MAWU A M’BAIBULO

Kodi Muli ndi Chikhulupiriro?

Kodi Muli ndi Chikhulupiriro?

Kuti tizisangalatsa Yehova, tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro. Komabe Baibulo limanena kuti “si anthu onse amene ali ndi chikhulupiriro.” (2 Ates. 3:2) Polankhula mawu amenewa, mtumwi Paulo ankanena za “anthu oipa kwambiri” omwe ankamuzunza ndipo ankafuna kupulumutsidwa kwa iwo. Koma zimene ananena pa nkhani ya chikhulupiriroyi zimakhudzanso anthu ena. Anthu ena safuna kuvomereza umboni woti kuli Mlengi. (Aroma 1:20) Anthu ena anganene kuti amakhulupirira Mulungu. Koma chikhulupiriro chimenechi si chomwe chimafunika kuti munthu azisangalatsa Yehova.

Tiyenera kukhulupirira kuti Yehova alipo ndiponso kuti amapereka mphoto kwa anthu amene ali ndi chikhulupiriro cholimba. (Aheb. 11:6) Chikhulupiriro ndi khalidwe limene munthu amakhala nalo mothandizidwa ndi mzimu woyera. Choncho kupemphera kwa Yehova, kungamuthandize munthu kuti alandire mzimuwu. (Luka 11:9, 10, 13) Njira inanso yaikulu imene munthu angalandirire mzimu woyera ndi kuwerenga Mawu a Mulungu omwe anawauzira pogwiritsa ntchito mzimuwo. Kenako, tiziganizira mozama zimene tawerenga n’kugwiritsa ntchito zomwe taphunzirazo. Tikamachita zimenezi, mzimu wa Yehova udzatithandiza pa moyo wathu ndipo tidzakhala ndi chikhulupiriro chomwe chimamusangalatsa.