NKHANI YOPHUNZIRA 36
Kodi Ndinu Okonzeka Kukhala Msodzi wa Anthu?
“Usachite mantha. Kuyambira lero uzisodza anthu amoyo.”—LUKA 5:10.
NYIMBO NA. 73 Tithandizeni Kukhala Olimba Mtima
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1. Kodi Yesu anauza chiyani asodzi 4, nanga asodziwo anachita chiyani?
OPHUNZIRA ena a Yesu monga Petulo, Andireya, Yakobo ndi Yohane ankagwira ntchito yausodzi. Tangoganizirani mmene anamvera pamene Yesu anawauza kuti: “Nditsatireni, ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.” * Kodi iwo anatani atamva zimenezi? Baibulo limanena kuti: “Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo n’kumutsatira.” (Mat. 4:18-22) Zimene anasankhazi zinasinthiratu moyo wawo. M’malo mogwira nsomba, iwo anayamba ‘kusodza anthu amoyo.’ (Luka 5:10) Masiku anonso, Yesu akupitiriza kuitana anthu a mitima yabwino omwe amakonda choonadi kuti akhale asodzi a anthu. (Mat. 28:19, 20) Kodi inuyo munavomera pamene Yesu anakuitanani kuti mukhale asodzi a anthu?
2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kusankha kukhala asodzi a anthu ndi nkhani yaikulu, nanga n’chiyani chingatithandize kusankha kuchita zimenezi?
2 N’kutheka kuti mwakhala mukuphunzira Baibulo ndipo mwasintha zinthu zambiri pa moyo wanu ndipo tsopano mukufunika kusankha ngati mukufuna kukhala wofalitsa wauthenga wabwino kapena ayi. Komabe ngati mukukayikira kuti simungakwanitse kuchita zimenezi, musataye mtima. N’kutheka kuti mukukayikira chifukwa mukudziwa kuti imeneyi ndi nkhani yaikulu. N’zoona kuti Baibulo limanena kuti Petulo komanso anzake aja, anasiya maukonde awo “nthawi yomweyo.” Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti Petulo ndi anzakewo anangosankha zinthu mopupuluma. Iwo anali atadziwa kale kuti Yesu ndi Mesiya miyezi 6 m’mbuyomo. (Yoh. 1:35-42) Mofanana ndi zimenezi, n’kutheka kuti nanunso mwaphunzira zambiri zokhudza Yehova komanso Yesu ndipo mukufuna kuti mupitirize kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Koma muyenera kuiganizira mosamala nkhaniyi musanasankhe zochita. Kodi n’chiyani chinathandiza Petulo, Andireya komanso ophunzira ena aja kuti asankhe kukhala otsatira a Yesu?
3. Kodi ndi makhalidwe ati amene angakuthandizeni kuti muzigwira bwino ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa ena?
3 Ophunzira oyambirira a Yesu ankakonda ntchito yawo yausodzi, ankaidziwa bwino, anali olimba mtima komanso anali opirira. Makhalidwe amenewa anawathandiza kwambiri kuti azigwira bwino ntchito yawo yolalikira uthenga wabwino. Munkhaniyi tikambirana zimene mungachite kuti nanunso mukhale ndi makhalidwe amenewa n’cholinga choti muzigwira bwino ntchito yolalikira uthenga wabwino komanso kuphunzitsa ena.
MUZIKONDA NTCHITO YOLALIKIRA
4. N’chifukwa chiyani Petulo ankagwira ntchito yausodzi?
4 Petulo ankagwira ntchito yausodzi kuti azisamalira banja lake koma zikuonekanso kuti ankaikonda kwambiri ntchito yakeyi. (Yoh. 21:3, 9-15) Koma kenako anayambanso kukonda ntchito yosodza anthu. Yehova anamuthandiza kwambiri kuti azigwira bwino ntchito imeneyi.—Mac. 2:14, 41.
5. Mogwirizana ndi Luka 5:8-11, n’chifukwa chiyani Petulo anachita mantha, nanga n’chiyani chingatithandize kuti nafenso tisamachite mantha?
5 Timalalikira chifukwa timakonda Yehova ndipo chimenechi n’chifukwa chachikulu chomwe timagwirira ntchito imeneyi. Kukonda Yehova kumatithandiza kuti tizigwirabe ntchito yolalikira ngakhale zitakhala kuti tikukayikira kuti sitingakwanitse. Pamene Yesu ankauza Petulo kuti akhale msodzi wa anthu anamuuza kuti: “Usachite mantha.” (Werengani Luka 5:8-11.) Pamenepa si kuti Petulo ankachita mantha ndi zimene zingachitike ngati atakhala wophunzira wa Yesu. M’malomwake, iye anadabwa kwambiri ndi kuchuluka kwa nsomba zimene Yesu anawathandiza kuti agwire. Iye anadziwa kuti Yesu wawathandiza kugwira nsombazo mozizwitsa ndipo zimenezi zinachititsa kuti azidziona kuti sanali woyenera kugwira ntchito ndi Yesu. Mofanana ndi Petulo, nanunso mukhoza kumachita mantha. Mwina mungamaone kuti simungakwanitse kuchita zonse zimene ophunzira a Khristu akuyenera kuchita. Ngati ndi choncho, yesetsani kuti muzikonda kwambiri Yehova, Yesu komanso anthu ena. Mukatero, mudzakhala ofunitsitsa kukhala msodzi wa anthu.—Mat. 22:37, 39; Yoh. 14:15.
6. Kodi ndi zifukwa zinanso ziti zimene zimatichititsa kuti tizigwira ntchito yolalikira?
6 Tiyeni tionenso zifukwa zina zimene zimatichititsa kuti tizigwira ntchito yolalikira. Timamvera lamulo la Yesu lakuti: “Pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga.” (Mat. 28:19, 20) Timalalikiranso kuti tithandize anthu “onyukanyuka ndi otayika,” amene amafunitsitsa kuphunzira choonadi chokhudza Ufumu wa Mulungu. (Mat. 9:36) Yehova amafuna kuti anthu kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.—1 Tim. 2:4.
7. Kodi lemba la Aroma 10:13-15, limasonyeza bwanji kuti ntchito yolalikira ndi yofunika?
7 Timafunitsitsa kugwira ntchito yolalikira chifukwa tikudziwa kuti idzathandiza anthu kuti adzapulumuke. Msodzi amagulitsa kapena kudya nsomba zimene wagwira. Koma ife timasodza anthu kapena kuti kuwathandiza kuti akhale ophunzira a Yesu n’cholinga choti adzapulumuke.—Werengani Aroma 10:13-15; 1 Timoteyo 4:16.
MUZIYESETSA KUIDZIWA BWINO NTCHITO YOLALIKIRA
8-9. Kodi msodzi ayenera kudziwa zinthu ziti, nanga n’chifukwa chiyani?
8 Mu nthawi ya Yesu, asodzi achiisiraeli ankafunika kudziwa mtundu wansomba zimene akufuna kugwira. (Lev. 11:9-12) Iwo ankafunikanso kudziwa kumene nsombazo zingapezeke. Nthawi zambiri nsomba zimapezeka malo amene kuli madzi abwino komanso zakudya zambiri. Koma kodi msodzi akhoza kupita nthawi iliyonse imene akufuna kuti akaphe nsomba? Mmishonale wina, yemwe amakhala pachilumba cha Pacific, anaphunzira kuti si nthawi iliyonse imene msodzi angapite kukapha nsomba. Tsiku lina m’bale wina wa kuderalo anam’pempha kuti apite kukapha nsomba. Ndiyeno mmishonaleyo anati, “tikumane mawa 9 koloko chakummawa.” Koma m’baleyo anayankha kuti, “Ayi, nsombatu sitipha choncho. Timapita nthawi imene nsombazo zingapezeke, osati nthawi imene ili yabwino kwa ifeyo.”
9 Ndi zimenenso asodzi a anthu a munthawi ya atumwi ankachita. Iwo ankapita m’malo amene anthu ankapezeka komanso pa nthawi imene angawapeze. Mwachitsanzo, otsatira a Yesu ankalalikira kukachisi, m’masunagoge, kunyumba ndi nyumba komanso m’misika. (Mac. 5:42; 17:17; 18:4) Nafenso tiyenera kuwadziwa bwino kwambiri anthu a m’gawo lathu. Tizikhala okonzeka kusintha zinthu pa moyo wathu kuti tizitha kulalikira pa nthawi komanso malo amene anthu angapezeke.—1 Akor. 9:19-23.
10. Kodi gulu la Yehova latipatsa zinthu ziti?
10 Msodzi amafunika kukhala ndi zipangizo zoyenerera komanso kudziwa mmene angazigwiritsire ntchito. Nafenso tiyenera kukhala ndi zipangizo zoyenerera zogwiritsa ntchito polalikira komanso kudziwa mmene tingazigwiritsire ntchito. Yesu anapereka malangizo omveka bwino kwa ophunzira ake a mmene angagwirire ntchito yolalikira. Anawauza zomwe ankafunika kutenga, komwe ankayenera kukalalikira komanso zoti akanene. (Mat. 10:5-7; Luka 10:1-11) Masiku ano, gulu la Yehova latipatsa Zinthu Zophunzitsira zimene zimatithandiza pogwira ntchito yolalikira. * Limatiphunzitsanso mmene tingazigwiritsire ntchito. Maphunziro amenewa amatithandiza kuti tizigwira ntchito yolalikira molimba mtima komanso mwaluso.—2 Tim. 2:15.
MUZILALIKIRA MOLIMBA MTIMA
11. N’chifukwa chiyani asodzi a anthu ayenera kukhala olimba mtima?
11 Asodzi amafunika kukhala olimba mtima. Nthawi zina amakumana ndi zinthu zomwe samayembekezera panyanja. Nthawi zambiri amagwira ntchito usiku ndiponso amatha kukumana ndi mphepo yoopsa. Nawonso asodzi a anthu amafunika kukhala olimba mtima. Tikangoyamba kulalikira komanso kudziwika monga wa Mboni za Yehova, tingakumane ndi mavuto ambiri. Mwachitsanzo, achibale athu angamatitsutse, anzathu angamatinyoze komanso ena angakane kumvetsera uthenga wathu. Koma sitiyenera kudabwa ndi zimenezi. Yesu anauza ophunzira ake kuti akamalalikira azidzakumana ndi anthu omwe azidzatsutsa uthenga wawo.—Mat. 10:16.
12. Mogwirizana ndi Yoswa 1:7-9, n’chiyani chingatithandize kukhala olimba mtima?
12 N’chiyani chingakuthandizeni kukhala olimba mtima? Choyamba, musamakayikire kuti Yesu akupitirizabe kutsogolera ntchito yolalikira. (Yoh. 16:33; Chiv. 14:14-16) Chachiwiri, muzikhulupirira zimene Yehova analonjeza zoti adzakusamalirani. (Mat. 6:32-34) Chikhulupiriro chanu chikamalimba, m’pamenenso mumayamba kukhala olimba mtima kwambiri. Petulo ndi anzake aja anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro cholimba pamene anasiya ntchito yawo yausodzi n’kuyamba kutsatira Yesu. Inunso munasonyeza kuti muli ndi chikhulupiriro cholimba pamene munauza anzanu komanso achibale anu kuti mwayamba kuphunzira Baibulo komanso kusonkhana ndi a Mboni za Yehova. Sitikukayikira kuti mwasintha zinthu zambiri pa moyo wanu kuti muzitsatira mfundo zolungama za Yehova. Kuchita zimenezi kumafunanso chikhulupiriro komanso kulimba mtima. Mukamapitiriza kuchita zinthu molimba mtima, musamakayikire kuti ‘Yehova Mulungu adzakhala nanu kulikonse kumene mungapite’.—Werengani Yoswa 1:7-9.
13. Kodi pemphero komanso kuganizira zimene Yehova wakhala akuchita m’mbuyomu, zingakuthandizeni bwanji kukhala olimba mtima?
13 Kodi chinanso n’chiyani chomwe chingakuthandizeni kukhala olimba mtima? Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala olimba mtima. (Mac. 4:29, 31) Yehova adzayankha mapemphero anu ndipo sadzakusiyani. Nthawi zonse iye ndi wokonzeka kukuthandizani. Komanso mukhoza kumaganizira mmene Yehova anapulumutsira anthu ena m’mbuyomu. Muziganiziranso mmene anakuthandizirani pa nthawi imene munkakumana ndi mavuto. Musamaiwale kuti anakupatsani mphamvu kuti muthe kusintha moyo wanu. Sitikukayikira kuti Mulungu amene anaolotsa anthu ake pa Nyanja Yofiira, angakuthandizeni kuti mukhale wophunzira wa Khristu. (Eks. 14:13) Muzikhulupirira kwambiri Yehova ngati mmene ankachitira wamasalimo yemwe anati: “Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa. Munthu wochokera kufumbi angandichite chiyani?”—Sal. 118:6.
14. Kodi mwaphunzira chiyani pa zimene zinachitikira mlongo Masae komanso Tomoyo?
14 Chinthu china chimene chingakuthandizeni kukhala olimba mtima ndi kuganizira mmene Yehova wathandizira anthu ena omwe mwachibadwa ndi amanyazi. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina dzina lake Masae. Iye anali wamanyazi ndipo ankaona kuti sangakwanitse kugwira ntchito yolalikira. Ankaona kuti kulankhulana ndi munthu yemwe sukumudziwa ndi kovuta ngati kukwera mpanda wautali kwambiri ndipo ankaganiza kuti sangakwanitse. Ngakhale zinali choncho iye anayesetsa kuti azikonda kwambiri Mulungu komanso anthu ena. Anazindikira kuti ntchito yolalikira ikufunika kugwiridwa mwansanga ndipo anapempha Yehova kuti amuthandize kuti azikonda kulalikira. Kenako anasiya kuchita mantha moti anachitapo upainiya wokhazikika. Yehova akhozanso kuthandiza ofalitsa atsopano kuti akhale ‘olimba mtima.’ Taganizirani zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Tomoyo. Tsiku limene anayamba kulalikira kunyumba ndi nyumba anakumana ndi munthu wovuta. Atangowaona, munthuyo anakalipa kuti: “Sindifuna kuti a Mboni za Yehova azibwera pakhomo panga pano.” Kenako anamenyetsa chitseko. Tomoyo sanachite mantha moti anauza mnzake amene anayenda naye kuti: “Wamva zimene munthu uja wanena? Sindinalankhule chilichonse koma anazindikira kuti ndine wa Mboni za Yehova. Zimenezi zandisangalatsa kwambiri.” Panopa Tomoyo ndi mpainiya wokhazikika.
MUZIKHALA OPIRIRA
15. N’chifukwa chiyani asodzi amafunika kukhala opirira, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi n’zofunikanso kwa Akhristu?
15 Asodzi omwe zinthu zimawayendera bwino amakhala opirira. Amachita zonse zimene angathe kuti ntchito yawo iyende bwino. Mwachitsanzo, amadzuka m’mawa kwambiri, amagwirabe ntchito mpaka atamaliza ndipo amachita zimenezi ngakhale pamene nyengo sili bwino. Nafenso timafunika kupilira kuti tigwire ntchito yathu mpaka pamapeto.—Mat. 10:22.
16. Kodi tingatani kuti tikhale opirira?
16 Kupirira si khalidwe limene timabadwa nalo. Nthawi zambiri anthufe timafuna kumangochita zinthu zomwe ndi zophweka. Komabe nthawi zina zinthu zofunika kwambiri sizimakhala zophweka. Choncho timafunika kupirira kuti tizichite. N’chifukwa chake timafunika kudziphunzitsa kuti tizitha kuchita zinthu zovuta. Yehova angatithandize kuchita zimenezi pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera.—Agal. 5:22, 23.
17. Malinga ndi 1 Akorinto 9:25-27, kodi mtumwi Paulo ankachita chiyani posonyeza kuti anali wopirira?
17 Mtumwi Paulo anali munthu wopirira. Iye anavomereza kuti ‘ankamenya’ thupi lake kuti azichita zinthu zoyenera. (Werengani 1 Akorinto 9:25-27.) Iye analimbikitsanso ena kuti azisonyeza khalidweli komanso kuti azichita zinthu zonse “moyenera ndi mwadongosolo.” (1 Akor. 14:40) Tiyenera kumachita khama kuti tizitumikira Yehova. Zimenezi zikuphatikizapo kulalikira uthenga wabwino komanso kuphunzitsa anthu nthawi zonse.—Mac. 2:46.
MUSAMAZENGEREZE
18. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova aziona kuti zinthu zikutiyendera bwino pa ntchito yathu yolalikira?
18 Msodzi amaona kuti zinthu zamuyendera bwino akagwira nsomba zambiri. Mosiyana ndi zimenezi, ifeyo sitiona kuti zinthu zikutiyendera bwino potengera kuchuluka kwa anthu omwe tawathandiza kuti alowe m’gulu la Mulungu. (Luka 8:11-15) Tikamapitiriza kulalikira uthenga wabwino komanso kuphunzitsa ena, Yehova amaona kuti zinthu zikutiyendera bwino. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa timakhala tikumumvera komanso tikumvera Mwana wake.—Maliko 13:10; Mac. 5:28, 29.
19-20. Kodi tili ndi chifukwa chapadera chiti chotichititsa kuti tizilalikira kwambiri panopa?
19 M’mayiko ena anthu saloledwa kusodza m’miyezi inayake. M’mayiko ngati amenewa, asodzi amalimbikira ntchito yawo miyezi imeneyi ikamayandikira. Monga asodzi a anthu, nafenso tikufunika kulimbikira kugwira ntchito yolalikira panopa. Tikutero chifukwa mapeto a dzikoli akuyandikira. Kwatsala kanthawi kochepa kuti tigwire ntchito yolalikirayi, yomwe ingapulumutse anthu. Choncho musamadikire kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino pa moyo wanu kuti muyambe kugwira nawo ntchito yofunikayi.—Mlal. 11:4.
20 Muyenera kuyesetsa panopa kuti muzikonda kwambiri ntchito yolalikira, muzidziwa bwino mfundo za m’Baibulo, muzigwira ntchito yolalikira molimba mtima komanso muzikhala opirira. Mukatero mudzakhala m’gulu la anthu oposa 8 miliyoni amene amalalikira uthenga wabwino padziko lonse ndipo mudzakhala ndi chimwemwe chimene Yehova amapereka. (Neh. 8:10) Muzilalikira mmene mungathere mpaka pamene Yehova adzanene kuti ntchitoyi yafika kumapeto. Munkhani yotsatira, tidzakambirana zinthu zitatu zimene zingatithandize kuti tipitirizebe kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.
NYIMBO NA. 66 Lengezani Uthenga Wabwino
^ ndime 5 Yesu anauza asodzi odzichepetsa komanso akhama kuti akhale ophunzira ake. Masiku anonso, Yesu akuitana anthu a makhalidwe ngati amenewa kuti akhale asodzi a anthu. Munkhaniyi tikambirana zimene ophunzira Baibulo angachite ngati akukayikira kuti sangakwanitse kukhala ophunzira a Yesu n’kumagwira nawo ntchito yolalikira uthenga wabwino.
^ ndime 1 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Mawu akuti “asodzi a anthu” akutanthauza anthu onse omwe amalalikira uthenga wabwino komanso kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Khristu.
^ ndime 10 Onani nkhani yakuti “Tiziphunzitsa Mfundo za Choonadi,” mu Nsanja ya Olonda ya October 2018, tsa. 11-16.
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA