Choonadi sichibweretsa “mtendere koma lupanga”

Choonadi sichibweretsa “mtendere koma lupanga”

“Musaganize kuti ndinabweretsa mtendere padziko lapansi, sindinabweretse mtendere koma lupanga.”​MAT. 10:34.

NYIMBO: 125, 135

1, 2. (a) Kodi panopa tingakhale ndi mtendere uti? (b) N’chifukwa chiyani panopa n’zosatheka kukhala pa mtendere ndi anthu onse? (Onani chithunzi choyambirira.)

TONSE timafuna kukhala moyo wamtendere, wopanda nkhawa. Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa amatipatsa “mtendere wa Mulungu,” umene ndi mtendere wamumtima womwe umatithandiza kuti tisamade nkhawa kwambiri. (Afil. 4:6, 7) Tikadzipereka kwa Yehova, timakhalanso pa “mtendere ndi Mulungu,” zomwe zikutanthauza kuti timakhala naye pa ubwenzi.​—Aroma 5:1.

2 Komabe nthawi ya Mulungu yoti tikhale pa mtendere ndi anthu onse sinafike. M’masiku otsirizawa, kukuchitika mikangano yambiri ndipo anthu ambiri ali ndi mtima wokonda kuyambana ndi anzawo. (2 Tim. 3:1-4) Akhristufe tiyenera kumenya nkhondo yolimbana ndi Satana ndiponso mfundo zabodza zimene amaphunzitsa. (2 Akor. 10:4, 5) Koma nthawi zambiri mtendere wathu umasokonekera chifukwa cha achibale athu omwe si Mboni. Ena angamanyoze mfundo zimene timakhulupirira, kutinena kuti tikugawanitsa banja lathu kapena angamatiopseze kuti tikapitiriza sazitionanso ngati achibale awo. Koma kodi tiyenera kukumbukira chiyani ngati achibale athu amatitsutsa? Nanga tingapirire bwanji mavuto amene amabwera chifukwa chotsutsidwa ndi achibale?

ZIMENE TIYENERA KUKUMBUKIRA NGATI ACHIBALE ATHU AMATITSUTSA

3, 4. (a) Kodi zimene Yesu ankaphunzitsa zikhoza kubweretsa mavuto otani? (b) Kodi ndi nthawi iti pamene kutsatira Yesu kumakhala kovuta kwambiri?

3 Yesu ankadziwa kuti zimene ankaphunzitsa zingagawanitse anthu, ndiponso kuti anthu amene amamutsatira ayenera kukhala olimba mtima chifukwa azitsutsidwa. Kutsutsidwaku kukhoza kuchititsa kuti anthu m’banja asamakhale mwamtendere. Yesu ananena kuti: “Musaganize kuti ndinabweretsa mtendere padziko lapansi, sindinabweretse mtendere koma lupanga. Pakuti ndinabwera kudzagawanitsa anthu. Ndinabwera kudzachititsa munthu kutsutsana ndi bambo ake, mwana wamkazi kutsutsana ndi mayi ake, ndiponso mtsikana wokwatiwa kutsutsana ndi apongozi ake aakazi. Kunena zoona, adani a munthu adzakhala a m’banja lake lenileni.”​—Mat. 10:34-36.

4 Ponena kuti “Musaganize kuti ndinabweretsa mtendere,” Yesu ankatanthauza kuti omvera ake ayenera kuganizira zimene zingachitike ngati atakhala otsatira ake. Uthenga umene Yesu ankalalikira ukanatha kugawanitsa anthu. N’zoona kuti cholinga cha Yesu chinali kulengeza uthenga wochokera kwa Mulungu, osati kugawanitsa anthu. (Yoh. 18:37) Komabe kutsatira mokhulupirika zimene ankaphunzitsa kungakhale kovuta ngati achibale komanso anzake a munthuyo ali osakhulupirira.

5. Kodi otsatira a Yesu amakumana ndi zotani?

5 Yesu anasonyeza kuti ena mwa mavuto amene otsatira ake ayenera kuwapirira ndi kutsutsidwa ndi achibale. (Mat. 10:38) Kuti asonyeze kuti ndi Akhristu enieni, otsatira a Yesu amapirira akamanyozedwa kapena kusalidwa ndi achibale awo. Komabe amapeza madalitso ambiri oposa zimene ataya.​—Werengani Maliko 10:29, 30.

6. Kodi tiyenera kukumbukira zinthu ziti ngati achibale athu amatitsutsa?

6 Achibale athu akamatitsutsa, timapitirizabe kuwakonda. Komabe tizikumbukira kuti tiyenera kukonda Yehova ndi Khristu kuposa achibalewo. (Mat. 10:37) Tizikumbukiranso kuti Satana angagwiritse ntchito chikondi chimene timakhala nacho pa achibale athu kuti atichititse kukhala osakhulupirika kwa Mulungu. Tiyeni tsopano tikambirane zinthu zina zimene tingakumane nazo komanso zimene tingachite kuti tipirire.

NGATI MWAMUNA KAPENA MKAZI WANU SI MBONI

7. Kodi munthu ayenera kuchita chiyani ngati mwamuna kapena mkazi wake ndi wosakhulupirira?

7 Baibulo limachenjeza kuti anthu amene amalowa m’banja “adzakhala ndi nsautso m’thupi mwawo.” (1 Akor. 7:28) Koma ngati mwamuna kapena mkazi wanu si wa Mboni, mavutowa akhoza kuchuluka. Komabe, muyenera kuiona nkhaniyi mmene Yehova amaionera. Ngakhale kuti mwamuna kapena mkazi wanuyo panopa safuna kukhala wotsatira wa Khristu, chimenechi si chifukwa chokwanira chopatukirana kapena kuthetsa banja. (1 Akor. 7:12-16) N’zoona kuti mwamuna wosakhulupirira sangatsogolere pa zinthu zauzimu, komabe muyenera kumulemekeza chifukwa cha udindo wake monga mutu wa banja. N’chimodzimodzinso ndi mkazi wosakhulupirira. Mwamuna wake, yemwe ndi Mkhristu, ayenerabe kumukonda kwambiri.​—Aef. 5:22, 23, 28, 29.

8. Kodi mungadzifunse mafunso otani ngati mkazi kapena mwamuna wanu akukuletsani zinthu zina zokhudza kulambira?

8 Nanga bwanji ngati mkazi kapena mwamuna wanu amakuletsani kuchita zinthu zina zokhudza kulambira? Mwachitsanzo, mlongo wina analetsedwa ndi mwamuna wake kulowa mu utumiki wakumunda masiku enaake pa mlungu. Ngati zoterezi zitakuchitikirani, muyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi pamenepa akundiletsa kutumikira Mulungu? Ngati sakundiletsa, kodi n’zotheka kuchita zimene akufunazo?’ Kukhala ololera kungakuthandizeni kuti muzikhala mwamtendere m’banja.​—Afil. 4:5.

9. Kodi Akhristu angaphunzitse bwanji ana awo kuti azilemekeza kholo lawo lomwe si Mboni?

9 Ngati mwamuna kapena mkazi wanu ndi wosakhulupirira, kuphunzitsa ana kumakhala kovuta. Mwachitsanzo, muyenera kuphunzitsa ana anu kutsatira lamulo la m’Baibulo lakuti: “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.” (Aef. 6:1-3) Koma nanga bwanji ngati mwamuna kapena mkazi wanuyo satsatira mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo? Inuyo muyenerabe kumamulemekeza kuti mupereke chitsanzo chabwino kwa ana. Muyenera kuganizira kwambiri zinthu zimene amachita bwino ndipo muzimuyamikira. Pakakhala ana anu, muzipewa kulankhula zimene mwamuna kapena mkazi wanu amalakwitsa. Muzifotokozera anawo kuti aliyense ali ndi ufulu wosankha kutumikira Yehova kapena ayi. Khalidwe labwino la ana anu likhoza kukopa mwamuna kapena mkazi wanuyo kuti nayenso ayambe kutumikira Mulungu.

Gwiritsani ntchito mpata uliwonse kuphunzitsa ana anu mfundo za m’Baibulo (Onani ndime 10)

10. Kodi makolo achikhristu angaphunzitse bwanji ana awo mfundo za m’Baibulo ngati mwamuna kapena mkazi wawo si Mboni?

10 Nthawi zina, mwamuna kapena mkazi wosakhulupirirayo angafune kuphunzitsa ana anu mfundo zabodza za ku chipembedzo chake kapena angafune kuti achite naye limodzi chikondwerero chinachake chosemphana ndi Malemba. Amuna ena osakhulupirira amaletsa akazi awo kuti asamaphunzitse ana awo Baibulo. Ngakhale zitakhala choncho, mkazi wachikhristu amayesetsa kupeza njira yophunzitsira anawo mfundo zoona za m’Baibulo. (Mac. 16:1; 2 Tim. 3:14, 15) Mwachitsanzo, mwina mwamuna wosakhulupirira sangalole kuti mkazi wake aziphunzira Baibulo ndi ana awo kapena kuwatenga kumisonkhano. Zikatere, mkaziyo ayenera kugonjera zimene mwamuna wake wanena komabe mwayi ukapezeka ayenera kufotokozera anawo zimene iyeyo amakhulupirira. Zimenezi zingawathandize kuphunzira makhalidwe abwino komanso mfundo zokhudza Yehova. (Mac. 4:19, 20) Komabe tiyenera kudziwa kuti anawo akadzakula adzasankha okha kutumikira Yehova kapena ayi.​—Deut. 30:19, 20. *

ZIMENE TIYENERA KUCHITA NGATI ACHIBALE ENA AMATITSUTSA

11. Kodi n’chiyani chingachititse kuti musiyane maganizo ndi achibale anu omwe si Mboni?

11 Mwina poyamba sitinafotokozere achibale athu kuti tayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova. Koma chikhulupiriro chathu chitayamba kukula tinaona kuti ndi bwino kuuza ena zimene tayamba kukhulupirira. (Maliko 8:38) Koma mwina kukhala wokhulupirika kwa Yehova kwachititsa kuti muzisiyana maganizo ndi achibale anu omwe si Mboni. Choncho tiyeni tikambirane zimene mungachite kuti muzikhala nawo mwamtendere koma n’kukhalabe okhulupirika kwa Yehova.

12. Kodi achibale athu angamatitsutse chifukwa chiyani, nanga ifeyo tiyenera kuchita chiyani kuti tiziwamvetsa?

12 Tiziyesetsa kuwamvetsa achibale athu. Ifeyo tikhoza kusangalala kwambiri kuti taphunzira mfundo zolondola za m’Baibulo koma achibale athu akhoza kuganiza kuti tikupusitsidwa kapena talowa gulu lolakwika. Akhoza kuganizanso kuti tasiya kuwakonda chifukwa choti tasiya kuchita nawo zikondwerero zina. Atha kumaonanso kuti tsogolo lathu silili bwino. Choncho kuti tiziwamvetsa, tiyenera kuyesetsa kuona zinthu mmene iwo akuzionera komanso kuwamvetsera bwino kuti tidziwe zimene zikuwadetsa nkhawa. (Miy. 20:5) Mtumwi Paulo ankayesetsa kumvetsa “anthu osiyanasiyana” n’cholinga choti akwanitse kuwauza uthenga wabwino, ndipo njira imeneyi ingatithandizenso ifeyo.​—1 Akor. 9:19-23.

13. Kodi tiyenera kulankhula bwanji ndi achibale athu omwe si Mboni?

13 Tizilankhula nawo mofatsa. Baibulo limanena kuti: “Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo.” (Akol. 4:6) Tiyenera kupempha Yehova kuti atipatse mzimu woyera n’cholinga choti tikamalankhula ndi achibale athu tizisonyeza makhalidwe amene mzimuwo umatulutsa. Si bwino kutsutsana nawo pa mfundo zilizonse zabodza zimene amakhulupirira. Iwo akalankhula kapena kuchita zinthu zotikhumudwitsa tiyenera kutsanzira atumwi. Paja Paulo analemba kuti: “Pamene akutinenera zachipongwe, timadalitsa. Pozunzidwa, timapirira. Ponyozedwa, timayankha mofatsa.”​—1 Akor. 4:12, 13.

14. Kodi chingachitike n’chiyani ngati titakhala ndi khalidwe labwino?

14 Tizikhala ndi makhalidwe abwino. N’zoona kuti kulankhula mofatsa kumathandiza pochita zinthu ndi achibale amene si Mboni. Koma kukhala ndi khalidwe labwino ndi kumene kumathandiza kwambiri. (Werengani 1 Petulo 3:1, 2, 16.) Tiziyesetsa kuchita zimene tingathe kuti achibale athu aone kuti a Mboni za Yehova amakhala ndi mabanja osangalala, amasamalira ana awo, amakhala ndi makhalidwe abwino komanso amakhala osangalala. Ngakhale achibale athu atapanda kuphunzira Baibulo tikhoza kukhala osangalala podziwa kuti tasangalatsa Yehova chifukwa cha kukhulupirika kwathu.

15. Kodi tingakonzekere bwanji kuti tisamakangane ndi achibale athu?

15 Tizikonzekera. Ndi bwino kuganizira zimene zingachititse kuti musiyane maganizo n’kuoneratu zimene mungachite kuti musakangane. (Miy. 12:16, 23) Mlongo wina wa ku Australia anati: “Apongozi anga aamuna ankatsutsa kwambiri choonadi. Choncho tisanawaimbire foni kuti tione ngati ali bwino, ine ndi mwamuna wanga tinkapempha Yehova kuti atithandize n’cholinga choti tisakhumudwe akatikwiyira. Tinkaganiziratunso nkhani zoti tikambirane nawo zomwe sangakwiye nazo. Sitinkalankhula nawo kwa nthawi yaitali poopa kuti tingayambe kukambirana kwambiri nkhani zachipembedzo zimene zingayambitse mikangano.”

16. Kodi mungatani kuti musamadziimbe mlandu chifukwa chosiyana maganizo ndi achibale anu?

16 N’zoona kuti sizingatheke kupeweratu kusiyana maganizo ndi achibale athu amene si Mboni. Ndipo zoterezi zikachitika tikhoza kudziimba mlandu makamaka chifukwa chakuti timawakonda kwambiri achibalewo ndipo sitifuna kuwakhumudwitsa. Komabe tizikumbukira kuti kusangalatsa Yehova n’kofunika kwambiri kuposa kusangalatsa achibale athu. Zimenezi zingathandize achibalewo kuzindikira kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo ndi nkhani yaikulu yomwe ingachititse kuti munthu adzapeze moyo kapena ayi. Kaya zinthu zili bwanji, tizikumbukira kuti sitingakakamize munthu kuti ayambe kuphunzira choonadi. M’malomwake tizingoyesetsa kuchita zinthu zimene zingawathandize kuona ubwino wotsatira mfundo za Yehova. Yehova amapereka kwa munthu aliyense ufulu wosankha kumutumikira kapena ayi.​—Yes. 48:17, 18.

WACHIBALE AKASIYA YEHOVA

17, 18. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni ngati wachibale wanu wasiya kutumikira Yehova?

17 Wachibale wathu akachotsedwa kapena akadzilekanitsa ndi mpingo, zimakhala zopweteka kwambiri ngati kuti wina watilasa ndi lupanga. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kupirira ngati zimenezi zachitika?

18 Musasiye kuchita zinthu zokhudza kulambira. Muzilimbitsa chikhulupiriro chanu powerenga Baibulo nthawi zonse, kukonzekera ndiponso kupezeka pamisonkhano yachikhristu, kugwira nawo ntchito yolalikira ndiponso kupemphera kwa Mulungu kuti akuthandizeni kupirira. (Yuda 20, 21) Koma bwanji ngati mukudzimva kuti mukungochita zinthuzo mwamwambo chabe? Musataye mtima. Kupitirizabe kuchita zinthu zauzimu kungathandize kuti maganizo anu akhalenso m’malo. Taganizirani chitsanzo cha munthu amene analemba Salimo 73. Iye anayamba kuona zinthu molakwika ndipo zinamuvutitsa kwambiri. Koma anasintha mmene ankaonera zinthu atafika pamalo olambirira Mulungu. (Sal. 73:16, 17) Nanunso zingakuyendereni bwino ngati mutapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika.

19. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mukugwirizana ndi chilango chimene Yehova wapereka?

19 Muzivomereza chilango cha Yehova. Chilango chimene Yehova amapereka chimakhala chothandiza kwa onse, kuphatikizapo wolakwayo, ngakhale kuti poyamba zimakhala zopweteka. (Werengani Aheberi 12:11.) Mwachitsanzo, Yehova amatiuza kuti ‘tileke kuyanjana’ ndi anthu ochimwa amene sakulapa. (1 Akor. 5:11-13) Ngakhale kuti zingakhale zopweteka, tiyenera kupewa kucheza ndi wachibale amene wachotsedwa, kaya polemberana makalata, mameseji, maimelo kapena njira zina.

20. Kodi sitiyenera kutaya mtima pa nkhani iti?

20 Musataye mtima. Chikondi “chimayembekezera zinthu zonse,” kuphatikizapo kuyembekezera kuti anthu amene anasiya Yehova adzabwerera. (1 Akor. 13:7) Ngati mutaona kuti wachibale wanu wayamba kusintha mtima wake, mungamupempherere kuti apeze mphamvu kuchokera m’Malemba ndipo avomere pamene Yehova akumupempha kuti: “Bwerera kwa ine.”​—Yes. 44:22.

21. Kodi muyenera kuchita chiyani ngati banja lanu lagawanika chifukwa choti mukutsatira Yesu?

21 Yesu ananena kuti ngati timakonda munthu aliyense kuposa mmene timakondera iyeyo, ndiye kuti sitingakhale wotsatira wake. Komabe, sankakayikira kuti otsatira ake adzapitirizabe kukhala okhulupirika kwa iye ngakhale atamatsutsidwa ndi achibale awo. Ngati kutsatira Yesu kwabweretsa “lupanga” m’banja lanu, muyenera kudalira Yehova kuti akuthandizeni kupirira. (Yes. 41:10, 13) Muzisangalala podziwa kuti Yehova ndi Yesu akusangalala nanu ndipo adzakupatsani mphoto ngati mutakhalabe okhulupirika.

^ ndime 10 Kuti mudziwe mfundo zina zothandiza pophunzitsa ana m’banja limene mwamuna kapena mkazi si Mboni, onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2002.