NKHANI YOPHUNZIRA 19
NYIMBO NA. 22 Ufumu Umene Ukulamulira Ubwere
Kodi Tikudziwa Chiyani pa Nkhani ya Mmene Yehova Adzaweruzire Anthu?
“Yehova sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe.”—2 PET. 3:9.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Nkhaniyi itithandiza kuti tizikhulupirira kuti Yehova adzaweruza anthu mwachilungamo.
1. N’chifukwa chiyani tinganene kuti panopa tikukhala mu nthawi yosangalatsa?
TIKUKHALA mu nthawi yosangalatsa kwambiri. Tsiku lililonse timaona maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa. Mwachitsanzo, tikuona “mfumu yakumpoto” ndi “mfumu yakum’mwera” akukangana polimbirana ulamuliro. (Dan. 11:40) Tikuonanso uthenga wabwino ukulalikidwa padziko lonse ndipo anthu mamiliyoni akusankha kutumikira Mulungu. (Yes. 60:22; Mat. 24:14) Timalandiranso chakudya chauzimu chochuluka “pa nthawi yoyenera.”—Mat. 24:45-47.
2. Kodi tingakhale otsimikiza za chiyani, nanga tiyenera kuzindikira chiyani?
2 Yehova akupitiriza kutithandiza kuti timvetse bwino zinthu zofunika zomwe zichitike posachedwapa. (Miy. 4:18; Dan. 2:28) Sitikukayikira kuti pamene chisautso chachikulu chizidzayamba, tidzakhala tikudziwa zonse zofunikira kuti tikhalebe okhulupirika pa nthawi yovutayi. Komabe tiyenera kuzindikira kuti pali zinthu zina zokhudza m’tsogolo zomwe sitikudziwa. Mu nkhaniyi, choyamba tikambirana chifukwa chake tasintha mmene tinkafotokozera zina mwa zinthu zimenezi. Kenako tikambirana zimene tikudziwa zokhudza zina mwa zinthu zomwe zichitike m’tsogolo komanso mmene Atate wathu wakumwamba adzachitire zinthu.
ZIMENE SITIKUDZIWA
3. Kodi poyamba tinkanena kuti Yehova adzasiya liti kupereka mwayi kwa anthu kuti akhale kumbali yake, nanga n’chifukwa chiyani tinkanena zimenezo?
3 Poyamba tinkafotokoza kuti chisautso chachikulu chikadzangoyamba, anthu sadzakhalanso ndi mwayi woti ayambe kukhulupirira Yehova kuti adzapulumuke pa Aramagedo. Tinkafotokoza zimenezi chifukwa tinkaganiza kuti chilichonse chokhudza Chigumula chinkaimira zinazake mu nthawi yathu. Mwachitsanzo, tinkaganiza kuti monga mmene Yehova anatsekera chitseko cha chingalawa Chigumula chisanayambe, pa chisautso chachikulu adzatsekanso chitseko kapena kuti sadzalola kuti aliyense wa m’dziko la Satanali ayambe kumutumikira.—Mat. 24:37-39.
4. Kodi panopa timaona kuti nkhani ya Chigumula imaimira zinazake? Fotokozani.
4 Kodi tiziona kuti chilichonse chomwe chinachitika mu nthawi ya Chigumula chinkaimira zinazake? Yankho ndi lakuti ayi. Chifukwa chiyani? Chifukwa palibe Malemba amene amafotokoza zimenezi. a N’zoona kuti Yesu anayerekezera “masiku a Nowa” ndi zochitika za m’masiku otsiriza. Koma sanasonyeze kuti chilichonse chomwe chinachitika mu nthawi ya Nowa, monga kutsekedwa kwa chitseko cha chingalawa, kunali ndi tanthauzo linalake. Komabe izi sizikutanthauza kuti sitingaphunzirepo kanthu pa nkhani ya Chigumula cha m’nthawi ya Nowa.
5. (a) Kodi Nowa anachita chiyani Chigumula chisanachitike? (Aheberi 11:7; 1 Petulo 3:20) (b) Pa nkhani ya ntchito yolalikira, kodi zochitika m’masiku athu ano zikufanana bwanji ndi m’nthawi ya Nowa?
5 Nowa atamva uthenga wochenjeza wa Yehova, anasonyeza chikhulupiriro pokhoma chingalawa. (Werengani Aheberi 11:7; 1 Petulo 3:20.) Mofanana ndi zimenezi, anthu omwe akumva uthenga wabwino wa Ufumu ayenera kumatsatira zimene akuphunzira. (Mac. 3:17-20) Petulo ananena kuti Nowa “ankalalikira za chilungamo cha Mulungu.” (2 Pet. 2:5) Komabe monga mmene taonera mu nkhani yapita ija, sitikudziwa ngati iye anayesetsa kulalikira kwa munthu aliyense padziko lapansi Chigumula chisanachitike. Masiku anonso timagwira nawo mwakhama ntchito yolalikira yomwe ikuchitika padziko lonse. Komabe, ngakhale titayesetsa bwanji, sitingathe kuuza munthu aliyense uthenga wabwino mapeto asanafike. Chifukwa chiyani?
6-7. N’chifukwa chiyani n’zosatheka kuuza munthu aliyense uthenga wabwino mapeto asanafike? Fotokozani.
6 Taganizirani zimene Yesu ananena zokhudza ntchito yathu yolalikira. Iye ananeneratu kuti uthenga wabwino udzalalikidwa “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni kwa anthu amitundu yonse.” (Mat. 24:14) Masiku ano, ulosiwu ukukwaniritsidwa kwambiri kuposa kale. Uthenga wa Ufumu ukufalitsidwa m’zilankhulo zoposa 1,000 ndipo webusaiti yathu ya jw.org, ikuthandiza anthu ambiri padziko lonse kuti amve uthenga wabwino.
7 Yesu anauzanso ophunzira ake kuti sadzamaliza “kuzungulira mizinda yonse” kapena kuti kulalikira kwa munthu wina aliyense iye asanabwere. (Mat. 10:23; 25:31-33) Mawu a Yesuwa akukwaniritsidwanso masiku ano. Anthu ambiri akukhala m’madera amene ntchito yathu ndi yoletsedwa. Komanso ana mahandiredi akubadwa pa miniti iliyonse. Timachita zonse zomwe tingathe kuti tilalikire uthenga wabwino kwa anthu a “fuko lililonse, chilankhulo chilichonse ndi mtundu uliwonse.” (Chiv. 14:6) Koma zoona ndi zakuti sitingathe kuuza munthu aliyense uthenga wabwino mapeto asanafike.
8. Kodi tingakhale ndi funso liti pa nkhani ya mmene Yehova adzaweruzire anthu m’tsogolo? (Onaninso zithunzi.)
8 Kuchokera pa zimene takambiranazi mwina tingakhale ndi funso lakuti: Nanga bwanji za anthu amene sanakhale ndi mwayi womva uthenga wabwino chisautso chachikulu chisanayambe? Kodi Yehova ndi Mwana wake amene wamupatsa udindo woweruza, adzawaweruza bwanji? (Yoh. 5:19, 22, 27; Mac. 17:31) Lemba lotsogolera nkhaniyi lanena kuti Yehova “sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe.” M’malomwake amafuna “kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9; 1 Tim. 2:4) Choncho tiyenera kudziwa kuti Yehova sanatiululire zonse zomwe adzachite, pa nkhani yoweruza anthu omwe sanamve uthenga wabwino. Ndipotu sakufunikira kuchita kutiuza zomwe wachita ndi zomwe adzachite.
9. Kodi Yehova watiululira zotani kudzera m’Mawu ake?
9 Kudzera m’Mawu ake, Yehova watiululira zina zimene adzachite. Mwachitsanzo, Baibulo limatiuza kuti Yehova adzaukitsa “osalungama” omwe analibe mwayi womva uthenga wabwino kuti asinthe zochita zawo. (Mac. 24:15; Luka 23:42, 43) Koma zimenezi zikubweretsanso mafunso ena ofunika.
10. Kodi ndi mafunso ena ati omwe tingakhale nawo?
10 Kodi anthu onse omwe adzafe pa nthawi ya chisautso chachikulu sadzakhala ndi chiyembekezo chodzaukitsidwa? Malemba amafotokoza momveka bwino kuti anthu otsutsa omwe Yehova ndi gulu lake la nkhondo adzawawononge pa Aramagedo sadzaukitsidwa. (2 Ates. 1:6-10) Koma bwanji za anthu amene adzafe pa nthawiyo chifukwa cha ukalamba, matenda, ngozi kapena kuphedwa ndi anthu anzawo? (Mla. 9:11; Zek. 14:13) Kodi ena mwa anthuwa angadzakhale m’gulu la “osalungama” omwe adzaukitsidwe m’dziko latsopano? Sitikudziwa.
ZIMENE TIKUDZIWA
11. Kodi pa Aramagedo anthu adzaweruzidwa potengera chiyani?
11 Tikudziwa zambiri zimene zidzachitike m’tsogolo. Mwachitsanzo, tikudziwa kuti pa Aramagedo, anthu adzaweruzidwa potengera mmene ankachitira zinthu ndi abale ake a Khristu. (Mat. 25:40) Amene adzaweruzidwe kuti ndi nkhosa, ndi amene anathandiza odzozedwa komanso Khristu. Tikudziwanso kuti ena mwa abale ake a Khristu adzakhala ali padzikoli chisautso chachikulu chikamadzayamba ndipo adzatengedwa kupita kumwamba Aramagedo itatsala pang’ono kuyamba. Pa nthawi imene abale ake a Khristu ali padzikoli, n’zotheka kuti anthu a mitima yabwino akhale ndi mwayi wowathandiza pa ntchito imene akugwira. (Mat. 25:31, 32; Chiv. 12:17) N’chifukwa chiyani kudziwa zimenezi kuli kofunika?
12-13. Kodi ena adzachita zotani akadzaona kuti “Babulo Wamkulu” wawonongedwa? (Onaninso zithunzi.)
12 Ngakhale chisautso chachikulu chikadzayamba, n’kutheka kuti ena omwe adzaone kuwonongedwa kwa “Babulo Wamkulu” adzakumbukira kuti a Mboni za Yehova ananenapo za zinthu zimenezi. Ndiye kodi ena amene adzaone zimenezi adzasintha mitima yawo?—Chiv. 17:5; Ezek. 33:33.
13 Zimenezi zingadzakhale zofanana ndi zimene zinachitika ku Iguputo m’nthawi ya Mose. Kumbukirani kuti “gulu la anthu a mitundu yosiyanasiyana” linachoka ku Iguputo limodzi ndi Aisiraeli. N’kutheka kuti ena mwa anthu amenewa anayamba kukhulupirira Yehova ataona kuti zimene Mose anachenjeza zokhudza miliri 10 zikuchitika. (Eks. 12:38) Ngati zimenezi zitadzachitika Babulo Wamkulu atawonongedwa, kodi tidzakhumudwa poona kuti anthu ayamba kutumikira Mulungu kutangotsala nthawi yochepa kuti mapeto afike? Ayi ndithu. Timafuna kutsanzira Atate wathu wakumwamba yemwe ndi “wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka komanso choonadi.” b—Eks. 34:6.
14-15. Kodi kuukitsidwa kwa munthu kukudalira kuti anafa liti kapenanso kuti ankakhala kuti? Fotokozani. (Salimo 33:4, 5)
14 Nthawi zina timamva ena akunena kuti, “Zingakhale bwino wachibale wanga atafa chisautso chachikulu chisanayambe kuti akhale ndi chiyembekezo chodzaukitsidwa.” N’kutheka kuti iwo anganene zimenezi ali ndi zolinga zabwino. Komatu kuukitsidwa kwa munthu sikukudalira kuti wafa pa nthawi iti. Yehova ndi Woweruza wolungama ndipo nthawi zonse amaweruza mwachilungamo. (Werengani Salimo 33:4, 5.) Choncho tingakhale otsimikiza kuti “Woweruza wa dziko lonse lapansi” adzachita zoyenera.—Gen. 18:25.
15 N’zomvekanso kunena kuti kuukitsidwa kwa munthu kuti akhale ndi moyo wosatha sikukudalira kumene ankakhala. N’zosamveka kuti Yehova adzaweruza anthu ambirimbiri kuti ndi “mbuzi” chifukwa chakuti ankakhala m’mayiko amene analibe mwayi woti amve uthenga wa Ufumu. (Mat. 25:46) Woweruza wolungama wa dziko lonse amaganizira kwambiri anthu amenewa kuposa ifeyo. Sitikudziwa mmene Yehova adzachitire zinthu pa nthawi ya chisautso chachikulu. N’kutheka kuti ena mwa anthu amenewa adzakhala ndi mwayi wophunzira zokhudza Yehova, kumukhulupirira komanso kuyamba kumutumikira pamene azidzayeretsa dzina lake.—Ezek. 38:16.
Chisautso chachikulu chikadzayamba, . . . kodi ena omwe adzaone zochitika pa nthawiyo adzasintha maganizo?
16. Kodi tadziwa zinthu ziti zokhudza Yehova? (Onaninso chithunzi.)
16 Kuphunzira Baibulo kwatithandiza kudziwa kuti Yehova amaona kuti anthu ndi amtengo wapatali. Iye anapereka moyo wa Mwana wake kuti tonsefe tipeze mwayi wodzakhala ndi moyo mpaka kalekale. (Yoh. 3:16) Yehova amatikonda kwambiri tonsefe. (Yes. 49:15) Amadziwa dzina la aliyense payekha. Ndipotu amatidziwa bwino kwambiri moti ngakhale titafa, iye adzatiukitsa chifukwa amadziwa chilichonse chokhudza ifeyo. (Mat. 10:29-31) Choncho tili ndi zifukwa zomveka zokhulupirira kuti Atate wathu wachikondi adzaweruza munthu aliyense mwachilungamo chifukwa iye ndi wanzeru, wolungama komanso wachifundo.—Yak. 2:13.
17. Kodi tidzakambirana chiyani mu nkhani yotsatira?
17 Popeza kuti tsopano tamvetsa bwino mfundo zimenezi, tiziona kuti ntchito yathu yolalikira ndi yofunika kugwiridwa mwamsanga kuposa kale. N’chifukwa chiyani tikutero? Nanga n’chiyani chingatilimbikitse kuti tizilalikira uthenga wabwino mwakhama? Tidzakambirana mayankho a mafunso amenewa mwatsatanetsatane munkhani yotsatira.
NYIMBO NA. 76 Kodi Mumamva Bwanji?
a Kuti mudziwe chifukwa chake pakhala kusinthaku, onani nkhani yakuti “Munavomereza Kuti Zimenezi Zichitike,” mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2015 tsamba 7-11.
b Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, atumiki onse a Yehova adzayesedwa pa kuukira kwa Gogi wa ku Magogi. Aliyense amene adzasankhe kukhala kumbali ya anthu a Mulungu pa nthawiyi, nayenso adzayesedwa.
c MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Zithunzi zosonyeza chifukwa chake ena sangakhale ndi mwayi womva uthenga wathu womwe ukulalikidwa padziko lonse: (1) Mayi akukhala kudera limene chipembedzo chachikulu kumeneko chimalepheretsa anthu kumva uthenga wabwino, (2) banja likukhala m’dziko limene zochitika zandale zimachititsa kuti kuphunzira za Yehova kukhale koletsedwa komanso koopsa, ndipo (3) bambo akukhala m’dera lovuta kufikako.
d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mtsikana yemwe anasiya choonadi akukumbukira zimene anaphunzira zokhudza kuwonongedwa kwa “Babulo Wamkulu.” Iye akusintha maganizo ndipo akubwerera kwa makolo ake omwe ndi a Mboni. Ngati zofanana ndi zimenezi zitachitika, tizitsanzira Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachifundo komanso wokoma mtima, n’kumasangalala kuti munthu wochimwa walapa.
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA