Ali ngati siliva woyengedwa mungʼanjo yadothi nthawi zokwanira 7.
Inu Yehova mudzawayangʼanira.
Aliyense wa iwo mudzamuteteza ku mʼbadwo uwu mpaka kalekale.”
Vesi 5 likufotokoza zimene Mulungu adzachitire anthu “ovutika.” Iye adzawapulumutsa.
Vesi 6 limawonjezera kuti “Mawu a Yehova ndi oyera. Ali ngati siliva woyengedwa.” Izi zikusonyeza mmene Akhristu onse odzipereka amamvera ponena za Mawu a Mulungu.—Sal. 18:30; 119:140.
Tsopano tiyeni tikambirane vesi lotsatira, la Salimo 12:7, lomwe limati: “Inu Yehova mudzawayangʼanira. Aliyense wa iwo mudzamuteteza ku mʼbadwo uwu mpaka kalekale.” Kodi mawu akuti “mudzawayang’anira” akunena za ndani?
Popeza mawu a muvesi 7 akubwera pambuyo pa mawu a muvesi 6 akuti, “mawu a Yehova,” ena angaganize kuti izi zikutanthauza kuti mawu akuti “mudzawayang’anira” akunena za mawu a Mulungu. Tikudziwa kuti iye wakhala akuyang’anira kapena kuti kuteteza Baibulo, ngakhale kuti anthu otsutsa ayesetsa kuliwononga komanso kuletsa kuti lisamapezeke.—Yes. 40:8; 1 Pet. 1:25.
Komabe, zimenenso vesi 5 limafotokoza ndi zoona. Yehova wakhala akuthandiza komanso kupulumutsa “ovutika” ndi “oponderezedwa,” ndipo apitirizabe kuchita zimenezi.—Yobu 36:15; Sal. 6:4; 31:1, 2; 54:7; 145:20.
Ndiye kodi mawu akuti “mudzawayang’anira” a muvesi 7 akutanthauza chiyani?
Nkhani yonse mu Salimoli ikusonyeza kuti mawu akuti “mudzawayang’anira,” akunena za anthu.