NKHANI YOPHUNZIRA 39

Munthu Amene Mumamukonda Akasiya Kutumikira Yehova

Munthu Amene Mumamukonda Akasiya Kutumikira Yehova

“Kawirikawiri . . . anali kumukhumudwitsa.”​—SAL. 78:40.

NYIMBO NA. 102 “Muthandize Ofookawo”

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi ena amamva bwanji munthu amene amamukonda akachotsedwa mumpingo?

KODI munthu wina amene mumamukonda anachotsedwapo mumpingo? Zimenezitu zimakhala zopweteka kwambiri. Mlongo wina dzina lake Hilda ananena kuti: “Mwamuna wanga wokhulupirika yemwe ndinakhala naye pabanja zaka 41 atamwalira, ndinkaona kuti chimenechi ndi chinthu chowawa kwambiri chimene sichinandichitikirepo. * Koma mwana wanga, mkazi wake komanso ana ake atasiya choonadi zinandiwawa kwambiri kuposa pamenepa.”

Yehova amamvetsa kuti zimakhala zowawa kwambiri munthu amene mumamukonda akasiya kumutumikira (Onani ndime 2-3) *

2-3. Mogwirizana ndi Salimo 78:40, 41, kodi Yehova amamva bwanji ena akasiya kumutumikira?

2 Taganizirani mmene Yehova zinamupwetekera kuona angelo ake ena akumupandukira. (Yuda 6) Ndiye taganiziraninso mmene ankamvera kuona anthu ake okondedwa Aisiraeli akumupandukira mobwerezabwereza. (Werengani Salimo 78:40, 41.) Musamakayikire kuti Atate wathu wachikondi zimamuwawanso munthu amene mumamukonda akasiya kumutumikira. Iye amamvetsa ululu umene mukumva mumtima mwanu. Mokoma mtima iye adzakulimbikitsani ndi kukuthandizani.

3 Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite kuti Yehova azitithandiza tikakumana ndi vuto limeneli. Tionanso mmene tingathandizire ena mumpingo, omwe achibale awo achotsedwa. Koma choyamba tiyeni tikambirane maganizo olakwika amene tiyenera kupewa.

MUZIPEWA KUDZIIMBA MLANDU

4. Kodi makolo ambiri amamva bwanji mwana wawo akasiya kutumikira Yehova?

4 Mwana akasiya kutumikira Yehova, kawirikawiri makolo amadziimba mlandu poganiza kuti pali zina zomwe akanachita kuti amuthandize kukhalabe m’choonadi. Mwana wake atachotsedwa, m’bale wina dzina lake Luke ananena kuti: “Ndinkaona kuti vuto ndi ineyo. Nthawi zina ndinkalota maloto oipa, ndinkalira komanso mtima unkandipweteka.” Mlongo wina dzina lake Elizabeth, yemwenso zimenezi zinamuchitikira ananena kuti: “Nthawi zina ndinkadzifunsa kuti, ‘kodi ndinalakwitsa chiyani monga mayi?’ Ndinkaona kuti ndinalephera kukhomereza choonadi mwa mwana wanga.”

5. Kodi limakhala vuto la ndani munthu akasiya kutumikira Yehova?

5 Tiyenera kukumbukira kuti tonsefe Yehova anatipatsa ufulu wosankha. Zimenezi zikutanthauza kuti aliyense angasankhe kumumvera kapena ayi. Ana ena omwe makolo awo sanali chitsanzo chabwino, amasankha kutumikira Yehova ndipo amakhalabe okhulupirika kwa iye. Pomwe ena omwe makolo awo anayesetsa kuwaphunzitsa mfundo za m’Malemba, akakula amasankha kusiya kutumikira Yehova. Zimenezi zikusonyeza kuti aliyense wa ife amafunika kusankha yekha kuti azitumikira Yehova. (Yos. 24:15) Choncho makolo amene muli ndi chisoni chifukwa choti ana anu asiya choonadi, musamaganize kuti limeneli ndi vuto lanu.

6. Kodi mwana angamve bwanji ngati mayi kapena bambo ake asiya kutumikira Mulungu?

6 Nthawi zina bambo kapena mayi angasiye choonadi ngakhalenso banja lake. (Sal. 27:10) Zimenezi zingasokoneze kwambiri ana omwe amaona kuti kholo lawolo ndi chitsanzo chawo. Esther yemwe bambo ake anachotsedwa, ananena kuti: “Nthawi zambiri ndinkalira chifukwa choti bambo anga sanangopatuka pachoonadi, koma anali atasankha kusiyiratu kutumikira Yehova. Ndimakonda bambo anga, choncho atachotsedwa ndinkadera nkhawa kwambiri za moyo wawo ndipo nthawi zambiri ndinkavutika maganizo.”

7. Kodi Yehova amamva bwanji akaona mwana amene kholo lake lachotsedwa mumpingo?

7 Ananu, dziwani kuti bambo kapena mayi anu akachotsedwa mumpingo, zimatikhudza kwambiri. Musamakayikire kuti Yehova nayenso amadziwa mmene mukumvera. Iye amakukondani komanso amasangalala mukapitiriza kukhalabe okhulupirika ndipo abale ndi alongo anu tonsefe timasangalalanso. Muzikumbukiranso kuti si inu amene mwachititsa kuti makolo anu asankhe molakwika. Monga tanena kale, Yehova anapatsa aliyense ufulu wosankha. Komanso Mkhristu aliyense amene anadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa, “ayenera kunyamula katundu wake.”​—Agal. 6:5.

8. Kodi anthu ena m’banja angamachite chiyani pamene akuyembekezera kuti wachibale wawo abwerere kwa Yehova? (Onaninso bokosi lakuti “ Bwererani kwa Yehova.”)

8 Munthu wina yemwe mumamukonda akasiya kutumikira Yehova, n’zomveka kuti mumayembekezera kuti tsiku lina adzabwerera kwa iye. Ndiye kodi muyenera kuchita chiyani pamene mukuyembekezera zimenezo? Muzichita zonse zimene mungathe kuti chikhulupiriro chanu chikhale cholimba. Mukamachita zimenezi muzipereka chitsanzo chabwino kwa anthu a m’banja lanu, mwinanso kwa amene wachotsedwayo. Zimenezi zingachititsenso kuti mupeze mphamvu zokuthandizani kupirira ululu umene mukumva. Tiyeni tikambirane zinthu zina zomwe mungachite kuti chikhulupiriro chanu chikhalebe cholimba.

ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUKHALEBE NDI CHIKHULUPIRIRO CHOLIMBA

9. Kodi mungatani kuti Yehova azikupatsani mphamvu? (Onaninso bokosi lakuti, “ Malemba Okulimbikitsani Amene Mumamukonda Akasiya Yehova.”)

9 Nthawi zonse muziyesetsa kuchita zinthu zokhudza kulambira. N’zofunika kwambiri kuti mupitirize kulimbitsa chikhulupiriro chanu komanso cha anthu ena m’banja lanu. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Yehova angakupatseni mphamvu mukamawerenga Mawu ake nthawi zonse, kuwaganizira mozama komanso kupezeka pamisonkhano. Joanna, yemwe bambo ake komanso mchemwali wake anasiya choonadi,, ananena kuti: “Mtima wanga umakhala m’malo ndikamawerenga za anthu otchulidwa m’Baibulo monga Abigayeli, Esitere, Yobu Yosefe ndi Yesu. Zitsanzo za anthu amenewa zimanditsitsimula moti ndimayamba kuganiza bwino. Ndimaonanso kuti nyimbo zathu zimandilimbikitsa kwambiri.”

10. Kodi lemba la Salimo 32:6-8, limasonyeza kuti tiyenera kuchita chiyani tikakhala ndi nkhawa?

10 Muzimufotokozera Yehova mmene mukumvera. Mukakhala ndi nkhawa musamasiye kupemphera kwa iye. Muzipempha Mulungu wathu wachikondi kuti akuthandizeni kuona zinthu mmene iyeyo amazionera ndiponso ‘akupatseni nzeru ndi kukulangizani njira yoti muyendemo.’ (Werengani Salimo 32:6-8.) N’zoona kuti nthawi zina zingakhale zovuta kuti mufotokozere Yehova mmene mukumveradi. Koma Yehova amamvetsa bwino mmene mukumvera mumtima. Iye amakukondani kwambiri ndipo amakulimbikitsani kuti muzimukhuthulira za mumtima mwanu.​—Eks. 34:6; Sal. 62:7, 8.

11. Mogwirizana ndi Aheberi 12:11, n’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kuti Yehova amapereka chilango chifukwa cha chikondi? (Onaninso bokosi lakuti, “ Kuchotsedwa Mumpingo Ndi Chilango Chosonyeza Chikondi cha Yehova.”)

11 Muzigwirizana ndi chigamulo chimene akulu apereka. Yehova ndi amene anakonza zoti anthu osalapa azichotsedwa mumpingo. Chilango chimene amapereka chimathandiza anthu onse kuphatikizapo wolakwayo. (Werengani Aheberi 12:11.) Anthu ena mumpingo angamanene kuti akulu sanaweruze bwino kuti munthu achotsedwe. Koma kumbukirani kuti anthu amenewa amakhala kuti sankafuna kuulula zinthu zoipa zimene munthu wolakwayo ankachita. Nthawi zambiri sitidziwa zonse zomwe zachitika. Choncho ndi nzeru kukhulupirira kuti akulu omwe anaweruza nkhaniyo anachita zonse zomwe angathe potsatira mfundo za m’Malemba komanso ‘kuweruzira Yehova.’​—2 Mbiri 19:6.

12. Kodi ndi madalitso otani omwe ena apeza chifukwa chogwirizana ndi chilango cha Yehova?

12 Mukamagwirizana ndi zimene akulu asankha zoti wachibale wanu achotsedwe, mukhoza kumuthandiza kuti abwerere kwa Yehova. Elizabeth yemwe tamutchula kale uja anavomereza kuti: “Zinali zovuta kwambiri kuti tisamalankhulane ndi mwana wathu wamkulu. Koma iye atabwerera kwa Yehova, anavomereza kuti ankafunikadi kuchotsedwa. Pamapeto pake iye ananena kuti amayamikira chifukwa cha zinthu zambiri zimene anaphunzirapo. Ndinazindikira kuti nthawi zonse chilango chochokera kwa Yehova chimakhala choyenera.” Mwamuna wake Mark anaonjezera kuti: “Patapita nthawi mwana wathu anandiuza kuti chinthu china chimene chinamuthandiza kuti abwerere kwa Yehova ndi choti sitinkachita naye zinthu ngakhale pang’ono. Ndikusangalala kuti Yehova anatithandiza kukhala omvera.”

13. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muziona zinthu moyenera?

13 Muzifotokoza mmene mukumvera kwa anzanu omwe amakumvetsani. Muzicheza ndi Akhristu olimba mwauzimu omwe angakuthandizeni kuti mupitirize kuona zinthu moyenera. (Miy. 12:25; 17:17) Joanna yemwe tamutchula kale uja anati: “Mumtimamu ndinkangomva ngati ndili ndekhandekha. Koma kucheza ndi anzanga odalirika kunandithandiza kuti ndipirire.” Ndiye kodi mungachite chiyani ngati mukuona kuti mumpingo ena alankhula zinthu zimene zachititsa kuti mumve kuwawa kwambiri?

14. N’chifukwa chiyani tiyenera “kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse”?

14 Muziwalezera mtima abale ndi alongo anu. Sitingayembekezere kuti aliyense azilankhula zinthu zoyenera. (Yak. 3:2) Tonsefe si angwiro. Choncho musamadabwe ngati ena zikuwavuta kulankhula zinthu zoyenera, kapenanso ngati mosadziwa alankhula zinthu zimene zakukhumudwitsani. Muzikumbukira malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake.” (Akol. 3:13) Mlongo wina yemwe wachibale wake anachotsedwa anafotokoza kuti: “Yehova anandithandiza kuti ndikhululukire abale omwe anandikhumudwitsa pa nthawi yomwe ankayesa kundilimbikitsa.” Ndiye kodi anthu a mumpingo angathandize bwanji achibale a munthu amene wachotsedwa?

ANTHU A MUMPINGO ANGATHANDIZE KWAMBIRI

15. Kodi tingatani kuti tithandize achibale a munthu amene wangochotsedwa kumene mumpingo?

15 Muzichita zinthu mokoma mtima ndi achibale a munthu amene wachotsedwa. Mlongo wina dzina lake Miriam ananena kuti mchimwene wake atachotsedwa, iye ankada nkhawa akaganiza zopita kumisonkhano. Iye anati: “Ndinkaopa zimene anthu angamanene. Koma panali anzanga abwino omwe anakhudzidwa ndi zomwe zinachitikazo ndipo sankanena zinthu zoipa zokhudza m’bale wanga amene anachotsedwayo. Chifukwa cha zomwe iwo anachitazi sindinkadziona kuti ndili ndekhandekha.” Mlongo wina ananena kuti: “Mwana wathu wamwamuna atachotsedwa anzathu anabwera kudzatilimbikitsa. Ena ankavomereza kuti sankadziwa choti anene. Iwo ankalira nane kapena kundilembera kalata yondilimbikitsa. Zimene anachitazi zinandithandiza kwambiri.”

Abale ndi alongo a mumpingo angasonyeze kuti amakonda achibale a munthu yemwe wachotsedwa powathandiza (Onani ndime 17) *

16. Kodi anthu a mumpingo angatani kuti apitirize kuthandiza achibale a munthu amene wachotsedwa?

16 Muzipitiriza kuthandiza achibale okhulupirika a munthu amene wachotsedwayo. Pa nthawiyi m’pamene amafunika kuwakonda komanso kuwalimbikitsa kuposa kale lonse. (Aheb. 10:24, 25) Nthawi zina achibale a munthu amene wachotsedwayo akhoza kumamva ngati akusalidwa mumpingo. Koma musamalole kuti azimva choncho. Achinyamata omwe makolo awo anasiya kutumikira Yehova amafunika kwambiri kuwayamikira komanso kuwalimbikitsa. Maria yemwe mwamuna wake anachotsedwa ndipo anasiya banja lawo ananena kuti: “Anzanga ankabwera kunyumba, kutiphikira chakudya ndipo ankandithandiza ndikamaphunzira ndi ana anga. Ankamva ululu umene ndinkamva ndipo ankalira nane limodzi. Ankalankhula zinthu zabwino anthu akamalankhula zinthu zabodza zokhudza ineyo. Iwo ankandilimbikitsa kwambiri.”​—Aroma 12:13, 15.

17. Kodi akulu angatani kuti azilimbikitsa anthu amene wachibale wawo wasiya kutumikira Yehova?

17 Akulu, muzigwiritsa ntchito mpata uliwonse umene wapezeka kuti muzilimbikitsa achibale a munthu amene wachotsedwa. Muli ndi udindo wapadera wotonthoza achibale a munthu amene wasiya kutumikira Yehova. (1 Ates. 5:14) Muziyesetsa kuwalimbikitsa misonkhano isanayambe komanso ikatha ndipo muziwayendera komanso kupemphera nawo limodzi. Muzilowa nawo mu utumiki kapenanso nthawi zina mungawaitane kuti adzakhale nawo pakulambira kwanu kwa pabanja. Akulu ayenera kusonyeza chikondi, chifundo ndiponso kusamalira nkhosa za Yehova zomwe zili ndi chisoni.​—1 Ates. 2:7, 8.

MUSAMATAYE MTIMA NDIPO MUZIPITIRIZA KUDALIRA YEHOVA

18. Mogwirizana ndi 2 Petulo 3:9, kodi Mulungu amafuna kuti anthu amene anasiya kumutumikira achite chiyani?

18 Yehova “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (Werengani 2 Petulo 3:9.) Ngakhale munthu atachita tchimo lalikulu, moyo wake umakhalabe wamtengo wapatali kwa Mulungu. Yehova anapereka nsembe ya dipo ya Mwana wake wokondedwa, yomwe ndi yokwera mtengo kwambiri kuti awombole anthu ochimwa. Mwachifundo Iye amachita zonse zomwe angathe kuti athandize anthu ngati amenewa kubwerera kwa iye. Ndipo monga mmene fanizo la Yesu lonena za mwana wolowerera limasonyezera, Yehova amayembekezera kuti iwo achitadi zimenezo. (Luka 15:11-32) Ambiri amene anasiya choonadi, pambuyo pake anabwerera kwa Atate wawo wachikondi ndipo abale ndi alongo anawalandira ndi manja awiri. Elizabeth yemwe tamutchula kale uja anasangalala kwambiri kuona mwana wake atabwezeretsedwa. Pokumbukira zimenezi iye anati: “Ndimayamikira kwambiri abale ndi alongo amene ankatilimbikitsa kuti tisataye mtima.”

19. N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kudalira Yehova?

19 Nthawi zonse tizidalira Yehova. Sangatipatse malangizo omwe angachititse kuti tikumane ndi mavuto. Iye ndi wowolowa manja komanso Atate yemwe amakonda kwambiri anthu omwe amamukonda komanso kumulambira. Dziwani kuti Yehova sadzakusiyani pa nthawi ya mavuto. (Aheb. 13:5, 6) Mark yemwe tamutchula kale uja ananena kuti: “Yehova satisiya ndipo tikakumana ndi mavuto amakhala nafe pafupi.” Iye adzapitiriza kukupatsani “mphamvu yoposa yachibadwa.” (2 Akor. 4:7) Choncho, mungathe kukhalabe okhulupirika komanso simungataye mtima ngakhale pamene munthu amene mumamukonda wasiya kutumikira Yehova.

NYIMBO NA. 44 Pemphero la Munthu Wovutika

^ ndime 5 Zimakhalatu zokhumudwitsa kwambiri munthu amene timamukonda akasiya kutumikira Yehova. Nkhaniyi ifotokoza mmene Mulungu amamvera zimenezi zikachitika. Ifotokozanso zimene achibale okhulupirika angachite kuti apirire ululu umene umakhalapo n’kupitiriza kukhalabe olimba mwauzimu. Tionanso zimene onse mumpingo angachite kuti azilimbikitsa komanso kuthandiza achibale a munthu amene wasiya kutumikira Yehova.

^ ndime 1 Mayina ena munkhaniyi asinthidwa.

^ ndime 79 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: M’bale akasiya banja lake komanso kutumikira Yehova, mkazi ndi ana ake amavutika.

^ ndime 81 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Akulu awiri akulimbikitsa banja lina la mumpingo wawo.