyenda panjira yolakwika, Yehova amawauza kuti: “Bwererani kwa ine ndipo ine ndibwerera kwa inu.” (Mal. 3:7) Tikakhala ndi vuto linalake, Yehova amafuna kuti tizichita khama poyesetsa kupewa zoipa. (Yes. 55:7) Tikamatero, iye amatithandiza kuti tikhale olimba mwauzimu, tisasokonezeke maganizo komanso tipeze mphamvu zotithandiza kugonjetsa maganizo ofuna kuchita zoipa.​—Gen. 4:7.

“MUSASOCHERETSEDWE”

7. Kodi Solomo anasokoneza bwanji ubwenzi wake ndi Yehova?

7 Pali zinthu zambiri zimene tingaphunzire pa chitsanzo cha Mfumu Solomo. Iye ali wachinyamata ankadalira Yehova kuti amupatse malangizo. Ndipo Yehova anamupatsa nzeru zambiri komanso udindo womanga kachisi waulemerero ku Yerusalemu. Koma Solomo anasokoneza ubwenzi wake ndi Yehova. (1 Maf. 3:12; 11:1, 2) Mulungu anapereka lamulo loletsa mafumu achiheberi kukwatira ‘akazi ambiri kuti mtima wawo ungapatuke.’ (Deut. 17:17) Koma Solomo sanamvere lamuloli moti anakwatira akazi 700 komanso anali ndi akazi ena apambali okwana 300. (1 Maf. 11:3) Ambiri mwa akaziwa sanali Aisiraeli ndipo ankalambira milungu yonyenga. Choncho Solomo sanamverenso lamulo la Mulungu loletsa kukwatira akazi amitundu ina.​—Deut. 7:3, 4.

8. Kodi Solomo anachitanso zinthu ziti zokhumudwitsa Yehova?

8 Solomo ankapatuka pang’onopang’ono panjira ya Yehova ndipo izi zinamuchititsa kuti achite machimo akuluakulu. Iye anamanga guwa la mulungu wonyenga dzina lake Asitoreti komanso la mulungu wina dzina lake Kemosi. Ndipo ankapita kumeneko ndi akazi ake n’kumakalambira milungu yonyengayo. Ndiye tangoganizani, malo amene anamanga maguwa amenewa anali paphiri loyang’anizana ndi Yerusalemu kumene anamanga kachisi wa Yehova. (1 Maf. 11:5-8; 2 Maf. 23:13) N’kutheka kuti Solomo ankadzinamiza kuti Yehova sangakhumudwe ndi kusamvera kwakeko chifukwa ankaperekanso nsembe kukachisi.

9. Kodi kusamvera kwa Solomo kunabweretsa mavuto ati?

9 Koma Yehova salekerera machimo. Baibulo limanena kuti: “Yehova anamukwiyira kwambiri Solomo chifukwa mtima wake unapatuka kwa Yehova . . . , amene anamuonekera kawiri konse. Pa nkhani imeneyi, Mulungu anali atamulamula kuti asatsatire milungu ina, koma iye sanasunge zimene Yehova analamula.” Zochita za Solomo zinachititsa kuti Yehova asiye kumukonda komanso kumuthandiza. Ana ake anataya mwayi wolamulira mtundu wonse wa Isiraeli chifukwa ufumuwo unagawikana ndipo anakumana ndi mavuto ambiri.​—1 Maf. 11:9-13.

10. Kodi n’chiyani chingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova?

10 Mofanana ndi Solomo, ubwenzi wathu ndi Yehova ukhoza kusokonekera mosavuta ngati timacheza kwambiri ndi anthu amene sadziwa kapena kulemekeza mfundo za Yehova. Anthu ena amatha kukhala m’gulu la Yehova koma ali ofooka mwauzimu ndipo angatisokoneze. Tingasokonezedwenso ndi achibale athu, anthu amene timakhala nawo pafupi ndiponso anzathu akuntchito kapena kusukulu omwe salambira Yehova. Mwachidule tingati tikamagwirizana kwambiri ndi munthu aliyense amene salemekeza mfundo za Yehova, pakapita nthawi munthuyo akhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova.

Kodi anthu amene mumacheza nawo sangasokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova? (Onani ndime 11)

11. Kodi tingadziwe bwanji ngati munthu wina ndi woyenera kugwirizana naye kapena ayi?

11 Werengani 1 Akorinto 15:33. Anthu ambiri amakhala ndi makhalidwe abwino ndipo ena amene si a Mboni sachita zinthu zoipa kwambiri. Ngati umu ndi mmene zilili ndi anzanu, kodi zikutanthauza kuti palibe vuto kugwirizana nawo kwambiri? Ndi bwino kudzifunsa kuti, Kodi kugwirizana kwambiri ndi anthu amenewa kungakhudze bwanji ubwenzi wanga ndi Yehova? Kodi ubwenziwo ukula kapena uchepa? Kodi anthuwo ali ndi mtima wotani? Mwachitsanzo, kodi amakonda kulankhula za mafashoni, ndalama, zipangizo zamakono, zosangalatsa kapena zinthu zina zakuthupi? Kodi amakonda kulankhula zonyoza ena kapena zotukwana? Pajatu Yesu ananena kuti: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.” (Mat. 12:34) Ngati mukuona kuti anzanu akhoza kusokoneza ubwenzi wanu ndi Yehova, ndi bwino kuti muchepetse kucheza nawo kapena kungosiyiratu ndipo muchite zimenezo mwamsanga.​—Miy. 13:20.

YEHOVA AMAFUNA KUTI TIKHALE ODZIPEREKA KWA IYE YEKHA

12. (a) Kodi Aisiraeli atangochoka ku Iguputo Yehova anawauza chiyani? (b) Kodi iwo anayankha bwanji atamva zimene Yehova anawauza?

12 Tingaphunzirenso zambiri tikaganizira zimene zinachitika Aisiraeli atangochoka kumene ku Iguputo. Anthu anasonkhana pafupi ndi phiri la Sinai. Pamalo amenewo Yehova anawathandiza kuzindikira kuti iye ndi amene akuwatsogoleradi. Phiri lonse linakutidwa ndi mtambo wakuda ndipo kunayamba kuchita mabingu, mphenzi ndi utsi komanso kunkamveka kulira kwamphamvu kwambiri kwa lipenga. (Eks. 19:16-19) Pa nthawi imeneyi, Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha.” Anawatsimikiziranso kuti iye adzakhala wokhulupirika kwa anthu onse amene amamukonda komanso kusunga malamulo ake. (Werengani Ekisodo 20:1-6.) Apa tingati Yehova ankauza anthu akewo kuti: “Mukakhala kumbali yanga, inenso ndidzakhala kumbali yanu.” Kodi zikanakhala kuti Yehova wakuuzani inuyo zimenezi mukanatani? N’zosachita kufunsa kuti mukanalonjeza kumumvera ngati mmene Aisiraeli anachitira. Paja “onse anayankhira pamodzi kuti: ‘Mawu onse amene Yehova wanena tidzachita.’” (Eks. 24:3) Koma pasanapite nthawi yaitali panachitika zinthu zina zimene zinayesa chikhulupiriro cha Aisiraeliwo.

13. Kodi chikhulupiriro cha Aisiraeli chinayesedwa bwanji?

13 Aisiraeli ataona mtambo wakuda, mphenzi komanso zizindikiro zina zochokera kwa Mulungu anachita mantha kwambiri. Iwo anapempha Mose kuti iye yekha azilankhulana ndi Yehova paphiri la Sinai kenako aziwafotokozera, ndipo Mose anavomera. (Eks. 20:18-21) Ndiyeno Mose anapita pamwamba pa phirilo ndipo anakhala kwa nthawi yaitali. Kodi pamenepa tingati Aisiraeliwo anasowa mtengo wogwira chifukwa choti mtsogoleri wawo wodalirika anali atachoka? Zikuoneka kuti chikhulupiriro cha Aisiraeliwo chinkaoneka cholimba pakakhala Mose. Tikutero chifukwa izi zitachitika iwo anauza Aroni kuti: “Tipangire mulungu woti atitsogolere, chifukwa sitikudziwa zimene zachitikira Mose, amene anatitulutsa m’dziko la Iguputo.”​—Eks. 32:1, 2.

14. Kodi Aisiraeli anali ndi maganizo olakwika ati, nanga Yehova anachita chiyani?

14 Anthuwo ankadziwa kuti kulambira mafano ndi tchimo lalikulu pamaso pa Yehova. (Eks. 20:3-5) Koma pasanapite nthawi yaitali, anayamba kulambira mwana wa ng’ombe wagolide. Ukutu kunali kusamvera, koma Aisiraeliwo ankadzipusitsa n’kumaganiza kuti adakali kumbali ya Yehova. Aroni anafika ponena kuti zimene ankachita polambira mwana wa ng’ombeyo zinali “chikondwerero cha Yehova.” Kodi Yehova anachita chiyani? Zinamupweteka kwambiri poona kuti anthuwo amusiya. Anauza Mose kuti ‘anthuwo achita zinthu zowawonongetsa ndipo apatuka mwamsanga pa njira imene anawalamula kuyendamo.’ Yehova anakwiya kwambiri moti anaganiza zopha Aisiraeli onsewo.​—Eks. 32:5-10.

15, 16. Kodi Mose ndi Aroni anasonyeza bwanji kuti anali kumbali ya Yehova? (Onani chithunzi choyambirira.)

15 Koma kenako Yehova anasintha maganizo ofuna kuwawonongawo. Iye anawachitira chifundo ndipo anapereka mpata woti anthuwo asonyeze kuti ali kumbali yake. (Eks. 32:14) Mose ataona kuti anthuwo akuchita zinthu motayirira, akufuula, kuimba komanso kuvinira fanolo, iye analiperapera. Kenako anawafunsa kuti: “Ndani ali kumbali ya Yehova? Abwere kwa ine.” Nthawi yomweyo Alevi onse “anayamba kusonkhana kwa Mose.”​—Eks. 32:17-20, 26.

16 Ngakhale kuti Aroni anapanga nawo mwana wa ng’ombeyo, analapa n’kupita kumbali ya Yehova limodzi ndi Alevi enawo. Apa tingati anthu amenewa anasonyeza kuti sakugwirizana ndi anthu ochimwawo. Iwo anachita zinthu mwanzeru chifukwa tsiku limeneli anthu masauzande angapo amene analambira fano anaphedwa. Koma anthu amene anali kumbali ya Yehova analonjezedwa kuti adzadalitsidwa.​—Eks. 32:27-29.

17. Kodi zimene Paulo ananena pa nkhani yolambira mwana wa ng’ombe zikutiphunzitsa chiyani?

17 Mtumwi Paulo atafotokoza za nkhani imeneyi ponena kuti: “Tsopano zinthu zimenezi zinakhala zitsanzo kwa ife, kuti ifenso . . . tisapembedze mafano, mmene ena mwa iwo anachitira. [Zitsanzo] zimenezi zinalembedwa kuti zitichenjeze ifeyo amene mapeto a nthawi zino atifikira. N’chifukwa chake amene akuyesa kuti ali chilili asamale kuti asagwe.” (1 Akor. 10:6, 7, 11, 12) Mawu a Paulowa akusonyeza kuti ngakhale anthu amene amalambira Yehova akhoza kuchita zinthu zolakwika. Anthu amene amagonja pa mayesero akhoza kuganiza kuti Yehova akuwakondabe. Koma kungofuna kapena kungonena kuti ndife okhulupirika kwa Yehova sikutanthauza kuti tili naye pa ubwenzi wabwino.​—1 Akor. 10:1-5.

18. Kodi ndi maganizo ati amene angachititse kuti tiyambe kusiya Yehova pang’onopang’ono, nanga zotsatira zake zingakhale zotani?

18 Mofanana ndi Aisiraeli amene anayamba kuda nkhawa Mose atachedwa kuphiri la Sinai, Akhristu masiku ano akhoza kuda nkhawa poganiza kuti tsiku la Yehova komanso dziko latsopano zikuchedwa. Mwina angayambe kuganiza kuti zinthu zimenezi zili kutali kwambiri kapena sizichitika n’komwe. Kupanda kusamala, maganizo amenewa akhoza kuchititsa munthu kuti aziika zinthu zakuthupi pamalo oyamba m’malo mwa zimene Mulungu amafuna. Mapeto ake tikhoza kuchita zinthu zimene poyamba sitinkaganiza n’komwe kuti tingazichite.

19. Kodi sitiyenera kuiwala mfundo iti? Perekani chifukwa.

19 Tisamaiwale kuti Yehova amafuna kuti tizimumvera ndi mtima wonse komanso tizidzipereka kwa iye yekha basi. (Eks. 20:5) Munthu akangosiya Yehova amakhala akuchita zofuna za Satana ndipo zotsatira zake zimakhala zangozi. N’chifukwa chake Paulo ananena kuti: “Sizingatheke kuti muzimwa za m’kapu ya Yehova komanso za m’kapu ya ziwanda. Sizingatheke kuti muzidya ‘patebulo la Yehova’ komanso patebulo la ziwanda.”​—1 Akor. 10:21.

TISASIYE YEHOVA

20. Kodi Yehova angatithandize bwanji ngati tayamba kuyenda panjira yolakwika?

20 Nkhani ya Kaini, Solomo komanso ya Aisiraeli paphiri la Sinai ikufanana pa mfundo imodzi. Onse anali ndi mpata woti ‘alape n’kutembenuka.’ (Mac. 3:19) Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova safulumira kutayiratu munthu amene walakwa. Mwachitsanzo, Yehova anakhululukira Aroni ataona kuti wasintha. Masiku anonso Yehova angatichenjeze pogwiritsa ntchito nkhani za m’Baibulo, za m’mabuku athu kapena malangizo ochokera kwa Mkhristu mnzathu. Tikamamvera machenjezo amenewa Yehova akhoza kutichitira chifundo.

21. Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani tikakumana ndi mayesero?

21 Koma kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova kuli ndi cholinga chake. (2 Akor. 6:1) Kumatipatsa mwayi woti tikane “moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko.” (Werengani Tito 2:11-14.) Popeza tili m’dziko loipali, tizikumanabe ndi zinthu zimene zingayese chikhulupiriro chathu. Tiyeni tiziyesetsa nthawi zonse kuti tizikhala kumbali ya Yehova chifukwa iye ndi ‘Mulungu wathu amene tiyenera kumuopa, kumutumikira ndiponso kum’mamatira.’​—Deut. 10:20.