NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA June 2020

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira August 3-30, 2020.

“Dzina Lanu Liyeretsedwe”

Nkhani yophunzira 23: August 3-9, 2020. Kodi ndi nkhani yofunika iti imene imakhudza anthu komanso angelo? N’chifukwa chiyani ili yofunika, nanga imatikhudza bwanji? Kumvetsa mayankho a mafunso amenewa kungatithandize kuti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova.

“Ndipatseni Mtima Wosagawanika Kuti Ndiope Dzina Lanu”

Nkhani yophunzira 24: August 10-16, 2020. Munkhaniyi tikambirana mawu ena a m’pemphero la Mfumu Davide opezeka pa Salimo 86:11, 12. Kodi kuopa dzina la Yehova kumatanthauza chiyani? N’chifukwa chiyani tiyenera kuopa dzinali? Kodi kuopa Mulungu kungatiteteze bwanji tikamayesedwa kuti tichite zinthu zoipa?

“Inetu Ndidzafunafuna Nkhosa Zanga”

Nkhani yophunzira 25: August 17-23, 2020. Kodi n’chifukwa chiyani anthu ena omwe akhala akutumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri, amafooka kapenanso kusiya kumutumikira? Kodi Mulungu amawaona bwanji anthuwa? Nkhaniyi iyankha mafunso amenewa. Itithandizanso kuona mmene Yehova anathandizira anthu ena akale omwe nthawi ina sanachite zimene anawauza.

“Bwererani Kwa Ine”

Nkhani yophunzira 26: August 24-30, 2020. Yehova akufuna kuti anthu amene anasiya kusonkhana komanso kulalikira abwererenso kwa iye. Yehova akuwauza kuti: “Bwererani kwa ine.” Pali zambiri zomwe tingachite kuti tiwathandize. Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite powathandiza kuti abwerere.