NKHANI YOPHUNZIRA 3

Kodi Tingateteze Bwanji Mtima Wathu?

Kodi Tingateteze Bwanji Mtima Wathu?

“Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenera kutetezedwa.”​MIY. 4:23.

NYIMBO NA. 36 Timateteza Mtima Wathu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-3. (a) N’chifukwa chiyani Yehova ankakonda Solomo, nanga Solomoyo anapeza madalitso otani? (b) Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?

SOLOMO anakhala mfumu ya Aisiraeli ali mnyamata. Atangoyamba kumene kulamulira, Yehova anaonekera kwa iye m’maloto ndipo anamuuza kuti: “Pempha chimene ukufuna kuti ndikupatse.” Solomo anayankha kuti: “Ndine mwana ndipo sindikudziwa zinthu zambiri. . . . Mupatse mtumiki wanune mtima womvera kuti ndiweruze anthu anu.” (1 Maf. 3:5-10) Solomo anapempha “mtima womvera” ndipo zimenezi zimasonyeza kuti anali wodzichepetsa. M’pake kuti Yehova ankamukonda kwambiri. (2 Sam. 12:24) Mulungu anasangalala kwambiri ndi zimene Solomo anapempha moti anamupatsa “mtima wanzeru ndi womvetsa zinthu.”​—1 Maf. 3:12.

2 Pamene Solomo anali wokhulupirika kwa Yehova, ankadalitsidwa kwambiri. Iye anapatsidwa mwayi womanga kachisi wodziwika ndi “dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.” (1 Maf. 8:20) Solomo anatchuka kwambiri chifukwa cha nzeru zimene Mulungu anamupatsa. Ndipo mfundo zimene ananena atauziridwa ndi Mulungu zinalembedwa m’mabuku atatu a m’Baibulo. Buku la Miyambo ndi limodzi mwa mabuku amenewa.

3 Mawu akuti mtima amapezeka malo oposa 100 m’buku la Miyambo. Mwachitsanzo, lemba la Miyambo 4:23 limati: “Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenera kutetezedwa.” Kodi palembali mawu akuti “mtima” amatanthauza chiyani? Tiyankha funso limeneli munkhaniyi. Nkhaniyi itithandizanso kupeza mayankho a mafunso awiri awa: Kodi Satana angasokoneze bwanji mtima wathu? Nanga tingauteteze bwanji? Kudziwa mayankho a mafunso ofunikawa kungatithandize kuti tikhalebe okhulupirika kwa Mulungu.

KODI MAWU AKUTI “MTIMA” AMATANTHAUZA CHIYANI?

4-5. (a) Kodi lemba la Salimo 51:6 limatithandiza bwanji kumvetsa tanthauzo la mawu akuti “mtima”? (b) Kodi zimene zimachitika ndi thupi lathu lenileni zimafanana bwanji ndi munthu wathu wamkati?

4 Pa Miyambo 4:23, mawu akuti “mtima” akutanthauza “munthu wamkati” kapena kuti “munthu wobisika.” (Werengani Salimo 51:6.) Choncho tinganene kuti mawu akuti “mtima” amanena za maganizo athu, mmene tikumvera mumtima, zolinga zathu komanso zimene timalakalaka. Tingati ndi mmene tilili mkati mwathu osati mmene timaonekera kwa anthu ena.

5 Kuti timvetse za munthu wathu wamkati, tiyeni tikambirane za thupi lathu lenileni. Choyamba, kuti tikhale athanzi timafunika kudya chakudya chabwino komanso kuchita masewera olimbitsa thupi. N’chimodzimodzinso ndi munthu wathu wamkati. Kuti tikhale athanzi timafunika chakudya chauzimu komanso kuchita zinthu zosonyeza kuti timakhulupirira Yehova. Mwachitsanzo, tiyenera kutsatira zimene timaphunzira komanso kuuza anthu ena zimene timakhulupirira. (Aroma 10:8-10; Yak. 2:26) Chachiwiri, munthu akhoza kuoneka kuti ndi wathanzi koma mkati mwa thupi lake ali ndi matenda. Mofanana ndi zimenezi, tingaganize kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba chifukwa choti timachita zinthu zokhudza kulambira koma mumtima mwathu titayamba kulakalaka zinthu zoipa. (1 Akor. 10:12; Yak. 1:14, 15) Tiyenera kukumbukira kuti Satana amafuna kutisokoneza kuti tiziyendera maganizo ake. Kodi iye angachite bwanji zimenezi? Nanga tingadziteteze bwanji?

KODI SATANA ANGASOKONEZE BWANJI MTIMA WATHU?

6. Kodi cholinga cha Satana ndi chiyani, nanga amagwiritsa ntchito njira ziti?

6 Satana ndi chigawenga chodzikonda komanso chosamvera Yehova ndipo amafuna kuti nafenso tizichita zomwezo. Koma sangatikakamize kutengera maganizo kapena zochita zake. Choncho amagwiritsa ntchito njira zina pofuna kutisokoneza. Mwachitsanzo, angagwiritse ntchito anthu a m’dzikoli omwe wawasocheretsa kale. (1 Yoh. 5:19) Iye amafuna kuti tizicheza nawo kwambiri ngakhale kuti timadziwa mfundo yoti kugwirizana ndi anthu oipa “kumawononga” maganizo ndi makhalidwe athu. (1 Akor. 15:33) Satana anagwiritsa ntchito njira imeneyi posokoneza Mfumu Solomo. Paja Solomo anakwatira akazi ambiri osalambira Yehova omwe pamapeto pake “anapotoza mtima” wake.​—1 Maf. 11:3.

Kodi mungateteze bwanji mtima wanu kuti Satana asausokoneze ndi maganizo ake? (Onani ndime 7) *

7. Kodi Satana amagwiritsanso ntchito chiyani pofuna kuti anthu atengere maganizo ake, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala?

7 Satana amagwiritsa ntchito mafilimu ndi mapulogalamu a pa TV pofuna kuti anthu azitengera maganizo ake. Iye amadziwa kuti nkhani zopeka zimasangalatsa komanso zimachititsa kuti munthu asinthe maganizo ndi zochita zake. Yesu ankagwiritsa ntchito mafanizo pofuna kuphunzitsa anthu m’njira yowafika pamtima. Mwachitsanzo, anafotokoza fanizo la Msamariya wachifundo komanso la mwana wolowerera amene anawononga cholowa chake. (Mat. 13:34; Luka 10:29-37; 15:11-32) Koma nkhani zopekedwa ndi anthu amene akuyendera maganizo a Satana zikhoza kutisokoneza. Choncho tiyenera kukhala oganiza bwino. N’zoona kuti tikhoza kusangalala ndi mafilimu komanso mapulogalamu ena a pa TV popanda kusokoneza maganizo athu. Koma tiyenera kukhala osamala. Tikamasankha zosangalatsa tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndikuphunzira chiyani pa zimene ndikuonerazi? Kodi sizingandichititse kuganiza kuti palibe vuto kumangochita zofuna za thupi langa?’ (Agal. 5:19-21; Aef. 2:1-3) Kodi muyenera kuchita chiyani mukazindikira kuti pulogalamu inayake ikulimbikitsa maganizo a Satana? Muyenera kuipeweratu ngati mmene mungapewere matenda oopsa.

8. Kodi makolo angathandize bwanji ana kuti aziteteza mitima yawo?

8 Ngati ndinu makolo, muli ndi udindo waukulu woteteza ana anu kuti asasokonezedwe ndi Satana. N’zosachita kufunsa kuti mumateteza ana anu kuti asadwale matenda alionse. Mwachitsanzo, mumaonetsetsa kuti pakhomo panu m’paukhondo komanso mumataya chilichonse chimene chingadwalitse inuyo kapena ana anu. Mofanana ndi zimenezi, muyenera kuteteza ana anu ku mafilimu, mapulogalamu a pa TV, masewera a pa kompyuta komanso mawebusaiti amene akhoza kuwachititsa kuti atengere maganizo a Satana. Yehova wakupatsani udindo wosamalira ana anu mwauzimu. (Miy. 1:8; Aef. 6:1, 4) Choncho musamaope kuika malamulo m’banja lanu omwe akugwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Muziuza ana anu zinthu zoyenera kuonera ndi zosayenera kuonera ndipo muziwathandiza kuzindikira zifukwa zake. (Mat. 5:37) Ndiyeno anawo akamakula, muziwathandiza kuti azigwiritsa ntchito mfundo za Yehova kuti azitha kuzindikira paokha zoyenera ndi zolakwika. (Aheb. 5:14) Muzikumbukiranso kuti ana amatsatira kwambiri zochita zanu kuposa zolankhula zanu.​—Deut. 6:6, 7; Aroma 2:21.

9. Kodi Satana amafuna kuti anthu azikhala ndi maganizo ati, nanga n’chifukwa chiyani maganizo amenewa ndi oopsa?

9 Satana amafunanso kutisokoneza potichititsa kuganiza kuti nzeru za anthu n’zabwino kusiyana ndi za Mulungu. (Akol. 2:8) Mwachitsanzo, iye amafuna kuti anthu aziganiza kuti chofunika kwambiri pa moyo ndi kupeza chuma. Anthu amene amayendera maganizo amenewa akhoza kupezadi chuma kapena osachipeza. Koma kaya chumacho achipeze kapena ayi, akhoza kukumana ndi mavuto. Tikutero chifukwa chakuti pofunafuna chumacho amatha kuwononga thanzi lawo, mabanja awo mwinanso ubwenzi wawo ndi Mulungu. (1 Tim. 6:10) Timayamikira kwambiri kuti Atate wathu wakumwamba, yemwe ndi wanzeru, amatithandiza kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ndalama.​—Mlal. 7:12; Luka 12:15.

KODI TINGATETEZE BWANJI MTIMA WATHU?

Mofanana ndi alonda akale, tiyenera kukhala maso n’kumapewa zinthu zoipa zimene zingasokoneze mtima wathu (Onani ndime 10-11) *

10-11. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti titeteze mtima wathu? (b) Kodi alonda ankachita chiyani, nanga chikumbumtima chathu chingafanane bwanji ndi mlonda?

10 Kuti titeteze mtima wathu tiyenera kuzindikira zinthu zimene zingatisokoneze n’kumazipewa mwamsanga. Mawu amene anamasuliridwa kuti ‘kuteteza’ pa Miyambo 4:23 amatikumbutsa za ntchito imene mlonda amagwira. Pa nthawi ya Mfumu Solomo, alonda ankaima pampanda wa mzinda n’kumachenjeza anthu akaona zoopsa. Mfundo imeneyi imatithandiza kudziwa zimene tiyenera kuchita kuti Satana asasokoneze maganizo athu.

11 Kale, alonda apampanda ankagwira ntchito mogwirizana ndi alonda apachipata. (2 Sam. 18:24-26) Iwo ankathandizana poteteza mzinda ndipo ankaonetsetsa kuti mageti atsekedwa pamene adani akubwera. (Neh. 7:1-3) Chikumbumtima chophunzitsidwa Baibulo * chimakhala ngati mlonda ndipo chimatichenjeza pamene Satana akufuna kuwononga mtima wathu kapena kuti pamene akuyesetsa kusokoneza maganizo athu, zolinga zathu kapena zimene timalakalaka. Chikumbumtima chathu chikatichenjeza tiyenera kumvera n’kuchita zinthu mwamsanga ngati mlonda amene watseka geti.

12-13. Kodi anthufe tikhoza kukopeka kuti tichite chiyani, koma tiyenera kuchita chiyani?

12 Tiyeni tikambirane chitsanzo cha mmene tingadzitetezere kuti tisasokonezedwe ndi maganizo a Satana. Yehova watiphunzitsa kuti ‘dama ndi chonyansa chamtundu uliwonse zisatchulidwe n’komwe pakati pathu.’ (Aef. 5:3) Koma kodi tingatani ngati anzathu akuntchito kapena kusukulu ayamba kulankhula za chiwerewere? Timadziwa kuti tiyenera “kukana moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko.” (Tito 2:12) Choncho chikumbumtima chathu, chomwe chili ngati mlonda, chikhoza kutichenjeza. (Aroma 2:15) Ndiye kodi zikatero, tingachimvere? Mwina tikhoza kukopeka n’kuyamba kumvetsera nkhani zawozo kapena kuona nawo zithunzi zimene akuona. Koma chofunika pa nthawi ngati imeneyi ndi kusintha mwamsanga nkhani kapena kuchokapo. Tikatero timakhala ngati tikutseka mageti a mtima wathu.

13 Timafunika kulimba mtima kuti tisamangotengera maganizo kapena zochita za anzathu. Chosangalatsa n’chakuti Yehova amaona zimene tikuyesetsa kuchita ndipo amatipatsa mphamvu komanso nzeru zotithandiza kuti tisamatengere maganizo a Satana. (2 Mbiri 16:9; Yes. 40:29; Yak. 1:5) Koma kodi ndi zinthu zina ziti zimene zingatithandize kuteteza mtima wathu?

TIZIKHALA MASO

14-15. (a) N’chifukwa chiyani timafunika kutsegula mtima wathu, nanga tingachite bwanji zimenezi? (b) Kodi lemba la Miyambo 4:20-22 limatithandiza bwanji kuti tizipindula kwambiri powerenga Baibulo? (Onaninso bokosi lakuti “ Zimene Mungachite Posinkhasinkha.”)

14 Kuti titeteze mtima wathu tiyeneranso kuutsegula kuti mulowe zinthu zabwino. Chitsanzo cha mzinda chija chingatithandizenso pa nkhaniyi. Mlonda ankatseka geti ngati kukubwera adani koma nthawi zina ankatsegula kuti anthu alowetse chakudya ndi zinthu zina zofunika. Mageti akanati azikhala otseka nthawi zonse ndiye kuti anthu amumzindawo akanafa ndi njala. Nafenso tiyenera kutsegula mtima wathu kuti muzilowa maganizo a Yehova.

15 Maganizo a Yehovawo tingawapeze m’Baibulo. Choncho tikamaliwerenga timalola maganizo akewo kusintha maganizo athu, mtima wathu komanso zochita zathu. Ndiye kodi tingatani kuti tizipindula kwambiri powerenga Baibulo? Kupemphera kumathandiza kwambiri. Mlongo wina anati: “Ndimapemphera ndisanayambe kuwerenga Baibulo ndipo ndimapempha Yehova kuti andithandize kuzindikira ‘zinthu zodabwitsa’ za m’Mawu ake.” (Sal. 119:18) Tiyeneranso kusinkhasinkha zimene tikuwerenga. Tikamapemphera, kuwerenga Mawu a Mulungu ndiponso kuwasinkhasinkha, mawuwo amafika “mkati mwa mtima” wathu ndipo timayamba kukonda maganizo a Yehova.​—Werengani Miyambo 4:20-22; Sal. 119:97.

16. Kodi JW Broadcasting ikuthandiza bwanji anthu?

16 Chinthu china chimene chingathandize kuti maganizo a Yehova azilowa mumtima mwathu ndi kuonera mapulogalamu a pa JW Broadcasting®. Banja lina linati: “Yehova wayankha mapemphero athu potipatsa mapulogalamu a mwezi uliwonse. Amatilimbikitsa kwambiri tikakhumudwa kapena tikamasowa ocheza nawo. Kunyumba kwathu timakonda kumvetsera nyimbo za pa JW Broadcasting. Timazimvetsera pophika, pokonza m’nyumba ngakhalenso tikamamwa tiyi.” Mapulogalamu amenewa amatithandiza kuti titeteze mtima wathu. Amatiphunzitsa kuti tiziyendera maganizo a Yehova n’kumapewa maganizo a Satana.

17-18. (a) Mogwirizana ndi 1 Mafumu 8:61, kodi kutsatira zimene Yehova amatiphunzitsa kumatithandiza bwanji? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Mfumu Hezekiya? (c) Malinga ndi pemphero la Davide lopezeka pa Salimo 139:23, 24, kodi tikhoza kupempherera chiyani?

17 Nthawi iliyonse imene taona ubwino wochita zinthu zoyenera, chikhulupiriro chathu chimalimba. (Yak. 1:2, 3) Timamva bwino podziwa kuti Yehova akusangalala nafe ndipo mtima wofuna kumukondweretsa umakula. (Miy. 27:11) Mayesero alionse amene tingakumane nawo amatipatsa mwayi wosonyeza kuti timatumikira Yehova ndi mtima wonse. (Sal. 119:113) Timasonyeza kuti timakonda Yehova kuchokera pansi pa mtima ndipo timafunitsitsa kumvera malamulo ake komanso kuchita zimene amafuna.​—Werengani 1 Mafumu 8:61.

18 Popeza si ife angwiro, nthawi zina timalakwitsa zinthu. Zimenezi zikachitika, tizingokumbukira chitsanzo cha Mfumu Hezekiya. Nayenso analakwitsa zinthu zina. Koma iye analapa ndipo anapitiriza kutumikira Yehova “ndi mtima wathunthu.” (Yes. 38:3-6; 2 Mbiri 29:1, 2; 32:25, 26) Choncho tiyeni tiziyesetsa kupewa kusokonezeka ndi maganizo a Satana. Komanso tizipempha Yehova kuti atipatse “mtima womvera.” (1 Maf. 3:9; werengani Salimo 139:23, 24.) Tingakhalebe okhulupirika kwa Yehova ngati nthawi zonse timayesetsa kuteteza mtima wathu.

NYIMBO NA. 54 “Njira Ndi Iyi”

^ ndime 5 Kodi tidzakhalabe okhulupirika kwa Yehova kapena tidzalola kuti Satana atisokoneze? Yankho la funso limeneli silidalira kukula kwa mayesero amene tingakumane nawo koma mmene tikutetezera mtima wathu. Kodi mawu akuti “mtima” amatanthauza chiyani? Kodi Satana angasokoneze bwanji mtima wathu? Nanga tingatani kuti tiuteteze? Mafunso amenewa ayankhidwa munkhaniyi.

^ ndime 11 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Yehova anatipatsa luso loti tizitha kufufuza maganizo athu, mtima wathu komanso zochita zathu n’kumadziweruza. M’Baibulo luso limeneli limatchedwa chikumbumtima. (Aroma 2:15; 9:1) Chikumbumtima chophunzitsidwa Baibulo chimagwiritsa ntchito mfundo za Yehova, zomwe zimapezeka m’Baibulo, kuti chiziweruza ngati zimene timaganiza, kuchita kapena kulankhula zili zabwino kapena ayi.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale wobatizidwa akuonera TV ndiye pabwera zinthu zolaula. Ayenera kusankha zochita.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlonda waona zinthu zoopsa kunja kwa mzinda. Kenako akuuza alonda apageti ndipo nthawi yomweyo akutseka getilo.