NKHANI YOPHUNZIRA 20

NYIMBO NA. 67 “Lalikira Mawu”

Chikondi Chizikulimbikitsani Kuti Mupitirize Kulalikira

Chikondi Chizikulimbikitsani Kuti Mupitirize Kulalikira

“Choyamba uthenga wabwino ukuyenera kulalikidwa kwa anthu amitundu yonse.”​—MALIKO 13:10.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona mmene chikondi chingatithandizire kuti tizilalikira mwakhama komanso ndi mtima wonse.

1. Kodi tinaphunzira chiyani pa msonkhano wapachaka wa mu 2023?

 PA MSONKHANO wa pachaka wa 2023, a panafotokozedwa zinthu zina zomwe zasintha pa mfundo zimene tinkakhulupirira komanso panali zilengezo zosangalatsa zokhudza ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, tinaphunzira kuti anthu ena angadzakhale ndi mwayi wokhala kumbali ya anthu a Yehova ngakhale pambuyo poti Babulo Wamkulu wawonongedwa. Tinauzidwanso kuti kuyambira November 2023, ofalitsa sazidzafunikiranso kuchitira lipoti zonse zimene achita mu utumiki. Kodi kusinthaku kukutanthauza kuti ntchito yolalikira si yofunikanso kwenikweni? Ayi, si choncho.

2. N’chifukwa chiyani tiyenera kugwira mwachangu ntchito yathu yolalikira? (Maliko 13:10)

2 Tsiku lililonse likamadutsa, nthawi yoti tilalikire imakhala ikuchepa kwambiri. Tikutero chifukwa choti nthawi yoti mapeto afike, imakhala ikuyandikira. Taganizirani zimene Yesu ananeneratu zokhudza ntchito yolalikira m’masiku otsiriza. (Werengani Maliko 13:10.) Mogwirizananso ndi zimene Mateyu analemba, Yesu ananena kuti uthenga wabwino udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, “mapeto” asanafike. (Mat. 24:14) Mawu amenewa, akunena za mapeto a dziko loipa la Satanali. Yehova wakhazikitsa ‘tsiku ndi ola’ lomwe zimenezi zichitike. (Mat. 24:36; 25:13; Mac. 1:7) Tsiku lililonse likamadutsa timakhala tikuyandikira ku nthawi imeneyi. (Aroma 13:11) Choncho, panopa tiyenera kupitirizabe kulalikira mpaka mapeto afike.

3. N’chiyani chimatilimbikitsa kuti tizilalikira?

3 Tikamaganizira za utumiki wathu, tingachite bwino kudzifunsa funso lofunika ili: N’chifukwa chiyani timalalikira uthenga wabwino? Mwachidule, chikondi ndi chomwe chimatilimbikitsa kuti tizilalikira. Tikamagwira ntchito yolalikira timasonyeza kuti timakonda uthenga wabwino, timakonda anthu ndipo koposa zonse, timakonda Yehova ndi dzina lake. Tiyeni tikambirane zinthu zimenezi chilichonse pachokha.

TIMALALIKIRA CHIFUKWA TIMAKONDA UTHENGA WABWINO

4. Kodi timamva bwanji tikalandira uthenga wabwino?

4 Kodi mumakumbukira mmene munamvera mutalandira uthenga wabwino, mwina wokhudza kubadwa kwa mwana kapenanso wokudziwitsani kuti mwalembedwa ntchito yomwe munkaifuna kwambiri? Mosakayikira munkafunitsitsa kuuza uthenga wabwinowu achibale anu komanso anzanu. Kodi ndi mmenenso munamvera mutamva uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, womwe ndi uthenga wabwino kwambiri kuposa uliwonse?

5. Kodi munamva bwanji mutamva koyamba uthenga wa choonadi chochokera m’Mawu a Mulungu? (Onaninso zithunzi.)

5 Taganizirani mmene munamvera mutamva koyamba choonadi cha m’Mawu a Mulungu. Munaphunzira kuti Atate wanu wakumwamba amakukondani, amafuna kuti mukhale m’banja lake la anthu omwe amamulambira, adzathetsa mavuto ndi zopweteka zonse, mukhoza kukhala ndi chiyembekezo chodzaonananso ndi okondedwa anu omwe anamwalira ndi zinanso zambiri. (Maliko 10:29, 30; Yoh. 5:28, 29; Aroma 8:38, 39; Chiv. 21:3, 4) Mfundo za choonadi zomwe munaphunzirazi zinakufikani pamtima. (Luka 24:32) Munkakonda kwambiri zimene munkaphunzirazo moti munkafunitsitsa kuuza aliyense.​—Yerekezerani ndi Yeremiya 20:9.

Titamva koyamba uthenga wabwino, tinkafunitsitsa kuuza aliyense choonadi chamtengo wapatali chomwe taphunzira (Onani ndime 5)


6. Kodi tikuphunzira chiyani pa zomwe zinachitikira Ernest ndi Rose?

6 Taganizirani zimene zinachitikira m’bale wina dzina lake Ernest. b Iye ali ndi zaka pafupifupi 10, bambo ake anamwalira. Ernest anati: “Ndinkadzifunsa kuti: ‘Kodi iwo apita kumwamba? Kodi sindidzawaonanso mpaka kalekale?’ Ndinkasirira ana ena omwe anali ndi bambo awo.” Nthawi zambiri Ernest ankapita kukagwada pamanda a bambo akewo n’kupemphera kuti: “Chonde Mulungu, ndikufuna kudziwa kumene kuli bambo anga.” Patapita zaka pafupifupi 17 kuchokera pamene bambo ake anamwalira, munthu wina anamupempha kuti aziphunzira naye Baibulo ndipo iye anavomera. Iye anasangalala kudziwa kuti akufa samadziwa kalikonse, ngati kuti ali mtulo tofa nato ndipo Baibulo limalonjeza kuti Mulungu adzawaukitsa. (Mlal. 9:5, 10; Mac. 24:15) Pamapeto pake, anapeza mayankho a mafunso omwe anamuvutitsa kwa zaka zambiri. Ernest ankasangalala ndi mfundo za choonadi zomwe ankaphunzira. Nayenso mkazi wake Rose anayamba kuphunzira ndipo ankakonda kuuza ena zomwe ankaphunzirazo. Iwo anabatizidwa mu 1978 ndipo ankalalikira mwakhama choonadi chamtengo wapatali kwa achibale awo, anzawo komanso ena onse omwe ankafuna kumvetsera. Zotsatira zake n’zakuti Ernest ndi Rose athandiza anthu oposa 70 kudziwa Yehova mpaka kufika pobatizidwa.

7. Kodi chimachitika n’chiyani tikamakonda ndi mtima wonse choonadi chopezeka m’Baibulo? (Luka 6:45)

7 Kunena zoona, tikamakonda mfundo za m’Baibulo ndi mtima wonse, timafunitsitsa kuuza aliyense zomwe taphunzira. (Werengani Luka 6:45.) Timamva ngati ophunzira a Yesu, omwe anati: “Sitingasiye kulankhula za zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.” (Mac. 4:20) Timakonda kwambiri choonadi moti timafunitsitsa kuuza ena za choonadicho mmene tingathere.

TIMALALIKIRA CHIFUKWA TIMAKONDA ANTHU

8. Kodi n’chiyani chimatilimbikitsa kuti tiziuza ena uthenga wabwino? (Onani bokosi lakuti  Muzikonda Anthu​—Muziwaphunzitsa.”) (Onaninso chithunzi.)

8 Mofanana ndi Yehova ndi Mwana wake, nafenso timakonda anthu. (Miy. 8:31; Yoh. 3:16) Timamvera chisoni anthu omwe “sadziwa Mulungu” ndiponso “alibe chiyembekezo.” (Aef. 2:12) Iwo akukumana ndi mavuto ambiri ndipo zimakhala ngati ali m’dzenje lakuya. Koma ife tili ndi chingwe chomwe tingawaponyere kuti tiwatulutsemo, chomwe ndi uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Chifukwa chakuti timawakonda komanso kuwamvera chisoni, timayesetsa kuti tiwauze uthenga wabwinowu. Uthengawu umawapatsa chiyembekezo, kuwathandiza kuti akhale ndi moyo wabwino panopa komanso umawapatsa chiyembekezo chodzapeza “moyo weniweniwo,” umene ndi moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu.​—1 Tim. 6:19.

Kukonda komanso kuchitira chifundo anthu kumatilimbikitsa kuti tiziyesetsa mmene tingathere kuti tiwauze uthenga wabwino (Onani ndime 8)


9. Kodi timachenjeza ena kuti m’tsogolomu muchitika chiyani, nanga n’chifukwa chiyani? (Ezekieli 33:7, 8)

9 Kukonda anthu kumatichititsanso kuti tiziwachenjeza kuti mapeto a dziko loipali ali pafupi. (Werengani Ezekieli 33:7, 8.) Timamvera chisoni anthu, kuphatikizapo achibale athu omwe satumikira Mulungu. Anthu ambiri amangochita zinthu zawo zatsiku ndi tsiku, osadziwa kuti kutsogoloku kukubwera “chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pachiyambi cha dziko mpaka lero, ndipo sichidzachitikanso.” (Mat. 24:21) Timafuna kuti iwo adziwe zimene zichitike pa nthawi yachiweruzo, pamene choyamba zipembedzo zonse zabodza zidzachotsedwa ndipo kenako maboma onse adzawonongedwa pa nkhondo ya Aramagedo. (Chiv. 16:14, 16; 17:16, 17; 19:11, 19, 20) Timapemphera kuti anthu ambiri amve uthenga wathu wochenjezawu n’kusankha kumatumikira Yehova panopa. Koma bwanji za anthu amene sakufuna kumvera chenjezoli panopa, kuphatikizapo achibale athu omwe timawakonda?

10. N’chifukwa chiyani n’zofunika kwambiri kuti tipitirizebe kuchenjeza anthu?

10 Monga tinaonera munkhani yapita ija, n’kutheka kuti Yehova angadzapulumutse anthu omwe adzasinthe maganizo awo pambuyo poona kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu. Ngati ndi choncho, ndiye kuti n’zofunika kwambiri kuti panopa tipitirize kuwachenjeza. Ganizirani izi: Zimene tingawauze panopa, angadzazikumbukire pa nthawiyo. (Yerekezerani ndi Ezekieli 33:33.) Mwina angadzakumbukire zimene tinawauza n’kusankha kuyamba kutumikira Mulungu nthawi isanathe. Mofanana ndi woyang’anira ndende wa ku Filipi, yemwe anasintha maganizo pambuyo pa “chivomerezi champhamvu,” n’kutheka kuti ena omwe panopa samvetsera uthenga wathu, angadzasinthe maganizo awo pambuyo poona zomwe zidzachitike Babulo Wamkulu akamadzawonongedwa.​—Mac. 16:25-34.

TIMALALIKIRA CHIFUKWA TIMAKONDA YEHOVA NDI DZINA LAKE

11. Kodi timapatsa bwanji Yehova ulemerero, ulemu ndi mphamvu? (Chivumbulutso 4:11) (Onaninso Zithunzi.)

11 Chifukwa chachikulu chomwe timalalikirira uthenga wabwino n’chakuti timakonda Yehova Mulungu komanso dzina lake loyera. Timaona kuti kulalikira ndi njira yotamandira Mulungu wathu yemwe timamukonda. (Werengani Chivumbulutso 4:11.) Timagwirizana ndi zimene angelo ananena, kuti Yehova Mulungu ndi woyenera kulandira ulemerero, ulemu ndi mphamvu kuchokera kwa atumiki ake omwe amamulambira mokhulupirika. Timamupatsa ulemerero ndi ulemu tikamauza ena umboni wosatsutsika wakuti iye ndi “amene analenga zinthu zonse” komanso kuti tili ndi moyo chifukwa cha iye. Timamupatsa mphamvu zathu tikamagwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso zinthu zathu polalikira mmene tingathere mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wathu. (Mat. 6:33; Luka 13:24; Akol. 3:23) Mwachidule, timakonda kuuza ena za Mulungu wathu yemwe timamukonda. Timalimbikitsidwanso kuuza ena za dzina lake komanso zimene limatanthauza. Chifukwa chiyani?

Timapatsa Yehova mphamvu zathu tikamagwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso zinthu zathu polalikira mmene tingathere mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wathu (Onani ndime 11)


12. Kodi timayeretsa bwanji dzina la Yehova tikamalalikira?

12 Kukonda Yehova kumatilimbikitsanso kuti tiziyeretsa dzina lake. (Mat. 6:9) Zimenezi zikutanthauza kuti timafunitsitsa kuuza ena kuti zinthu zoipa zomwe Satana amanena zokhudza Yehova si zoona. (Gen. 3:1-5; Yobu 2:4; Yoh. 8:44) Tikamalalikira, timafunitsitsa kuuza anthu onse omwe angamvetsere zoona zenizeni zokhudza Yehova. Timafuna kuti aliyense adziwe kuti khalidwe lake lalikulu ndi chikondi, amalamulira mwachilungamo ndiponso kuti posachedwapa Ufumu wake uthetsa mavuto onse n’kubweretsa mtendere ndi chimwemwe kwa anthu. (Sal. 37:10, 11, 29; 1 Yoh. 4:8) Tikamauza anthu zinthu ngati zimenezi zokhudza Yehova, timakhala tikuyeretsa dzina lake. Timasangalalanso chifukwa timadziwa kuti tikuchita zinthu mogwirizana ndi dzina lathu. N’chifukwa chiyani tikutero?

13. N’chifukwa chiyani timasangalala kudziwika kuti ndife a Mboni za Yehova? (Yesaya 43:10-12)

13 Yehova watisankha kuti tikhale “mboni” zake. (Werengani Yesaya 43:10-12.) Zaka zingapo zapitazo, kalata ina yochokera ku Bungwe Lolamulira inati: “Mwayi waukulu womwe aliyense angakhale nawo ndi wodziwika monga wa Mboni za Yehova.” c N’chifukwa chiyani zili choncho? Taganizirani chitsanzo ichi. Ngati mutafuna kuti munthu wina akakhale mboni pa mlandu wanu kukhoti, mumasankha munthu yemwe mukumudziwa komanso kumukhulupirira, yemwe mbiri yake ingachititse kuti umboni wakewo ena aukhulupirire. Choncho potisankha kuti tikhale Mboni zake, zikusonyeza kuti Yehova amatidziwa bwino komanso kutikhulupirira kuti tingauze ena kuti iye yekha ndi amene ali Mulungu woona. Timaona kuti ndi mwayi wamtengo wapatali kukhala Mboni zake, ndipo timafuna kugwiritsa ntchito mpata uliwonse pothandiza ena kuti adziwe dzina lake komanso kutsutsa mabodza ambirimbiri omwe amanenedwa okhudza iye. Tikamachita zimenezi, timakhala tikuchita zinthu mogwirizana ndi dzina lathu, lakuti Mboni za Yehova.​—Sal. 83:18; Aroma 10:13-15.

TIPITIRIZABE KULALIKIRA MPAKA MAPETO

14. Kodi ndi zinthu zosangalatsa ziti zomwe tikuyembekezera m’tsogolomu?

14 Tikuyembekezeratu zinthu zosangalatsa kwambiri patsogolopa. Ndi Madalitso a Yehova, tikuyembekezera kuona anthu ambiri akuphunzira choonadi chisautso chisanayambe. Tasangalalanso kudziwa kuti ngakhale pa nthawi yovuta kwambiri ya chisautso chachikulu tingadzaone anthu ambiri akuchoka m’dziko loipa la Satanali n’kuyamba kutamanda nafe limodzi Yehova.​—Mac. 13:48.

15-16. Kodi tipitiriza kuchita chiyani ndipo mpaka liti?

15 Padakali pano tili ndi ntchito yambiri yoti tigwire. Tili ndi mwayi wogwira nawo ntchito yomwe sidzachitikanso yolengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse. Pa nthawi imodzimodziyo tiyenera kupitiriza kuchenjeza anthu zomwe zichitike. Anthu akufunika adziwe kuti mapeto a dziko loipali ali pafupi kwambiri. Ndiyeno nthawi ya chiweruzo ikadzafika, iwo adzadziwa kuti uthenga umene tinkalalikira unali wochokera kwa Yehova Mulungu.​—Eze. 38:23.

16 Ndiye kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani? Chifukwa chokonda uthenga wabwino, anthu komanso koposa zonse kukonda Yehova Mulungu ndi dzina lake, tipitiriza kulalikira mofunitsitsa, mwachangu komanso mwakhama mpaka Yehova atanena kuti “Basi mwamaliza!”

NYIMBO NA. 54 “Njira Ndi Iyi”

a Msonkhano wapachaka unachitika pa 7 October 2023, m’Nyumba ya Msonkhano ku Newburgh ku New York m’dziko la United States. Pambuyo pake mbali yoyamba ya pulogalamuyi inaonetsedwa pa JW Broadcasting mu November 2023 ndipo mbali yachiwiri inaonetsedwa mu pulogalamu ya January 2024.

b Onani nkhani yakuti “Baibulo Limasintha Anthu​—Ndinapeza Mayankho Ogwira Mtima a Mafunso Anga,” mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2015.