NKHANI YOPHUNZIRA 22

Muziyesetsa Kuti Kuphunzira Kuzikuthandizani!

Muziyesetsa Kuti Kuphunzira Kuzikuthandizani!

“Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”​AFIL. 1:10.

NYIMBO NA. 35 “Muzitsimikizira Kuti Zinthu Zofunika Kwambiri Ndi Ziti”

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. N’chifukwa chiyani anthu ambiri zimawavuta kuphunzira?

MASIKU ano pamafunika khama kuti tizipeza zofunika pa moyo. Abale ambiri amagwira ntchito maola ambiri kuti asamalire mabanja awo. Pomwe ena amayenda mtunda wautali tsiku lililonse kuti akafike kuntchito. Enanso amagwira ntchito zotopetsa kuti apeze zofunika pa moyo. Tsiku likamatha amakhala atatoperatu moti safuna kuphunzira.

2. Kodi inuyo mumaphunzira nthawi yanji?

2 Ngakhale zili choncho, tiyenera kupeza nthawi yoti tiziphunzira mwakhama Mawu a Mulungu komanso zinthu zina zimene gulu latipatsa. Tiyenera kumaphunzira kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ukhale wolimba komanso kuti tidzapeze moyo wosatha. (1 Tim. 4:15) Ena amadzuka m’mawa kwambiri tsiku lililonse kuti aziphunzira Mawu a Mulungu pambuyo poti apuma usiku komanso kulibe phokoso. Enanso amapeza maminitsi ochepa madzulo kuti aphunzire Mawu a Mulungu komanso kuganizira zimene aphunzira.

3-4. Kodi gulu lasintha zinthu ziti, nanga n’chifukwa chiyani?

3 Malinga ndi zimene takambiranazi, kupeza nthawi yophunzira n’kofunika kwambiri. Koma kodi tiyenera kuphunzira chiyani? Mwina mungaone kuti pali zambiri zoti tiwerenge moti simungakwanitse kumaliza zonse. Ena amakwanitsa kuwerenga komanso kuonera zinthu zonse zimene timapatsidwa. Koma ena zimawavuta kupeza nthawi yochitira zonsezi. Bungwe Lolamulira limadziwa zimenezi. Choncho gulu lachepetsako zinthu zowerenga zimene limatipatsa.

4 Mwachitsanzo, Buku Lapachaka la Mboni za Yehova linasiya kusindikizidwa chifukwa nkhani zambiri zolimbikitsa zimapezeka pa jw.org® komanso m’mapulogalamu a JW Broadcasting®. Ndipo magazini ogawira a Nsanja ya Olonda komanso Galamukani! ayamba kutuluka katatu kokha pa chaka. Sikuti zimenezi zasintha n’cholinga choti tizikhala ndi nthawi yambiri yochita zinthu zina. Koma cholinga ndi choti tizikhala ndi nthawi yokwanira kuti tiziphunzira “zinthu zofunika kwambiri.” (Afil. 1:10) Tiyeni tsopano tikambirane zimene tingachite kuti tiziyamba n’kuphunzira zinthu zofunika kwambiri komanso kuti zimene timaphunzirazo zizitithandiza.

MUZIYAMBA NDI ZINTHU ZOFUNIKA KWAMBIRI

5-6. Kodi ndi zinthu ziti zimene tiyenera kuziphunzira mosamala?

5 Kodi tiyenera kuyamba n’kuphunzira zinthu ziti? Chofunika kwambiri ndi kupeza nthawi tsiku lililonse yophunzira Mawu a Mulungu. Panopa, machaputala oti tiziwerenga pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uliwonse anachepetsedwa. Anachita zimenezi kuti tizikhala ndi nthawi yokwanira yoganizira zimene tawerenga komanso kufufuza mfundo zina. Cholinga chathu chisamangokhala kumaliza kuwerenga malemba amene tapatsidwawo. Koma tizikhala ndi cholinga choti zimene tikuwerenga m’Baibulo zizitifika pamtima komanso zizitithandiza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova.​—Sal. 19:14.

6 Koma kodi ndi zinthu zina ziti zimene tiyenera kuphunzira mosamala? Ndi bwinonso kukonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda, Phunziro la Baibulo la Mpingo komanso nkhani zina zapamisonkhano. Tiyeneranso kumawerenga magazini onse a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!

7. Kodi tiyenera kudandaula ngati sitingathe kuwerenga kapena kuonera zinthu zonse zimene zimapezeka pawebusaiti yathu kapena pa JW Broadcasting?

7 Mwina munganene kuti zimenezi n’zoona, koma nanga bwanji zinthu zambirimbiri zimene zimaikidwa pa jw.org komanso pa JW Broadcasting? Kuti timvetse nkhaniyi, yerekezerani kuti mwapita kulesitilanti ndipo mwapeza kuti kuli zakudya zabwino zambirimbiri. Sikuti mungakwanitse kudya zakudya zonsezo koma mungasankhe zimene mungakwanitse kudya basi. N’chimodzimodzi ndi zinthu zimene zimapezeka pawebusaiti yathu kapena pa JW Broadcasting. Ngati simungakwanitse kuwerenga kapena kuonera zonse, musamadandaule. Muzingowerenga kapena kuonera zimene mungakwanitse. Tsopano tiyeni tikambirane zimene zimafunika pophunzira komanso zimene tingachite kuti kuphunzirako kuzitithandiza kwambiri.

PAMAFUNIKA KHAMA KUTI TIPHUNZIRE BWINO

8. Kodi ndi zinthu ziti zimene tingachite tikamaphunzira Nsanja ya Olonda, nanga zingatithandize bwanji?

8 Kuphunzira kumatanthauza kuwerenga ndi cholinga chofuna kumvetsa bwino zimene mukuwerengazo. Sikutanthauza kumangowerenga mofulumira n’kulemba mizere kunsi kwa mayankho. Mwachitsanzo, tikamakonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda, choyamba tiziwerenga kachigawo kakuti “Zimene Tiphunzire” kamene kamakhala kumayambiriro kwa nkhaniyo. Chachiwiri, tiziganizira mutu wa nkhaniyo, timitu komanso mafunso obwereza. Chachitatu, tiziwerenga nkhaniyo mofatsa komanso mosamala. Tiziganiziranso chiganizo chimene chili ndi mfundo yaikulu yamundime iliyonse, chomwe nthawi zambiri chimakhala choyambirira. Chiganizochi chingatithandize kudziwa zimene tiphunzire mundime imene tikuwerengayo. Mukamawerenga nkhaniyo muziona kugwirizana pakati pa ndime iliyonse ndi timitu komanso mutu wa nkhaniyo. Muzionanso mawu aliwonse achilendo komanso mfundo zimene mungafune kufufuza kuti muzimvetse bwino.

9. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira kwambiri malemba tikamaphunzira Nsanja ya Olonda, nanga tingachite bwanji zimenezi? (b) Mogwirizana ndi lemba la Yoswa 1:8, kodi tiyenera kuchitanso zinthu ziti tikawerenga malemba?

9 Tikamaphunzira Nsanja ya Olonda timakhala kuti tikuphunziranso Baibulo. Choncho tiziganizira kwambiri malemba, makamaka amene adzawerengedwe pa phunzirolo. Tizionanso kugwirizana pakati pa mawu ofunika a m’malembawo ndi mfundo yaikulu yamundimeyo. Tizisinkhasinkhanso malemba amene tawerengawo komanso kuona mmene tingawagwiritsire ntchito pa moyo wathu.​—Werengani Yoswa 1:8.

Makolo, muyenera kuphunzitsa ana anu zimene ayenera kuchita akamaphunzira (Onani ndime 10) *

10. Malinga ndi Aheberi 5:14, n’chifukwa chiyani makolo ayenera kuthandiza ana awo kuti azidziwa mmene angaphunzirire komanso kufufuza zinthu?

10 Makolo ambiri amafuna kuti ana awo azisangalala pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja mlungu uliwonse. Koma ngakhale kuti makolo ayenera kudziwa komanso kukonzekera zimene angachite pa nthawi ya kulambira, sayenera kuganiza kuti mlungu uliwonse azichita zinthu zapadera kapena zosangalatsa kwambiri. N’zoona kuti nthawi zina banja likhoza kuonera JW Broadcasting kapena kuchita zinthu zapadera ngati kuyerekezera kupanga chingalawa. Koma ndi bwinonso kuthandiza ana kuti azidziwa mmene angaphunzirire. Mwachitsanzo, mungawaphunzitse kukonzekera misonkhano kapena kufufuza nkhani yokhudza zimene zachitika kusukulu. (Werengani Aheberi 5:14.) Ngati ana amaphunzira kunyumba, sangavutike kumvetsera kumisonkhano ya mpingo kapena ikuluikulu pamene mavidiyo sakuonetsedwa. Kuchuluka kwa nthawi imene tingachite kulambirako kumadalira msinkhu wa ana komanso mmene anawo alili.

11. N’chifukwa chiyani tiyenera kuthandiza anthu amene timaphunzira nawo Baibulo kudziwa mmene angaphunzirire paokha?

11 Anthu amene timaphunzira nawo Baibulo amafunikanso kudziwa mmene angaphunzirire paokha. Munthu akangoyamba kuphunzira, timasangalala kumuona akulemba mizere kunsi kwa mayankho pokonzekera phunziro lake kapena misonkhano. Koma tiyenera kuwaphunzitsanso mmene angaphunzirire kapena kufufuza zinthu paokha. Ubwino wa zimenezi ndi wakuti akakumana ndi vuto, sangathamangire kukafunsa abale ndi alongo, koma adzafufuza okha m’mabuku zoyenera kuchita.

MUZIKHALA NDI CHOLINGA POPHUNZIRA

12. Kodi tingakhale ndi zolinga zotani pophunzira?

12 Ngati simukonda kuwerenga mwina mungaganize kuti n’zosatheka kusangalala pophunzira. Koma n’zotheka. Ndi bwino kuyamba n’kuphunzira kwa nthawi yochepa kenako n’kumawonjezera nthawiyo pang’onopang’ono. Muyenera kukhala ndi cholinga pophunzirapo. N’zoona kuti cholinga chathu chachikulu chiyenera kukhala choti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova. Koma tingakhale ndi zolinga zina monga kupeza yankho la funso limene tafunsidwa kapena kudziwa zochita pa vuto linalake limene takumana nalo.

13. (a) Kodi wachinyamata angachite zinthu ziti pokonzekera kukafotokoza kusukulu zimene amakhulupirira? (b) Kodi mungatsatire bwanji mfundo ya pa Akolose 4:6?

13 Mwachitsanzo, kodi ndinu wachinyamata ndipo muli pasukulu? Anzanu onse akhoza kumakhulupirira kuti kuimba nawo nyimbo ya fuko n’kofunika. Ndiyeno inuyo mumafuna kuwafotokozera zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhaniyi koma mumadzikayikira. Zikatero chofunika kuchita n’kuifufuza nkhaniyi. Pofufuzapo mungakhale ndi zolinga ziwiri. Choyamba, mungafune kutsimikizira panokha kuti sitiyenera kukhala mbali ya dziko. Chachiwiri, mungafune kupeza njira yabwino yofotokozera zimene mumakhulupirirazo. (Yoh. 17:16; 1 Pet. 3:15) Mwina mungayambe ndi kudzifunsa kuti, ‘Kodi anzanga angapereke zifukwa ziti zosonyeza kuti tiyenera kuimba nyimbo ya fuko?’ Kenako mungafufuze nkhaniyi m’mabuku athu. Mukatero mudzaona kuti kufotokoza zimene mumakhulupirira si kovuta ngati mmene munkaganizira. Anthu ambiri amaganiza kuti ayenera kuimba nawo nyimboyi chifukwa choti munthu wina amene amamulemekeza anawauza kuti aziimba. Mukangopeza mfundo imodzi kapena ziwiri mukhoza kukayankha bwinobwino munthu amene akufunadi kudziwa zoona pa nkhaniyi.​—Werengani Akolose 4:6.

KODI MUNGATANI KUTI MUZIKONDA KUPHUNZIRA?

14-16. (a) Kodi mungatani kuti mumvetse buku la m’Baibulo lomwe simukulidziwa bwino? (b) Kodi malemba amene ali kumapeto kwa ndime 16 angakuthandizeni bwanji kumvetsa buku la Amosi? (Onaninso bokosi lakuti “ Muzikhala Ngati Mukuona Anthu Otchulidwa M’Baibulo.”)

14 Tiyerekeze kuti kumisonkhano tidzakambirana za buku lina laling’ono lamaulosi ndipo inuyo simukudziwa zambiri zokhudza bukulo. Choyamba, mungachite bwino kukhala ndi chidwi choti mudziwe zimene mneneriyo analemba. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

15 Mwina mungayambe ndi kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikudziwa zotani zokhudza mneneriyu? Kodi anali munthu wotani, ankakhala kuti, nanga ankagwira ntchito yotani?’ Zinthu ngati zimenezi zingakuthandizeni kumvetsa mawu kapena mafanizo amene anagwiritsa ntchito. Mukamawerenga Baibulo muziona mawu amene amasonyeza mmene wolembayo analili.

16 Chachiwiri, mungachite bwino kudziwa nthawi imene analemba buku lake. Mungapeze zimenezi mosavuta pachigawo chakuti “Mabuku a M’baibulo ndi Tsatanetsatane Wake” chomwe chili kumapeto kwa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika. Komanso mukhoza kuona tchati cha aneneri ndi mafumu chomwe chikupezeka mu Kabuku Kothandiza Kuphunzira Mawu a Mulungu pachigawo cha 3-A ndi 3-B. Ngati mukuphunzira za buku la m’Baibulo lamaulosi mungachite bwino kufufuza mmene zinthu zinalili pa nthawi imene bukulo linkalembedwa. Mwachitsanzo, mungadzifunse kuti, ‘Kodi mneneriyo ankafuna kuti anthu asinthe zinthu ziti? Nanga pa nthawi yake panalinso aneneri ena? Kuti mudziwe zonsezi mwina mungafunike kufufuza m’mabuku angapo. Mwachitsanzo, kuti tidziwe bwinobwino zimene zinkachitika pa nthawi imene Amosi anali mneneri, tingafunike kuona nkhani za m’mabuku a 2 Mafumu ndi 2 Mbiri, omwe amapezeka pa malifalensi apalemba la Amosi 1:1. Mukhozanso kuwerenga zimene Hoseya analemba chifukwa ankakhala nthawi yofanana ndi Amosi. Zonsezi zingakuthandizeni kuti mumvetse mmene zinthu zinalili pa nthawi ya Amosi.​—2 Maf. 14:25-28; 2 Mbiri 26:1-15; Hos. 1:1-11; Amosi 1:1.

MUZICHITA CHIDWI NDI ZINTHU ZING’ONOZING’ONO

17-18. Perekani chitsanzo, kaya chamundimeyi kapena chanu, chosonyeza kuti kuchita chidwi ndi zinthu zing’onozing’ono kungathandize kuti kuphunzira kukhale kosangalatsa.

17 Ndi bwino kuchita chidwi ndi zinthu mukamawerenga Baibulo. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mukuwerenga chaputala 12 m’buku la Zekariya chomwe chinalosera za imfa ya Mesiya. (Zek. 12:10) Mutafika pavesi 12 mukuwerenga kuti “banja la nyumba ya Natani” lidzalira kwambiri Mesiya akadzaphedwa. Ndiye m’malo mongopitiriza kuwerenga, mukudzifunsa kuti, ‘Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa banja la Natani ndi Mesiya?’ Pofuna kupeza yankho la funsoli, mukuyamba kufufuza. Mukupeza kuti pavesili pali lifalensi ya 2 Samueli 5:14 ndipo ikunena kuti Natani anali mwana wa Mfumu Davide. Lifalensi ina ndi ya Luka 3:31 ndipo ikusonyeza kuti Yesu anali mbadwa ya Natani kudzera mwa Mariya. (Onani Nsanja ya Olonda ya August 2017, tsamba 32, ndime 4.) Ndiyeno mwayamba kuchita chidwi kwambiri. Munkadziwa kuti Baibulo linaneneratu kuti Yesu adzakhala mwana wa Davide. (Mat. 22:42) Koma Davide anali ndi ana aamuna oposa 20. Choncho mukudabwa kwambiri kuona kuti Zekariya ananeneratu kuti banja la Natani ndi limene lidzalira kwambiri chifukwa cha imfa ya Yesu.

18 Taganizirani chitsanzo china. Chaputala choyamba cha Luka chimanena kuti mngelo Gabirieli anabwera kudzauza Mariya kuti adzabereka mwana wamwamuna. Ananena kuti: “Ameneyu adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba. Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu wa Davide atate wake. Iye adzalamulira monga mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya.” (Luka 1:32, 33) Mwina tingaganizire kwambiri mawu oyamba a Gabirieli akuti Yesu “adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba.” Koma mngeloyo ananenanso kuti Yesu “adzalamulira monga mfumu.” Ndiye tingadzifunse kuti, ‘Kodi Mariya ankaganiza kuti mawuwa akutanthauza chiyani? Kodi ankaganiza kuti akutanthauza kuti Yesu adzalowa m’malo mwa Mfumu Herode kapena wolamulira wina wa Isiraeli yemwe adzabwera pambuyo pake?’ Ngati Yesu akanakhala mfumu ya Isiraeli, Mariya akanakhala mayi a mfumu ndipo iye ndi banja lake akanapita kukakhala kunyumba yachifumu. Koma Baibulo silinena kuti Mariya anafunsa Gabirieli chilichonse pa nkhaniyi. Palibenso lemba lililonse losonyeza kuti Mariya anapempha kuti akhale ndi malo apamwamba mu Ufumu ngati mmene ophunzira awiri a Yesu anachitira. (Mat. 20:20-23) Mfundo imeneyi imatitsimikizira kuti Mariya analidi wodzichepetsa kwambiri.

19-20. Mogwirizana ndi Yakobo 1:22-25 ndi 4:8, kodi tiyenera kukhala ndi zolinga ziti pophunzira?

19 Tisaiwale kuti cholinga chathu chachikulu pophunzira Mawu a Mulungu komanso mabuku athu ndi kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Timafunanso kudziwa kuti ndife ‘anthu otani,’ nanga tikufunika kusintha zinthu ziti kuti tizisangalatsa Mulungu. (Werengani Yakobo 1:22-25; 4:8.) Choncho tisanayambe kuphunzira tiyenera kupempha Yehova kuti atipatse mzimu wake woyera. Tiyeneranso kumupempha kuti atithandize kupindula kwambiri ndi zimene tiphunzire komanso kuti tizidziona mmene iyeyo amationera.

20 Tiyeni tonsefe tiziyesetsa kukhala ngati munthu amene wolemba masalimo anamufotokoza kuti: “Amakondwera ndi chilamulo cha Yehova, ndipo amawerenga ndi kusinkhasinkha chilamulo chake usana ndi usiku. . . . Ndipo zochita zake zonse zidzamuyendera bwino.”​—Sal. 1:2, 3.

NYIMBO NA. 88 Ndidziwitseni Njira Zanu

^ ndime 5 Yehova watipatsa zinthu zambiri zoti tiziphunzira, kuwerenga komanso kuonera. Nkhaniyi itithandiza kudziwa zoyenera kuphunzira komanso zimene tingachite kuti kuphunzirako kuzitithandiza kwambiri.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Makolo akusonyeza ana awo zimene angachite pokonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda.

^ ndime 63 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale akufufuza kuti amudziwe bwino Amosi amene analemba buku la m’Baibulo. Zithunzi zomwe zili kumbuyo kwake zikusonyeza zimene m’baleyo akuona m’maganizo ake pamene akuwerenga ndiponso kusinkhasinkha nkhaniyi.