Akulu Achikhristu Ndi Antchito Anzathu Otipatsa Chimwemwe
“Ndife antchito anzanu kuti mukhale ndi chimwemwe.”—2 AKOR. 1:24.
1. Kodi Paulo anakondwera atamva chiyani ponena za Akhristu a ku Korinto?
M’CHAKA cha 55 C.E., mtumwi Paulo anali mumzinda wa Torowa. Koma ali kumeneko, sanasiye kuganizira za abale a ku Korinto. Miyezi ingapo m’mbuyomo, zinamupweteka mumtima atamva kuti abale a ku Korinto anali kukangana. Popeza ankawadera nkhawa ngati ana ake, iye anawalembera kalata yowapatsa malangizo. (1 Akor. 1:11; 4:15) Anatumizanso wantchito mnzake Tito kuti akawathandize. Anamuuza kuti akakawathandiza abwere ku Torowa n’kudzamuuza mmene zinthu zilili kumeneko. Choncho Paulo anali kudikira Tito ku Torowa ndipo anali wofunitsitsa kumva mmene zinthu zilili ku Korinto. Koma Tito sanabwere. Kodi Paulo anachita chiyani? Iye ananyamuka ulendo wa pamadzi wopita ku Makedoniya ndipo anasangalala kwambiri atakumana naye kumeneko. Tito anafotokoza kuti abale a ku Korinto anatsatira malangizo a m’kalata yake ndipo anali ofunitsitsa kumuona. Paulo atamva zimenezi, ‘anakondwera kwambiri.’—2 Akor. 2:12, 13; 7:5-9.
2. (a) Kodi Paulo analembera Akorinto mawu ati onena za chikhulupiriro ndiponso chimwemwe? (b) Kodi tiyankha mafunso ati m’nkhani ino?
2 Pasanapite nthawi yaitali, Paulo analemberanso Akorinto kalata ina. Iye anawauza kuti: “Sikuti ndife olamulira chikhulupiriro chanu, koma ndife antchito anzanu kuti mukhale ndi chimwemwe, pakuti ndinu okhazikika chifukwa cha chikhulupiriro chanu.” (2 Akor. 1:24) Kodi mawu a Paulo amenewa ankatanthauza chiyani? Nanga mawuwa angathandize bwanji akulu masiku ano?
AMATITHANDIZA KUKHALA NDI CHIKHULUPIRIRO NDI CHIMWEMWE
3. (a) Kodi Paulo ankatanthauza chiyani ponena kuti: “Ndinu okhazikika chifukwa cha chikhulupiriro chanu”? (b) Kodi akulu masiku ano amatsatira bwanji chitsanzo cha Paulo?
3 Paulo anatchula mbali ziwiri zofunika kwambiri za kulambira Mulungu. Anatchula chikhulupiriro ndiponso chimwemwe. Ponena za chikhulupiriro, iye analemba kuti: “Sikuti ndife olamulira chikhulupiriro chanu, . . . pakuti ndinu okhazikika chifukwa cha chikhulupiriro chanu.” Apa Paulo anasonyeza kuti ankadziwa zoti abale a ku Korinto anali olimba m’chikhulupiriro, osati chifukwa cha iye kapena munthu wina aliyense, koma chifukwa chakuti iwowo ankakhulupirira Mulungu. Choncho anaona kuti sayenera kulamulira chikhulupiriro cha abale akewo ndiponso analibe maganizo amenewo. Iye ankakhulupirira kuti abalewo anali Akhristu okhulupirika ndipo ankafuna kusangalatsa Mulungu. (2 Akor. 2:3) Masiku anonso, akulu amatsatira chitsanzo cha Paulo pokhulupirira kuti abale awo ali ndi chikhulupiriro ndiponso amatumikira Mulungu ndi zolinga zabwino. (2 Ates. 3:4) Akulu sakhazikitsa malamulo okhwima mu mpingo. M’malomwake, iwo amathandiza abale kutsatira mfundo za m’Malemba ndiponso malangizo amene gulu la Yehova limapereka. Akulu a masiku ano si olamulira chikhulupiriro cha abale awo.—1 Pet. 5:2, 3.
4. (a) Kodi Paulo ankatanthauza chiyani ponena kuti: “Ndife antchito anzanu kuti mukhale ndi chimwemwe”? (b) Kodi akulu masiku ano amatsanzira bwanji Paulo?
4 M’kalata yake, Paulo ananenanso kuti: “Ndife antchito anzanu kuti mukhale ndi chimwemwe.” Ponena kuti “antchito anzanu,” Paulo anali kunena za iyeyo ndiponso anzake apamtima. Tikutero chifukwa chakuti m’kalata yomweyi, Paulo anakumbutsa Akorinto za anzake apamtima awiri polemba kuti: “Yesu . . . analalikidwa pakati panu kudzera mwa ineyo, Silivano, ndi Timoteyo.” (2 Akor. 1:19) Komanso m’makalata ake, iye akanena kuti “antchito anzake,” nthawi zonse ankanena za anzake apamtima monga Apolo, Akula, Purisika, Timoteyo, Tito ndiponso anzake ena. (Aroma 16:3, 21; 1 Akor. 3:6-9; 2 Akor. 8:23) Choncho pamene anati: “Ndife antchito anzanu kuti mukhale ndi chimwemwe,” Paulo ankatsimikizira Akhristu a ku Korinto kuti iyeyo ndiponso anzakewo ankafunitsitsa kuchita zonse zimene angathe kuthandiza onse mu mpingowo kukhala achimwemwe. Nawonso akulu achikhristu ndi ofunitsitsa kuchita zimenezi. Iwo amafuna kuchita zonse zimene angathe kuthandiza abale awo ‘kutumikira Yehova mokondwera.’—Sal. 100:2; Afil. 1:25.
5. Kodi abale ndi alongo ena anafunsidwa funso liti? Kodi tiziganizira chiyani tikamakambirana zimene iwo anayankha?
5 Posachedwapa, abale ndi alongo ena okhulupirika m’mayiko osiyanasiyana anapemphedwa kuti ayankhe funso. Funso lake linali lakuti, “Kodi ndi zinthu ziti zimene mkulu ananena kapena kuchita zomwe zakuthandizani kukhala wachimwemwe?” Tiyeni tikambirane zimene abale ndi alongowo ananena. Tikamakambirana zimenezi, muziyerekezera ndi zimene inuyo mukananena poyankha funsolo. Muziganiziranso zimene mungachite pothandiza anthu mu mpingo wanu kukhala achimwemwe. a
“MONI KWA PERESIDA, WOKONDEDWA WATHU”
6, 7. (a) Kodi akulu angatsanzire bwanji Yesu, Paulo ndi atumiki ena a Mulungu? (b) N’chifukwa chiyani abale amasangalala tikamakumbukira mayina awo?
6 Abale ndi alongo athu ambiri amanena kuti amasangalala kwambiri akulu akamasonyeza kuti amawaganizira. Akulu akhoza kuchita zimenezi potengera chitsanzo cha Davide, Elihu ndiponso Yesu. (Werengani 2 Samueli 9:6; Yobu 33:1; Luka 19:5.) Atumiki a Yehova onsewa anasonyeza kuti amaganizira anthu ena powatchula mayina awo. Nayenso Paulo anadziwa kufunika kokumbukira ndiponso kugwiritsa ntchito mayina a Akhristu anzake. Pomaliza kalata yake ina, anapereka moni kwa abale ndi alongo oposa 25 ndipo anawatchula onse mayina awo. Mwachitsanzo anatchula Peresida, yemwe anali mlongo amene Paulo ananena za iye kuti: “Moni kwa Peresida, wokondedwa wathu.”—Aroma 16:3-15.
7 Akulu ena amavutika kukumbukira mayina. Koma mkulu akamayesetsa kukumbukira, zili ngati akuuza abale ndi alongo kuti, ‘Ndinu ofunika kwa ine.’ (Eks. 33:17) Akulu amapangitsa abale kusangalala akamakumbukira mayina awo powatchula kuti apereke ndemanga pa Phunziro la Nsanja ya Olonda ndiponso pa misonkhano ina.—Yerekezerani ndi Yohane 10:3.
“WACHITA NTCHITO ZAMBIRI POTUMIKIRA AMBUYE”
8. Kodi Paulo anatsatira chitsanzo cha Yehova ndi Yesu pa nkhani yofunika iti?
8 Paulo anasonyezanso kuti amaganizira ena powayamikira mochokera pansi pa mtima. Kuchita zimenezi kumapangitsanso Akhristu anzathu kukhala achimwemwe. M’kalata yomweyo, imene Paulo ananena kuti ankafunitsitsa kuthandiza abale ake kukhala achimwemwe, ananenanso kuti: “Ndimakunyadirani kwambiri.” (2 Akor. 7:4) Mawu amenewa ayenera kuti analimbikitsa kwambiri abale a ku Korinto. Paulo ananenanso mawu ngati amenewa m’makalata ake opita ku mipingo ina. (Aroma 1:8; Afil. 1:3-5; 1 Ates. 1:8) Paulo atatchula Peresida m’kalata yake yopita ku mpingo wa ku Roma, ananenanso za iye kuti: “Mayi ameneyu wachita ntchito zambiri potumikira Ambuye.” (Aroma 16:12) Mlongo wokhulupirika ameneyu ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri ndi mawuwa. Paulo ankatsatira chitsanzo cha Yehova ndiponso Yesu pa nkhani yoyamikira ena.—Werengani Maliko 1:9-11; Yohane 1:47; Chiv. 2:2, 13, 19.
9. N’chifukwa chiyani kuyamikirana kumathandiza anthu mu mpingo kukhala achimwemwe?
9 Masiku anonso, akulu amadziwa kufunika konena mawu oyamikira abale awo. (Miy. 3:27; 15:23) Mkulu akachita zimenezi, zili ngati akuuza abale ake kuti: ‘Ndaona zimene mwachita ndipo ndimakukondani.’ Abale ndi alongo amafuna kwambiri kumva mawu olimbikitsa ochokera kwa akulu. Mlongo wina wa zaka zoposa 50 ananena kuti: “Kuntchito, anthu sandiyamikira. Iwo sakondana koma amangokonda kupikisana. Choncho mkulu akandiyamikira pa zinthu zimene ndachita mu mpingo, ndimalimbikitsidwa ndiponso zimandipatsa mphamvu. Zimandichititsa kumva kuti Atate wanga wakumwamba amandikonda.” M’bale wina amene akulera yekha ana awiri ankamvanso chimodzimodzi. Posachedwapa, mkulu wina anamuyamikira mochokera pansi pa mtima. Kodi m’baleyu anamva bwanji? Iye anati: “Zimene mkuluyu ananena zinandipatsa mphamvu kwambiri.” Mkulu akamayamikira abale ndi alongo mochokera pansi pa mtima, amawalimbikitsa kwambiri ndipo amawathandiza kukhala achimwemwe. Zimenezi zingawathandizenso kuti apitirize kuyenda ‘mosatopa’ panjira yopita ku moyo.—Yes. 40:31.
“MUWETE MPINGO WA MULUNGU”
10, 11. (a) Kodi akulu angatsatire bwanji chitsanzo cha Nehemiya? (b) N’chiyani chingathandize mkulu kukagawira mphatso yauzimu pa ulendo waubusa?
10 Pali njira ina yofunika imene akulu angasonyezere kuti amaganizira abale ndi alongo ndiponso kuwathandiza kukhala achimwemwe. Akulu akaona anthu amene akufunika kuwalimbikitsa, ayenera kuwathandiza mwamsanga. (Werengani Machitidwe 20:28.) Akulu akamachita zimenezi, amatsanzira atumiki okhulupirika akale. Mwachitsanzo, Nehemiya ataona kuti abale ake ena achiyuda abwerera m’mbuyo potumikira Mulungu, nthawi yomweyo anawalimbikitsa. (Neh. 4:14) Masiku anonso, akulu ayenera kuchita zomwezo. Iwo angachite bwino kuchita zimene angathe kuthandiza Akhristu anzawo kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu. Ngati n’zotheka, amawayendera m’nyumba zawo kuti awalimbikitse. Akamatero, amayesetsa ‘kuwagawira mphatso inayake yauzimu.’ (Aroma 1:11) N’chiyani chingathandize akulu kuchita zimenezi?
11 Mkulu asanapite ku ulendo waubusa, ayenera kuganizira kaye za munthu yemwe akufuna kukamulimbikitsayo. Mwachitsanzo, angafunike kudzifunsa kuti: ‘Kodi munthuyo akukumana ndi mavuto otani? Kodi ndingakanene zinthu zotani zimene zingamulimbikitse? Kodi ndi malemba ati kapena nkhani za anthu ati a m’Baibulo zimene zikugwirizana ndi mavuto omwe akukumana nawo pa moyo wake? Mkulu akachitiratu zimenezi asanapite kukacheza ndi munthuyo, zingamuthandize kuti akalankhule zinthu zimene zingakhaledi zolimbikitsa. Ndiyeno pamene akucheza nawo, angachite bwino kuwalola kuti afotokoze maganizo awo. Pamene akufotokoza, iye afunika kumvetsera mwatcheru. (Yak. 1:19) Mlongo wina anati: “Zimakhala zolimbikitsa kwambiri mkulu akamakumvetsera mwachidwi.”—Luka 8:18.
12. Kodi ndi ndani mu mpingo amene amafunika kulimbikitsidwa ndipo n’chifukwa chiyani?
12 Kodi ndi anthu ati amene amafunikira ulendo waubusa? Mtumwi Paulo analangiza akulu achikhristu anzake kuti: “Mukhale tcheru ndi . . . gulu lonse la nkhosa.” Izi zikusonyezeratu kuti aliyense mu mpingo amafunika kulimbikitsidwa, kuphatikizapo ofalitsa ndiponso apainiya omwe akhala akutumikira mokhulupirika kwa zaka zambiri. N’chifukwa chiyani nawonso amafunika kulimbikitsidwa ndi akulu? N’chifukwa chakuti ngakhale anthu otumikira Mulungu mokhulupirika nthawi zina amavutika kupirira mavuto a m’dziko loipali. Pa nkhaniyi, kukambirana zimene zinachitikira Mfumu Davide kungatithandize kumvetsa kuti nawonso atumiki okhulupirika a Mulungu amafunikira thandizo kuchokera kwa atumiki anzawo.
“ABISAI . . . ANATHANDIZA DAVIDE”
13. (a) Kodi Isibi-benobi anaukira Davide pa nthawi iti? (b) N’chiyani chinathandiza Abisai kupulumutsa Davide?
13 Davide atangodzozedwa kukhala mfumu, anakamenyana ndi Goliati. Goliati anali wa m’fuko la Arefai omwe anali ziphona. Davide anali wolimba mtima kwambiri ndipo anapha chiphonachi. (1 Sam. 17:4, 48-51; 1 Mbiri 20:5, 8) Patapita zaka zambiri, Davide anamenyananso ndi chiphona china pamene Aisiraeli anali pa nkhondo ndi Afilisiti. Chiphonachi dzina lake linali Isibi-benobi, yemwenso anali wa m’fuko la Arefai. (2 Sam. 21:16) Koma panthawiyi, chiphonachi chinatsala pang’ono kupha Davide. Sikuti izi zinachitika chifukwa choti Davide anasiya kulimba mtima koma chifukwa chakuti iye anachepa mphamvu. Baibulo limati: “Davide anatopa.” Isibi-benobi atangoona kuti Davide watopa, ‘anaganiza zoti amuphe.’ Koma chiphonachi chisanaponye lupanga, “nthawi yomweyo Abisai mwana wa Zeruya anathandiza Davide ndipo anakantha Mfilisitiyo ndi kumupha.” (2 Sam. 21:15-17) Apatu Davide anapulumukira m’kamwa mwa mbuzi. Mosakayikira, Davide anayamikira kwambiri kuti Abisai anali tcheru ndi zimene zinali kumuchitikira ndipo anamuthandiza mwamsanga pamene moyo wake unali pa ngozi. Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chiyani?
14. (a) N’chiyani chingatithandize kugonjetsa mavuto akuluakulu okhala ngati Goliati? (b) Kodi akulu angathandize bwanji anthu kukhalanso olimba ndiponso achimwemwe? Perekani chitsanzo.
14 Anthu a Yehovafe padziko lonse lapansi tikutumikira Mulungu ngakhale kuti Satana ndi anthu ake akuyesetsa kutisokoneza. Ena a ife talimbana ndi mavuto akuluakulu okhala ngati Goliati ndipo tawagonjetsa chifukwa chodalira Yehova. Komabe nthawi zina timatopa ndiponso kukhumudwa chifukwa chokhalira kulimbana ndi mavuto a m’dzikoli. Tikafooka choncho, timakhala pa ngozi yogonjetsedwa ndi mavuto amene tikanatha kulimbana nawo bwinobwino. Pa nthawi ngati zimenezi, thandizo limene mkulu angapereke lingatilimbikitse ndiponso kutithandiza kukhalanso ndi chimwemwe. Zimenezi zachitikira abale ndi alongo ambiri. Mwachitsanzo, mlongo wina wa zaka zoposa 60, amene akuchita upainiya, anati: “Nthawi ina m’mbuyomu, sindinkamva bwino m’thupi ndipo ndinkatopa kwambiri ndikalowa mu utumiki. Mkulu wina anazindikira kuti ndikuoneka wofooka ndipo anandithandiza. Tinakambirana nkhani ina yolimbikitsa ya m’Baibulo. Ndinatsatira malangizo ake ndipo zinandithandiza.” Mlongoyu ananenanso kuti: “Ndimathokoza kwambiri kuti mkuluyo anandisonyeza chikondi. Anazindikira kuti ndinafooka n’kundithandiza.” Zimatilimbikitsa kwambiri kudziwa kuti akulu amatikonda ndipo amachita nafe chidwi. Komanso, mofanana ndi Abisai, iwo amakhala okonzeka kutithandiza.
“MUDZIWE CHIKONDI CHIMENE NDILI NACHO . . . PA INU”
15, 16. (a) N’chifukwa chiyani abale ankakonda kwambiri Paulo? (b) N’chifukwa chiyani timakonda akulu athu mu mpingo?
15 Akulu amakhala ndi ntchito yambiri. Nthawi zina usiku, iwo sagona chifukwa chodera nkhawa abale ndi alongo, kuwapempherera kapena kuwathandiza. (2 Akor. 11:27, 28) Komabe iwo amagwira ntchito yawo mosangalala ndiponso mwakhama ngati mmene ankachitira Paulo. Iye analembera Akorinto kuti: “Ndidzagwiritsa ntchito zinthu zanga zonse ndipo ndidzadzipereka ndi moyo wanga wonse chifukwa cha miyoyo yanu.” (2 Akor. 12:15) Chifukwa chokonda abale ake, Paulo ankadzipereka kwambiri kuti awathandize. (Werengani 2 Akorinto 2:4; Afil. 2:17; 1 Ates. 2:8) M’pake kuti abale ankamukonda kwambiri Paulo.—Mac. 20:31-38.
16 Ifenso timakonda kwambiri akulu athu amene amatisamalira mwachikondi ndipo timathokoza Yehova m’mapemphero athu kuti amawagwiritsa ntchito kutithandiza. Iwo amatithandiza kukhala achimwemwe chifukwa amatiganizira ndipo amatilimbikitsa akabwera kudzacheza nafe. Timayamikiranso kuti akulu ndi okonzeka kutithandiza pamene tikuvutika kupirira mavuto a m’dzikoli. Akulu achikhristu amenewa alidi ‘antchito anzathu kuti tikhale ndi chimwemwe.’
a Abale ndi alongowo anafunsidwanso kuti, “Kodi mumafuna kuti mkulu akhale ndi khalidwe liti?” Ambiri mwa iwo ananena kuti amafuna kuti akhale wochezeka. Tidzakambirana khalidwe lofunika limeneli m’magazini yam’tsogolo.
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA