Muzifunafuna Chuma Chenicheni

Muzifunafuna Chuma Chenicheni

“Dzipezereni mabwenzi ndi chuma chosalungama.”—LUKA 16:9.

NYIMBO: 32, 154

1, 2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti osauka azipezekabe m’dziko la Satanali?

MASIKU ANO zinthu sizikuyenda mwachilungamo pa nkhani zachuma. Achinyamata ambiri amafufuza ntchito koma samaipeza. Ndipo ena amalolera kuika moyo wawo pa ngozi kuti asamukire kumayiko olemera. Koma m’mayiko olemerawo mumapezekanso anthu osauka. Ndipo kusiyana kwa pakati pa olemera ndi osauka kukuwonjezereka kwambiri. Ochita kafukufuku posachedwapa anapeza kuti pa anthu 100 alionse, munthu mmodzi wolemera kwambiri amakhala ndi chuma chofanana ndi chuma chonse cha anthu 99 otsalawo. Kaya zimenezi n’zoona kapena ayi, chomwe tonse tikudziwa n’chakuti pali anthu mabiliyoni ambiri amene ndi osauka kwambiri pomwe ena ali ndi chuma choti anthu ambiri sangachimalize pa moyo wawo wonse. Yesu ankadziwa kuti zimenezi zidzachitika ndipo ananena kuti: “Osaukawo muli nawo nthawi zonse.” (Maliko 14:7) N’chifukwa chiyani pali osauka ambiri chonchi m’dziko la Satanali?

2 Yesu ankadziwa kuti zinthu sizingayende mwachilungamo pa nkhani zachuma mpaka Ufumu wa Mulungu udzabwere. Dziko la Satanali lili ndi mbali zitatu zikuluzikulu. Pali andale, achipembedzo komanso “amalonda,” amene amatchulidwa pa Chivumbulutso 18:3. Anthu a Mulungu amapeweratu ndale ndiponso chipembedzo chonyenga koma ambiri sangapeweretu zamalonda m’dzikoli.

3. Kodi tikambirana mafunso ati?

3 Akhristufe tingachite bwino kudzifufuza pa nkhani ya malondayi podzifunsa mafunso awa: ‘Kodi ndingagwiritse ntchito bwanji chuma changa posonyeza kuti ndine wokhulupirika kwa Mulungu? Nanga ndingapewe bwanji kuchita kwambiri zamalonda? Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti anthu a Mulungu amamudalira kwambiri m’masiku ovuta ano?’

FANIZO LA MTUMIKI WOSALUNGAMA

4, 5. (a) Kodi n’chiyani chinachitikira mtumiki wamufanizo la Yesu? (b) Kodi Yesu anapereka malangizo otani kwa otsatira ake?

4 Werengani Luka 16:1-9. Fanizo la Yesu la mtumiki wosalungama ndi lothandiza kwambiri. Mtumikiyu atanenezedwa kuti ankasakaza chuma, anachita zinthu mwanzeru kuti ‘apeze mabwenzi’ omwe angamuthandize akadzachotsedwa ntchito. * Apa sikuti Yesu ankalimbikitsa ophunzira ake kuti azichita zachinyengo kuti apeze zofunika pa moyo wawo. Iye ananena kuti izi n’zimene “ana a m’dziko lino amachita” komabe anagwiritsa ntchito fanizoli pofuna kuti ophunzirawo amvetse mfundo ina.

5 Yesu ankadziwa kuti otsatira ake ambiri adzavutika kupeza zofunika pa moyo m’dziko lopanda chilungamoli ngati mmenenso zinalili ndi mtumiki wamufanizoyo. N’chifukwa chake anauza otsatira ake kuti: “Dzipezereni mabwenzi ndi chuma chosalungama, kuti chumacho chikatha, [Yehova ndi Yesu] akakulandireni m’malo okhala amuyaya.” Kodi ifeyo tingaphunzirepo chiyani pa malangizo a Yesuwa?

6. Kodi tikudziwa bwanji kuti sichinali cholinga cha Mulungu kuti anthu azichita malonda?

6 Ngakhale kuti Yesu sananene chifukwa chake ananena kuti “chuma chosalungama,” Baibulo limasonyeza kuti sichinali cholinga cha Mulungu kuti anthu azichita malonda. Yehova anapatsa Adamu ndi Hava zinthu zonse zimene ankafunikira pa moyo wawo. (Gen. 2:15, 16) Pakati pa Akhristu odzozedwa oyambirira “panalibe ngakhale mmodzi wonena kuti zinthu zimene anali nazo zinali zayekha. Zonse zimene anali nazo zinali za onse.” (Mac. 4:32) Mneneri Yesaya analosera za nthawi imene anthu onse sadzasowa chilichonse. (Yes. 25:6-9; 65:21, 22) Koma panopa otsatira a Yesu ayenera kuchita zinthu mwanzeru pogwiritsa ntchito “chuma chosalungama” kuti apeze zofunika pa moyo kwinaku akutumikira Mulungu.

TIZIGWIRITSA NTCHITO MWANZERU CHUMA CHOSALUNGAMA

7. Kodi Yesu anapereka malangizo otani pa Luka 16:10-13?

7 Werengani Luka 16:10-13. Mtumiki wotchulidwa mufanizo la Yesu anapeza mabwenzi n’cholinga choti adzamuthandize zikadzamuvuta. Koma Yesu sankalimbikitsa zolinga zadyera pamene ankauza otsatira ake kuti apeze mabwenzi kumwamba. Mavesi otsatira, amasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa kugwiritsa ntchito “chuma chosalungama” ndi kukhala wokhulupirika kwa Mulungu. Mfundo ya Yesu inali yoti n’zotheka kugwiritsa ntchito bwino chuma chosalungamacho kuti tikhale okhulupirika. Kodi tingachite bwanji zimenezi?

8, 9. Kodi anthu ena asonyeza bwanji kuti ndi okhulupirika pogwiritsa ntchito chuma chosalungama?

8 Njira imodzi imene tingasonyezere kuti ndife okhulupirika pogwiritsa ntchito chuma chathu chosalungama ndi kupereka ndalama zothandizira pa ntchito imene Yesu ananeneratu kuti izichitika masiku ano. (Mat. 24:14) Mwachitsanzo, mtsikana wina wamng’ono wa ku India anali ndi kabokosi kamene ankaponyamo ndalama ndipo pena ankalolera kuti asakhale ndi zidole kuti achite zimenezi. Bokosilo litadzaza anapereka ndalamazo kuti zithandize pa ntchito yolalikira. Ku India komweko kuli m’bale wina amene ali ndi munda wa kokonati ndipo amapereka kokonati wambiri ku ofesi ina ya omasulira mabuku. Iye atazindikira kuti abale a ku ofesiyo amagula kokonati, anaona kuti kupereka kokonatiyo kungathandize kwambiri kusiyana ndi kupereka ndalama. Apatu m’baleyu anaganiza mwanzeru. Nawonso abale a ku Greece amapereka mafuta a maolivi, tchizi komanso zakudya zina ku banja la Beteli.

9 M’bale wina wa ku Sri Lanka atasamukira kudziko lina, anapereka malo ake kuti anthu azichitirapo misonkhano yampingo ndi ikuluikulu komanso kuti kuzigona atumiki a nthawi zonse. M’baleyu analolera kuchita zimenezi kuti athandize abale ndi alongo ovutika a m’dzikoli. M’mayiko ena amene ntchito yathu ndi yoletsedwa, abale ndi alongo amalola kuti anthu azisonkhana m’nyumba zawo. Izi zimathandiza kuti apainiya komanso abale ena ovutika apeze malo ochitira misonkhano popanda kulipira ndalama.

10. Kodi timadalitsidwa bwanji tikakhala ndi mtima wopatsa?

10 Zitsanzo zimene takambiranazi zikusonyeza kuti anthu a Mulungu akuyesetsa kukhala ‘okhulupirika pa zinthu zazing’ono.’ (Luka 16:10) Iwo akugwiritsa ntchito mwanzeru chuma chawo podziwa kuti si chofunika kwambiri tikachiyerekezera ndi chuma chauzimu. Kodi iwo amamva bwanji akachita zimenezi? Amazindikira kuti mtima wopatsa ungawathandize kupeza “chuma chenicheni.” (Luka 16:11) Mlongo wina amene amakonda kupereka ndalama zothandizira pa ntchito za Ufumu anafotokoza mmene Mulungu wamudalitsira. Iye anati: “Ndimaona kuti kukhala ndi mtima wopatsa kumandithandiza kwambiri. Ndikamapatsa anthu zinthu zambiri, mtima wofuna kusonyeza chikondi kwa anthu umakulanso kwambiri. Ndimaona kuti ndimayambanso kukhala wokhululuka kwambiri, woleza mtima komanso sinditaya mtima ndikakhumudwitsidwa kapena kupatsidwa malangizo.” Anthu ambiri azindikira kuti mtima wopatsa umawathandiza kukhalanso ndi makhalidwe ena osangalatsa Mulungu.​—Sal. 112:5; Miy. 22:9.

11. (a) Kodi mtima wopatsa umasonyeza bwanji kuti ndife anzeru? (b) Kodi gulu lathandiza bwanji kuti pakhale kufanana pa nkhani ya ndalama? (Onani chithunzi choyambirira.)

11 Munthu akamapereka chuma chake pothandiza ntchito za Ufumu amasonyezanso nzeru m’njira ina. Tikutero chifukwa choti amakhala akugwiritsa ntchito zinthu zake pothandiza ena. Mwachitsanzo, abale ndi alongo ena ali ndi chuma koma sangakwanitse kuchita utumiki wa nthawi zonse kapena kusamukira kudziko lina. Koma ndalama zimene amapereka zimathandiza kuti anthu ena achite bwino utumiki wawo. (Miy. 19:17) Zopereka zathu zimathandiza kuti tizitha kusindikiza mabuku komanso kuti ntchito yolalikira iziyenda bwino m’mayiko osauka komwe anthu ambiri akuphunzira Baibulo. Kwa zaka zambiri, m’mayiko ena monga ku Congo, ku Madagascar ndi ku Rwanda, Mabaibulo anali odula kwambiri moti abale ankafunika kugwira ntchito mlungu umodzi kapenanso mwezi wathunthu kuti apeze ndalama zogulira Baibulo. Ena ankalolera kuti asagule chakudya n’cholinga choti akhale ndi Baibulo. Koma panopa zinthu zasintha chifukwa cha zopereka za anthu ambiri komanso chifukwa choti gulu lathandiza kuti “pakhale kufanana” pa nkhani ya ndalama. (Werengani 2 Akorinto 8:13-15.) Choncho Mabaibulo akumasuliridwa m’zilankhulo zambiri komanso kutumizidwa kwa aliyense mumpingo ndipo ngakhale ophunzira Baibulo akhoza kuwapeza. Apa tingati anthu opereka komanso olandira akukhala ndi mwayi wokhala mabwenzi a Yehova.

TIZIPEWA KUCHITA KWAMBIRI ZAMALONDA

12. Kodi Abulahamu anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira Mulungu?

12 Njira ina yothandizira kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova ndi kufunafuna “chuma chenicheni” m’malo mochita kwambiri zamalonda. Abulahamu, yemwe anali ndi chikhulupiriro cholimba, anamvera Yehova ndipo anachoka mumzinda wotukuka wa Uri n’kumakakhala m’mahema. Iye sanasiye kulimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova. (Aheb. 11:8-10) Nthawi zonse ankadalira Mulungu podziwa kuti amapereka “chuma chenicheni.” Ankapewanso kuchita chilichonse chosonyeza kuti ankadalira chuma osati Mulungu. (Gen. 14:22, 23) Yesu ankalimbikitsa anthu kuti akhale ndi chikhulupiriro choterechi pamene anauza mnyamata wina wachuma kuti: “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndipo ndalama zake upatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba, ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.” (Mat. 19:21) Zikuoneka kuti mnyamatayo analibe chikhulupiriro ngati cha Abulahamu, komabe pali anthu ena amene amakhulupirira Mulungu ndi mtima wonse.

13. (a) Kodi Paulo anapereka malangizo ati kwa Timoteyo? (b) Kodi ifeyo tingatsatire bwanji malangizo amenewo?

13 Nayenso Timoteyo anali ndi chikhulupiriro cholimba. Paulo ananena kuti Timoteyo anali “msilikali wabwino wa Khristu Yesu” ndipo anamuuzanso kuti: “Msilikali amene ali pa nkhondo sachita nawo zamalonda zimene anthu wamba amachita, pofuna kukondweretsa amene anamulemba usilikali.” (2 Tim. 2:3, 4) Masiku anonso otsatira a Yesu, omwe akuphatikizapo atumiki a nthawi zonse oposa 1 miliyoni, amachita zonse zimene angathe kuti azitsatira malangizo a Paulo. Iwo amayesetsa kuti asatengeke ndi otsatsa malonda kapena maganizo a m’dzikoli, m’malomwake amakumbukira mfundo yakuti: “Wobwereka amakhala kapolo wa wobwereketsayo.” (Miy. 22:7) Satana amafuna kuti tiziwononga nthawi yathu komanso mphamvu zathu zonse pochita zamalonda. Zinthu zina zimene tingachite m’dzikoli zikhoza kuchititsa kuti tikhale ndi ngongole kwa nthawi yaitali. Mwachitsanzo, kugula nyumba yaikulu, kupita kuyunivesite, kugula galimoto yapamwamba komanso mwambo wa ukwati wapamwamba zingachititse kuti tikhale ndi ngongole yaikulu. Timasonyeza kuti ndife anzeru tikamapewa ngongole n’kumakhala ndi moyo wosalira zambiri. Tikatero timakhala ndi mpata wotumikira Mulungu m’malo mokhala kapolo wa dzikoli.​—1 Tim. 6:10.

14. Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani? Perekani zitsanzo.

14 Kuti tikhale ndi moyo wosalira zambiri, tiyenera kuika zinthu zofunika pamalo oyamba. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi banja lina limene linali ndi bizinezi yaikulu koma ankafunitsitsa kuti ayambenso utumiki wa nthawi zonse. Choncho anagulitsa bizinezi yawo, boti lawo komanso zinthu zina. Kenako anadzipereka kuti akathandize nawo pomanga likulu lathu ku Warwick ku New York. Iwo anali ndi mwayi wogwira ntchito ku Beteli limodzi ndi mwana wawo wamkazi ndi mwamuna wake. Anathanso kugwira ntchito limodzi ndi makolo a m’baleyo kwa milungu ingapo ku Warwick. Chitsanzo china ndi cha mpainiya wina wa ku Colorado m’dziko la United States yemwe masiku ena ankagwira ntchito kubanki ina. Abwana ake anasangalala kwambiri ndi mmene ankagwirira ntchito moti ankafuna kumukweza pa ntchito komanso kumuwonjezera ndalama kuwirikiza katatu zimene ankalandira poyamba. Koma zimenezi zikanachititsa kuti ayambe kugwira ntchito tsiku lililonse. Popeza zimenezi zikanasokoneza utumiki wake, anakana ntchito yapamwambayi. Apa tangotchula zitsanzo zochepa chabe za abale ndi alongo amene alolera kusiya zinthu zina n’cholinga choti azichita zambiri potumikira Yehova. Nafenso tikamayesetsa kuika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba, timasonyeza kuti timaona ubwenzi wathu ndi Mulungu komanso chuma chauzimu kukhala zofunika kwambiri kuposa chuma cha m’dzikoli.

CHUMA CHA M’DZIKOLI CHIKADZATHA

15. Kodi ndi kulemera kotani kumene kumapangitsa munthu kukhala wosangalala?

15 Kukhala ndi chuma cha m’dzikoli si umboni woti Mulungu akutidalitsa. Yehova amadalitsa anthu “olemera pa ntchito zabwino.” (Werengani 1 Timoteyo 6:17-19.) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina wa ku Italy dzina lake Lucia *. Mlongoyu atamva zoti ku Albania kukufunika ofalitsa ambiri anasamukira kudzikolo mu 1993. Iye analibe ndalama koma anadalira Yehova ndi mtima wonse kuti akamuthandiza. Iye anaphunzira chilankhulo cha m’dzikoli ndipo anaphunzitsa anthu oposa 60 mpaka kufika pobatizidwa. Atumiki a Yehova ena amalalikira m’mayiko amene anthu ambiri samvetsera chonchi. Koma chilichonse chimene tingachite pothandiza anthu kuti ayambe kuyenda pamsewu wopita ku moyo wosatha chimakhala cha mtengo wapatali kwa ifeyo komanso kwa anthu amene timawaphunzitsawo.​—Mat. 6:20.

16. (a) Kodi n’chiyani chidzachitikire amalonda? (b) Popeza tikudziwa zimene zidzachitike m’tsogolo, kodi tiyenera kukhala ndi maganizo otani pa nkhani ya chuma cha m’dzikoli?

16 Yesu ananena kuti “chumacho chikatha” osati “ngati chingathe.” (Luka 16:9) Apa ankatanthauza kuti chumacho chidzatha ndithu. Mavuto azachuma amene akugwetsa mabanki ndi mabizinezi masiku ano ndi aang’ono tikayerekezera ndi zimene zichitike posachedwapa padziko lonse. Posachedwapa, mbali zonse za dziko la Satanali, zomwe ndi andale, achipembedzo komanso amalonda zidzatheratu. Mneneri Ezekieli ndi Zefaniya ananeneratu kuti golide ndi siliva zimene amalonda akhala akugwiritsa ntchito kwa nthawi yaitali zidzakhala zopanda ntchito. (Ezek. 7:19; Zef. 1:18) Kodi munthu angamve bwanji ataona kuti watsala pang’ono kufa kenako n’kuzindikira kuti walephera kupeza chuma chenicheni chifukwa choti ankatanganidwa ndi kufunafuna “chuma chosalungama”? Zikhoza kufanana ndi munthu amene wakhala akugwira ntchito kwa moyo wake wonse kuti apeze ndalama zambirimbiri koma n’kuzindikira kuti ndalama zonsezo n’zachinyengo. (Miy. 18:11) Popeza n’zosakayikitsa kuti chuma cha m’dzikoli chidzatha, tiyeni tiyesetse kuchigwiritsa ntchito mwanzeru kuti ‘tipeze mabwenzi’ kumwamba. Chilichonse chimene timachita chothandiza pa ntchito za Ufumu wa Yehova chimachititsa kuti tikhale olemera mwauzimu.

17, 18. Kodi anthu amene ali pa ubwenzi ndi Mulungu akuyembekezera zinthu ziti?

17 Ufumu wa Mulungu ukadzabwera, sipadzakhala kulipira lendi kapena kugula nyumba. Chakudya chidzakhala chambiri komanso chaulere ndipo sipadzakhala kugula mankhwala. Anthu a Yehova adzakhala ndi zinthu zabwino kwambiri padzikoli. Anthu azidzagwiritsa ntchito golide, siliva ndi miyala yamtengo wapatali pokongoletsa zinthu osati pochita bizinezi. Matabwa olimba, miyala komanso zitsulo zidzakhala zaulere ndipo anthu azidzamangira nyumba zawo zokongola. Anzathu azidzasangalala kutithandiza pomanga nyumbazi popanda kufuna malipiro. Padzakhala njira yabwino yothandiza kuti munthu aliyense padzikoli akhale ndi zinthu zofunika.

18 Zimene tafotokozazi ndi zinthu zochepa chabe zimene anthu adzapeze chifukwa chokhala ndi mabwenzi kumwamba. Atumiki a Yehova adzasangalala kwambiri akadzamva mawu a Yesu akuti: “Bwerani, inu amene mwadalitsidwa ndi Atate wanga. Lowani mu ufumu umene anakonzera inu kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa dziko.”​—Mat. 25:34.

^ ndime 4 Yesu sananene ngati mtumikiyo anachitadi zimene anamunenezazo. Mawu achigiriki amene anamasuliridwa kuti ‘kuneneza’ pa Luka 16:1 angatanthauze kunamizira munthu. Ndipo mfundo yaikulu ya Yesu inagona pa zimene mtumikiyo anachita atanenezedwa, osati chifukwa chimene anamuchotsera ntchito.

^ ndime 15 Mbiri ya moyo wa Lucia Moussanett ili mu Galamukani! ya July 8, 2003, tsamba 28-32.