NKHANI YOPHUNZIRA 9
NYIMBO NA. 75 “Ine Ndilipo! Nditumizeni!”
Kodi Ndinu Okonzeka Kudzipereka kwa Yehova?
“Yehova ndidzamubwezera chiyani pa zabwino zonse zimene wandichitira?”—SAL. 116:12.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Nkhaniyi itithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso kuti tizifuna kudzipereka kwa iye n’kubatizidwa.
1-2. Kodi munthu ayenera kuchita chiyani asanabatizidwe?
PA ZAKA 5 zapitazi, anthu oposa 1 miliyoni abatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova. Mofanana ndi Timoteyo wa m’nthawi ya atumwi, ambiri mwa anthuwa anaphunzira choonadi kuyambira ali ‘akhanda.’ (2 Tim. 3:14, 15) Ena anaphunzira atakula, ndipo enanso atakalamba. Chaposachedwapa, mayi wina yemwe ankaphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova, anabatizidwa ali ndi zaka 97.
2 Ngati mukuphunzira Baibulo kapena makolo anu ndi a Mboni, n’kutheka kuti mukuganizira zobatizidwa. Chimenechitu ndi cholinga chabwino kwambiri. Komabe musanabatizidwe, muyenera kudzipereka kwa Yehova. Nkhaniyi ifotokoza zimene kudzipereka kumatanthauza. Ikuthandizaninso kuona chifukwa chake simuyenera kuchita mantha kudzipereka ndi kubatizidwa ngati mukuona kuti mwakonzeka kutero.
KODI KUDZIPEREKA N’KUTANI?
3. Perekani zitsanzo za anthu omwe anadzipereka kwa Yehova.
3 Baibulo likamanena za kudzipereka, limanena za munthu yemwe wasankha kuti achite zinazake zopatulika. Aisiraeli anali mtundu wodzipereka kwa Yehova. Koma Aisiraeli ena ankadzipereka kwa Yehova mwapadera. Mwachitsanzo, Aroni ankavala “chizindikiro chopatulika cha kudzipereka,” chomwe chinali kachitsulo konyezimira kagolide komwe kankakhala panduwira yake. Kachitsuloka kankasonyeza kuti iye anapatulidwa kuti azitumikira mwapadera monga mkulu wa ansembe mu Isiraeli. (Lev. 8:9) Nawonso Anaziri ankadzipereka kwa Yehova m’njira yapadera. Mawu akuti “Mnaziri,” omwe amachokera ku mawu a Chiheberi akuti nazirʹ amatanthauza “Wopatulidwa” kapena “Wodzipereka.” Anaziri ankafunika kutsatira malamulo enaake apadera omwe ankapezeka m’Chilamulo cha Mose.—Num. 6:2-8.
4. (a) Kodi munthu yemwe wadzipereka kwa Yehova amasonyeza bwanji kuti wapatulidwa mwapadera? (b) Kodi ‘kudzikana’ kumatanthauza chiyani? (Onaninso chithunzi.)
4 Munthu akadzipereka kwa Yehova, amasankha kukhala wophunzira wa Yesu Khristu ndipo amaona kuti kuchita chifuniro cha Mulungu n’kofunika kwambiri pa moyo wake. Ndiye kodi kudzipereka kumaphatikizapo chiyani? Yesu anati: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha.” (Mat. 16:24) Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “kudzikana wekha” anganenedwenso kuti “kudziletsa kuchita chinachake.” Monga mtumiki wodzipereka wa Yehova, tiyenera kudziletsa kuti tisachite chilichonse chimene Yehova sasangalala nacho. (2 Akor. 5:14, 15) Zimenezi zikuphatikizapo kukana kuchita “ntchito za thupi” monga chiwerewere. (Agal. 5:19-21; 1 Akor. 6:18) Kodi kudziletsa pa zinthu ngati zimenezi kungakhale kovuta? Ayi, makamaka ngati timakonda Yehova ndipo sitikayikira kuti kumvera malamulo ake kumatithandiza kuti zinthu zizitiyendera bwino. (Sal. 119:97; Yes. 48:17, 18) M’bale wina dzina lake Nicholas ananena kuti: “Mukhoza kusankha kuti muziona malamulo a Yehova ngati zitsulo za ndende zomwe zikukulepheretsani kuchita zimene mukufuna kapena ngati zitsulo za kumalo osungira nyama zotchinga kuti mikango isakuvulazeni.”
5. (a) Kodi munthu amadzipereka bwanji kwa Yehova? (b) Kodi kudzipereka n’kosiyana bwanji ndi kubatizidwa? (Onaninso chithunzi.)
5 Kodi munthu amadzipereka bwanji kwa Yehova? Amamulonjeza m’pemphero kuti azilambira iye yekha komanso kuti aziika zimene Yehovayo amafuna pamalo oyamba. Apa amakhala akulonjeza Yehova kuti adzapitiriza kumukonda ndi ‘mtima wake wonse, moyo wake wonse, maganizo ake onse ndi mphamvu zake zonse.’ (Maliko 12:30) Munthu amadzipereka ali kwayekha ndipo imakhala nkhani ya pakati pa iyeyo ndi Yehova. Koma kubatizidwa kumachitika pagulu ndipo kumatsimikizira ena kuti munthuyo anadzipereka. Kudzipereka ndi lonjezo lopatulika ndipo mumafunika kumalikwaniritsa. Nayenso Yehova amayembekezera kuti muzilikwaniritsa.—Mlal. 5:4, 5.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIMAYENERA KUDZIPEREKA KWA YEHOVA?
6. Kodi n’chiyani chimamuchititsa munthu kuti adzipereke kwa Yehova?
6 Chifukwa chachikulu chomwe chimatichititsa kuti tidzipereke kwa Yehova ndi choti timamukonda. Sikuti chikondichi chimangotengera mmene tikumvera. M’malomwake, chimabwera chifukwa ‘chodziwa zinthu molondola’ komanso ‘kumvetsetsa zinthu zauzimu’ zomwe zachititsa kuti muzikonda kwambiri Mulungu. (Akol. 1:9) Kuphunzira Malemba kwakuthandizani kutsimikizira kuti (1) Yehova ndi weniweni, (2) Baibulo ndi Mawu ake ouziridwa, ndiponso (3) iye amagwiritsa ntchito gulu lake pokwaniritsa cholinga chake.
7. Kodi munthu ayenera kumachita chiyani asanadzipereke kwa Mulungu?
7 Anthu amene amadzipereka kwa Yehova amadziwa mfundo zoyambirira zopezeka m’Mawu a Mulungu ndipo amazitsatira pa moyo wawo. Amayesetsa mmene angathere kuuza ena zimene amakhulupirira. (Mat. 28:19, 20) Amakonda kwambiri Yehova ndipo amafunitsitsa kulambira iye yekha. Kodi izi ndi zimene inunso mukuchita? Mukakhala ndi chikondi ngati chimenechi, simudzaona kudzipereka komanso kubatizidwa ngati zinthu zomwe timangochita pofuna kusangalatsa amene amatiphunzitsa Baibulo, makolo athu komanso simudzaziona ngati zimene timangochita potsanzira anzathu.
8. Kodi kuyamikira kungakuthandizeni bwanji kuti mudzipereke kwa Yehova? (Salimo 116:12-14)
8 Zingakhale zosavuta kuti mudzipereke kwa Yehova ngati mumaganizira zinthu zonse zimene wakuchitirani. (Werengani Salimo 116:12-14.) Baibulo limanena kuti Yehova ndi amene amapereka “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.” (Yak. 1:17) Mphatso yaikulu kwambiri imene anatipatsa ndi nsembe ya Mwana wake, Yesu. Tangoganizani, dipo lachititsa kuti zikhale zotheka kuti mukhale pa ubwenzi ndi Yehova. Komanso lathandiza kuti mukhale ndi mwayi wodzakhala ndi moyo mpaka kalekale. (1 Yoh. 4:9, 10, 19) Kudzipereka ndi njira yabwino yosonyezera kuti mukuyamikira chikondi chachikulu chimene Yehova wakusonyezani komanso madalitso onse omwe wakupatsani. (Deut. 16:17; 2 Akor. 5:15) Nkhani yokhudza kuyamikira yafotokozedwa mu phunziro 46, mfundo 4, m’buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, yomwe palinso vidiyo ya 3 minitsi yakuti, Kupereka Mphatso Kwa Mulungu.
KODI NDINU OKONZEKA KUDZIPEREKA KOMANSO KUBATIZIDWA?
9. N’chifukwa chiyani munthu sayenera kudzikakamiza kuti adzipereke kwa Yehova?
9 Mwina mungamaone kuti simunakonzeke kuti mudzipereke komanso kubatizidwa. N’kuthekanso kuti mukufunika kusintha zinthu zina kuti muzitsatira mfundo za Yehova. Kapenanso mukufunika nthawi yambiri kuti mulimbitse chikhulupiriro chanu. (Akol. 2:6, 7) Sikuti ophunzira onse amapita patsogolo mofanana ndiponso ana samakhala okonzeka kudzipereka komanso kubatizidwa pa msinkhu wofanana. Muziyesa kuona mmene mukupitira patsogolo mogwirizana ndi zomwe mungakwanitse ndipo musamadziyerekezere ndi munthu wina.—Agal. 6:4, 5.
10. Kodi muyenera kutani ngati mukuona kuti simunakonzeke kuti mudzipereke komanso kubatizidwa? (Onaninso bokosi lakuti “ Amene Anakulira M’mabanja a Mboni.”)
10 Ngakhale mutaona kuti simunakonzeke kudzipereka kwa Yehova, muzipitirizabe kukhala ndi cholinga chimenechi. Muzimupempha kuti akuthandizeni kukonza zomwe mukufunika kusintha. (Afil. 2:13; 3:16) Dziwani kuti iye adzamva pemphero lanu ndipo adzakuthandizani.—1 Yoh. 5:14.
CHIFUKWA CHAKE ENA AMAZENGEREZA
11. Kodi Yehova angatithandize bwanji kuti tikhalebe okhulupirika kwa iye?
11 Anthu ena ngakhale kuti amakhala atakonzeka, amazengereza kuti adzipereke komanso kubatizidwa. Iwo angamaganize kuti, ‘Bwanji ngati pambuyo pake nditachita tchimo lalikulu n’kuchotsedwa?’ Ngati muli ndi maganizo amenewa, dziwani kuti Yehova adzakupatsani chilichonse chomwe mukufunikira kuti “mukhale ndi khalidwe logwirizana ndi zimene [iye] amafuna, kuti muzimusangalatsa pa chilichonse.” (Akol. 1:10) Iye adzakupatsaninso mphamvu kuti muzichita zoyenera. Yehova wasonyeza kuti angachite zimenezi chifukwa wathandizapo kale anthu ambiri kuti azichita zoyenera. (1 Akor. 10:13) N’chifukwa chake pamakhala anthu ochepa kwambiri omwe amachotsedwa mumpingo. Yehova amathandiza anthu ake kuti akhalebe okhulupirika.
12. Kodi tingatani kuti tipewe kuchita tchimo lalikulu?
12 Munthu aliyense yemwe si wangwiro amayesedwa kuti achite zinthu zoipa. (Yak. 1:14) Komabe, mungathe kusankha zomwe mungachite mukakumana ndi mayesero. Mfundo ndi yakuti inuyo ndi amene muli ndi udindo wosankha zimene mukufuna kuchita pa moyo wanu. Ngakhale kuti ena amatsutsa zimenezi, mungathe kudziphunzitsa kuti musamalakelake zinthu zoipa. Choncho ngakhale mutayamba kulakalaka zinthu zoipa, mungadziletse kuti musazichite. Kuti zimenezi zitheke, muzipemphera tsiku lililonse, muzikhala ndi chizolowezi chophunzira Mawu a Mulungu panokha, muzipezeka pamisonkhano komanso muziuza ena zimene mumakhulupirira. Kuchita zimenezi nthawi zonse kungakuthandizeni kuti muzikwaniritsa lonjezo lanu la kudzipereka. Ndiponso musamaiwale kuti Yehova adzakuthandizani.—Agal. 5:16.
13. Kodi Yosefe anatipatsa chitsanzo chotani?
13 Zingakhale zosavuta kuti mukwaniritse kudzipereka kwanu ngati mutasankhiratu zimene mungachite mutakumana ndi mayesero. Baibulo limatifotokozera za anthu angapo omwe anachita zimenezi, ngakhale kuti nawonso sanali angwiro. Mwachitsanzo, mkazi wa Potifara anayesa mobwerezabwereza kumukopa Yosefe. Koma iye ankadziwa kale zoyenera kuchita. Baibulo limatiuza kuti iye ‘anakana,’ ndipo anati: “Ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi nʼkuchimwira Mulungu?” (Gen. 39:8-10) Apa n’zoonekeratu kuti Yosefe ankadziwa zimene angachite mkaziyo asanayambe n’komwe kumukopa. Zimenezi zinamuthandiza kuti achite zoyenera atakumana ndi mayeserowo.
14. Kodi tingatani kuti tizitha kukana kuchita zoipa?
14 Kodi mungatani kuti mukhalebe okhulupirika ngati Yosefe? Muzisankhiratu panopa zimene mungachite mutakumana ndi mayesero. Muziphunzira kukana mwamsanga zinthu zimene Yehova amadana nazo ndipo musamaziganizire n’komwe. (Sal. 97:10; 119:165) Zimenezi zidzakuthandizani kuti musachite tchimo chifukwa mudzakhala mukudziwa kale zoyenera kuchita.
15. Kodi munthu angasonyeze bwanji kuti “amamufunafuna [Yehova] ndi mtima wonse?” (Aheberi 11:6)
15 N’kutheka kuti inuyo mumadziwa kuti munapeza choonadi ndipo mukufuna kutumikira Yehova ndi mtima wanu wonse koma mukuzengereza kuti mudzipereke komanso kubatizidwa. Ngati ndi choncho, mungachite zimene Mfumu Davide anachita. Mungapemphe Yehova kuti: “Ndifufuzeni inu Mulungu, ndipo mudziwe mtima wanga. Ndifufuzeni ndipo mudziwe maganizo anga amene akundidetsa nkhawa. Muone ngati mwa ine muli chilichonse choipa, ndipo munditsogolere mʼnjira yamuyaya.” (Sal. 139:23, 24) Yehova amadalitsa anthu omwe “amamufunafuna ndi mtima wonse.” Mukamayesetsa kuti mukwaniritse cholinga chanu choti mudzipereke ndiponso kubatizidwa, mumasonyeza kuti mumamufunafuna ndi mtima wonse.—Werengani Aheberi 11:6.
PITIRIZANI KUYANDIKIRA YEHOVA
16-17. Kodi Yehova amakoka bwanji anthu omwe anakulira m’mabanja a Mboni? (Yohane 6:44)
16 Yesu ananena kuti ophunzira ake amakokedwa ndi Yehova. (Werengani Yohane 6:44.) Mfundoyitu ndi yochititsa chidwi ndipo taganizirani mmene imakukhudzirani. Yehova amaona kenakake kabwino mwa munthu aliyense amene amamukoka. Iye amaona munthuyo monga “chuma chake chapadera.” (Deut. 7:6) Umu ndi mmene amakuoneraninso inuyo.
17 Mwina ndinu mwana ndipo makolo anu ndi a Mboni. Ndiye n’kutheka kuti mungamaone kuti mukutumikira Yehova chifukwa makolo anu ndi a Mboni osati chifukwa choti iye wakukokani. Komabe Baibulo limanena kuti: “Yandikirani Mulungu ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yak. 4:8; 1 Mbiri 28:9) Choncho inuyo mukayambapo kumuyandikira Yehova, nayenso amakuyandikirani. Sikuti Yehova amangokuonani monga munthu amene ali m’gulu lake koma iye amakoka munthu aliyense payekha kuphatikizapo amene anakulira m’banja la Mboni. Munthu ameneyu akayamba kuyandikira Yehova, nayenso amamuyandikira monga mmene taonera pa Yakobo 4:8.—Yerekezerani ndi 2 Atesalonika 2:13.
18. Kodi tidzakambirana chiyani mu nkhani yotsatira? (Salimo 40:8)
18 Mukadzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa mumakhala mukutsanzira Yesu. Iye anadzipereka mofunitsitsa kwa Atate wake kuti azichita zilizonse zomwe amuuza. (Werengani Salimo 40:8; Aheb. 10:7) Mu nkhani yotsatira tidzakambirana zimene zingakuthandizeni kuti muzitumikirabe Yehova mokhulupirika mukabatizidwa.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
-
Kodi kudzipereka kwa Yehova kumatanthauza chiyani?
-
Kodi kuyamikira kungakuthandizeni bwanji kuti mudzipereke kwa Yehova?
-
Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muzipewa kuchita tchimo?
NYIMBO NA. 38 Mulungu Adzakulimbitsa
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA