NKHANI YOPHUNZIRA 26

NYIMBO NA. 8 Yehova Ndiye Pothawirapo Pathu

Muzidalira Yehova Yemwe ndi Thanthwe Lanu

Muzidalira Yehova Yemwe ndi Thanthwe Lanu

“Palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.”​—1 SAM. 2:2.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiphunzira za makhalidwe amene amachititsa Yehova kuti akhale thanthwe komanso mmene tingamutsanzirire.

1. Pa Salimo 18:46, kodi Davide anayerekezera Yehova ndi chiyani?

 M’DZIKOLI, mavuto adzidzidzi akhoza kusokoneza kapena kusinthiratu moyo wathu. Koma mtima wathu umakhala m’malo podziwa kuti tili ndi Yehova Mulungu amene angatithandize. Munkhani yapita ija tinakumbutsidwa kuti Yehova ndi Mulungu wamoyo ndipo ndi wokonzeka kutithandiza. Iye akatithandiza zimatitsimikizira kuti “Yehova ndi wamoyo.” (Werengani Salimo 18:46.) Koma atangonena kuti Yehova ndi wamoyo, Davide anatchulanso Mulungu kuti “Thanthwe langa.” N’chifukwa chiyani iye anayerekezera Yehova Mulungu wamoyo ndi thanthwe lomwe ndi lopanda moyo?

2. Kodi tiphunzira chiyani pa zimene Davide ananena kuti Yehova ndi “thanthwe langa”?

2 Munkhaniyi tiona chifukwa chake Yehova amayerekezeredwa ndi thanthwe komanso zimene fanizoli limatiphunzitsa zokhudza iye. Tiphunziranso zimene tingachite kuti tizimudalira monga thanthwe lathu. Pomaliza tiona mmene tingatsanzirire makhalidwe a Yehova.

N’CHIFUKWA CHIYANI YEHOVA AMATCHEDWA THANTHWE?

3. Kodi mawu akuti “thanthwe” amagwiritsidwa ntchito bwanji m’Baibulo? (Onani chithunzi chapachikuto.)

3 Baibulo limayerekezera Yehova ndi “thanthwe” pofuna kutithandiza kumvetsa makhalidwe amene ali nawo. Nthawi zambiri mawuwa amapezeka munkhani zomutamanda zosonyeza kuti palibe wofanana naye. Malo oyamba pamene Yehova amatchulidwa kuti “Thanthwe” ndi pa Deuteronomo 32:4. Komanso popemphera, Hana ananena kuti “palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.” (1 Sam. 2:2) Habakuku anatchulanso Yehova kuti “Thanthwe langa.” (Hab. 1:12) Amene analemba Salimo 73 anatchulanso Mulungu kuti “thanthwe la mtima wanga.” (Sal. 73:26) Ndiponso Yehova mwiniwakeyo anadzitchula kuti thanthwe. (Yes. 44:8) Tiyeni tikambirane makhalidwe atatu amene amachititsa Yehova kuti akhale ngati thanthwe komanso zimene tingachite kuti tizimuona ngati “thanthwe lathu.”​—Deut. 32:31.

Anthu a Mulungu amaona kuti Yehova ndi thanthwe lawo (Onani ndime 3)


4. Kodi Yehova amakhala bwanji malo othawirako? (Salimo 94:22)

4 Yehova ndi malo othawirako. Mofanana ndi thanthwe lalikulu lomwe munthu angabisaleko mphepo yamkuntho, Yehova amatiteteza pa nthawi yomwe tikukumana ndi mavuto. (Werengani Salimo 94:22.) Amatiteteza kuti mavutowo asawononge ubwenzi wathu ndi iye. Amatilonjezanso kuti adzathetsa chilichonse chimene chimatidetsa nkhawa komanso mavuto onse.​—Ezek. 34:25, 26.

5. Kodi tingatani kuti Yehova akhale malo athu othawirako?

5 Njira imodzi imene tingapitire kwa Yehova ngati thanthwe lathu, ndi kupemphera kwa iye. Tikapemphera, Yehova amatipatsa mtendere wake womwe umateteza maganizo ndi mtima wathu. (Afil. 4:6, 7) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi M’bale Artem, yemwe anamangidwa chifukwa cha zimene amakhulupirira. Iye ankafunsidwa mafunso kawirikawiri ndi munthu wankhanza yemwe ankamuopseza komanso kumuchititsa manyazi. Artem anati: “Nthawi zonse akandiitana ndinkada nkhawa. . . . Ndinkapemphera kwa Yehova. Ndinkamupempha kuti andipatse mtendere wa mumtima komanso nzeru. Ngakhale kuti munthuyo ankachita zonsezi, mtima wanga unali m’malo. . . . Chifukwa chakuti Yehova ankandithandiza, zinkakhala ngati ndaima kuseri kwa khoma lamiyala.”

6. N’chifukwa chiyani nthawi zonse tiyenera kudalira Yehova? (Yesaya 26:3, 4)

6 Yehova ndi wodalirika. Mofanana ndi thanthwe lomwe silisunthasuntha, Yehova nthawi zonse amakhala wokonzeka kuti atithandize. Tiyenera kumudalira chifukwa iye ndi “Thanthwe lamuyaya.” (Werengani Yesaya 26:3, 4.) Iye adzakhalapo nthawi zonse kuti akwaniritse malonjezo ake, ayankhe mapemphero athu ndiponso azitithandiza. Tingadalirenso Yehova chifukwa chakuti amakhala wokhulupirika kwa anthu amene amamutumikira. (2 Sam. 22:26) Iye sadzaiwala zimene timachita ndipo adzatipatsa mphoto.​—Aheb. 6:10; 11:6.

7. Kodi chingachitike n’chiyani tikamakhulupirira kwambiri Yehova? (Onaninso chithunzi.)

7 Yehova amakhala Thanthwe lathu tikamamudalira ndi mtima wonse. Timakhulupirira kuti zinthu zimatiyendera bwino tikamamumvera ngakhale pa nthawi yovuta. (Yes. 48:17, 18) Tikamaona akutithandiza m’pamenenso timamukhulupirira kwambiri. Timakhulupirira kuti Yehova yekha ndi amene angatithandize kupirira mavuto ngakhale atakhala aakulu kwambiri. Ngakhale zitakhala kuti palibe aliyense wotithandiza, timazindikira kuti Yehova ndi wodalirika. M’bale Vladimir anati: “Pa nthawi imene ndinatsekeredwa m’ndende m’pamene ndinkaona kuti ubwenzi wanga ndi Yehova ndi wolimba kwambiri. Ndinaphunzira kukhulupirira Yehova chifukwa ndinali ndekhandekha ndipo palibe aliyense amene akanandithandiza.”

Timaona kuti Yehova ndi Thanthwe lathu tikamamudalira ndi mtima wonse (Onani ndime 7)


8. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova sasintha? (b) Kodi kuona kuti Yehova ndi Thanthwe lathu kumatithandiza bwanji? (Salimo 62:6, 7)

8 Yehova sasintha. Mofanana ndi thanthwe lalikulu, Yehova amakhala chimodzimodzi nthawi zonse. Iye sasintha makhalidwe ake komanso cholinga chake. (Mal. 3:6) Adamu ndi Hava atakana kumumvera mu Edeni, Yehova sanasinthe cholinga chake. Mogwirizana ndi zimene Mtumwi Paulo analemba, Yehova “sangadzikane.” (2 Tim. 2:13) Zimenezi zikutanthauza kuti kaya pachitike zotani, kaya anthu ena achite zotani, Yehova sadzasintha makhalidwe ake, cholinga chake komanso mfundo zake. Popeza Yehova sasintha, timadziwa kuti iye adzatithandiza pa nthawi yovuta, komanso adzakwaniritsa malonjezo ake m’tsogolo.​—Werengani Salimo 62:6, 7.

9. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Tatyana?

9 Timaona kuti Yehova ndi Thanthwe lathu tikamaganizira makhalidwe ake komanso cholinga chake. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tisasokonezeke maganizo tikakumana ndi mayesero. (Sal. 16:8) Izi ndi zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Tatyana, yemwe anali pa ukaidi wosachoka pakhomo chifukwa cha zimene amakhulupirira. Iye anati: “Ndinkakhala ndekhandekha. Poyamba zinali zovuta. Ndipo nthawi zambiri ndinkakhumudwa.” Koma ataganizira kugwirizana pakati pa mayesero ake ndi cholinga cha Yehova anatha kupirira ndipo maganizo ake anakhala m’malo. Iye anati: “Kumvetsa chifukwa chake izi zinkachitika kunandithandiza kukumbukira kuti ndikukumana ndi mavutowa chifukwa chotumikira Yehova. Zimenezi zandithandiza kuti ndisamaganizire kwambiri za ineyo.”

10. Kodi tingatani kuti Yehova akhale Thanthwe lathu panopa?

10 M’tsogolomu, tidzakumana ndi mayesero amene adzafuna kuti tizidalira Yehova kuposa kale. Inoyi ndi nthawi yoti tizikhulupirira kwambiri kuti Yehova adzatipatsa chilichonse chimene timafunikira kuti tipitirize kumutumikira mokhulupirika. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiziwerenga nkhani za m’Baibulo komanso zokhudza atumiki a Yehova a masiku ano. Tiziona mmene Mulungu wasonyezera kuti ali ngati thanthwe pothandiza atumiki ake. Tiziganizira mozama nkhani zimenezi. Tikatero tiziona kuti Yehova ndi Thanthwe lathu.

TIZITSANZIRA MAKHALIDWE A YEHOVA

11. N’chifukwa chiyani tiyenera kutsanzira makhalidwe a Yehova? (Onaninso bokosi lakuti “ Zolinga Zimene Achinyamata Angakhale Nazo.”)

11 Takambirana mmene Yehova amasonyezera kuti ali ngati thanthwe. Tsopano tiyeni tikambirane mmene tingatsanzirire makhalidwe ake. Tikamayesetsa kutsanzira makhalidwewa, tidzalimbikitsa kwambiri abale ndi alongo athu. Mwachitsanzo, Yesu anapatsa Simoni dzina lakuti Kefa (limene kumasulira kwake ndi “Petulo”), ndipo limatanthauza “Mwala.” (Yoh. 1:42) Zimenezi zinasonyeza kuti iye adzalimbikitsa anthu ena mumpingo ndiponso kuwathandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Akulu mumpingo amayerekezeredwa ndi “mthunzi wa thanthwe lalikulu.” Mawu amenewa akusonyeza mmene amatetezera anthu mumpingo. (Yes. 32:2) Tonsefe, kaya ndi abale kapena alongo, tikhoza kulimbikitsa anthu mumpingo tikamatsanzira makhalidwe a Yehova.​—Aef. 5:1.

12. Kodi tingatani kuti tikhale malo othawirako a abale ndi alongo athu?

12 Tizikhala malo othawirako. Nthawi zina tingafunike kupereka malo othawirako kwa abale athu ngati kwachitika ngozi zachilengedwe, zipolowe kapena nkhondo. Pamene zinthu zikuipiraipira ‘m’masiku otsirizawa,’ mosakayikira tidzafunika kuthandizana ndi abale ndi alongo athu. (2 Tim. 3:1) Tingafunikenso kulimbikitsa abale athu amene akuda nkhawa komanso kuwathandiza kuti ubwenzi wawo ndi Yehova ukhale wolimba. Njira imodzi imene tingachitire zimenezi ndi kuwalandira bwino pa Nyumba ya Ufumu ndipo zimenezi zingathandize kuti anthu mumpingo azikondana. M’dzikoli, anthu amachitirana nkhanza ndipo izi zimachititsa kuti ena azida nkhawa komanso azimva kuti sakondedwa. Choncho abale ndi alongo akafika pa misonkhano, tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tiwathandize kumva kuti amakondedwa komanso ndi otetezeka.

13. Kodi akulu angatani kuti azikhala malo othawirako pa nthawi ya mavuto? (Onaninso chithunzi.)

13 Akulu akhoza kukhala malo othawirako kwa abale ndi alongo amene akukumana ndi mavuto osiyanasiyana. Pakachitika ngozi zachilengedwe, kapena pakafunika thandizo la kuchipatala la mwamsanga, akulu amayesetsa kuti athandize abale ndi alongo. Iwo amawalimbikitsanso ndi mfundo za m’Baibulo. Abale ndi alongo amamasuka kupita kwa mkulu ngati akudziwa kuti iye ndi wofatsa, woganizira ena komanso amamvetsera. Makhalidwe ngati amenewa amathandiza ena kumva kuti amakondedwa ndipo zimakhala zosavuta kuti iwo atsatire malangizo ochokera m’Baibulo amene mkuluyo angapereke.​—1 Ates. 2:7, 8, 11.

Akulu amakhala malo othawirako, abale ndi alongo akakumana ndi mavuto osiyanasiyana (Onani ndime 13) a


14. Kodi tingatani kuti tikhale anthu odalirika?

14 Tizikhala odalirika. Timafuna kuti anthu ena azitidalira makamaka pa nthawi ya mavuto. (Miy. 17:17) Kodi tingatani kuti tikhale anthu odalirika? Tiyenera kuyesetsa kusonyeza makhalidwe abwino nthawi zonse. Mwachitsanzo, tiziyesetsa kukwaniritsa zimene talonjeza komanso kuyesetsa kusunga nthawi. (Mat. 5:37) Munthu wina akavutika, tiziyesetsanso kumuthandiza. Kuwonjezera pamenepo, tizikwaniritsa ntchito imene tapatsidwa ndiponso tizitsatira malangizo ake.

15. Kodi akulu odalirika amathandiza bwanji mpingo?

15 Akulu odalirika amathandiza kwambiri mpingo. Kodi iwo amachita bwanji zimenezi? Ofalitsa sada nkhawa akadziwa kuti akhoza kulankhula ndi mkulu nthawi ina iliyonse, makamaka woyang’anira kagulu kawo. Ofalitsa amamvanso kuti amakondedwa akadziwa kuti akulu ndi okonzeka kuwathandiza. Ndipo akulu akamapereka malangizo ochokera m’Baibulo komanso mabuku athu osati maganizo awo, abale ndi alongo amawakhulupirira. Abale ndi alongo amakhulupiriranso mkulu amene saulula nkhani zachinsinsi komanso amene amachita zimene walonjeza.

16. Kodi ifeyo komanso anthu ena timapindula bwanji tikamakhala osasintha pochita zinthu zoyenera?

16 Tizikhala osasintha. Tikhoza kukhala chitsanzo chabwino kwa anthu ena ngati sitisintha pochita zoyenera ndiponso kutsatira mfundo za m’Baibulo posankha zochita. Tikamayesetsa kulimbitsa chikhulupiriro chathu komanso kudziwa zinthu zambiri, timakhazikika m’choonadi. Sitivutika kusankha zochita ndipo sititengeka mosavuta ndi ziphunzitso zabodza komanso maganizo a m’dzikoli. (Aef. 4:14; Yak. 1:6-8) Kukhulupirira Yehova komanso malonjezo ake kumatithandiza kuti tisagwedezeke tikamva uthenga woipa. (Sal. 112:7, 8) Tingathenso kuthandiza anthu amene akukumana ndi mayesero.​—1 Ates. 3:2, 3.

17. Kodi akulu amathandiza bwanji anthu ena kuti akhale odekha?

17 Akulu ayenera kukhala osachita zinthu mopitirira malire, oganiza bwino, ochita zinthu mwadongosolo ndiponso ololera. Amuna amenewa amathandiza anthu mumpingo kukhala odekha, komanso kukhulupirira kwambiri Yehova ‘pogwira mwamphamvu mawu okhulupirika.’ (Tito 1:9; 1 Tim. 3:1-3) Chitsanzo cha akulu komanso maulendo awo aubusa, zimathandiza ofalitsa kuti nthawi zonse azipezeka pamisonkhano, azilowa mu utumiki komanso aziphunzira paokha. Abale ndi alongo akakumana ndi mavuto amene akuwadetsa nkhawa, akulu amawalimbikitsa kuti aziganizira kwambiri za Yehova ndiponso zolinga zake.

18. N’chifukwa chiyani tiyenera kutamanda Yehova komanso kuyesetsa kuti tikhale naye pa ubwenzi mpaka kalekale? (Onaninso bokosi lakuti “ Zimene Tingachite Kuti Tikhale pa Ubwenzi ndi Yehova.”)

18 Pambuyo pokambirana makhalidwe a Yehova, tikhoza kulankhula ngati Mfumu Davide amene anati: “Atamandike Yehova, Thanthwe langa.” (Sal. 144:1) Yehova adzapitiriza kukhala Mulungu wodalirika. Pa moyo wathu wonse mpaka titakalamba, tizikhulupirira kuti apitiriza kutithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi. Ndipo tikhoza kunena kuti, “Iye ndi Thanthwe langa.”​—Sal. 92:14, 15.

NYIMBO NA. 150 Bwerani kwa Mulungu Kuti Mupulumuke

a MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo akulankhula momasuka ndi akulu pa Nyumba ya Ufumu.