NKHANI YOPHUNZIRA 13
NYIMBO NA. 127 Mtundu wa Munthu Amene Ndiyenera Kukhala
Musamakayikire Kuti Yehova Amasangalala Nanu
“Umandisangalatsa kwambiri.”—LUKA 3:22.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tiona zimene tingachite kuti tisamakayikire kuti Yehova amasangalala nafe.
1. Kodi atumiki ena okhulupirika a Yehova amavutika ndi maganizo ati?
N’ZOLIMBIKITSA kudziwa kuti Yehova amasangalala ndi anthu ake onse monga gulu. Baibulo limati: “Yehova amasangalala ndi anthu ake.” (Sal. 149:4) Komabe nthawi zina ena angamakayikire n’kumadzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova amasangalala ndi ineyo pandekha?’ Ambiri mwa atumiki okhulupirika a Yehova akale nthawi zinanso ankavutika ndi maganizo ngati amenewa.—1 Sam. 1:6-10; Yobu 29:2, 4; Sal. 51:11.
2. Kodi ndi anthu ati amene Yehova amasangalala nawo?
2 Baibulo limasonyeza kuti anthu omwe si angwiro akhoza kusangalatsa Yehova. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyenera kukhulupirira Yesu Khristu komanso kubatizidwa. (Yoh. 3:16) Tikatero timasonyeza poyera kuti talapa machimo athu ndipo talonjeza kuti tizichita zimene Mulungu amafuna. (Mac. 2:38; 3:19) Yehova amasangalala akaona tikuchita zimenezi n’cholinga choti tikhale naye pa ubwenzi. Iye amasangalala nafe n’kumationa ngati anzake apamtima tikamapitiriza kuchita zimene tingathe pokwaniritsa zimene tinalonjeza podzipereka.—Sal. 25:14.
3. Kodi tsopano tikambirana za chiyani?
3 N’chifukwa chiyani nthawi zina ena angamamve ngati Mulungu sasangalala nawo? Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amasangalala nafe? Nanga kodi Mkhristu angatani kuti asamakayikire kuti Mulungu amasangalala naye?
N’CHIFUKWA CHIYANI ENA AMAGANIZA KUTI YEHOVA SASANGALALA NAWO?
4-5. Ngakhale nthawi zina titadziona ngati achabechabe, kodi tingakhale otsimikiza za chiyani?
4 Ambiri a ife takhala tikuvutika ndi maganizo odziona ngati achabechabe kuyambira tili ana. (Sal. 88:15) M’bale wina dzina lake Adrián ananena kuti: “Nthawi zonse ndinkadziona ngati wachabechabe. Ndinkapemphera kuti banja lathu lidzalowe m’dziko latsopano, ngakhale kuti ineyo sindinkaona kuti ndine woyenera kukalowa m’dzikolo.” Tony, yemwe sanakulire m’banja la Mboni ananena kuti: “Makolo anga sanandiuzepo kuti amandikonda kapena kundinyadira. Zimenezi zinkandichititsa kuti ndiziona kuti palibe chomwe ndingachite kuti ndiziwasangalatsa.”
5 Ngati ifenso nthawi zina timavutika ndi maganizo odziona ngati achabechabe, tizikumbukira kuti Yehova ndi amene anatikoka. (Yoh. 6:44) Iye amaona zabwino mwa ife zimene eni akefe sitiziona ndiponso amadziwa mtima wathu. (1 Sam. 16:7; 2 Mbiri 6:30) Choncho tisamakayikire akamatiuza kuti ndife amtengo wapatali.—1 Yoh. 3:19, 20.
6. Kodi mtumwi Paulo ankamva bwanji chifukwa cha machimo amene anachita m’mbuyomo?
6 Tisanaphunzire choonadi, ambirife tinkachita zinthu zimene timadziimba nazo mlandu mpaka pano. (1 Pet. 4:3) Ngakhale Akhristu okhulupirika amalimbanabe ndi mtima wofuna kuchita zoipa. Kodi inuyo mumadziimbanso mlandu? Ngati ndi choncho, dziwani kuti atumiki a Yehova okhulupirika ambiri akhala akudziimba mlandu. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo ankadzimvera chisoni akaganizira zomwe ankalakwitsa. (Aroma 7:24) N’zoona kuti Paulo analapa machimo ake n’kubatizidwa. Komabe iye anadzitchula kuti “ndine wamng’ono kwambiri pa atumwi onse” komanso “wochimwa kwambiri.”—1 Akor. 15:9; 1 Tim. 1:15.
7. Kodi tizikumbukira chiyani pa nkhani ya zomwe tinalakwitsa m’mbuyo?
7 Atate wathu wakumwamba amatilonjeza kuti azitikhululukira tikalapa. (Sal. 86:5) Choncho tikamadzimvera chisoni chifukwa cha machimo amene tinachita tisamakayikire zimene Yehova wanena kuti watikhululukira.—Akol. 2:13.
8-9. Kodi tingathetse bwanji maganizo oona kuti palibe chimene tingachite kuti tisangalatse Yehova?
8 Tonsefe timafuna kuti tizitumikira Yehova mmene tingathere. Komabe, ena akhoza kumaona kuti palibe chomwe angachite kuti Mulungu azisangalala nawo. Mlongo wina dzina lake Amanda ananena kuti: “Nthawi zambiri ndimaganiza kuti kuchita zonse zomwe tingathe potumikira Yehova kumatanthauza kuti nthawi zonse ndizichita zambiri. Choncho ndinkayesetsa kuti ndizichita zambiri kuposa zimene ndingakwanitse. Koma ndikalephera ndinkakhumudwa ndipo ndinkaganiza kuti nayenso Yehova wakhumudwa nane.”
9 Ndiye kodi tingatani kuti tithetse maganizo omaona kuti palibe chomwe tingachite kuti tisangalatse Yehova? Tizikumbukira kuti Yehova amatimvetsa ndipo ndi wololera. Iye samayembekezera kuti tichita zimene sitingakwanitse. Ndipo amayamikira zilizonse zimene timayesetsa kuchita. Komanso muziganizira zitsanzo za m’Baibulo za anthu amene anatumikira Yehova ndi mtima wawo wonse. Mwachitsanzo, taganizirani za Paulo. Iye anagwira ntchito mwakhama kwa zaka zambiri, kuyenda maulendo ataliatali komanso kuyambitsa mipingo yambiri. Koma pamene zinthu zinasintha pa moyo wake n’kumalephera kuchita zambiri pa ntchito yolalikira, kodi Mulungu sankasangalala naye? Ayi. Iye anapitiriza kuchita zimene akanakwanitsa ndipo Mulungu anamudalitsa. (Mac. 28:30, 31) Mofanana ndi zimenezi, nthawi zina zimene timachita potumikira Yehova zikhoza kusintha. Koma chofunika kwambiri kwa iye ndi cholinga chimene tikuchitira zinthuzo. Tsopano tiyeni tikambirane njira zina zimene Yehova amasonyezera kuti amasangalala nafe.
KODI YEHOVA AMATISONYEZA BWANJI KUTI AMASANGALALA NAFE?
10. Kodi ‘tingamve’ bwanji Yehova akutiuza kuti amasangalala nafe? (Yohane 16:27)
10 Kudzera m’Baibulo. Yehova amafunitsitsa kuuza anthu omwe amawakonda kuti amasangalala nawo. Malemba amatchula nthawi ziwiri pomwe iye anauza Yesu kuti ndi Mwana wake wokondedwa ndipo amasangalala naye. (Mat. 3:17; 17:5) Kodi mungakonde kumva Yehova akukutsimikizirani kuti amasangalala nanu? Iye salankhula nafe mwachindunji koma amatilankhula kudzera m’Mawu ake. ‘Tingamve’ mawu a Yehova onena kuti amasangalala nafe tikamawerenga mawu a Yesu m’mabuku a Uthenga Wabwino. (Werengani Yohane 16:27.) Yesu ankatsanzira ndendende makhalidwe a Atate wake. Choncho tikamawerenga kuti Yesu ankasangalala ndi otsatira ake okhulupirika, omwe sanali angwiro, timadziwa kuti Yehova amasangalalanso ndi ifeyo.—Yoh. 15:9, 15.
11. Kodi tikamakumana ndi mavuto ndiye kuti Yehova sakusangalala nafe? (Yakobo 1:12)
11 Kudzera m’zochita zake. Yehova amafunitsitsa kutithandiza. Mwachitsanzo, amatipatsa zimene timafunikira. Nthawi zina amalola kuti tikumane ndi mavuto, ngati mmene anachitira ndi Yobu yemwe anali wolungama. (Yobu 1:8-11) Tikakumana ndi mavuto sizitanthauza kuti Mulungu sakusangalala nafe. M’malomwake, zimenezi zimatipatsa mwayi wosonyeza kuti timakonda kwambiri Mulungu ndipo timamukhulupirira. (Werengani Yakobo 1:12.) Timaona kuti iye amatisamalira mwachikondi akamatithandiza kupirira.
12. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene zinachitikira Dmitrii?
12 Taganizirani zimene zinachitikira m’bale wina wa ku Asia dzina lake Dmitrii. Ntchito yake inatha ndipo anakhala miyezi yambiri asanapeze ina. Dmitrii anaganiza zochita zambiri pa ntchito yolalikira, zomwe zinasonyeza kuti amadalira Yehova. Miyezi yambiri inadutsa koma sankapezabe ntchito. Kenako anayamba kudwala kwambiri moti ankangokhala chigonere. Iye anayamba kukayikira ngati anali mwamuna komanso bambo wabwino ndiponso ngati Yehova ankasangalalabe naye. Ndiyeno madzulo a tsiku lina, mwana wake wamkazi analemba papepala mawu opezeka pa Yesaya 30:15, akuti: “Mudzakhala amphamvu mukakhala odekha komanso mukasonyeza kuti mukundidalira.” Anabweretsa pepalalo pamene anagonapo n’kunena kuti, “Adadi, mukayamba kuona kuti simukumva bwino, muzikumbukira lemba limeneli.” Dmitrii anazindikira kuti Yehova ankathandiza banja lake kupeza chakudya, zovala komanso malo okhala. Iye anati: “Zomwe ndinkafunikira kuchita ndi kukhala wodekha komanso kupitiriza kudalira Mulungu wanga.” Ngati inunso mukukumana ndi mayesero ngati amenewa musamakayikire kuti Yehova amakukondani ndipo adzakuthandizani kupirira.
13. Kodi Yehova angagwiritse ntchito ndani pofuna kutisonyeza kuti akusangalala nafe, nanga angachite bwanji zimenezi?
13 Kudzera mwa Akhristu anzathu. Yehova amagwiritsa ntchito abale ndi alongo athu pofuna kutisonyeza kuti amasangalala nafe. Mwachitsanzo, angachititse ena kuti alankhule mawu otilimbikitsa pa nthawi yoyenera. Izi ndi zimene zinachitikira mlongo wina wa ku Asia yemwe ankada nkhawa kwambiri. Ntchito inali itamuthera ndiponso anayamba kudwala kwambiri. Kenako mwamuna wake anachita tchimo lalikulu n’kuchotsedwa pa udindo monga mkulu. Mlongoyu anati: “Sindinkamvetsa chifukwa chake zonsezi zinkachitika. Ndinkaganiza kuti mwina ndachita chinachake cholakwika ndipo Yehova sakusangalala nane.” Mlongo wathuyu anapempha Yehova kuti amutsimikizire kuti akusangalala naye. Kodi Yehova anamutsimikizira bwanji? Iye anati: “Akulu analankhula nane ndipo ananditsimikizira kuti Yehova amandikonda.” Patapita nthawi anapemphanso Yehova kuti amuthandize. Mlongoyu anati: “Tsiku lomwelo ndinalandira kalata yochokera kwa abale ndi alongo mumpingo. Pamene ndinkawerenga mawu awo olimbikitsa, ndinaona kuti Yehova wayankha pemphero langa.” Nthawi zonse Yehova amasonyeza kuti amasangalala nafe kudzera m’mawu olimbikitsa omwe ena angatiuze.—Sal. 10:17.
14. Kodi ndi njira ina iti yomwe Yehova amasonyezera kuti akusangalala nafe?
14 Yehova amasonyezanso kuti amasangalala nafe pogwiritsa ntchito Akhristu anzathu kuti atipatse malangizo ngati pakufunika kutero. Mwachitsanzo, m’nthawi ya atumwi, iye anagwiritsa ntchito mtumwi Paulo kuti alembere Akhristu anzake makalata 14. M’makalatawo munali malangizo amphamvu koma achikondi. N’chifukwa chiyani Yehova anauzira Paulo kuti alembe malangizowa? Yehova ndi Bambo wachikondi ndipo amalangiza ana ake “omwe amasangalala nawo.” (Miy. 3:11, 12) Choncho tikalandira malangizo a m’Baibulo, tiziona kuti umenewo ndi umboni wosonyeza kuti Mulungu akusangalala nafe. (Aheb. 12:6) Kodi ndi zinthu zinanso ziti zomwe zimasonyeza kuti Yehova akusangalala nafe?
UMBONI WINA WOSONYEZA KUTI MULUNGU AMASANGALALA NAFE
15. Kodi Yehova amapereka mzimu woyera kwa ndani, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi zili zolimbikitsa?
15 Yehova amapereka mzimu woyera kwa anthu omwe amasangalala nawo. (Mat. 12:18) Choncho tizidzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndakhala ndikusonyeza makhalidwe omwe mzimu wa Mulungu umatithandiza kukhala nawo?’ Kodi panopa mukuona kuti ndinu woleza mtima kwambiri mukayerekezera ndi mmene munalili musanaphunzire za Yehova? Zoona n’zakuti mukamasonyeza kwambiri makhalidwe amene mzimu woyera wakuthandizani kukhala nawo, m’pamenenso mumaona umboni wambiri wosonyeza kuti Mulungu akusangalala nanu.—Onani bokosi lakuti “ Makhalidwe Amene Anthu Amakhala Nawo Mothandizidwa ndi Mzimu Woyera.”
16. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito ndani kuti alalikire uthenga wabwino, nanga inuyo mumamva bwanji chifukwa cha zimenezi? (1 Atesalonika 2:4)
16 Yehova anapereka ntchito yolalikira uthenga wabwino kwa anthu amene amasangalala nawo. (Werengani 1 Atesalonika 2:4.) Taonani mmene mlongo wina dzina lake Jocelyn anapindulira chifukwa cholalikira uthenga wabwino. Tsiku lina iye anadzuka ali ndi nkhawa. Jocelyn anati: “Ndinalibiretu mphamvu moti ndinkangodziona ngati wachabechabe. Koma ndinkachita upainiya ndipo tsikuli linali loti ndilowe mu utumiki. Choncho ndinapemphera ndipo ndinalowa mu utumiki.” Tsiku limenelo Jocelyn anakumana ndi mayi wokoma mtima dzina lake Mary, yemwe anavomera kuphunzira Baibulo. Patapita miyezi ingapo, Mary anafotokozera Jocelyn kuti pamene ankagogoda pachitseko, iye anali akupemphera kwa Mulungu kuti amuthandize. Poganizira zimene zinachitikazi, Jocelyn anati: “Ndinamva ngati Yehova akundiuza kuti, ‘Ndimasangalala nawe.’” N’zoona kuti si anthu onse omwe angamvetsere tikamalalikira. Koma tisamakayikire kuti Yehova amasangalala tikamayesetsa kuuza anthu ena uthenga wabwino.
17. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Vicky’ ananena zokhudza dipo? (Salimo 5:12)
17 Yehova amagwiritsa ntchito dipo kuti lithandize anthu amene amasangalala nawo. (1 Tim. 2:5, 6) Koma bwanji ngati mtima wathu umatsutsabe zoti Yehova amasangalala nafe ngakhale kuti timakhulupirira dipo ndiponso tinabatizidwa? Kumbukirani kuti mtima wathu sitingaukhulupirire nthawi zonse koma tingakhulupirire Yehova. Iye amaona kuti anthu amene amakhulupirira dipo ndi olungama ndipo amawalonjeza kuti adzawadalitsa. (Werengani Salimo 5:12; Aroma 3:26) Kuganizira kwambiri za dipo kunathandiza Vicky. Tsiku lina ataganizira kwambiri za dipo, ananena kuti: “Yehova wakhala akuleza nane mtima kwa nthawi yaitali, koma zinali ngati ndikumuuza kuti, ‘Inuyo simungakonde munthu ngati ineyo. Nsembe ya Mwana wanu siingaphimbe machimo anga.’” Ataganizira kwambiri za mphatso ya dipo anayamba kumva kuti Yehova amamukonda. Ifenso tikamaganizira kwambiri za dipo tidzayamba kumva kuti Yehova amatikonda.
18. Ngati tikupitiriza kukonda Atate wathu wakumwamba, sitiyenera kukayikira za chiyani?
18 Ngakhale titayesetsa kutsatira mfundo zimene takambiranazi, nthawi zina tikhoza kukhumudwa n’kumakayikira ngati Yehova akusangalala nafe. Zikatero muzikumbukira kuti iye amasangalala ndi anthu “amene akupitiriza kumukonda.” (Yak. 1:12) Choncho pitirizani kukhala pa ubwenzi ndi Yehova komanso kuona njira zimene amasonyezera kuti akusangalala nanu. Nthawi zonse musamaiwale kuti Yehova “sali kutali ndi aliyense wa ife.”—Mac. 17:27.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
-
N’chifukwa chiyani ena amaganiza kuti Yehova sakusangalala nawo?
-
Kodi ndi njira zina ziti zimene Yehova amasonyezera kuti akusangalala nafe?
-
N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti Yehova amasangalala nafe?
NYIMBO NA. 88 Ndidziwitseni Njira Zanu
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA