Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Potsatira malamulo a m’Baibulo onena za ntchito yoyenera ya magazi, kodi Mboni za Yehova zimaziona motani njira zakuchipatala zogwiritsa ntchito magazi ako omwe pokupatsa chithandizo?

M’malo mongosankha malinga ndi zimene akulingalira kapena zimene wauzidwa ndi achipatala, Mkristu aliyense ayenera kulingalira mozama zimene Baibulo limanena. Ndi nkhani yokhudza iyeyo ndi Yehova.

Yehova, amene ndiye mwini miyoyo yathu, analamula kuti magazi sayenera kudyedwa. (Genesis 9:3, 4) M’Chilamulo chimene anapatsa Aisrayeli akale, Mulungu anawaletsa kugwiritsa ntchito magazi chifukwa chakuti amaimira moyo. Analamula kuti: “Moyo wa nyama ukhala m’mwazi; ndipo ndakupatsani uwu pa guwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu.” Bwanji munthu atapha nyama kuti akadye? Mulungu anati: “Azikhetsa [“azitaya,” NW] mwazi wake, naufotsere ndi dothi.” a (Levitiko 17:11, 13) Yehova ananena lamulo limeneli mobwerezabwereza. (Deuteronomo 12:16, 24; 15:23) Buku lachiyuda lotchedwa Soncino Chumash limati: “Magaziwo sayenera kusungidwa koma ayenera kutayidwa pansi chifukwa ndi osayenera kudya.” Palibe Mwisrayeli aliyense amene anayenera kutenga, kusunga, ndi kugwiritsa ntchito magazi a cholengedwa china, chomwe moyo wake mwiniwake ndi Mulungu.

Kuyambira pamene Mesiya anafa, anthu salinso okakamizika kutsatira Chilamulo cha Mose. Komano, Mulungu amaonabe magazi kukhala opatulika. Posonkhezeredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, atumwi analangiza Akristu ‘kusala mwazi.’ Limenelo linali lamulo lalikulu. Pankhani ya khalidwe, lamulolo linali lofunika mofanana ndi malamulo akuti apeŵe dama kapena kupembedza mafano. (Machitidwe 15:28, 29; 21:25) Pamene kupereka magazi ndi kuika anthu magazi kunafala m’zaka za m’ma 1900, Mboni za Yehova zinadziŵa kuti kuchita zimenezo n’kosemphana ndi Mawu a Mulungu. b

Nthaŵi zina, dokotala amatha kuuza wodwala kuti apereke magazi ake kutatsala milungu ingapo kuti am’pange opaleshoni (m’Chingelezi njirayi imatchedwa preoperative autologous blood donation, kapena kuti PAD mwachidule) kuti ngati wodwalayo angadzafune magazi, adzamuike magazi ake omwe osungidwawo. Koma kutenga magazi kumeneku, kuwasunga, ndi kumuikanso wodwalayo kukuwombana mwachindunji ndi zimene zikunenedwa m’Levitiko ndi m’Deuteronomo. Magazi sayenera kusungidwa; ayenera kutayidwa​—kuwabwezera kwa Mulungu, tingatero kunena kwake. N’zoona kuti masiku ano sitikulamulidwa ndi Chilamulo cha Mose. Koma ngakhale zili tero, Mboni za Yehova zimamvera mfundo zachikhalidwe zimene Mulungu anaphatikizamo, ndipo iwo n’ngotsimikiza mtima ‘kusala mwazi.’ Pachifukwa chimenecho, sitipereka magazi, komanso sitisungitsa magazi athu kuti adzatiikenso chifukwa magazi oterowo n’ngoyenera ‘kutayidwa.’ Njira imeneyo n’njotsutsana ndi lamulo la Mulungu.

Njira zina kapena kupima kwina koloŵetsapo magazi a wodwalayo sikumawombana mwachindunji ndi mfundo za Mulungu zachikhalidwe zimene wazinena. Mwachitsanzo, Akristu ambiri alola kuti awatenge magazi kuti akawapime, ndipo pambuyo pake magaziwo amatayidwa. Madokotala angafunenso kuchita njira zina zocholoŵana zokhudza magazi a wodwala.

Mwachitsanzo, popanga munthu opaleshoni, nthaŵi zina magazi angawapatutse kutuluka m’thupi kukaloŵa m’makina ena mwa njira yotchedwa hemodilution m’Chingelezi. Magazi amene amatsala m’thupi la wodwala amakhala osungunuka kwambiri. Pambuyo pake, magazi amene atulukawo amawaloŵetsanso m’thupi, zomwe zimapangitsa kuti wodwalayo akhalenso ndi magazi okwanira bwino. Mofananamo, magazi amene amatuluka pabala angatengedwe n’kusefedwa kotero kuti maselo ofiira amabwezeretsedwa m’thupi la wodwalayo; njira imeneyi yopulumutsa maselo ofiira amaitcha cell salvage m’Chingelezi. Nthaŵi zinanso, magazi amawadutsitsa m’makina amene amachita ntchito yoyenera kuchitidwa ndi chiwalo china cha m’thupi (mwachitsanzo, mtima, mapapu, kapena impso) kwa kanthaŵi ndithu. Ndiyeno magazi a m’makinawo amakaloŵanso m’thupi la wodwalayo. Njira inanso ndiyo yakuti magazi amawaloŵetsa m’makina (otchedwa centrifuge) olekanitsa zigawo zosiyanasiyana za m’magazi kuti achotsemo zigawo zina zoyambitsa mavuto kapena zowonongeka. Kapena cholinga chake chingakhale kutengamo chigawo chinachake m’magazimo ndi kuchigwiritsa ntchito pamalo ena pathupi la wodwalayo. Palinso njira ina yopimira imene amatenga magazi ochepa kuti awasakanize ndi mankhwala, kenako magaziwo amawabwezera mwa wodwalayo.

Zochitika zake zingakhale zosiyanasiyana, ndipo achipatala adzapezabe njira zina, mankhwala ena, ndi njira zina zopimira munthu. Si kwa ife kulongosola zochitika zonsezo chimodzi ndi chimodzi ndi kutchula chosankha. Mkristu ayenera kudzisankhira yekha njira imene magazi ake adzasamalidwira pa opaleshoni, popimidwa, kapena pamene akulandira chithandizo chamankhwala cha mtundu uliwonse. Ayenera kufunsiratu dokotala kapena katswiri wa m’chipatala amene adzam’samalira ponena za zimene adzachita ndi magazi ake pom’samalira. Ndiyeno asankhe mogwirizana ndi chikumbumtima chake. (Onani bokosi.)

Akristu ayenera kukumbukira kudzipatulira kwawo kwa Mulungu ndiponso choyenera chawo cha ‘kum’konda ndi mtima wawo wonse, moyo wawo wonse, mphamvu yawo yonse, ndi nzeru zawo zonse.’ (Luka 10:27) Mosiyana ndi anthu ambiri m’dziko, Mboni za Yehova zimasamala kwambiri unansi wawo wabwino ndi Mulungu. Wopatsa Moyo akulimbikitsa onse kusonyeza chikhulupiriro m’magazi okhetsedwa a Yesu. Timaŵerenga kuti: “Tili ndi mawomboledwe mwa mwazi wake [Yesu Kristu], chikhululukiro cha zochimwa [zathu].”​—Aefeso 1:7.

[Mawu a M’munsi]

a Pulofesa Frank H. Gorman analemba kuti: “Tinganene kuti kutayira pansi magazi ndiko kusonyeza ulemu pa moyo wa nyamayo komanso, pochita zimenezo, munthu amalemekeza Mulungu, amene analenga ndi kupitirizabe kusamalira moyowo.”

b Nsanja ya Olonda yachingelezi ya July 1, 1951, inayankha mafunso akuluakulu okhudza nkhaniyi, kusonyeza chifukwa chake kuikidwa magazi operekedwa ndi anthu ena kuli kosafunika.

[Bokosi/​Zitunzi patsamba 31]

MAFUNSO OTI MUDZIFUNSE NOKHA

Ngati ena mwa magazi anga adzawatulutsa m’thupi mwanga n’kuwaloŵetsa m’makina ena mmenenso mwina angakhalemo kanthaŵi, kodi chikumbumtima changa chidzandilola kuonanso magazi amenewo ngati angabe, kuti ndi osafunikira ‘kutayidwa pansi’?

Kodi chikumbumtima changa chophunzitsidwa Baibulo chingandivutitse ngati pondipima kapena pondipatsa chithandizo chinachake m’chipatala anditenga magazi pang’ono, n’kuwapanga zina ndi zina, kenako n’kuwabwezeranso m’thupi mwanga (kapena pathupi langa)?