NKHANI YOPHUNZIRA 18

NYIMBO NA. 1 Makhalidwe a Yehova

Muzikhulupirira “Woweruza wa Dziko Lonse Lapansi” Yemwe Ndi Wachifundo

Muzikhulupirira “Woweruza wa Dziko Lonse Lapansi” Yemwe Ndi Wachifundo

“Ndinu Woweruza wa dziko lonse lapansi. Ndiye kodi simuchita chilungamo?”​—GEN. 18:25.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Nkhaniyi itithandiza kumvetsa kuti Yehova adzachita zinthu mwachifundo komanso mwachilungamo poukitsa anthu osalungama.

1. Kodi Yehova anaphunzitsa Abulahamu mfundo yolimbikitsa iti?

 ZAKA zambiri m’mbuyomu, Mulungu anatuma mngelo kuti akauze Abulahamu kuti iye akufuna kuwononga mizinda ya Sodomu ndi Gomora. Abulahamu ankakhulupirira kwambiri Mulungu komabe zimenezi zinamuvuta kumvetsa. Choncho anafunsa kuti: “Kodi zoona muwonongadi olungama pamodzi ndi oipa? . . . Ndinu Woweruza wa dziko lonse lapansi. Ndiye kodi simuchita chilungamo?” Yehova anathandiza moleza mtima mnzake wapamtimayu kudziwa mfundo yofunika kwambiri yakuti: Iye sadzawononga anthu olungama. Mfundo imeneyi ndi yothandiza komanso yolimbikitsa kwa tonsefe masiku ano.​—Gen. 18:23-33.

2. N’chiyani chikutitsimikizira kuti Yehova amaweruza mwachilungamo komanso mwachifundo?

2 Kodi tingatsimikize bwanji kuti Yehova amaweruza anthu mwachilungamo komanso mwachifundo? Timatsimikizira zimenezi chifukwa “Yehova amaona mumtima” mwa munthu. (1 Sam. 16:7) N’zoona kuti iye ‘amadziwa bwino mtima wa munthu aliyense.’ (1 Maf. 8:39; 1 Mbiri 28:9) Zimenezitu ndi zochititsa chidwi kwambiri. Yehova ndi wanzeru kwambiri choncho sitingamvetse chifukwa chake amasankhira kuchita zinthu zina. Mpake kuti mtumwi Paulo anauziridwa kulemba kuti: “Ziweruzo zake [za Yehova Mulungu] ndi zovuta kuzimvetsa.”​—Aroma 11:33.

3-4. Kodi nthawi zina tingakhale ndi mafunso ati, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi? (Yohane 5:28, 29)

3 Komabe nthawi zina tikhoza kumakhala ndi mafunso ngati amene Abulahamu anali nawo. Mwachitsanzo, tingadzifunse kuti: ‘Kodi pali chiyembekezo chilichonse kwa anthu omwe Yehova anawawononga monga ngati a ku Sodomu ndi Gomora? Kodi n’kutheka kuti ena mwa iwo adzakhala m’gulu la “osalungama” omwe adzaukitsidwe?’​—Mac. 24:15.

4 Tiyeni tikambirane zimene tikudziwa pa nkhani ya kuukitsidwa kwa akufa. Posachedwapa, tathandizidwa kumvetsa tanthauzo la kuukitsidwa kwa anthu “kuti alandire moyo” ndi kuukitsidwa “kuti aweruzidwe.” a (Werengani Yohane 5:28, 29.) Zimenezi zachititsa kuti tisinthenso mmene timamvera mfundo zina ndipo munkhaniyi komanso yotsatira, tikambirana za kusintha kumeneku. Pa nkhani yoti Yehova amaweruza anthu mwachilungamo, choyamba tikambirana zimene sitikudziwa kenako zimene tikudziwa.

ZIMENE SITIKUDZIWA

5. Kodi m’mbuyomu mabuku athu akhala akufotokoza zotani zokhudza anthu amene anawonongedwa ku Sodomu ndi Gomora?

5 M’mbuyomu, mabuku athu akhala akufotokoza zimene zidzachitikire anthu omwe Yehova anawaweruza kuti ndi osalungama. Tinkanena kuti palibe chiyembekezo choti anthu amene Yehova anawawononga, monga a ku Sodomu ndi Gomora, adzaukitsidwa. Koma pambuyo popemphera ndi kuphunzira mosamala nkhaniyi, sitinganene zimenezi motsimikiza.

6. Kodi ndi zitsanzo ziti za anthu osalungama amene Yehova anawaweruza, nanga sitikudziwa chiyani?

6 Tiyeni tiganizire nkhani zingapo. Baibulo limafotokoza nthawi zingapo pamene Yehova anapereka chiweruzo kwa anthu osalungama. Mwachitsanzo, anthu ambirimbiri anafa pa nthawi ya Chigumula. Yehova analamulanso anthu ake kuti akawononge mitundu 7 ya anthu a m’Dziko Lolonjezedwa. Pa nthawi inanso, mngelo wa Yehova anapha asilikali a Asuri 185,000, usiku umodzi. (Gen. 7:23; Deut. 7:1-3; Yes. 37:36, 37) Pa nkhani zonsezi, Baibulo silifotokoza zambiri zomwe zingatipangitse kuganiza kuti Yehova anaweruza kuti anthu amenewa awonongedwe ndipo asadzaukitsidwe. N’chifukwa chiyani tikutero?

7. Kodi sitikudziwa chiyani zokhudza anthu amene anawonongedwa pa Chigumula kapena amene anaphedwa pamene Aisiraeli ankagonjetsa dziko la Kanani? (Onani chithunzi chapachikuto.)

7 Sitikudziwa mmene Yehova anaweruzira munthu aliyense payekha komanso ngati anthu omwe anaphedwawo anali ndi mwayi wophunzira za iye komanso kulapa. Pa nkhani ya nthawi ya Chigumula, Baibulo limanena kuti Nowa “ankalalikira za chilungamo cha Mulungu.” (2 Pet. 2:5) Koma silinena kuti pa nthawi yomwe ankamanga chingalawa chachikulucho, Nowa ankayesetsanso kuti alalikire kwa munthu aliyense padziko lapansi. N’chimodzimodzinso ndi anthu a ku Kanani. Sitikudziwa ngati anthu onse oipawo anali ndi mwayi wophunzira za Yehova ndiponso kusintha.

Nowa ndi anthu a m’banja lake akumanga chingalawa. Sizikudziwika ngati pa nthawi imene ankamanga chingalawayo, Nowa ndi banja lake anakonza zoti alalikire kwa munthu aliyense padziko lapansi Chigumula chisanafike. (Onani ndime 7)


8. Kodi sitikudziwa zinthu ziti zokhudza anthu a ku Sodomu ndi Gomora?

8 Nanga bwanji za anthu a ku Sodomu ndi Gomora? Loti yemwe anali munthu wolungama, ankakhala pakati pawo. Koma kodi tikudziwa ngati Loti analalikira kwa anthu onsewo? Ayi. N’zoona kuti iwo anali oipa koma kodi onsewo ankadziwa kuti izi n’zabwino ndipo izi n’zoipa? Kumbukirani kuti gulu la amuna a mumzindawo linkafuna kugwiririra alendo a Loti. Baibulo limanena kuti pachigulupo “panali anyamata komanso achikulire.” (Gen. 19:4; 2 Pet. 2:7) Ndiye kodi tingatsimikize kuti Yehova Mulungu yemwe ndi wachifundo, anaweruza kuti anthu onsewo afe ndipo asadzaukitsidwe? Yehova anatsimikizira Abulahamu kuti mumzindawo munalibe anthu olungama ngakhale 10. (Gen. 18:32) Iwo anali osalungama choncho Yehova anawaweruza mwachilungamo powawononga chifukwa cha zimene ankachita. Ndiye kodi tinganene motsimikiza kuti palibe aliyense wa anthu amenewo, adzakhale m’gulu la “osalungama” omwe adzaukitsidwe? Ayi, sitingatero.

9. Kodi sitikudziwa zinthu ziti zokhudza Solomo?

9 Koma m’Baibulo timawerenganso za anthu olungama amene anadzakhala osalungama. Chitsanzo ndi Mfumu Solomo. Iye anaphunzitsidwa bwino njira za Mulungu ndipo Yehova anamudalitsa kwambiri, koma kenako anayamba kulambira milungu yabodza. Machimo ake anakwiyitsa kwambiri Yehova ndipo Aisiraeli anavutika ndi zotsatira zake kwa zaka zambiri. N’zoona kuti Malemba amanena kuti Solomo “anaikidwa m’manda” limodzi ndi makolo ake, kuphatikizapo Davide yemwe anali wokhulupirika. (1 Maf. 11:5-9, 43; 2 Maf. 23:13) Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti basi ndiye kuti Solomo adzaukitsidwa? Baibulo silinena kalikonse. Ena angamaganize kuti Solomo adzaukitsidwa chifukwa Baibulo limanena kuti “munthu amene wafa sakhalanso ndi mlandu wa machimo ake.” (Aroma 6:7) Zimenezi ndi zoona koma sizikutanthauza kuti anthu onse amene anafa adzaukitsidwa, ngati kuti munthu akafa, ndiye kuti basi ali ndi ufulu wodzakhalanso ndi moyo. Kuukitsidwa ndi mphatso yomwe Mulungu wachikondi amapereka. Ndipo amaipereka kwa anthu omwe iye akufuna kuwapatsa mwayi womutumikira mpaka kalekale. (Yobu 14:13, 14; Yoh. 6:44) Ndiye kodi Solomo adzalandira mphatso imeneyi? Yehova yekha ndi amene akudziwa. Koma chomwe ife tikudziwa n’choti Yehova adzachita zinthu mwachilungamo.

ZIMENE TIKUDZIWA

10. Kodi Yehova amamva bwanji pa nkhani yowononga anthu? (Ezekieli 33:11) (Onaninso chithunzi.)

10 Werengani Ezekieli 33:11. Yehova amatiuza mmene amamvera pa nkhani yoweruza anthu. Mtumwi Petulo anabwereza zimene mneneri Ezekieli analemba. Iye anati “Yehova . . . sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe.” (2 Pet. 3:9) Mfundo yolimbikitsayi imatithandiza kudziwa kuti Yehova safulumira kuwonongeratu anthu. Iye ndi wachifundo chachikulu ndipo amasonyeza chifundocho ngati pakufunika kutero.

Anthu ambiri osalungama adzaukitsidwa n’kupatsidwa mwayi woti aphunzire za Yehova. (Onani ndime 10)


11. Ndi anthu ati amene sadzaukitsidwa ndipo tikudziwa bwanji zimenezi?

11 Kodi ndi zinthu ziti zimene tikudziwa za anthu amene sadzaukitsidwa? Baibulo limangotchula zitsanzo zochepa. b Yesu ananena kuti Yudasi Isikarioti sadzaukitsidwa. c (Maliko 14:21; Yoh. 17:12) Yudasi, modziwa komanso mwadala, anachita zinthu motsutsana ndi Yehova Mulungu ndiponso Mwana wake. (Maliko 3:29) Yesu ananenanso kuti atsogoleri a chipembedzo ena amene ankamutsutsa alibenso chiyembekezo chakuti adzauka. (Mat. 23:33; Yoh. 19:11) Mtumwi Petulo anachenjezanso kuti anthu ampatuko osalapa, sadzaukitsidwa.​—Aheb. 6:4-8; 10:29.

12. Kodi tikudziwa zotani zokhudza chifundo cha Yehova? Perekani zitsanzo.

12 Nanga kodi ndi zinthu ziti zomwe tikudziwa zokhudza chifundo cha Yehova? Nanga wasonyeza bwanji kuti “sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe”? Taganizirani mmene anasonyezera chifundo kwa anthu ena amene anachita machimo akuluakulu. Mfumu Davide anachita machimo akuluakulu monga chigololo komanso kupha munthu. Koma Davide analapa ndipo Yehova anamuchitira chifundo n’kumukhululukira. (2 Sam. 12:1-13) Mfumu Manase anachita zinthu zoipa kwambiri kwa nthawi yaitali pa moyo wake. Ngakhale zinali choncho, Yehova anamuchitira chifundo n’kumukhululukira chifukwa chakuti analapa. (2 Mbiri 33:9-16) Zitsanzo zimenezi zikutikumbutsa kuti Yehova amasonyeza chifundo ngati pali zifukwa zosonyezera chifundocho. Iye adzaukitsa anthu ngati amenewa chifukwa chozindikira kuti anachita machimo akuluakulu ndipo analapa.

13. (a) N’chifukwa chiyani Yehova anachitira chifundo anthu a ku Nineve? (b) Kodi Yesu ananena chiyani zokhudza anthu a ku Nineve?

13 Timadziwanso kuti Yehova anasonyeza chifundo kwa anthu a ku Nineve. Mulungu anauza Yona kuti: “Ndaona zoipa zomwe akuchita.” Koma iwo atalapa machimo awo, Yehova anawachitira chifundo n’kuwakhululukira. Yehova anasonyeza chifundo kuposa Yona. Yona atakwiya, Mulungu anamukumbutsa kuti anthu a ku Nineve ‘sankadziwa kusiyanitsa zoyenera ndi zolakwika.’ (Yona 1:1, 2; 3:10; 4:9-11) Pambuyo pake, Yesu anagwiritsa ntchito chitsanzo chimenechi pophunzitsa anthu zokhudza chilungamo ndi chifundo cha Yehova. Yesu ananena kuti anthu a ku Nineve amene analapa “adzauka pa Tsiku la Chiweruzo.”​—Mat. 12:41.

14. Kodi chidzachitike n’chiyani anthu a ku Nineve ‘akadzaukitsidwa kuti aweruzidwe’?

14 Kodi anthu a ku Nineve ‘adzauka pa chiweruzo’ chiti? Yesu anaphunzitsa kuti anthu ena “adzauka kuti aweruzidwe.” (Yoh. 5:29) Iye ankanena za Ulamuliro [Wake] wa Zaka 1,000, pomwe anthu ‘olungama ndi osalungama omwe adzaukitsidwe.’ (Mac. 24:15) Kwa anthu osalungama, kumeneku kudzakhala ‘kuuka kuti aweruzidwe.’ Izi zikutanthauza kuti Yehova ndi Yesu azidzaona ngati anthuwo akumvera komanso kutsatira zimene adzaphunzitsidwe. Mwachitsanzo, ngati anthu ena a ku Nineve adzakane kulambira Yehova, adzaweruzidwa kuti asakhalenso ndi moyo. (Yes. 65:20) Koma anthu onse amene adzasankhe kulambira Yehova mokhulupirika, adzaweruzidwa kuti akhale ndi moyo mpaka kalekale.​—Dan. 12:2.

15. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kunena kuti onse amene anawonongedwa ku Sodomu ndi Gomora sadzaukitsidwa? (b) Kodi mawu a pa Yuda 7 amatanthauza chiyani? (Onani bokosi lakuti “ Kodi Yuda Ankatanthauza Chiyani?”)

15 Yesu ananena kuti chilango cha anthu amene ankakana zimene iye ankaphunzitsa chidzakhala chopweteka kwambiri “pa Tsiku la Chiweruzo” kuposa chilango cha anthu a ku Sodomu ndi Gomora. (Mat. 10:14, 15; 11:23, 24; Luka 10:12) Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani? Mwina tikhoza kumaganiza kuti pa nthawiyi Yesu ankagwiritsa ntchito fanizo lokokomeza. Koma zikuoneka kuti si choncho, tikaganizira zimene ananena zokhudza anthu a ku Nineve. Zikuoneka kuti zimene Yesu ananena silinali fanizo koma zenizeni. “Tsiku la Chiweruzo” limene analitchula m’maulendo onsewa linali limodzi. Mofanana ndi anthu a ku Nineve, anthu a ku Sodomu ndi Gomora anachita zinthu zoipa koma anthu a ku Nineve anali ndi mwayi wolapa. Komanso kumbukirani zimene Yesu ananena zokhudza anthu amene ‘adzaukitsidwe kuti aweruzidwe.’ Ankaphatikizapo anthu “amene ankachita zoipa.” (Yoh. 5:29) Choncho zikuoneka kuti anthu ena a ku Sodomu ndi Gomora akhoza kudzaukitsidwa. N’kutheka kuti ena mwa anthuwo adzaukitsidwa ndipo tingadzakhale ndi mwayi wowaphunzitsa za Yehova ndi Yesu Khristu.

16. Kodi tikudziwa chiyani pa nkhani ya mmene Yehova amasankhira anthu oti adzawaukitse? (Yeremiya 17:10)

16 Werengani Yeremiya 17:10. Lembali likutithandiza kupeza mfundo yaikulu pa zimene tikudziwa. Nthawi zonse Yehova ‘amafufuza mtima, amafufuza maganizo a mkati mwa mtima wa munthu.’ Choncho pa nkhani ya kuukitsa anthu, Yehova adzachitira munthu aliyense “mogwirizana ndi zochita zake.” Adzachita zinthu mwamphamvu komanso mwachifundo ngati pakufunika kutero. Choncho tisamafulumire kuganiza kuti munthu winawake alibe chiyembekezo choti adzaukitsidwa, pokhapokha ngati tatsimikiza kuti Baibulo limanena zimenezo.

“WOWERUZA WA DZIKO LONSE LAPANSI” ADZACHITA “CHILUNGAMO”

17. Kodi chidzachitike n’chiyani kwa anthu amene anamwalira?

17 Kungochokera pamene Adamu ndi Hava anakhala kumbali ya Satana poukira Yehova Mulungu, anthu mabiliyoni ambiri akhala akufa. ‘Imfa ndi mdani’ woopsa kwambiri. (1 Akor. 15:26) Ndiye kodi n’chiyani chidzachitikire anthu onsewa? Anthu ochepa, okwana 144,000 omwe ndi otsatira okhulupirika a Khristu, adzaukitsidwa n’kupatsidwa moyo wosafa kumwamba. (Chiv. 14:1) Amuna ndi akazi okhulupirika amene ankakonda Yehova, adzakhala m’gulu la anthu ‘olungama amene adzaukitsidwe’ ndipo adzapatsidwa moyo wosatha padziko lapansi ngati angakhale okhulupirika mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu komanso akadzayesedwa komaliza. (Dan. 12:13; Aheb. 12:1) Komanso mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, anthu “osalungama” kuphatikizapo amene sanatumikirepo Yehova, kapena amene “ankachita zoipa,” adzapatsidwa mwayi woti asinthe njira zawo n’kukhala okhulupirika. (Luka 23:42, 43) Koma pali anthu ena omwe Yehova anasankha kuti asadzaukitsidwe n’komwe. Anthu amenewa anali oipa kwambiri ndipo anatsimikiza mtima kutsutsana ndi Yehova komanso zolinga zake.​—Luka 12:4, 5.

18-19. (a) N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzaweruza mwachilungamo anthu amene anamwalira? (Yesaya 55:8, 9) (b) Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

18 Kodi tingakhale otsimikiza kuti nthawi zonse Yehova amaweruza anthu mwachilungamo? Inde. Abulahamu ankadziwa kuti Yehova ndi “Woweruza wa dziko lonse lapansi” yemwe ndi wangwiro, wanzeru komanso wachifundo. Iye waphunzitsa bwino Mwana wake ndipo wamupatsa udindo wonse woweruza. (Yoh. 5:22) Iye pamodzi ndi Mwana wakeyu amadziwa zimene zili mumtima mwa munthu. (Mat. 9:4) Choncho akamadzaweruza munthu aliyense adzachita zinthu ‘mwachilungamo.’

19 Tiyeni tisamakayikire ngakhale pang’ono kuti Yehova amadziwa zonse. Timadziwa kuti iye ndi woyenera kuweruza osati ifeyo. (Werengani Yesaya 55:8, 9.) Choncho nkhani yonse yoweruzayi timaisiya m’manja mwa iyeyo ndi Mwana wake. Ndipo Mwana wakeyu ndi Mfumu imene imatsanzira Atate wake posonyeza chilungamo ndi chifundo. (Yes. 11:3, 4) Koma kodi Yehova ndi Yesu adzaweruza bwanji anthu pa nthawi ya chisautso chachikulu? Kodi ndi zinthu ziti zimene sitikudziwa? Nanga ndi zinthu ziti zimene tikudziwa? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso amenewa.

NYIMBO NA. 57 Tizilalikira kwa Anthu a Mitundu Yonse

b Pa nkhani yokhudza Adamu, Hava ndi Kaini, onani w22.6 24:15.

c Mawu akuti mwana wachiwonongeko omwe anagwiritsidwa ntchito pa Yohane 17:12 amatanthauza kuti pamene Yudasi anafa, palibenso chiyembekezo choti adzaukitsidwa.