NKHANI YOPHUNZIRA 37

“Dzanja Lako Lisapume”

“Dzanja Lako Lisapume”

“Bzala mbewu zako m’mawa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo.”​MLAL. 11:6.

NYIMBO NA. 68 Tizifesa Mbewu za Ufumu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Kodi zimene lemba la Mlaliki 11:6 limanena zikugwirizana bwanji ndi ntchito yolalikira?

M’MAYIKO ena, anthu amafuna kuphunzira zambiri akamva uthenga wabwino moti amasangalala kwambiri ndi uthengawo. Pomwe m’mayiko ena, anthu sachita chidwi ndi nkhani za Mulungu kapena Baibulo. Kodi anthu a m’dera lanu amatani akamva uthenga wabwino? Kaya amachita zotani, Yehova amafuna tipitirizebe kulalikira mpaka ntchitoyi itafika kumapeto.

2 Yehova anaikiratu nthawi yomwe tidzasiye kugwira ntchito yolalikira, “ndipo kenako mapeto adzafika.” (Mat. 24:14, 36) Komano kodi tingasonyeze bwanji kuti tikumvera mawu akuti “dzanja lako lisapume”? *​—Werengani Mlaliki 11:6.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Munkhani yapita ija, tinakambirana zinthu 4 zomwe tiyenera kuchita kuti tikhale “asodzi a anthu.” (Mat. 4:19) Munkhaniyi, tikambirana zinthu zitatu zimene zingatithandize kupitirizabe kulalikira, ngakhale tikukumana ndi mavuto. Tiona kufunika kwa (1) kuona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri, (2) kukhala oleza mtima komanso (3) kulimbitsa chikhulupiriro chathu.

MUZIONA KUTI NTCHITO YOLALIKIRA NDI YOFUNIKA KWAMBIRI

4. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tizionabe kuti ntchito imene Yehova anatipatsa ndi yofunika kwambiri?

4 Yesu anauza ophunzira ake zokhudza makhalidwe a anthu komanso zimene zidzachitike m’masiku otsiriza. Iye ankadziwa kuti zinthu zimenezi zingachititse otsatira ake kusiya kuona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri. Choncho anauza ophunzira ake kuti “khalanibe maso.” (Mat. 24:42) Mu nthawi ya Nowa, panali zinthu zambiri zimene zinkachititsa anthu kuti azinyalanyaza uthenga umene ankawauza. Zangati zimenezi zingachitikenso masiku ano. (Mat. 24:37-39; 2 Pet. 2:5) Choncho tiyenera kuyesetsa kuti tipitirizebe kuona ntchito imene Yehova anatipatsa kukhala yofunika kwambiri.

5. Kodi lemba la Machitidwe 1:6-8 limanena kuti ntchito yolakira idzafika pati?

5 Tiyenera kumaona kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi yofunika kwambiri masiku ano. Yesu ananeneratu kuti otsatira ake adzapitirizabe kulalikira pambuyo poti waphedwa ndipo adzalalikira kuposa mmene iyeyo anachitira. (Yoh. 14:12) Yesu ataphedwa, ophunzira ake ena anabwerera kuntchito yausodzi. Ndiyeno ataukitsidwa, anathandiza ophunzira akewo kugwira nsomba zambiri. Atachita zimenezi, Yesu anakumbutsa ophunzira ake kuti ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu ndi yofunika kwambiri kuposa ntchito ina iliyonse. (Yoh. 21:15-17) Atangotsala pang’ono kupita kumwamba, Yesu anauza ophunzira ake kuti ntchito yolalikira yomwe anayambitsayi, idzafalikira m’madera ambiri. (Werengani Machitidwe 1:6-8.) Patapita zaka zambiri, Yesu anaonetsa mtumwi Yohane masomphenya onena zimene zidzachitike mu “tsiku la Ambuye.” * M’masomphenyawo Yohane anaona zinthu zochititsa chidwi kwambiri. Iye anaona mngelo ali ndi “uthenga wabwino wosatha, woti aulengeze kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse.” (Chiv. 1:10; 14:6) Apa n’zoonekeratu kuti Yehova amafuna kuti tizigwira nawo ntchito yolakira, yomwe ikuchitika padziko lonse mpaka itafika kumapeto.

6. N’chiyani chingatithandize kuti tiziona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri?

6 Kuganizira mmene Yehova amatithandizira tikamagwira ntchitoyi, kungatithandize kuti tiziiona kuti ndi yofunika kwambiri. Mwachitsanzo, amatipatsa chakudya chauzimu chochuluka kwambiri kudzera m’mabuku, zinthu zongomvetsera, m’mavidiyo komanso webusaiti yathu. Tangoganizani, pofika pano webusaiti yathu ili m’zinenero zoposa 1,000. (Mat. 24:45-47) M’dzikoli anthu ambiri sagwirizana chifukwa amasiyana maganizo pankhani za ndale, chipembedzo komanso chuma. Ngakhale zili choncho, atumiki a Yehova oposa 8 miliyoni ndi ogwirizana kwambiri padziko lonse. Mwachitsanzo, Lachisanu pa 19 April 2019, a Mboni za Yehova padziko lonse, anaonera vidiyo ya lemba la tsiku. Madzulo a tsikuli, anthu okwana 20,919,041 anasonkhana pamwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Tikamaona kuti ndi mwayi waukulu kugwira nawo ntchitoyi komanso kuona mmene ikupitira patsogolo, timafunitsitsa kupitiriza kugwira ntchito yolalikira uthenga wa Ufumu mwakhama.

Yesu sanalole kuti chilichonse chimusokoneze pamene ankagwira ntchito yake yolalikira (Onani ndime 7)

7. Kodi chitsanzo cha Yesu chingatithandize bwanji kuti tiziona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri?

7 Chinthu china chomwe chingatithandize kuti tiziona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri, ndi kutengera chitsanzo cha Yesu. Iye sankalola kusokonezedwa ndi chilichonse akamagwira ntchito yolalikira. (Yoh. 18:37) Sanakopeke pamene Satana “anamuonetsa maufumu onse a padziko ndi ulemerero wawo”, komanso anakana pamene anthu ena ankafuna kumuveka ufumu. (Mat. 4:8, 9; Yoh. 6:15) Yesu sanalole kuti mtima wokonda chuma umusokoneze komanso sanasiye kulalikira, ngakhale anthu ena ankamutsutsa kwambiri. (Luka 9:58; Yoh. 8:59) Ngati titatsatira malangizo a mtumwi Paulo pamene tikukumana ndi mayesero, tingapitirizebe kuona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika. Iye analimbikitsa Akhristu kuti azitengera chitsanzo cha Yesu ‘kuti asatope ndiponso kulefuka.’​—Aheb. 12:3.

MUZIKHALA OLEZA MTIMA

8. Kodi munthu woleza mtima amatani, nanga n’chifukwa chiyani khalidweli ndi lofunika makamaka panopa?

8 Munthu woleza mtima, amayembekezerabe mpaka zinthu zitasintha. Timafunika kukhala oleza mtima chifukwa nthawi zina timakumana ndi mavuto amene timafunitsitsa atatha. Komanso timafuna zinthu zimene takhala tikuziyembekezera kwa nthawi yaitali zitachitika. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mneneri Habakuku, yemwe ankafunitsitsa kuti chiwawa chimene chinkachitika ku Yuda chithe. (Hab. 1:2) Nawonso ophunzira a Yesu ankafunitsitsa Ufumu wa Mulungu utabwera “nthawi yomweyo,” kuti udzawapulumutse ku ulamuliro wankhanza wa Aroma. (Luka 19:11) Nafenso timayembekezera mwachidwi nthawi imene Ufumu wa Mulungu udzachotse zoipa zonse, n’kubweretsa dziko lomwe mudzakhale anthu omvera Mulungu. (2 Pet. 3:13) Komabe tikufunika kuyembekezera moleza mtima kufikira pamene Yehova adzachite zimenezi. Tsopano tiyeni tikambirane njira zina zomwe Yehova amatithandizira kuti tikhale oleza mtima.

9. Kodi ndi zinthu ziti zimene zimasonyeza kuti Yehova ndi woleza mtima?

9 Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kuleza mtima. Iye anapereka nthawi yokwanira kwa Nowa kuti amange chingalawa komanso kuti agwire ntchito yake monga “mlaliki wa chilungamo.” (2 Pet. 2:5; 1 Pet. 3:20) Komanso Yehova ankamvetsera mwatcheru pamene Abulahamu anamufunsa mobwerezabwereza, zokhudza cholinga chake chofuna kuononga anthu oipa a mumzinda wa Sodomu ndi Gomora. (Gen. 18:20-33) Kwa zaka zambiri, Yehova anachitanso zinthu moleza mtima ndi mtundu wosakhulupirika wa Aisiraeli. (Neh. 9:30, 31) Masiku anonso Yehova amasonyeza kuti amalezera mtima anthu onse amene amafuna kukhala naye pa ubwenzi, powapatsa nthawi yokwanira yoti “alape.” (2 Pet. 3:9; Yoh. 6:44; 1 Tim. 2:3, 4) Chitsanzo cha Yehova chimatithandiza kuti nafenso tipitirizebe kulalikira komanso kuphunzitsa anthu moleza mtima. Yehova amatiphunzitsanso kukhala oleza mtima, pogwiritsa ntchito chitsanzo chimene chili m’Mawu ake.

Mofanana ndi mlimi wakhama yemwe amaleza mtima, ifenso timadikira moleza mtima kuti tione zotsatira za ntchito yathu (Onani ndime 10-11)

10. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa chitsanzo cha mlimi chopezeka pa Yakobo 5:7, 8?

10 Werengani Yakobo 5:7, 8Chitsanzo cha mlimi chingatithandize kuti tikhale oleza mtima. N’zoona kuti mbewu zina zimakula mofulumira. Komabe mbewu zambiri zomwe zimatulutsa chakudya, zimatenga nthawi yayitali kuti zikhwime. Ku Isiraeli nthawi yolima inkatenga miyezi 6. Mlimi ankadzala mbewu zake mvula yoyambirira ikangogwa ndipo ankakolola mbewuzo zikakhwima chakumapeto kwa nyengo ya dzinja. (Maliko 4:28) Nafenso tingachite bwino kwambiri kukhala oleza mtima ngati mlimi. Komabe kuchita zimenezi sikophweka.

11. Kodi kuleza mtima n’kofunika bwanji pa ntchito yathu yolalikira?

11 Nthawi zambiri anthu ochimwafe, timafuna kuona zotsatira za ntchito yathu nthawi yomweyo. Koma ngati tikufuna tikolole mbewu m’munda wathu, tiyenera kumausamalira. Mwachitsanzo tiyenera kulima, kudzala, kupalira komanso kuthirira. Nayonso ntchito yophunzitsa anthu imafuna khama. Zimatenga nthawi kuti tithandize ophunzira Baibulo athu kusiya kukhala ndi mtima watsankho n’kuyamba kukonda ena. Kuleza mtima kungatithandizenso kuti tisafooke anthu ena akapanda kumvetsera uthenga wathu. Tingafunikebe kukhala oleza mtima, ngakhale titakumana ndi anthu omvetsera. Tikutero chifukwa sitingakakamize ophunzira Baibulo wathu kuti asinthe mofulumira kwambiri. Ngakhalenso ophunzira a Yesu nthawi zina ankavutika kumvetsa zimene Yesu ankawaphunzitsa. (Yoh. 14:9) Tizikumbukira kuti ifeyo tikhoza kudzala komanso kuthirira koma Mulungu ndi amene amakulitsa.​—1 Akor. 3:6.

12. Kodi tingasonyeze bwanji kuleza mtima tikamalalikira achibale athu?

12 Nthawi zina tingavutike kukhala oleza mtima tikamalalikira achibale athu. Zikatere, mfundo imene imapezeka pa Mlaliki 3:1, 7 ingatithandize. Lembali limati pali “nthawi yokhala chete ndi nthawi yolankhula.” Khalidwe lathu labwino lingathandize achibale athu kumvetsera uthenga wabwino. Komabe nthawi zonse tingachite bwino kukhala okonzeka kuti tiziwauza zokhudza Yehova. (1 Pet. 3:1, 2) Tiyenera kumagwira ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa mwakhama koma tikamachita zimenezi tizilezera mtima anthu onse kuphatikizapo achibale athu.

13-14. Kodi ndi zitsanzo ziti za kuleza mtima zimene tiyenera kutsanzira?

13 Tingaphunzirenso kukhala oleza mtima kuchokera kwa anthu okhulupirika otchulidwa m’Baibulo komanso kwa atumiki okhulupirika amasiku ano. Habakuku ankafunitsitsa zinthu zoipa zitatha, koma anasonyeza kuti anali woleza mtima pamene ananena kuti: “Ine ndidzaimabe pamalo a mlonda.” (Hab. 2:1) Mtumwi Paulo ananena kuti ankafunitsitsa ‘atamaliza utumiki wake.’ Komabe, anapitiriza “kuchitira umboni mokwanira za uthenga wabwino” moleza mtima.​—Mac. 20:24.

14 Tiyeni tione chitsanzo cha banja lina lomwe linamaliza maphunziro a Sukulu ya Giliyadi ndipo anatumizidwa kudziko lina lomwe kuli a Mboni ochepa komanso anthu ambiri si Akhristu. M’dzikolo anthu ambiri sankafuna kuphunzira Baibulo. Koma anzawo ena omwe anali nawo ku Sukulu ya Giliyadi omwe ankatumikira m’mayiko ena, ankawauza kuti amaphunzira Baibulo ndi anthu ambiri ndipo ena anabatizidwa. Komabe banjali linapitirizabe kulalikira ngakhale kuti anthu ambiri a m’gawo lawo sankamvetsera. Atalalikira kwa zaka 8 m’gawoli, anasangalala ataona munthu mmodzi yemwe ankaphunzira naye Baibulo atabatizidwa. Kodi tikuphunzira chiyani pa zitsanzo za anthu otchulidwa m’Baibulo komanso atumiki okhulupirika amasiku ano? Atumiki okhulupirikawa sanasiye kuchita khama komanso sanapumitse manja awo ndipo Yehova anawadalitsa chifukwa cha kuleza mtima kwawo. Tiyeni ‘tizitsanzira anthu amene mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima, analandira zinthu zimene Mulungu analonjeza monga cholowa chawo.’​—Aheb. 6:10-12.

MUZILIMBITSA CHIKHULUPIRIRO CHANU

15. Kodi kulimbitsa chikhulupiriro chathu kungatithandize bwanji kuti tisasiye kugwira ntchito yolalikira?

15 Timakhulupirira kwambiri uthenga umene timalalikira, choncho timafunitsitsa kuuzako anthu ena mmene tingathere. Timakhulupiriranso kuti malonjezo amene amapezeka m’Baibulo adzakwaniritsidwa. (Sal. 119:42; Yes. 40:8) Taonanso maulosi ambiri a m’Baibulo akukwaniritsidwa masiku ano. Komanso taona anthu akusintha moyo wawo chifukwa choti ayamba kutsatira mfundo za m’Baibulo. Zimenezi zimatithandiza kutsimikizira kuti uthenga wabwino ndi ofunika kwa munthu aliyense.

16. Mogwirizana ndi Salimo 46:1-3, kodi kukhulupirira Yehova komanso Yesu kungatithandize bwanji kuti tipitirizebe kulalikira?

16 Timakhulupiriranso Yehova yemwe ndi mwini wake wa uthenga umene timalalikirawu komanso timakhulupirira Yesu yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. (Yoh. 14:1) Kaya tikukumana ndi zotani, Yehova adzakhalabe pothawira pathu ndi mphamvu yathu. (Werengani Salimo 46:1-3) Komanso sitikukayikira kuti Yesu akupitirizabe kutsogolera ntchito yolalikira, pogwiritsa ntchito mphamvu zimene Yehova anamupatsa.​—Mat. 28:18-20.

17. Perekani chitsanzo chosonyeza chifukwa chake tiyenera kupitirizabe kugwira ntchito yolalikira?

17 Chikhulupiriro chimatithandiza kuti tisamakaikire kuti Yehova adzadalitsa khama lathu ndipo nthawi zina angachite zimenezi m’njira imene sitimayembekezera. (Mlal. 11:6) Mwachitsanzo, tsiku lililonse anthu ambiri amadutsa pamalo amene timalalikira, pogwiritsa ntchito matebulo komanso mashelefu. Kodi njira yolalikirira imeneyi ndi yothandiza? Kwambiri! Mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2014, muli nkhani ya mtsikana yemwe ankaphunzira pa yunivesite ina ndipo ankafuna kulemba nkhani yokhudza a Mboni za Yehova. Mtsikanayo analephera kupeza kumene kunali Nyumba ya Ufumu, koma pasukulu yawo yomweyo anaona tebulo yokhala ndi mabuku yomwe abale ndi alongo ena ankagwiritsa ntchito polalikira. Patebuloyo anapezapo zimene ankafuna kuti alembe nkhani yake. Patapita nthawi anabatizidwa n’kukhala wa Mboni ndipo panopa ndi mpainiya wokhazikika. Nkhani ngati zimenezi zimatilimbikitsa kuti tipitirizebe kulalikira, chifukwa zimasonyeza kuti pali anthu ambiri amene akufuna kumva uthenga wabwino.

MUSAPUMITSE MANJA ANU

18. N’chifukwa chiyani sitikayikira kuti ntchito yolalikira idzatha pa nthawi imene Yehova akufuna?

18 Timadziwa kuti ntchito yolalikira idzatha pa nthawi yake. Taganizirani zimene zinachitika mu nthawi ya Nowa. Yehova anasonyeza kuti amachita zinthu pa nthawi yake. Zaka 120 chigumula chisanachitike, Yehova anaikiratu nthawi yakuti chidzayambe. Patadutsa zaka zambiri, Yehova anauza Nowa kuti amange chingalawa. Mwina kwa zaka 40 kapena 50 chigumula chisanachitike, Nowa anapitirizabe kugwira ntchito mwakhama. Ngakhale anthu sankamvetsera, iye anapitirizabe kuwachenjeza mpaka pamene Yehova anamuuza kuti ayambe kulowetsa zinyama m’chingalawacho. Kenako nthawi yake itakwana “Yehova anatseka chitseko.”​—Gen. 6:3; 7:1, 2, 16.

19. Kodi ndi zinthu ziti zimene zichitike posachedwapa?

19 Posachedwapa Yehova atiuza kuti ntchito yolalikira yafika pamapeto, kenako adzaononga dziko la Satanali n’kubweretsa dziko latsopano, lomwe mudzakhale anthu amene amamvera Mulungu. Kufikira nthawi imeneyo, tiyeni tipitirizebe kutsanzira Nowa, Habakuku ndi atumiki ena omwe sanapumitse manja awo. Choncho tiyeni tipitirize kumaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri. Tipitirizenso kukhala oleza mtima komanso kulimbitsa chikhulupiriro chathu mwa Yehova ndi malonjezo ake.

NYIMBO NA. 75 “Ine Ndilipo Nditumizeni!”

^ ndime 5 Ophunzira Baibulo omwe akusintha moyo wawo, analimbikitsidwa munkhani yapita ija kuti ayambe kulalikira uthenga wabwino. Munkhaniyi tikambirana zinthu zitatu zomwe zingathandize ofalitsa onse, atsopano komanso akale, kuti apitirizebe kugwira ntchito yolalikira uthenga wabwino, mpaka Yehova atanena kuti ntchitoyi yafika kumapeto.

^ ndime 2 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Munkhaniyi, mawu akuti “dzanja lako lisapume” akutanthauza kuti tiyenera kupitirizabe kugwira ntchito yolalikira uthenga wabwino, mpaka Yehova atanena kuti yafika kumapeto.

^ ndime 5 “Tsiku la Ambuye” linayamba pamene Yesu anakhala Mfumu mu 1914, ndipo lidzatha kumapeto kwa ulamuliro wake wa zaka 1,000.