NKHANI YOPHUNZIRA 24

NYIMBO NA. 24 Bwerani Kuphiri la Yehova

Pitirizani Kukhala Alendo a Yehova Mpaka Kalekale

Pitirizani Kukhala Alendo a Yehova Mpaka Kalekale

“Inu Yehova, ndi ndani amene angakhale mlendo mutenti yanu?”​—SAL. 15:1.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona zimene tingachite kuti tipitirize kukhala anzake a Yehova komanso zimene amayembekezera kuti tizichitira anzake.

1. Kodi lemba la Salimo 15:1-5 lingatithandize bwanji?

 MUNKHANI yapita ija tinaphunzira kuti anthu omwe adzipereka kwa Yehova angathe kukhala alendo mutenti yake yophiphiritsa ngati atamayesetsa kukhala naye pa ubwenzi. Koma kodi tingatani kuti tikhale naye pa ubwenzi? Salimo 15 limafotokoza zambiri pa nkhaniyi. (Werengani Salimo 15:1-5.) Salimoli limafotokoza mfundo zimene zingatithandize kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu.

2. Kodi n’chiyani chomwe mwina chinachititsa Davide kutchula tenti ya Yehova?

2 Salimo 15 limayamba ndi mawu akuti: “Inu Yehova, ndi ndani amene angakhale mlendo mutenti yanu? Ndi ndani amene angakhale m’phiri lanu lopatulika?” (Sal. 15:1) Ponena za “tenti” ya Yehova, Davide ayenera kuti ankaganizira za chihema chomwe kwa kanthawi chinali ku Gibiyoni. Iye anatchulanso za ‘phiri lopatulika’ la Mulungu mwina poganizira za phiri la Ziyoni ku Yerusalemu. Paphirili, lomwe lili makilomita angapo kumwera kwa Gibiyoni, ndi pamene Davide anaikapo tenti yomwe munali likasa la pangano mpaka pa nthawi imene kachisi anamangidwa.​—2 Sam. 6:17.

3. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita chidwi ndi zimene zili mu Salimo 15? (Onaninso chithunzi.)

3 N’zoona kuti Aisiraeli ambiri sankaloledwa kutumikira pachihema ngakhalenso kulowa mkati mwake mmene munkakhala likasa. Komabe atumiki onse okhulupirika a Yehova akanatha kukhala alendo mutenti yake yophiphiritsa poyesetsa kuti akhale anzake. Ndipo izi ndi zomwe tonsefe timafuna. Salimo 15 likutchula makhalidwe amene tiyenera kukhala nawo kuti tikhalebe anzake a Yehova.

Aisiraeli a mu nthawi ya Davide, ankatha kuona m’maganizo mwawo zimene kukhala mlendo mutenti ya Yehova kumatanthauza (Onani ndime 3)


MUZIYENDA MOSALAKWITSA ZINTHU NDIPO MUZICHITA ZABWINO

4. Kodi tikudziwa bwanji kuti kungobatizidwa sikokwanira kuti Yehova azisangalala nafe? (Yesaya 48:1)

4 Lemba la Salimo 15: 2 limanena kuti mnzake wa Mulungu ayenera ‘kuyenda mosalakwitsa zinthu, ndipo amachita zinthu zabwino.’ Mawu akuti ‘kuyenda’ komanso ‘kuchita’ akutanthauza kuchita zinazake mosalekeza. Koma kodi n’zothekadi ‘kuyenda mosalakwitsa zinthu’? Inde. Ngakhale kuti palibe munthu wangwiro, Yehova angatione kuti ndife munthu ‘wosalakwitsa zinthu’ ngati timayesetsa kumumvera. Tikadzipereka n’kubatizidwa timakhala kuti tangoyambapo kuyenda ndi Mulungu. Kumbukirani kuti kale kungokhala Mwisiraeli sikunkapangitsa munthu kukhala mlendo wa Yehova. Panali anthu ena omwe sankachita zinthu ‘kuchokera pansi pa mtima ndipo sankachita zoyenera.’ (Werengani Yesaya 48:1.) Mwisiraeli wokhulupirika ankafunika kuphunzira malamulo a Yehova n’kumawatsatira. Masiku anonso kuti Mulungu azisangalala nafe, pamafunika zambiri kuposa kungobatizidwa n’kumasonkhana ndi mpingo. Timafunika kupitiriza ‘kuchita zinthu zabwino.’ Kodi tingachite bwanji zimenezi?

5. Kodi kumvera Yehova pa zinthu zonse kumaphatikizapo chiyani?

5 Kwa Yehova ‘kuyenda mosalakwitsa zinthu’ komanso ‘kuchita zinthu zabwino,’ kumatanthauza zambiri osati kungopezeka kapena kuchita zambiri pamisonkhano. (1 Sam. 15:22) Tiyenera kuyesetsa kuti tizimvera Mulungu pa chilichonse ngakhale pamene tili kwatokha. (Miy. 3:6; Mlal. 12:13, 14) Ndi bwino kuyesetsa kumvera Yehova ngakhale pa zinthu zooneka ngati zing’onozing’ono. Kuchita zimenezi kumasonyeza kuti timamukonda ndipo iye amasangalala nafe.​—Yoh. 14:23; 1 Yoh. 5:3.

6. Mogwirizana ndi Aheberi 6:10-12, kodi chofunika kwambiri ndi chiyani kuposa zimene takhala tikuchita m’mbuyomu?

6 Yehova amayamikira kwambiri zinthu zabwino zimene tinamuchitira m’mbuyomu. Komabe zimenezo pazokha si zokwanira kuti tipitirize kukhala mutenti ya Yehova. Mfundo imeneyi ikuonekera bwino pa Aheberi 6:10-12. (Werengani.) Yehova samaiwala zimene tinachita m’mbuyomu koma amafuna tizimutumikira ndi mtima wonse “mpaka mapeto.” Iye adzakhala mnzathu mpaka kalekale “tikapanda kutopa.”​—Agal. 6:9.

MUZILANKHULA ZOONA MUMTIMA MWANU

7. Kodi kulankhula zoona mumtima mwathu kumaphatikizapo chiyani?

7 Kuti munthu avomerezedwe kukhala mlendo mutenti ya Yehova ayenera “kulankhula zoona mumtima mwake.” (Sal. 15:2) Apa sikuti akungotanthauza kupewa kunama. Yehova amafuna kuti nthawi zonse tizikhala oona mtima. (Aheb. 13:18) Zimenezi ndi zofunika “chifukwa Yehova amanyansidwa ndi munthu wachiphamaso, koma anthu owongoka mtima amakhala nawo pa ubwenzi wolimba.”​—Miy. 3:32.

8. Kodi ndi khalidwe liti lomwe tiyenera kupewa?

8 Anthu amene ‘amalankhula zoona mumtima mwawo,’ samayerekezera kukhala omvera akakhala pagulu n’kumaphwanya malamulo a Mulungu akakhala kwaokha. (Yes. 29:13) Amapewa kuchita zinthu mwachiphamaso. Munthu wachiphamaso amayamba kukayikira ngati malamulo a Yehova alidi anzeru. (Yak. 1:5-8) Munthu wotereyo samvera Yehova pa zinthu zimene iyeyo amaziona kuti ndi zing’onozing’ono. Akaona kuti sanakumane ndi mavuto chifukwa cha kusamverako, amalimba mtima n’kumapitirizabe kuphwanya malamulo a Mulungu ndipo kulambira kwake kumakhala kwachinyengo. (Mlal. 8:11) Koma ife timafuna kukhala oona mtima pa zinthu zonse.

9. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene zinachitika Yesu atakumana koyamba ndi Natanayeli? (Onaninso chithunzi.)

9 Tingathe kuona ubwino wokhala oona mtima tikaganizira zimene zinachitika Yesu atakumana koyamba ndi Natanayeli. Filipo atamubweretsa Natanayeli kwa Yesu, panachitika chinthu china chochititsa chidwi. Ngakhale kuti Yesu anali asanakumanepo ndi Natanayeli, iye ananena kuti: “Onani Mwisiraeli ndithu, amene mwa iye mulibe chinyengo.” (Yoh. 1:47) Yesu ayenera kuti ankaona kuti ena mwa ophunzira ake anali oona mtima koma anaona kuti Natanayeli anali woona mtima kwambiri. Mofanana ndi tonsefe, Natanayeli sanali wangwiro koma ankayesetsa kupewa chinyengo. Yesu anachita chidwi ndi zimenezi ndipo anayamikira Natanayeli. Zingakhaletu zosangalatsa kwambiri ngati Yesu atamationa choncho.

Filipo anabwera kwa Yesu ndi Natanayeli, amene mwa iye munalibe chinyengo. Kodi ndi mmene ifenso tilili? (Onani ndime 9)


10. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kugwiritsa ntchito molakwika mphatso ya kulankhula? (Yakobo 1:26)

10 Mfundo zambiri za mu Salimo 15 zimakhudza mmene timachitira zinthu ndi anzathu. Salimo 15:3 limanena kuti mlendo mutenti ya Yehova “sanena miseche ndi lilime lake, sachitira mnzake choipa chilichonse, ndipo sanyoza anzake.” Kugwiritsa ntchito mawu athu molakwika kungatilepheretse kukhala alendo m’nyumba ya Yehova.​—Werengani Yakobo 1:26.

11. Kodi miseche n’chiyani, nanga ndi chiyani chimene chimachitikira munthu wamiseche amene sakulapa?

11 Wolemba masalimo anatchulanso zokhudza miseche. Kodi miseche n’chiyani? Mwachidule ndi kunena zinthu zabodza zimene zingawononge mbiri ya munthu wina. Munthu wamiseche yemwe sakulapa amachotsedwa mumpingo.​—Yer. 17:10.

12-13. Kodi ndi pa zochitika ngati ziti pomwe tingachitire anzathu zoipa mosadziwa? (Onaninso chithunzi.)

12 Salimo 15:3 limatikumbutsanso kuti mlendo m’nyumba ya Yehova sachitira anzake zoipa ndipo sanyoza ena. Kodi munthu angachitire bwanji ena zoipa?

13 Tingachitire ena zoipa pofalitsa zinthu zabodza zokhudza iwowo. Mwachitsanzo: (1) mlongo wasiya utumiki wa nthawi zonse, (2) banja lina silikutumikiranso pa Beteli kapena (3) m’bale sakutumikiranso ngati mkulu kapena mtumiki wothandiza. Kodi ndi bwino kungoganiza zimene zachititsa kusinthako n’kumauza ena zimene tikuganizazo? Pakhoza kukhala zifukwa zimene zachititsa zomwe ifeyo sitikuzidziwa. Kumbukirani kuti mlendo mutenti ya Yehova, “sachitira mnzake choipa chilichonse, ndipo sanyoza anzake.”

Miseche ikhoza kuchititsa kuti tifalitse nkhani zoipa zokhudza anthu ena (Onani ndime 12-13)


MUZILEMEKEZA ANTHU AMENE AMAOPA YEHOVA

14. Kodi alendo a Yehova amapewa bwanji “anthu onyansa”?

14 Salimo 14:4 limanena kuti mnzake wa Yehova “sagwirizana ndi munthu aliyense wonyansa.” Kodi tingachite bwanji zimenezi? Popeza si ife angwiro, sitingadziwe ngati munthu ali wonyansa kapena kuti woipa. Chifukwa chiyani tikutero? Mwina mwachibadwa tikhoza kumakonda anthu ena chifukwa cha makhalidwe awo n’kumaipidwa ndi anthu ena. Choncho tiyenera kupewa kugwirizana ndi anthu amene Yehova amawaona kuti ndi “onyansa.” (1 Akor. 5:11) Anthu amenewa akuphatikizapo amene amachita zoipa osalapa, amene amanyoza zimene timakhulupirira kapenanso amene amafuna kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova.​—Miy. 13:20.

15. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza “anthu amene amaopa Yehova”?

15 Lemba la Salimo 15:4 limatilimbikitsa kuti tizilemekeza “anthu amene amaopa Yehova.” Choncho timayesetsa kupeza njira zosonyezera kukoma mtima komanso ulemu kwa anzake a Yehova. (Aroma 12:10) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Njira imodzi imene yatchulidwa pa Salimo 15:4, ndi yakuti munthu amene ndi mlendo mutenti ya Yehova, “sasintha zimene walonjeza ngakhale zinthu zitakhala kuti sizili bwino kwa iye.” Kusakwaniritsa zomwe talonjeza kungapweteke anthu ena. (Mat. 5:37) Mwachitsanzo, Yehova amayembekezera kuti anzake azilemekeza lumbiro la ukwati. Amasangalalanso makolo akamakwaniritsa zomwe alonjeza ana awo. Kukonda Mulungu komanso anzathu, kudzatilimbikitsa kuti tiziyesetsa kukwaniritsa zomwe talonjeza.

16. Kodi tingasonyezenso m’njira iti kuti timalemekeza anzake a Yehova?

16 Njira inanso imene tingasonyezere kuti timalemekeza anzake a Yehova ndi kukhala ochereza komanso opatsa. (Aroma 12:13) Kucheza ndi abale ndi alongo athu kumathandiza kuti tizigwirizana nawo kwambiri komanso tizigwirizana ndi Yehova. Ndipotu tikakhala ochereza, timakhala tikutsanzira Yehova.

TIZIPEWA KUKONDA NDALAMA

17. N’chifukwa chiyani Salimo 15 likutchula nkhani ya ndalama?

17 Baibulo limati mlendo wa Yehova “sakongoza ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja, ndipo salandira chiphuphu kuti akhotetse mlandu wa munthu wosalakwa.” (Sal. 15:5) N’chifukwa chiyani mu Salimoli akutchula ndalama? Chifukwa ngati timakonda kwambiri ndalama, tingayambe kumaona kuti ndi zofunika kwambiri kuposa anthu komanso ubwenzi wathu ndi Yehova. (1 Tim. 6:10) Kale anthu ena ankadyera abale awo osauka masuku pamutu powalipiritsa chiwongola dzanja pa ndalama zimene anawabwereka. Komanso oweruza ena ankalandira ziphuphu ndipo ankaweruza anthu osalakwa mopanda chilungamo. Yehova amadana ndi zinthu ngati zimenezi.​—Ezek. 22:12.

18. Kodi tingadzifunse mafunso ati kuti tidziwe maganizo athu pa nkhani ya ndalama? (Aheberi 13:5)

18 Dzifunseni kuti: ‘Kodi nthawi zonse ndimangoganizira za ndalama komanso zimene ndingagule? Kodi ndikabwereka ndalama, ndimachedwa kubweza poganiza kuti amene wandibwereka ndalamayo sakuzifuna? Kodi kukhala ndi ndalama kumandichititsa kuti ndizidziona ngati wofunika koma n’kumalephera kuthandiza ena? Kodi ndimaona kuti abale ndi alongo ena ndi okonda ndalama chabe chifukwa choti ali ndi ndalamazo? Kodi ndimakonda kucheza ndi anthu olemera n’kumapewa anthu osauka?’ Tili ndi mwayi waukulu wokhala alendo a Yehova, choncho kuti tipitirize kukhala anzake tiyenera kupewa kukonda ndalama. Tikamachita zimenezi Yehova sadzatisiya.​—Werengani Aheberi 13:5.

YEHOVA AMAKONDA ANTHU OMWE NDI ANZAKE

19. N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tizichita zinthu zonse zotchulidwa mu Salimo 15?

19 Salimo 15 limamaliza ndi mawu akuti: “Munthu aliyense amene amachita zimenezi, sadzagwedezeka.” (Sal. 15:5) Apa wolemba masalimoyu ankafotokoza chifukwa chake Yehova amafuna kuti tizichita zonse zimene zatchulidwa mu Salimoli. Iye amafuna kuti tizisangalala. Choncho amatipatsa malangizo omwe amatithandiza kupeza madalitso komanso kukhala otetezeka.​—Yes. 48:17.

20. Kodi alendo a Yehova akuyembekezera chiyani?

20 Alendo a Yehova akuyembekezera zinthu zabwino kwambiri. Odzozedwa ambiri okhulupirika adzalandira “malo ambiri okhalamo” omwe Yesu wawakonzera kumwamba. (Yoh. 14:2) Omwe ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi akuyembekezera kudzaona kukwaniritsidwa kwa malonjezo omwe ali pa Chivumbulutso 21:3. Kunena zoona, timaona kuti ndi mwayi waukulu kukhala anzake a Yehova komanso alendo mutenti yake mpaka kalekale.

NYIMBO NA. 39 Tipange Dzina Labwino Ndi Mulungu