NKHANI YOPHUNZIRA 38
Muzichita Zinthu Mwanzeru pa Nthawi Yomwe Zinthu Zikuyenda Bwino
“M’dzikolo munalibe chosokoneza chilichonse, komanso palibe anachita naye nkhondo pa zaka zimenezi, chifukwa Yehova anam’patsa mpumulo.”—2 MBIRI 14:6.
NYIMBO NA. 60 Akamvera Adzapeza Moyo
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1. Kodi ndi pa nthawi iti pomwe zimakhala zovuta kutumikira Yehova?
KODI ndi nthawi iti yomwe zingakhale zovuta kutumikira Yehova? Kodi ndi pa nthawi yomwe mukukumana ndi mavuto kapena ndi pa nthawi yomwe zinthu zikuyenda bwino? Tikakumana ndi mavuto zimakhala zosavuta kudalira Yehova. Koma kodi timatani zinthu zikamayenda bwino? Kodi timaiwala kuti kutumikira Mulungu n’kofunika? Yehova amadziwa kuti zimenezi zingachitike. N’chifukwa chake anachenjeza Aisiraeli.—Deut. 6:10-12.
2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Asa ndi chitsanzo chabwino?
2 Mfumu Asa ndi chitsanzo chabwino chifukwa anachita zinthu mwanzeru podalira Yehova ndi mtima wake wonse. Iye anatumikira Yehova pa nthawi yovuta komanso pa nthawi imene zinthu zinali bwino. Kuyambira ali wamng’ono, “Asa anatumikira Yehova ndi mtima wathunthu.” (1 Maf. 15:14.) Asa anasonyeza kuti ankatumikira Yehova ndi mtima wonse pamene anathetsa kulambira konyenga ku Yuda. Baibulo limanena kuti “iye anachotsa maguwa ansembe achilendo, anagwetsa malo okwezeka, anaphwanya zipilala zopatulika ndi kudula mizati yopatulika.” (2 Mbiri 14:3, 5) Anachotsanso agogo ake aakazi a Maaka pa udindo wawo monga amayi a mfumu. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Chifukwa chakuti agogo akewo ankalimbikitsa anthu kulambira fano.—1 Maf. 15:11-13.
3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
3 Asa anachita zinthu zinanso zambiri. Mwachitsanzo, anathandiza anthu a ku Yuda kuti ayambirenso kutumikira Yehova. Yehova anadalitsa Asa komanso anthu a ku Yuda powapatsa mtendere. * Kwa zaka 10 mu ulamuliro wake, “m’dzikolo munalibe chosokoneza chilichonse.” (2 Mbiri 14:1, 4, 6) Munkhaniyi tikambirana zimene Asa anachita pa nthawi ya mtendereyi. Kenako tikambirana chitsanzo cha Akhristu a m’nthawi ya atumwi, omwe mofanana ndi Asa, anachita zinthu mwanzeru pa nthawi ya mtendere. Pomaliza tiyankha funso lakuti: Kodi mungachite bwanji zinthu mwanzeru ngati m’dziko lomwe mukukhala, boma silinaletse ntchito yathu?
ZIMENE ASA ANACHITA PA NTHAWI YA MTENDERE
4. Malinga ndi 2 Mbiri 14:2, 6, 7, kodi Asa anagwiritsa ntchito bwanji nthawi ya mtendere?
4 Werengani 2 Mbiri 14:2, 6, 7. Asa anauza anthu kuti Yehova ndi amene ‘anawapatsa mpumulo pakati pa adani awo onse owazungulira.’ Iye sankaona kuti nthawi ya mtendereyi inali nthawi yoti azingosangalala. M’malo mwake anayamba kumanga mizinda, mipanda, nsanja komanso mageti. Iye anauza anthu a ku Yuda kuti: “Malo m’dzikoli akadalipo.” Kodi Asa ankatanthauza chiyani? Iye ankatanthauza kuti m’dzikolo munalibe adani omwe akanawalepheretsa kuti aziyenda komanso kumanga mwaufulu. Iye analimbikitsa anthuwo kuti agwiritse ntchito bwino nthawi ya mtendereyi.
5. N’chifukwa chiyani Asa anawonjezera gulu lake la nkhondo?
5 Asa anagwiritsanso ntchito nthawi ya mtendereyi powonjezera gulu lake la nkhondo. (2 Mbiri 14:8) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti sankadalira Yehova? Ayi. M’malomwake, Asa ankadziwa kuti ndi udindo wake monga mfumu kuthandiza anthu kuti akonzekere mavuto amene akanabwera m’tsogolo. Iye ankadziwa kuti mtendere womwe unalipowo sudzakhalapo mpaka kalekale ndipo n’zimene zinachitikadi.
ZIMENE AKHRISTU A M’NTHAWI YA ATUMWI ANACHITA PA NTHAWI YA MTENDERE
6. Kodi Akhristu a m’nthawi ya atumwi anagwiritsa ntchito bwanji nthawi ya mtendere?
6 Ngakhale kuti Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankazunzidwa, nthawi zina ankakhala pa mtendere. Ndiye kodi ankatani pa nthawi ya mtendereyi? Amuna ndi akazi okhulupirikawa ankalalikira uthenga wabwino mwakhama. Baibulo limanena kuti anthu amenewa ‘ankayenda moopa Yehova.’ Iwo anapitirizabe kulalikira uthenga wabwino, ndipo zotsatira zake zinali zakuti mpingowo unapitirizabe “kukulirakulira.” N’zoonekeratu kuti Yehova anadalitsa khama limene anasonyeza pa nthawi ya mtendereyi.—Mac. 9:26-31.
7-8. Kodi Paulo ndi anzake ankatani akapeza mwayi wolalikira? Fotokozani.
7 Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankagwiritsa ntchito mwayi uliwonse kuti azilalikira uthenga wabwino. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo ataona kuti angalalikire kwa anthu ambiri ku Efeso, anakhalabe mumzindawo n’kumalalikira.—1 Akor. 16:8, 9.
8 Paulo komanso Akhristu ena analinso ndi mwayi wolalikira kwa anthu ena mu 49 C.E. pamene atumwi ndi akulu ku Yerusalemu anathetsa nkhani ya mdulidwe. (Mac. 15:23-29) Paulo ndi anzake atadziwitsa mipingo zimene atumwi ndi akuluwo anasankha, anthu onse m’mipingo anayamba kulalikira mwakhama “uthenga wabwino wa mawu a Yehova.” (Mac. 15:30-35) Kodi zotsatira zake zinali zotani? Baibulo limanena kuti “mipingo inapitiriza kulimba m’chikhulupiriro ndipo chiwerengero chinapitiriza kuwonjezeka tsiku ndi tsiku.”—Mac. 16:4, 5.
MUZIGWIRITSA NTCHITO BWINO NTHAWI YA MTENDERE
9. Kodi zinthu zili bwanji m’mayiko ambiri? Nanga tingadzifunse funso lotani?
9 M’mayiko ambiri abale athu amagwira ntchito yolalikira mwaufulu. Kodi umu ndi mmene zilili m’dziko lanu? Ngati ndi choncho mungachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ufulu umenewu ndikuugwiritsa ntchito bwanji?’ Masiku otsiriza ano ndi nthawi yosangalatsa kwa anthu a Yehova, chifukwa iwo akuchita khama kugwira ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu, yomwe ikupita patsogolo kwambiri. (Maliko 13:10) Pali zinthu zambiri zomwe tingachite pogwira ntchito imeneyi.
10. Kodi lemba la 2 Timoteyo 4:2 limatilimbikitsa kuchita chiyani?
10 Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mwanzeru nthawi imene tili pa mtendere? (Werengani 2 Timoteyo 4:2.) Mungachite bwino kuona mmene zinthu zilili pa moyo wanu, kapena kusintha zina ndi zina kuti inuyo kapena wina m’banja mwanu, awonjezere zochita mu utumiki, mwina kuchita upainiya. Ino si nthawi yomasonkhanitsa chuma kapena zinthu. Tikutero chifukwa zinthu zimenezi sitingadzapulumuke nazo limodzi pa chisautso chachikulu.—Miy. 11:4; Mat. 6:31-33; 1 Yoh. 2:15-17.
11. Kodi ofalitsa ena achita chiyani kuti azilalikira uthenga wabwino kwa anthu ambiri?
11 Ofalitsa ambiri aphunzira chinenero china kuti azichigwiritsa ntchito polalikira komanso kuphunzitsa anthu. Gulu la Yehova limatipatsa zinthu zambiri zomwe zimatithandiza kuti tizilalikira m’zinenero zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, m’chaka cha 2010, mabuku athu ankapezeka m’zinenero pafupifupi 500. Koma pofika pano, mabukuwa amapezeka m’zinenero zoposa 1,000.
12. Kodi anthu amakhudzidwa bwanji akamva uthenga wa Ufumu m’chinenero chawo? Perekani chitsanzo.
12 Kodi anthu zimawakhudza bwanji akamva uthenga wa m’Mawu a Mulungu m’chinenero chawo? Taganizirani za chitsanzo cha mlongo wina yemwe anasangalala kwambiri ndi msonkhano wachigawo womwe unachitikira mumzinda wa Memphis, ku Tennessee, m’dziko la United States. Msonkhanowo unachitika m’Chikinyarwanda, chinenero chimene chimalankhulidwa ku Rwanda, Congo (Kinshasa), ndi ku Uganda. Msonkhanowo utatha, mlongoyo ananena kuti: “Aka ndi koyamba kuti ndithe kumvetsa bwinobwino mfundo zonse za pamsonkhano kuchokera pamene ndinabwera ku United States kuno zaka 17 zapitazo.” N’zoonekeratu kuti mfundo za pamsonkhanowu zinamufika pamtima mlongoyu chifukwa zinali m’chinenero chake. Ngati n’zotheka, kodi mungaphunzire chinenero china kuti muzithandiza anthu amene amalankhula chinenerocho m’gawo lanu? Ngati m’gawo lanu muli anthu amene amamva bwino chinenero chinachake, mungachite bwino kuchiphunzira kuti muziwathandiza. Mungapeze madalitso ambiri ngati mutayesetsa kuchita zimenezi.
13. Kodi abale athu a ku Russia anagwiritsa ntchito bwanji nthawi ya mtendere?
13 M’mayiko ena, abale athu alibe ufulu wolalikira. Izi zimachitika chifukwa nthawi zina maboma amatha kuletsa ntchito yathu yolalikira. Mwachitsanzo, taganizirani za abale athu ku Russia. Abalewa anazunzidwa kwa zaka zambiri. Koma m’mwezi wa March 1991, boma linawalola kuti azilambira mwaufulu. Pa nthawi imeneyo ku Russia kunali ofalitsa pafupifupi 16,000. Patadutsa zaka 20, chiwerengerochi chinawonjezeka n’kufika pa ofalitsa oposa 160,000. Pamenepa n’zoonekeratu kuti abale athuwa anachita zinthu mwanzeru pamene anali ndi mwayi wolalikira mwaufulu. Tikutero chifukwa chakuti nthawi ya mtendereyo sinapitirire. Koma ngakhale kuti zinthu zinasintha m’dziko lawo, akutumikirabe Yehova mwakhama. Amachita chilichonse chomwe angathe kuti azitumikira Yehova.
NTHAWI YA MTENDERE SIDZAKHALAPO MPAKA KALEKALE
14-15. Kodi Yehova anathandiza bwanji Asa?
14 Mu ulamuliro wa Asa, nthawi ya mtendere sinakhalepo mpaka kalekale. Gulu lalikulu la asilikali oposa 1 miliyoni linabwera kuchokera ku Itiyopiya. Mtsogoleri wa gululo, dzina lake Zera, ankaona kuti asilikali ake agonjetsa Yuda. Asa sankadalira kuchuluka kwa asilikali omwe anali nawo, koma ankadalira Mulungu wake Yehova. Iye anapemphera kuti: “Tithandizeni Yehova Mulungu wathu chifukwa tikudalira inu, ndipo tabwera m’dzina lanu kudzamenyana ndi khamuli.”—2 Mbiri 14:11.
15 Gulu la asilikali ochokera ku Itiyopiya linali lalikulu kuwirikiza kawiri kuposa gulu lankhondo la Asa. Komabe Asa ankadziwa kuti Yehova ndi wamphamvu ndipo akhoza kuthandiza anthu ake. Yehova sanagwiritse anthuwa fuwa la moto. Gulu lankhondo lochokera ku Itiyopiya lija linagonjetsedwa mochititsa manyazi.—2 Mbiri 14:8-13.
16. Kodi tikudziwa bwanji kuti nthawi ya mtendere sidzakhalapo mpaka kalekale?
16 Sitikudziwa kuti n’chiyani chomwe chidzatichitikire m’tsogolomu. Koma zimene tikudziwa n’zakuti mtendere umene anthu a Mulungu ali nawo panopa sudzakhalapo mpaka kalekale. Ndipotu Yesu ananeneratu kuti m’masiku otsiriza “mitundu yonse idzadana” ndi ophunzira ake. (Mat. 24:9) Nayenso mtumwi Paulo ananena kuti “onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.” (2 Tim. 3:12) Satana “ali ndi mkwiyo waukulu” ndipo kungakhale kudzinamiza kuganiza kuti tingamangoyenda moyera.—Chiv. 12:12.
17. Kodi tingakumane ndi mayesero otani m’tsogolomu?
17 Posachedwapa tonse tikumana ndi mayesero aakulu. Padzikoli padzachitika “chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko mpaka tsopano.” (Mat. 24:21) Pa nthawiyo, achibale athu akhoza kudzatiukira ndipo ntchito yathu ikhoza kudzaletsedwa. (Mat. 10:35, 36) Kodi pa nthawiyo aliyense wa ife azidzadalira Yehova kuti amuthandize ndi kumuteteza ngati mmene Asa anachitira?
18. Mogwirizana ndi Aheberi 10:38, 39, n’chiyani chingatithandize kukonzekera zomwe zikubwera m’tsogolo?
18 Yehova wakhala akutithandiza kukonzekera zinthu zimene zikubwera kutsogoloku. Iye akutsogolera “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azitipatsa “chakudya pa nthawi yoyenera” kuti tikhale olimba mwauzimu. (Mat. 24:45) Koma aliyense wa ife ayenera kuyesetsa kuti azikhulupirira kwambiri Yehova.—Werengani Aheberi 10:38, 39.
19-20. Mogwirizana ndi 1 Mbiri 28:9, kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi?
19 Mofanana ndi Mfumu Asa, tiyenera ‘kumafunafuna Yehova.’ (2 Mbiri 14:4; 15:1, 2) Timayamba kufunafuna Yehova tikamaphunzira za iye komanso kubatizidwa. Timachita zonse zimene tingathe kuti tizikonda kwambiri Yehova. Kuti tidziwe mmene timachitira pa nkhaniyi, tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimafika pamisonkhano nthawi zonse?’ Tikakhala pamisonkhano timapeza mphamvu zotithandiza kuti tipitirizebe kutumikira Yehova. (Mat. 11:28) Tingadzifunsenso kuti, ‘Kodi ndimaphunzira Baibulo pandekha nthawi zonse?’ Ngati mumakhala ndi banja lanu, kodi mumachita kulambira kwa pabanja mlungu uliwonse? Kapena ngati mumakhala nokha, kodi mumapeza nthawi yoti muziphunzira Mawu a Mulungu mlungu uliwonse? Komanso kodi mumayesetsa kugwira nawo ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu?
20 N’chifukwa chiyani tikufunika kudzifunsa mafunso amenewa? Baibulo limanena kuti Yehova amafufuza zimene zili m’maganizo mwathu komanso m’mitima yathu. Nafenso tiyenera kuchita zomwezo. (Werengani 1 Mbiri 28:9.) Ndiye tikaona kuti tikufunika kusintha zolinga zimene tili nazo, komanso mmene timaganizira tizipempha Yehova kuti atithandize. Inoyo ndi nthawi yoti tizikonzekera mayesero amene akubwera kutsogolo. Musalole kuti chilichonse chikulepheretseni kugwiritsira ntchito mwanzeru nthawi ya mtendere.
NYIMBO NA. 62 Nyimbo Yatsopano
^ ndime 5 Kodi mumakhala m’dziko lomwe mumatha kulambira Yehova mwaufulu? Ngati ndi choncho, kodi mukuigwiritsa ntchito bwanji nthawi ya mtendereyi? Nkhaniyi ikuthandizani kuona zomwe mungachite kuti muzitsanzira Asa yemwe anali Mfumu ya Yuda komanso Akhristu a munthawi ya atumwi. Anthu amenewa anachita zinthu mwanzeru pa nthawi imene zinthu zinali bwino.
^ ndime 3 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Mawu akuti “mtendere” sakungotanthauza nthawi imene kulibe nkhondo. Mawu a Chiheberi omwe anamasuliridwa kuti mtendere amatanthauzanso kukhala ndi thanzi, chitetezo komanso moyo wabwino.
^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mfumu Asa anachotsa agogo ake aakazi paudindo wokhala amayi a mfumu chifukwa ankalimbikitsa kulambira konyenga. Anthu amene anali kumbali ya Asa, anatengera chitsanzo chake powononga mafano.
^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Banja likusintha zinthu zina pa moyo wawo kuti likatumikire kumene kukufunika ofalitsa ambiri.
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA