Tizitsanzira Yehova pa Nkhani ya Chifundo
“Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo.”—EKS. 34:6.
NYIMBO: 142, 12
1. Kodi Mulungu anauza Mose zinthu ziti, nanga n’chifukwa chiyani anachita zimenezi?
PA NTHAWI ina Mulungu anauza Mose dzina lake komanso makhalidwe ake. Makhalidwe oyamba amene anatchula anali chifundo ndi chisomo. (Werengani Ekisodo 34:5-7.) Yehova akanatha kunena za mphamvu ndi nzeru zake koma sanachite zimenezo. M’malomwake ananena za makhalidwe amene amasonyeza kuti ndi wofunitsitsa kuthandiza anthu ake. Anachita zimenezi chifukwa choti pa nthawiyo Mose ankafunika kutsimikiziridwa kuti Mulungu amuthandiza. (Eks. 33:13) Nafenso tingalimbikitsidwe kudziwa kuti Mulungu ndi wachifundo komanso wachisomo. Chifundo chimatanthauza kumvera anthu ena chisoni n’kumafunitsitsa kuwathandiza. Munkhaniyi tikambirana za khalidwe limeneli.
2, 3. (a) N’chiyani chimasonyeza kuti tinalengedwa ndi mtima wachifundo? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kudziwa zimene Baibulo limanena pa nkhani ya chifundo?
2 Anthufe tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. Choncho popeza Yehova ndi wachifundo, ngakhale anthu amene sadziwa Mulungu amatha kusonyeza khalidweli. (Gen. 1:27) M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu amene anasonyeza chifundo. Mwachitsanzo, muli nkhani ya mahule awiri amene ankakanganirana mwana. Koma Solomo atalamula kuti mwanayo adulidwe, mayi weniweni anachitira mwanayo chifundo. Iye sanafune kuti mwanayo aphedwe moti ankaona kuti bola angotengedwa ndi mnzakeyo. (1 Maf. 3:23-27) Chitsanzo china ndi cha mwana wa Farao yemwe anapulumutsa Mose ali mwana. Iye anadziwa kuti mwanayo ndi wachiheberi ndipo ayenera kuphedwa. Koma “anamumvera chisoni” ndipo anasankha zoti amulere ngati mwana wake.—Eks. 2:5, 6.
3 N’chifukwa chiyani tiyenera kuona kuti chifundo ndi khalidwe lofunika? Zili choncho chifukwa Baibulo limatiuza kuti tizitsanzira Yehova. (Aef. 5:1) Ngakhale kuti tinalengedwa ndi mtima wachifundo, anthufe si angwiro ndipo nthawi zambiri timachita zinthu modzikonda. Nthawi zina zimativuta kusiya zofuna zathu n’cholinga choti tithandize anthu ena. Ndipo vuto limeneli ndi lalikulu kwa anthu ena. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiziganizira anthu ena? Choyamba, tiyeni tikambirane mmene Yehova wasonyezera chifundo komanso mmene anthu ena achisonyezera. Kenako, tikambirana mmene tingatsanzirire Mulungu komanso ubwino wochita zimenezi.
YEHOVA NDI CHITSANZO CHABWINO KWAMBIRI
4. (a) N’chifukwa chiyani Yehova anatumiza angelo ku Sodomu? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Loti ndi banja lake?
4 M’Baibulo muli nkhani zambiri zosonyeza kuti Yehova ndi wachifundo. Chitsanzo china ndi zimene zinachitikira Loti. Iye anali wolungama ndipo “anavutika mtima kwambiri” chifukwa cha khalidwe lotayirira limene linkachitika ku Sodomu ndi Gomora. Mulungu anaona kuti anthu amakhalidwe oipawo ayenera kuphedwa. (2 Pet. 2:7, 8) Choncho anatumiza angelo kuti akapulumutse Loti. Angelowo anauza Loti ndi banja lake kuti achoke m’mizindayo mwamsanga. Baibulo limanena kuti: “Pamene iye anali kuzengereza, [angelowo], mwa chifundo cha Yehova pa iye, anagwira dzanja iyeyo, mkazi wake, ndi ana ake aakazi awiriwo, n’kuwatulutsa kukawasiya kunja kwa mzinda.” (Gen. 19:16) Nkhani imeneyi ikusonyeza kuti Yehova amadziwa bwino mavuto amene atumiki ake okhulupirika amakumana nawo.—Yes. 63:7-9; Yak. 5:11; 2 Pet. 2:9.
5. Kodi mfundo ya pa 1 Yohane 3:17 ingatithandize bwanji kukhala achifundo?
5 Sikuti Yehova amangosonyeza chifundo, koma amaphunzitsanso anthu ake kuti azikhala achifundo. Chitsanzo ndi lamulo limene anapatsa Aisiraeli pa nkhani yolanda munthu chovala chake kuti chikhale chikole. (Werengani Ekisodo 22:26, 27.) Munthu wopanda chifundo akhoza kulanda chofunda cha munthu amene ali ndi ngongole n’kumusiya kuti agone osafunda. Koma Yehova sankafuna kuti anthu ake azikhala oipa mtima choncho. Ankafuna kuti azikhala achifundo. Kodi tikuphunzira chiyani pa lamulo limeneli? Tikadziwa vuto limene m’bale wathu ali nalo, lomwe tikhoza kuthandizapo, si bwino kungomusiya chifukwa zingakhale ngati tamusiya kuti agone osafunda.—Akol. 3:12; Yak. 2:15, 16; werengani 1 Yohane 3:17.
6. Kodi tikuphunzira chiyani pa chifundo chimene Yehova ankachitira Aisiraeli akachimwa?
6 Yehova ankachitiranso chifundo Aisiraeli akachimwa. Baibulo limanena kuti: “Yehova Mulungu wa makolo awo anapitiriza kuwatumizira machenjezo kudzera mwa amithenga ake. Anawatumiza mobwerezabwereza chifukwa ankamvera chisoni anthu akewo ndiponso malo ake okhala.” (2 Mbiri 36:15) Nafenso tiyenera kuchitira chifundo anthu amene akhoza kulapa machimo awo n’kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Yehova safuna kuti aliyense adzawonongedwe pa chisautso chachikulu. (2 Pet. 3:9) Choncho panopa tiyeni tipitirize kuchitira anthu chifundo polalikira uthenga wochenjeza.
7, 8. Kodi n’chiyani chinachititsa banja lina kuona kuti Yehova walichitira chifundo?
7 Pali nkhani zinanso zosonyeza kuti Mulungu ndi wachifundo. Nkhani ina ndi yokhudza mnyamata wina wazaka 12 dzina lake Milan. Pa nthawi ya nkhondo yapachiweniweni m’zaka za m’ma 1990, Milan, mng’ono wake ndiponso makolo ake anakwera basi yochoka ku Bosnia kupita ku Serbia. Iwo ankapita kumsonkhano wachigawo limodzi ndi a Mboni ena ndipo makolo a Milan ankayembekezera kukabatizidwa kumsonkhanoko. Atafika paboda asilikali anatsitsa banjali chifukwa cha mtundu wawo n’kuuza abale enawo kuti azipita. Atalisunga banjali kwa masiku awiri, mkulu wa asilikaliwo analankhula ndi abwana ake pa wailesi meseji, n’kufunsa kuti banjalo alichite chiyani. Popeza mkuluyo anali pafupi ndi banjalo, aliyense anamva abwana akewo akumuuza kuti: “Tangopita nawoni panja n’kukawaombera!”
8 Ndiyeno mkuluyo akulankhula ndi asilikali ena, panafika anthu awiri achilendo n’kuuza banjalo chapansipansi kuti nawonso ndi a Mboni. Anthuwo anali atamva nkhani ya banjali kwa anthu a m’basi ija. Iwo anauza Milan ndi mng’ono wake kuti akwere m’galimoto yawo kuti adutse nawo pabodapo chifukwa asilikali sankalimbana ndi ana. Kenako anauza makolo a anawo kuti azungulire kuseri kwa ofesi ya asilikaliwo n’kukakumana nawo mbali ina. Milan anadabwa ndi zimene anthuwo ananena. Makolo ake anafunsa anthuwo kuti: “Kodi mukuganiza kuti asilikali amenewa angatilekerere tikunyamuka?” Koma iwo atayamba kuyenda, asilikaliwo ankangowayang’ana osalankhula chilichonse. Makolowo anakakumana ndi ana awowo mbali ina ya bodayo. Kenako anapitiriza ulendo wawo wopita kumsonkhano ndipo ankaona kuti Yehova anayankha mapemphero awo pa nthawi yovuta kwambiriyi. N’zoona kuti Malemba amasonyeza kuti si nthawi zonse pamene Yehova amapulumutsa anthu ake m’njira yodabwitsa chonchi. (Mac. 7:58-60) Koma Milan ananena kuti: “Mmene Yehova anatipulumutsira pamenepa zinali ngati angelo angotseka maso asilikaliwo.”—Sal. 97:10.
9. Kodi Yesu anachita chiyani ataona anthu omvetsa chisoni? (Onani chithunzi choyambirira.)
9 Yesu anaperekanso chitsanzo chabwino pa nkhani ya chifundo. Iye anamvera chisoni anthu ambiri amene anakumana nawo chifukwa “anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” Ndiye kodi iye anatani? Baibulo limanena kuti: “Anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Mat. 9:36; werengani Maliko 6:34.) Yesu anali wosiyana kwambiri ndi Afarisi omwe sankafuna ngakhale pang’ono kuthandiza anthu wamba. (Mat. 12:9-14; 23:4; Yoh. 7:49) Kodi inuyo mumachitiranso chifundo anthu amene ali ndi njala yofuna kumva Mawu a Yehova?
10, 11. Kodi kusonyeza chifundo n’koyenera pa nthawi ina iliyonse? Fotokozani.
10 Koma zimenezi sizikutanthauza kuti chifundo chiyenera kusonyezedwa pa nthawi ina iliyonse. Munkhani za m’Baibulo zimene takambiranazi, zinali zoyenera kuti Mulungu asonyeze chifundo. Koma zimene Sauli anachita poganiza kuti n’chifundo zinali zolakwika. Iye sanamvere Mulungu chifukwa sanaphe Agagi, yemwe anali mdani wa anthu a Mulungu. Sanaphenso ziweto zimene iyeyo ankaona kuti ndi zabwino. Izi zinachititsa kuti Yehova aone kuti Sauli si woyeneranso kukhala mfumu ya Isiraeli. (1 Sam. 15:3, 9, 15) Yehova ndi woweruza wabwino chifukwa amaona zimene zili mumtima wa munthu ndipo amadziwa ngati ndi woyenera kuchitiridwa chifundo kapena ayi. (Maliro 2:17; Ezek. 5:11) Posachedwapa, iye adzawononga anthu onse amene samumvera. (2 Ates. 1:6-10) Pa nthawiyo, iye sadzachitira chifundo anthu amene wawaweruza kuti akuyenera kuphedwa. Koma adzapha anthu oipawo pofuna kusonyeza chifundo kwa anthu olungama amene adzapulumuke.
11 Si udindo wathu kuweruza anthu kuti akuyenera kuphedwa kapena kukhala ndi moyo. M’malomwake, tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tiwathandize. Ndiye kodi tingasonyeze bwanji chifundo kwa anzathu? Tiyeni tikambirane njira zingapo.
ZIMENE TINGACHITE POSONYEZA CHIFUNDO
12. Kodi mungasonyeze bwanji chifundo kwa anthu ena?
12 Tizithandiza anthu tsiku ndi tsiku. Anthu amene amayesetsa kutsanzira Yesu ayenera kusonyeza chifundo kwa Akhristu anzawo komanso kwa anthu ena. (Yoh. 13:34, 35; 1 Pet. 3:8) Mawu oti chifundo amatanthauzanso “kuvutikira limodzi ndi ena.” Choncho munthu wachifundo amamvera ena chisoni akamavutika ndipo amawathandiza. Inunso muziyesetsa kupeza njira zimene mungachitire zimenezi. Mwachitsanzo, ngati munthu wina ali ndi kantchito kenakake, mukhoza kumuthandiza.—Mat. 7:12.
13. Kodi anthu a Mulungu amasonyeza bwanji chifundo pakachitika ngozi?
13 Tizithandiza anthu pakachitika ngozi. Anthu ambiri amachitira chifundo anzawo akakumana ndi ngozi. Ndipo anthu a Yehova amadziwika kuti zoterezi zikachitika, amathandiza kwambiri. (1 Pet. 2:17) Mwachitsanzo, mlongo wina ku Japan ankakhala kudera limene kunasefukira madzi chifukwa cha chivomerezi mu 2011. Iye ananena kuti ‘analimbikitsidwa kwambiri’ ataona anthu ambiri ochokera ku Japan komweko komanso kumayiko ena atabwera kudzathandiza kukonza zinthu zimene zinawonongeka. Iye analemba kuti: “Zimenezi zinandithandiza kudziwa kuti Yehova amatikonda. Ndinaonanso kuti abale ndi alongo apadziko lonse amatikonda komanso amatipempherera.”
14. Kodi mungathandize bwanji anthu odwala komanso okalamba?
14 Tizithandiza anthu odwala komanso okalamba. Tikamaona anthu akuvutika chifukwa cha uchimo umene tinatengera kwa Adamu, timafuna kuwachitira chifundo. Tonsefe timalakalaka matenda ndi ukalamba zitatha. N’chifukwa chake timapemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere. Komanso timachita zimene tingathe pothandiza anzathu amene akuvutika. Wolemba mabuku wina analemba zimene zinachitikira mayi ake amene anali okalamba komanso ankadwala matenda a mu ubongo. Tsiku lina anadziipitsira ndipo pamene ankayesetsa kuti akonze zovala zawo, anthu ena anagogoda pakhomo. Anthuwo anali a Mboni awiri omwe ankakonda kubwera kudzacheza nawo. Alongowo anafunsa mayiwo ngati pali chinachake chimene angawathandize. Mayiwo anayankha kuti, “Ee kungoti n’zochititsa manyazi.” Komabe alongowo anawathandiza bwinobwino. Kenako anapangira mayiwo tiyi ndipo anapitiriza kucheza nawo. Mwana wawoyo anayamikira kwambiri ndipo analemba kuti: “A Mboniwo anachita bwino kwambiri. Iwo amachitadi zinthu zimene amaphunzitsa.” Kodi inuyo mumachitira chifundo anthu odwala komanso okalamba n’kumachita zonse zimene mungathe powathandiza?—Afil. 2:3, 4.
15. Kodi timakhala ndi mwayi wotani tikamalalikira?
15 Tizithandiza anthu kuti adziwe Mawu a Mulungu. Tikamaona anthu akuvutika komanso kuda nkhawa timafuna kuwalimbikitsa ndi Mawu a Mulungu. Njira yabwino yochitira zimenezi ndi kuwaphunzitsa za Mulungu komanso zimene Ufumu wake udzatichitire. Tikhozanso kuwathandiza kuti aone ubwino wotsatira mfundo za m’Baibulo. (Yes. 48:17, 18) Kodi inuyo mungawonjezere zimene mumachita mu utumiki? Paja ntchito imeneyi imalemekeza Yehova komanso imasonyeza kuti mumachitira chifundo anthu ena.—1 Tim. 2:3, 4.
KUCHITIRA ENA CHIFUNDO KUMAKUTHANDIZANINSO INUYO
16. Kodi kuchitira ena chifundo kumatithandizanso bwanji ifeyo?
16 Akatswiri azamaganizo amanena kuti kusonyeza chifundo kumathandiza munthu kukhala wathanzi, wosangalala komanso kuti azigwirizana ndi anzake. Munthu akathandiza anzake amamva bwino mumtima, nkhawa zake zimachepa ndipo saganizira kwambiri zinthu zokhumudwitsa. Zonsezi zikusonyeza kuti kuchitira ena chifundo kumatithandizanso ifeyo. (Aef. 4:31, 32) Akhristu amene amathandiza anthu ena amakhala ndi chikumbumtima chabwino chifukwa chodziwa kuti akutsatira mfundo za makhalidwe abwino. Mtima wachifundo umathandiza munthu kukhala wabwino kwa ana ake, mwamuna kapena mkazi wake komanso kwa anzake. Ndipo anthu amene amakonda kuthandiza anzawo nawonso akhoza kuthandizidwa akakumana ndi vuto.—Werengani Mateyu 5:7; Luka 6:38.
17. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchitira ena chifundo?
17 Koma sikuti tizingochitira ena chifundo n’cholinga choti ifeyo tipezepo phindu. Cholinga chachikulu pochitira ena chifundo chizikhala kutsanzira Yehova Mulungu wathu wachifundo komanso kumulemekeza. (Miy. 14:31) Iye amapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani imeneyi. Ndiye tiyeni tonse tizichita zonse zimene tingathe pomutsanzira. Tikamachita zimenezi, tidzayamba kukondana kwambiri ndi abale ndi alongo athu komanso kugwirizana ndi anthu ena.—Agal. 6:10; 1 Yoh. 4:16.
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA