NKHANI YOPHUNZIRA 25

Musamakhumudwitse “Tianati”

Musamakhumudwitse “Tianati”

“Musanyoze mmodzi wa tianati.”​—MAT. 18:10.

NYIMBO NA. 113 Yehova Amatipatsa Mtendere

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi Yehova anachita chiyani ndi aliyense wa ife?

YEHOVA anatikokera tonsefe kwa iye. (Yoh. 6:44) Tangoganizirani zimenezi. Pamene Yehova ankafufuza mitima ya anthu mabiliyoni padzikoli anaona kanthu kena kamtengo wapatali mwa inu. Anaona kuti muli ndi mtima wabwino ndipo mukhoza kumukonda. (1 Mbiri 28:9) Yehova amakudziwani, amakumvetsani komanso amakukondani. Zimenezitu ndi zolimbikitsa kwambiri.

2. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti Yehova amakonda nkhosa yake iliyonse?

2 Yehova amakukondani kwambiri ndipo amakondanso abale ndi alongo anu onse. Pofuna kutithandiza kumvetsa mfundoyi, Yesu anayerekezera Yehova ndi m’busa. Ngati nkhosa imodzi pa nkhosa 100 itasochera, kodi m’busa amachita chiyani? Iye ‘amasiya nkhosa 99 zija m’phiri ndi kupita kukafunafuna yosocherayo.’ Akaipeza, samaikwiyira koma amasangalala. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Nkhosa iliyonse ndi yofunika kwa Yehova. Yesu anati: “Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.”​—Mat. 18:12-14.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Sitingafune kufooketsa kapena kukhumudwitsa abale ndi alongo athu. Ndiye kodi tingatani kuti tisamakhumudwitse ena? Nanga tiyenera kuchita chiyani ngati wina watikhumudwitsa? Munkhaniyi tikambirana mafunso amenewa. Koma choyamba tiyeni tikambirane zokhudza “tianati,” zomwe zafotokozedwa m’chaputala 18 cha buku la Mateyu.

KODI “TIANATI” NDI NDANI?

4. Kodi “tianati” ndi ndani?

4 “Tianati” ndi ophunzira a Yesu a misinkhu yonse. Posatengera msinkhu wawo, iwo ali ngati “ana aang’ono” chifukwa choti amafunitsitsa kuphunzitsidwa ndi Yesu. (Mat. 18:3) Ngakhale kuti amasiyana komwe amachokera, zikhalidwe, mmene amaonera zinthu komanso moyo wawo, onse amakhulupirira Khristu ndipo iye amawakonda kwambiri.​—Mat. 18:6; Yoh. 1:12.

5. Kodi Yehova amamva bwanji wina akakhumudwitsa kapena kuvulaza mtumiki wake?

5 Anthu onse omwe ndi “tianati” ndi amtengo wapatali kwa Yehova. Kuti timvetse mmene iye amawaonera, tiyeni tiganizire mmene ifenso timaonera ana. Timawaona kuti ndi amtengo wapatali. Choncho timafuna kuwateteza chifukwa chakuti alibe mphamvu, sadziwa zinthu zambiri komanso alibe nzeru zimene anthu akuluakulu ali nazo. N’zoona kuti sitifuna kuona aliyense atakhumudwitsidwa kapena atavulazidwa koma zimatikhudza kwambiri ngakhalenso kutikwiyitsa kumene munthu akachitira zimenezi mwana. Mofanana ndi zimenezi, Yehova amafuna kutiteteza ndipo zimamukhudza kwambiri ngakhalenso kumukwiyitsa munthu wina akakhumudwitsa kapena kuvulaza mtumiki wake.​—Yes. 63:9; Maliko 9:42.

6. Mogwirizana ndi 1 Akorinto 1:26-29, kodi dziko limawaona bwanji ophunzira a Yesu?

6 Kodi ophunzira a Yesu ali ngati ‘tiana’ m’njira inanso iti? Kodi dziko limaona kuti anthu ofunika kwambiri ndi ati? Olemera, otchuka komanso amphamvu ndi amene amaonedwa choncho. Koma ophunzira a Yesu amaonedwa ngati osafunika komanso ‘tiana.’ (Werengani 1 Akorinto 1:26-29.) Komatu Yehova sawaona choncho.

7. Kodi Yehova amafuna kuti tiziwaona bwanji abale ndi alongo athu?

7 Yehova amakonda atumiki ake onse kaya akhala akumutumikira kwa zaka zambiri kapena angoyamba kumene choonadi. Abale ndi alongo athu onse ndi ofunika kwa Yehova choncho ayenera kukhalanso ofunika kwa ife. Timafunika ‘kukonda gulu lonse la abale,’ osati ochepa okha. (1 Pet. 2:17) Tiyenera kukhala ofunitsitsa kuchita chilichonse chomwe tingathe kuti tiziwateteza komanso kuwasamalira. Ngati tazindikira kuti takhumudwitsa winawake sitiyenera kuzisiya n’kumaona kuti munthuyo akukokomeza zinthu moti akungofunika kutikhululukira. Koma kodi anthu ena amakhumudwa chifukwa chiyani? Abale ndi alongo ena amadziona kuti ndi osafunika mwina chifukwa cha mmene anakulira. Enanso angoyamba kumene choonadi ndipo sanaphunzire mmene angachitire zinthu akalakwiridwa. Kaya zinthu zili bwanji, tizichita zimene tingathe kuti tikhalenso pamtendere ndi ena. Kuwonjezera pamenepa munthu amene amakonda kukhumudwa ndi zochita za ena, ayenera kuzindikira kuti limeneli si khalidwe labwino ndipo afunika kusintha. Kuchita izi kungawathandize kukhala ndi mtendere wamumtima komanso angamagwirizane ndi ena.

MUZIONA ENA KUKHALA OKUPOSANI

8. Kodi mu nthawi ya Yesu anthu ambiri anali ndi maganizo otani omwenso anakhudza ophunzira ake?

8 Kodi n’chiyani chimene chinachititsa kuti Yesu anene zokhudza ‘tiana’? Ophunzira ake anali atamufunsa kuti: “Ndani kwenikweni amene adzakhala wamkulu kwambiri mu ufumu wakumwamba?” (Mat. 18:1) Pa nthawiyo Ayuda ambiri ankaona kuti kukhala ndi udindo ndi chinthu chofunika kwambiri. Katswiri wina wamaphunziro anati: “Anthu ankaona kuti chinthu chofunika kwambiri ndi kulemekezedwa, kutchuka komanso kuti anthu ambiri aziwakonda.”

9. Kodi ophunzira a Yesu ankayenera kuchita chiyani?

9 Yesu ankadziwa kuti ophunzira ake ayenera kuchita khama kuti achotse maganizo a mpikisano omwe anali ofala pakati pa Ayuda. Iye anawauza kuti: “Amene ali wamkulu kwambiri pa nonsenu akhale ngati wamng’ono kwambiri pa nonsenu, ndipo amene ali mtsogoleri akhale wotumikira.” (Luka 22:26) Munthu amasonyeza kuti ndi “wamng’ono kwambiri” ngati ‘amaona ena kukhala omuposa.’ (Afil. 2:3) Tikamayesetsa kukhala ndi maganizo amenewa, m’pamenenso timapewa kukhumudwitsa ena.

10. Kodi ndi malangizo ati a Paulo amene tiyenera kumakumbukira?

10 Abale ndi alongo athu onse amatiposa pa zinthu zina. Zimenezi zimakhala zosavuta kuvomereza tikamaganizira makhalidwe abwino amene ali nawo. Tiyenera kumakumbukira malangizo amene mtumwi Paulo anapereka kwa Akhristu a ku Korinto akuti: “Kodi akukupangitsa kukhala wosiyana ndi ena ndani? Inde, uli ndi chiyani chimene sunachite kulandira? Ndiye ngati unachita kulandira zinthu zimenezo, n’chifukwa chiyani ukudzitama ngati kuti sunachite kulandira?” (1 Akor. 4:7) Choncho tiyenera kusamala kuti tisayambe kudziona kuti ndife ofunika kwambiri kuposa ena. Mwachitsanzo, ngati m’bale amakamba nkhani mwaluso kapena ngati mlongo savutika kuyambitsa maphunziro a Baibulo, ayenera kuonetsetsa kuti ulemu wonse ukupita kwa Yehova.

MUZIKHULULUKA NDI “MTIMA WONSE”

11. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa fanizo la Yesu la mfumu ndi kapolo wake?

11 Yesu atangochenjeza otsatira ake kuti asamakhumudwitse ena, anafotokoza fanizo lonena za mfumu ndi kapolo wake. Mfumuyo inakhululukira kapoloyo ngongole yaikulu imene sakanatha kubweza. Koma kenako kapolo ameneyu sankafuna kukhululukira kapolo mnzake ngongole imene inali yochepa kwambiri. Pa mapeto pake mfumuyo inamuika m’ndende kapolo wopanda chifundoyo. Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Yesu anati: “Mofanana ndi zimenezi, Atate wanga wakumwamba adzathana ndi inu ngati aliyense wa inu sakhululukira m’bale wake ndi mtima wonse.”​—Mat. 18:21-35.

12. Ngati sitimakhululuka, kodi zingakhudze bwanji anthu ena?

12 Zimene anachita kapoloyo sizinakhudze iye yekha, zinakhudzanso ena. Choyamba iye anachitira nkhanza kapolo mnzake ‘pokam’pereka kundende mpaka pamene adzabweze ngongoleyo.’ Chachiwiri iye anakhumudwitsa akapolo anzake. Iwo “ataona zimene zinachitikazo anamva chisoni kwambiri.” Mofanana ndi zimenezi, zomwe timachita zimakhudzanso anthu ena. Ngati mnzathu watilakwira ndipo ife sitikufuna kumukhululukira, kodi chingachitike n’chiyani? Choyamba akhoza kukhumudwa chifukwa sitinamusonyeze chifundo komanso chikondi. Chachiwiri, tingakhumudwitsenso ena mumpingo ngati atazindikira kuti sitili pamtendere ndi m’bale wathuyo.

Kodi mupitiriza kusunga chakukhosi, kapena mukhululuka ndi mtima wonse? (Onani ndime 13-14) *

13. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira mpainiya wina?

13 Tikakhululukira abale ndi alongo athu timamva bwino ndipo timachititsanso kuti iwowo amve bwino. Zimenezi ndi zomwe zinachitikiranso mlongo wina yemwe tangomutchula kuti Crystal. Iye anakhumudwitsidwa ndi mlongo wina mumpingo ndipo anati: “Mlongoyo ankandilankhula ndi mawu opweteka moti ndinkangomva ngati ndabayidwa ndi mpeni. Sindinkafuna n’komwe kuyenda naye mu utumiki. Zimenezi zinachititsa kuti ndisamachite khama pa ntchito yolalikira komanso ndisamasangalale.” Crystal ankaona kuti ali ndi zifukwa zomveka zomuchititsa kuti akhumudwe. Komabe iye sanapitirize kumusungira chakukhosi mlongoyo kapena kumangoganizirabe za nkhaniyo. M’malomwake, iye anadzichepetsa n’kugwiritsa ntchito malangizo a m’Malemba opezeka munkhani yakuti “Khululukani Kuchokera Mumtima,” yomwe ili mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1999. Choncho iye anamukhululukira mlongoyo ndipo anati: “Tsopano ndazindikira kuti tonsefe tikuyesetsa kuti tivale umunthu watsopano ndipo Yehova amatikhululukira tsiku lililonse. Panopa ndikumva bwino kwambiri mumtima ndipo ndinayambiranso kukhala wosangalala.”

14. Mogwirizana ndi Mateyu 18:21, 22, kodi n’kutheka kuti mtumwi Petulo ankavutika kuchita chiyani, nanga tikuphunzira chiyani pa zimene Yesu anamuyankha?

14 Timadziwa kuti timayenera kukhululukira ena ndipo zimenezi ndi zofunika kwambiri. Komabe nthawi zina zingamativute kuti tichite zimenezi. N’kutheka kuti nayenso mtumwi Petulo ankamva choncho. (Werengani Mateyu 18:21, 22.) Ndiye kodi chingatithandize n’chiyani? Choyamba, muziganizira kwambiri zimene Yehova wakukhululukirani. (Mat. 18:32, 33) Iye amatikhululukira ndi mtima wonse ngakhale kuti sitinali anthu oyenera kukhululukidwa. (Sal. 103:8-10) Ndiye ifenso, “tiyenera kukondana.” Choncho nkhani yokhululukira ena si nkhani yochita kusankha, ndi zomwe timayenera kuchitira abale ndi alongo athu. (1 Yoh. 4:11) Chachiwiri, tiziganizira zimene zimachitika tikakhululukira ena. Tikhoza kuthandiza munthu amene watilakwirayo, kulimbikitsa mgwirizano mumpingo, kuteteza ubwenzi wathu ndi Yehova komanso zingatithandize kuti tizimva bwino mumtima. (2 Akor. 2:7; Akol. 3:14) Ndipo chomaliza, tizipemphera kwa Mulungu yemwe amafuna tizikhululukira ena. Musamalole Satana kusokoneza mtendere umene muli nawo ndi Akhristu anzanu. (Aef. 4:26, 27) Nthawi zonse timafunika kuthandizidwa ndi Yehova kuti tisakodwe mumsampha wa Satana.

MUSALOLE KUTI ZOCHITA ZA ENA ZIKUKHUMUDWITSENI

15. Mogwirizana ndi Akolose 3:13, kodi tingatani ngati takhumudwa ndi zochita za m’bale kapena mlongo?

15 Bwanji ngati Mkhristu mnzanu wachita zinthu zimene zakukhumudwitsani kwambiri? Kodi muyenera kuchita chiyani? Muzichita zonse zimene mungathe kuti mukhale nayenso pamtendere. Muzimuuza Yehova m’pemphero mmene mukumvera. Muzimupempha kuti adalitse munthu amene wakukhumudwitsaniyo komanso akuthandizeni kuona makhalidwe abwino amene munthuyo ali nawo omwe amachititsa Yehova kumukonda. (Luka 6:28) Ngati simungathe kunyalanyaza zimene m’bale wanu wakuchitirani, muziganizira njira yabwino yoti mulankhule naye. (Mat. 5:23, 24; 1 Akor. 13:7) Nthawi zonse ndi bwino kumaganiza kuti m’bale wathuyo sanachite kufuna kuti atikhumudwitse. Mukamakambirana naye muzimuthandiza kuona kuti mukumvetsa kuti sanali ndi zolinga zolakwika. Nanga bwanji ngati sakufuna kuti mukambirane? Baibulo limati “pitirizani kulolerana,” choncho musasiye kumulezera mtima m’bale wanuyo. (Werengani Akolose 3:13.) Koma chofunika kwambiri n’chakuti musamusungire chakukhosi chifukwa zimenezi zingasokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova. Musalole kuti zochita za ena zikukhumudwitseni. Mukamachita zimenezi mudzasonyeza kuti mumakonda kwambiri Yehova kuposa china chilichonse.​—Sal. 119:165.

16. Kodi tonsefe tili ndi udindo wotani?

16 Timaona kuti ndi mwayi wamtengo wapatali kutumikira Yehova mogwirizana monga “gulu” limodzi la nkhosa lotsogoleredwa ndi “m’busa mmodzi.” (Yoh. 10:16) Buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu pa tsamba 165 limati: “Pamene mukusangalala ndi mgwirizano umenewu, muyenera kukumbukiranso kuti muli ndi udindo wothandiza kuti mgwirizanowu usathe.” Choncho ‘tiziyesetsa kuona abale ndi alongo athu mmene Yehova amawaonera.’ Yehova amationa kuti tonsefe ndife ‘tiana’ tamtengo wapatali. Kodi umu ndi mmene inunso mumaonera abale ndi alongo anu? Yehova amaona komanso amayamikira zonse zimene mumachita powathandiza komanso kuwasamalira.​—Mat. 10:42.

17. Kodi ndife otsimikiza mtima kuchita chiyani?

17 Timakonda Akhristu anzathu ndipo ndife ‘otsimikiza mtima kuti tisaikire m’bale wathu chokhumudwitsa kapena chopunthwitsa.’ (Aroma 14:13) Timaona abale ndi alongo athu kukhala otiposa ndipo timafunitsitsa kuwakhululukira ndi mtima wonse. Choncho sitiyenera kulola zochita za ena kutikhumudwitsa. M’malomwake tiyeni ‘tizitsatira zinthu zobweretsa mtendere ndiponso zolimbikitsana.”​—Aroma 14:19.

NYIMBO NA. 130 Muzikhululuka

^ ndime 5 Popeza si ife angwiro, nthawi zina tingalankhule kapena kuchita zinthu zimene zingakhumudwitse abale ndi alongo athu. Ndiye zikatere tiyenera kuchita chiyani? Kodi timayesetsa kuti tikhalenso pamtendere ndi abale athuwo? Nanga kodi timapepesa mofulumira? Kapena kodi timaona kuti ngati akhumudwa ndi vuto lawo osati lathu? Kapenanso bwanji ngati sitichedwa kukhumudwa ndi zimene alankhula kapena kuchita? Kodi timadzikhululukira n’kumanena kuti ndi mmene ndilili basi? Kapena kodi timaona kuti limeneli ndi vuto lathu ndipo tiyenera kusintha?

^ ndime 53 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo wakhumudwa ndi zochita za mlongo wina mumpingo. Atakambirana nkhaniyo kwaokha, akhululukirana ndipo tsopano akulalikira limodzi mosangalala.