NKHANI YOPHUNZIRA 40

“Muziteteza Zinthu Zimene Mulungu Wakupatsani”

“Muziteteza Zinthu Zimene Mulungu Wakupatsani”

“Timoteyo, sunga bwino chimene chinaikidwa m’manja mwako.”​1 TIM. 6:20.

NYIMBO NA. 29 Tizichita Zinthu Zogwirizana ndi Dzina Lathu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Mogwirizana ndi 1 Timoteyo 6:20, kodi Timoteyo anapatsidwa chiyani?

NTHAWI zambiri timasungitsa ena zinthu zathu zamtengo wapatali. Mwachitsanzo, timasungitsa ndalama zathu kubanki. Tikatero, timakhulupirira kuti ndalamazo sizingasowe kapena kubedwa. Choncho n’zosavuta kuti timvetse zimene kusungitsa munthu wina zinthu zimene timaona kuti ndi zamtengo wapatali kumatanthauza.

2 Werengani 1 Timoteyo 6:20. Mtumwi Paulo anakumbutsa Timoteyo kuti anapatsidwa chinthu chinachake chamtengo wapatali, chomwe ndi choonadi chokhudza cholinga chimene Mulungu ali nacho kwa anthu. Timoteyo anapatsidwanso mwayi ‘wolalikira mawu’ komanso ‘wogwira ntchito ya mlaliki.’ (2 Tim. 4:2, 5) Choncho Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti aziteteza zinthu zimene anapatsidwa. Mofanana ndi Timoteyo, nafenso tapatsidwa zinthu zamtengo wapatali. Kodi zinthu zake ndi ziti? Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuteteza zinthu zamtengo wapatali zimene Yehova watipatsa?

TAPATSIDWA CHOONADI CHAMTENGO WAPATALI

3-4. N’chifukwa chiyani choonadi cha m’Baibulo ndi chamtengo wapatali?

3 Yehova anatipatsa choonadi chamtengo wapatali chomwe chimapezeka m’Mawu ake, Baibulo. Choonadichi ndi chamtengo wapatali chifukwa chimatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova. Komanso chimafotokoza zimene tingachite kuti tikhale osangalala. Tikaphunzira choonadi n’kumayesetsa kutsatira mfundo zake, timamasuka ku ukapolo wa ziphunzitso zabodza komanso makhalidwe oipa.​—1 Akor. 6:9-11.

4 Chinanso chimene chimachititsa kuti choonadi cha m’Mawu a Mulungu chikhale chamtengo wapatali ndi choti Yehova amachiulula kwa anthu odzichepetsa komanso amene ali ndi “maganizo abwino.” (Mac. 13:48) Anthu odzichepetsawa amavomereza kuti kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ndi amene amatiphunzitsa mfundo za m’Baibulo masiku ano. (Mat. 11:25; 24:45) Sitingathe kumvetsa Baibulo popanda kuthandizidwa ndipo palibe chinthu chamtengo wapatali kuposa kumvetsa mfundo za m’Baibulo.​—Miy. 3:13, 15.

5. Kodi Yehova watipatsanso chinthu china chiti?

5 Yehova watipatsanso mwayi wophunzitsa ena choonadi chokhudza iyeyo komanso zolinga zake. (Mat. 24:14) Uthenga umene timalalikira ndi wamtengo wapatali, chifukwa umathandiza anthu kukhala m’banja la Yehova komanso umawathandiza kuti adzapeze moyo wosatha. (1 Tim. 4:16) Ndiye kaya timakwanitsa kuchita zambiri mu utumiki kapena ayi, tikuthandiza pa ntchito yofunika kwambiri imene ikuchitika masiku ano. (1 Tim. 2:3, 4) Ndi mwayi waukulu kukhala antchito anzake a Mulungu.​—1 Akor. 3:9.

MUSATAYE ZIMENE MWAPATSIDWA

Timoteyo anapitiriza kutumikira Yehova pa nthawi imene ena anasankha kusiya kumutumikira (Onani ndime 6)

6. Kodi n’chiyani chinachitikira anthu ena omwe anasiya kuyamikira zinthu zimene anapatsidwa?

6 Mu nthawi ya Timoteyo, Akhristu ena sanayamikire mwayi umene anali nawo wokhala antchito anzake a Mulungu. Mwachitsanzo, Dema anataya mwayi wake wotumikira limodzi ndi Paulo chifukwa chokonda zinthu za m’dzikoli. (2 Tim. 4:10) Zikuoneka kutinso Fugelo ndi Heremogene nawonso anasiya utumiki wawo chifukwa choopa kuti adzazunzidwa ngati mmene Paulo anazunzidwira. (2 Tim. 1:15) Hemenayo, Alekizanda ndi Fileto anayamba mpatuko ndipo anasiya choonadi. (1 Tim. 1:19, 20; 2 Tim. 2:16-18) Poyamba anthu onsewa ankakonda Yehova, koma kenako anasiya kuona kuti zinthu zimene anapatsidwa ndi zamtengo wapatali.

7. Kodi Satana amagwiritsa ntchito njira ziti pofuna kuti tizichita zofuna zake?

7 Kodi Satana amachita zotani pofuna kutitayitsa zinthu zamtengo wapatali zimene Yehova watipatsa? Tiyeni tione zina mwa njira zimene amagwiritsa ntchito. Iye amagwiritsa ntchito zosangalatsa komanso zinthu ngati TV, mafilimu, intaneti, manyuzipepala, mabuku ndi magazini. Amachita zimenezi pofuna kutichititsa kuti tiziganiza komanso kuchita zinthu m’njira imene ingachititse kuti tisiye kukonda Yehova ndiponso kumvera malamulo ake. Iye amayesa kutiopseza pogwiritsa ntchito anzathu kapena kutizunza kuti tisiye kulalikira. Amayesanso kutikopa kuti tizimvetsera zinthu zimene ampatuko “monama amati ndiye ‘kudziwa zinthu,’” n’cholinga choti tisiye choonadi.​—1 Tim. 6:20, 21.

8. Kodi zimene zinachitikira M’bale Daniel zikutiphunzitsa chiyani?

8 Ngati sitingasamale, tingayambe kusiya choonadi pang’onopang’ono. Chitsanzo ndi m’bale wina dzina lake Daniel, * yemwe ankakonda masewera apakompyuta. Iye anati: “Ndinayamba kuchita masewera apakompyuta ndili ndi zaka pafupifupi 10. Poyamba, ndinkachita masewera omwe ankaoneka kuti ndi abwinobwino koma pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kuchita masewera amene anali achiwawa komanso a zamizimu.” Kenako m’baleyu anayamba kuchita masewerawa kwa maola pafupifupi 15, tsiku lililonse. Iye anapitiriza kunena kuti: “Pansi pamtima ndinkadziwa kuti masewera amene ndinkachitawo komanso nthawi imene ndinkathera ndikuchita masewerawa, zinkachititsa kuti pang’ono ndi pang’ono ubwenzi wanga ndi Yehova usokonekere. Masewerawo anandisokoneza kwambiri moti ndinayamba kuona kuti sindikufunikiranso kumatsatira zimene Baibulo limanena.” Zimenezi zikusonyeza kuti ngati sitingasamale, zosangalatsa zingatichititse kuti tisiye kugwira mwamphamvu choonadi. Ngati zimenezi zitachitika, tikhoza kutaya zinthu zamtengo wapatali zimene Yehova watipatsa.

ZIMENE TINGACHITE KUTI TIGWIRE MWAMPHAMVU CHOONADI

9. Mogwirizana ndi 1 Timoteyo 1:18, 19, kodi Paulo anayerekezera Timoteyo ndi ndani?

9 Werengani 1 Timoteyo 1:18, 19. Paulo anayerekezera Timoteyo ndi msilikali ndipo anamulimbikitsa kuti apitirize “kumenya nkhondo yabwino.” Nkhondo imene Paulo ankanena inali yauzimu. Kodi Akhristu amafanana bwanji ndi asilikali amene akumenya nkhondo ndipo monga asilikali a Khristu tiyenera kukhala ndi makhalidwe ati? Tiyeni tikambirane zinthu 5 zimene tikuphunzira kuchokera m’chitsanzo cha Paulo. Zinthu zimenezi zingatithandize kuti tigwire mwamphamvu choonadi.

10. Kodi munthu wodzipereka kwa Mulungu amachita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani nafenso tiyenera kukhala odzipereka kwa Mulungu?

10 Muzikhala odzipereka kwa Mulungu. Msilikali wabwino amakhala wokhulupirika. Iye amamenya nkhondo mwamphamvu pofuna kuteteza anthu amene amawakonda komanso zinthu zimene amaziona kuti ndi zamtengo wapatali. Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti akhale wodzipereka kwa Mulungu kapena kuti akhale wokhulupirika kwa Mulungu. (1 Tim. 4:7) Tikamakonda kwambiri Mulungu m’pamenenso timafunitsitsa kugwira mwamphamvu choonadi.​—1 Tim. 4:8-10; 6:6.

Pambuyo pogwira ntchito tsiku lonse, tingafunike kudzikakamiza kupita kumisonkhano koma timapeza madalitso ambiri tikamachita zimenezi (Onani ndime 11)

11. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tizichita zinthu zoyenera?

11 Muziyesetsa kuchita zinthu zoyenera. Msilikali amafunika kuchita khama kuti nthawi iliyonse azikhala wokonzeka kumenya nkhondo. Timoteyo anapitirizabe kukhala wolimba mwauzimu chifukwa anatsatira malangizo amene Paulo anamupatsa akuti athawe zilakolako zoipa, ayesetse kukhala ndi makhalidwe abwino komanso azicheza ndi Akhristu anzake. (2 Tim. 2:22) Kuchita zimenezi kumafuna kudziletsa. Timafunika kudziletsa kuti tipambane pankhondo yolimbana ndi zilakolako zathupi. (Aroma 7:21-25) Komanso timafunika kudziletsa kuti tipitirizebe kuvula umunthu wakale ndi kuvala watsopano. (Aef. 4:22, 24) Ndiponso pambuyo pogwira ntchito tsiku lonse timatopa, komabe timafunika kudzikakamiza kuti tikasonkhane.​—Aheb. 10:24, 25.

12. Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito bwino Baibulo?

12 Msilikali amayenera kuyeserera kugwiritsa ntchito zida zake. Kuti akhale ndi luso amafunika kumachita zimenezi nthawi zonse. Nafenso tiyenera kukhala aluso tikamagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. (2 Tim. 2:15) Tingaphunzire ena mwa malusowa pamisonkhano yathu. Koma kuti tithandize ena kukhulupirira kuti mfundo za m’Baibulo zingawathandize, tiyenera kumaliphunzira nthawi zonse. Tiyenera kumagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu polimbitsa chikhulupiriro chathu. Kuchita zimenezi kumafuna zambiri osati kungowerenga Baibulo. Kumafuna kuti tiziganizira mozama zimene tikuwerenga komanso kufufuza m’mabuku athu kuti tizimvetsa molondola Malemba n’kumawagwiritsa ntchito pa moyo wathu. (1 Tim. 4:13-15) Tikatero m’pamene tingakwanitse kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu pophunzitsa ena. Izi zikutanthauza kuti tiyenera kuchita zambiri osati kungowawerengera mavesi a m’Baibulo. Tiyenera kuthandiza anthuwo kumvetsa mavesiwo komanso mmene angawagwiritsire ntchito. Tikamayesetsa kuphunzira Baibulo patokha nthawi zonse, tikhoza kumagwiritsa ntchito bwino Mawu a Mulungu pophunzitsa ena.​—2 Tim. 3:16, 17.

13. Mogwirizana ndi Aheberi 5:14, n’chifukwa chiyani tiyenera kumachita zinthu mozindikira?

13 Muzikhala ozindikira. Msilikali amafunika kuganizira zinthu zoopsa zimene angakumane nazo komanso mmene angazipewere. Ifenso tiyenera kuzindikira zinthu zimene zingativulaze n’kumayesetsa kuzipewa. (Miy. 22:3; werengani Aheberi 5:14.) Mwachitsanzo, timafunika kusankha zosangalatsa mwanzeru. Nthawi zambiri pa TV komanso m’mafilimu amaonetsa zinthu zachiwerewere. Mulungu sasangalala ndi zinthu zimenezi ndipo ngati munthu atapitiriza kuonera mafilimu amenewa, akhoza kugwera m’mavuto. Timapewa zosangalatsa zoterezi chifukwa zikhoza kutichititsa kuti tisiye kukonda Yehova.​—Aef. 5:5, 6.

14. Kodi kuzindikira kunathandiza bwanji M’bale Daniel?

14 M’bale Daniel amene tamutchula kale uja, anazindikira kuti kuchita masewera apakompyuta achiwawa komanso a zamizimu n’koipa. Iye anafufuza mu Watchtower Library nkhani zimene zinamuthandiza kuti alimbane ndi vuto lakeli. Kodi zimenezi zinamuthandiza bwanji? M’baleyu anasiya kuchita masewera oipawa ndiponso anasiya kucheza ndi anzake omwe ankachita nawo masewerawo. Iye anati: “M’malo mochita masewerawa, ndinayamba kugwiritsa ntchito nthawi yanga pochita zinthu zina komanso kucheza ndi anzanga a mumpingo.” M’bale Daniel panopa ndi mpainiya komanso mkulu.

15. N’chifukwa chiyani kukhulupirira nkhani zabodza n’koopsa?

15 Mofanana ndi Timoteyo, nafenso tiyenera kuzindikira kuopsa kwa nkhani zabodza zimene ampatuko amafalitsa. (1 Tim. 4:1, 7; 2 Tim. 2:16) Mwachitsanzo, iwo angamafalitse nkhani zabodza zokhudza abale athu kapena kutichititsa kuti tiyambe kukayikira gulu la Yehova. Nkhani ngati zimenezi zingafooketse chikhulupiriro chathu. Tiyenera kupewa kukhulupirira mabodzawa. N’chifukwa chiyani tiyenera kutero? Chifukwa nkhani zabodzazi zimafalitsidwa ndi “anthu opotoka maganizo ndi osadziwa choonadi,” omwe cholinga chawo ndi “kukangana ndi anthu ndiponso kutsutsana pa mawu.” (1 Tim. 6:4, 5) Iwo amafuna kuti tizikhulupirira mabodza awowo n’kuyamba kukayikira abale athu.

16. Kodi tiyenera kupewa zinthu zosokoneza ziti?

16 Muzipewa zinthu zosokoneza. Monga “msilikali wabwino wa Khristu Yesu,” Timoteyo ankafunika kupewa kusokonezedwa ndi zinthu zina n’kumaika maganizo ake onse pa utumiki. (2 Tim. 2:3, 4) Mofanana ndi Timoteyo, nafenso tiyenera kupewa kulakalaka chuma. Tikutero chifukwa “chinyengo champhamvu cha chuma” chingatichititse kusiya kukonda Yehova, kuyamikira Mawu ake komanso kuuza ena Mawu akewo. (Mat. 13:22) Tiyenera kumakhala moyo wosalira zambiri n’kumagwiritsa ntchito nthawi yathu komanso mphamvu zathu kuti tipitirize “kufunafuna ufumu choyamba.”​—Mat. 6:22-25, 33.

17-18. Kodi tingatani kuti titeteze ubwenzi wathu ndi Yehova?

17 Muzikhala okonzeka kuchita zinthu mwamsanga. Msilikali amafunika kukonzekereratu zimene angachite kuti adziteteze. Ifenso kuti titeteze zinthu zimene Yehova watipatsa tiyenera kuchita zinthu mwamsanga tikaona zinthu zimene zingatisokoneze pomutumikira. Kodi n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezi? Tiyenera kukonzekereratu zimene tingachite kuti tidziteteze.

18 Mwachitsanzo, anthu akasonkhana muholo inayake kuti aonerere zochitika zinazake, zochitikazo zisanayambe amadziwitsidwa kumene kuli makomo otulukira patachitika ngozi. N’chifukwa chiyani amafunika kuchita zimenezi? Amatero kuti adzathe kuthawa mwamsanga ngati patachitika ngozi. Mofanana ndi zimenezi, nafenso tiyenera kuoneratu khomo lotulukira ngati mwadzidzidzi pogwiritsa ntchito intaneti, poonera filimu kapena poonera pulogalamu ya pa TV taona zinthu zolaula, zachiwawa kapena nkhani za ampatuko. Tikadziwiratu zoyenera kuchita ngati zoterezi zitachitika, tingathe kuchita zinthu mwamsanga poteteza ubwenzi wathu ndi Yehova kuti tikhalebe oyera pamaso pake.​—Sal. 101:3; 1 Tim. 4:12.

19. Kodi tingapeze madalitso otani tikamapitiriza kuteteza zinthu zamtengo wapatali zimene Yehova watipatsa?

19 Tiyenera kuteteza zinthu zamtengo wapatali zimene Yehova watipatsa zomwe ndi choonadi cha m’Baibulo komanso kuphunzitsa ena. Tikamachita zimenezi, tidzakhala ndi chikumbumtima choyera, moyo watanthauzo komanso tidzakhala osangalala chifukwa chothandiza ena kudziwa Yehova. Yehova adzatithandiza kuti tipitirizebe kuteteza zinthu zamtengo wapatali zimene watipatsa.​—1 Tim. 6:12, 19.

NYIMBO NA. 127 Mtundu wa Munthu Amene Ndiyenera Kukhala

^ ndime 5 Tili ndi mwayi waukulu wodziwa choonadi komanso kuphunzitsa ena. Nkhaniyi itithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tisataye mwayi umenewu.

^ ndime 8 Dzina lasinthidwa.