NKHANI YOPHUNZIRA 21

Tisapusitsidwe ndi “Nzeru za M’dzikoli”

Tisapusitsidwe ndi “Nzeru za M’dzikoli”

“Kwa Mulungu nzeru za m’dzikoli n’zopusa.”1 AKOR. 3:19.

NYIMBO NA. 98 Malemba Anauziridwa ndi Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi Mawu a Mulungu amatipatsa chiyani?

ANTHUFE tikhoza kupirira kapena kuthana ndi vuto lililonse chifukwa chakuti Yehova ndi Mlangizi wathu wamkulu. (Yes. 30:20, 21) Mawu ake amatipatsa zinthu zonse zofunika kuti munthu akhale “woyenerera bwino ndi wokonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (2 Tim. 3:17) Tikamatsatira mfundo za m’Baibulo timakhala anzeru kuposa anthu amene amaona kuti ndi bwino kutsatira “nzeru za m’dzikoli.”​—1 Akor. 3:19; Sal. 119:97-100.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Munkhaniyi tiona kuti nzeru za m’dzikoli zimagwirizana ndi zimene anthufe timalakalaka. Choncho tingamavutike kupewa kuganiza komanso kuchita zinthu zimene anthu a m’dzikoli amaganiza ndi kuchita. M’pake kuti Baibulo limatichenjeza kuti: “Samalani: mwina wina angakugwireni ngati nyama, mwa nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu.” (Akol. 2:8) Munkhaniyi tikambirana zimene zinachitika kuti anthu ambiri ayambe kukhulupirira mabodza awiri. Kenako tiona chifukwa chake tinganene kuti nzeru za m’dzikoli ndi zopusa koma nzeru za m’Mawu a Mulungu ndi zapamwamba kuposa chilichonse cha m’dzikoli.

MAGANIZO A ANTHU ANASINTHA PA NKHANI YA MAKHALIDWE ABWINO

3-4. Kodi maganizo a anthu ambiri ku United States anasintha bwanji pa nkhani ya makhalidwe abwino?

3 M’zaka zoyambirira za m’ma 1900, maganizo a anthu ambiri ku United States anasintha pa nkhani ya makhalidwe abwino. Poyamba, anthu ambiri ankakhulupirira kuti anthu okwatirana okha ndi amene ayenera kugonana ndipo nkhani zoterezi sankakonda kuzitchula pagulu. Koma maganizo amenewa anasintha kwambiri.

4 M’zaka za m’ma 1920 makhalidwe a anthu anasintha kwambiri. Munthu wina wochita kafukufuku ananena kuti: “Zinthu monga mafilimu, masewero, nyimbo, mabuku komanso zinthu zotsatsira malonda zinkalimbikitsa kugonana.” Pa nthawiyo anthu anayamba kuvina m’njira yochititsa anthu kuganizira zachiwerewere ndipo anasinthanso kavalidwe. Mogwirizana ndi zimene Baibulo linalosera zokhudza masiku otsiriza, anthu anayamba kukhala “okonda zosangalatsa.”​—2 Tim. 3:4.

Anthu a Yehova sapusitsidwa ndi maganizo a anthu a m’dzikoli omwe sayendera mfundo za makhalidwe abwino (Onani ndime 5) *

5. Kodi maganizo a anthu asintha bwanji pa nkhani ya makhalidwe abwino kuyambira zaka za m’ma 1960?

5 M’zaka za m’ma 1960 anthu ambiri anayamba kuona kuti palibe vuto ngati anthu akukhala limodzi popanda kukwatirana, amuna kapena akazi okhaokha akugonana komanso ngati anthu akuthetsa banja popanda zifukwa zomveka. Ndipo zosangalatsa zambiri zinayamba kusonyeza zinthu zokhudza kugonana. Kodi zotsatira za zonsezi ndi zotani? Wolemba mabuku wina analemba kuti popeza “anthu ambiri asiya kutsatira mfundo za makhalidwe abwino” akhala akukumana ndi mavuto ambiri. Mwachitsanzo, mabanja akutha, ana akuleredwa ndi kholo limodzi, anthu akuvutika maganizo ndipo ambiri amakonda kuonera zolaula. Kufala kwa matenda opatsirana pogonana monga Edzi kumapereka umboni wakuti nzeru za m’dzikoli ndi zopusa.​—2 Pet. 2:19.

6. Kodi maganizo a anthu a m’dzikoli pa nkhani yogonana amagwirizana bwanji ndi zimene Satana amafuna?

6 Maganizo a anthu a m’dzikoli pa nkhani yogonana amagwirizana ndi zimene Satana amafuna. N’zosachita kufunsa kuti Satana amasangalala kuona kuti anthu amagwiritsa ntchito molakwika mphatso ya ukwati komanso kugonana imene Mulungu anapereka. (Aef. 2:2) Anthu achiwerewere amasonyeza kuti sayamikira mphatso ya kubereka imene Yehova anapereka komanso khalidweli lingawalepheretse kudzalandira moyo wosatha.​—1 Akor. 6:9, 10.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA PA NKHANI YA KUGONANA

7-8. Kodi Baibulo limatithandiza bwanji kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya kugonana?

7 Anthu amene amayendera nzeru za m’dzikoli amanyoza mfundo za m’Baibulo ndipo amaona kuti n’zosatheka kuzitsatira. Iwo angafunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu anatilenga m’njira yoti tizilakalaka kugonana koma n’kumatiuza kuti tizidziletsa?’ Funso limeneli limabwera chifukwa cha maganizo olakwika oti munthu ayenera kuchita chilichonse chimene akulakalaka. Koma maganizo amenewa ndi osiyana ndi zimene Baibulo limanena. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amatilemekeza chifukwa anatilenga m’njira yoti tizikwanitsa kudziletsa kuti tisamachite zinthu zolakwika zimene timalakalaka. (Akol. 3:5) Yehova waperekanso mphatso ya ukwati ndipo anthu okwatiranawo akhoza kumagonana. (1 Akor. 7:8, 9) Anthuwo akhoza kumagonana popanda kudziimba mlandu kapena kuda nkhawa ngati mmene zimakhalira munthu akachita chiwerewere.

8 Mosiyana ndi nzeru za m’dzikoli, Baibulo limatithandiza kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya kugonana. N’zoona kuti limanena kuti kugonana kungakhale kosangalatsa. (Miy. 5:18, 19) Koma limanenanso kuti: “Aliyense wa inu akhale woyera mwa kudziwa kulamulira thupi lake m’njira yoyera kuti mukhale olemekezeka pamaso pa Mulungu, osati mwa chilakolako chosalamulirika cha kugonana, ngati chimene anthu a mitundu ina osadziwa Mulungu ali nacho.”​—1 Ates. 4:4, 5.

9. (a) Kodi anthu a Yehova analimbikitsidwa bwanji kuti azitsatira nzeru za m’Mawu a Mulungu chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900? (b) Kodi pa 1 Yohane 2:15, 16 pali malangizo anzeru otani? (c) Malinga ndi Aroma 1:24-27, kodi tiyenera kupewa kutengera makhalidwe oipa ati?

9 Chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, anthu a Yehova sanapusitsidwe ndi maganizo olakwika a anthu amene ‘sankathanso kuzindikira makhalidwe abwino.’ (Aef. 4:19) Iwo ankayesetsa kutsatirabe mfundo za Yehova. Nsanja ya Olonda ya May 15, 1926 inanena kuti “mwamuna kapena mkazi ayenera kukhala woyera pa zimene amachita komanso kuganiza, makamaka pochita zinthu ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi mnzake.” M’malo motengera maganizo a anthu a m’dzikoli, anthu a Yehova ankayendera nzeru zapamwamba za m’Mawu a Mulungu. (Werengani 1 Yohane 2:15, 16.) Kunena zoona, timayamikira kwambiri Mawu a Mulungu. Timayamikiranso kuti Yehova amatipatsa chakudya chauzimu pa nthawi yoyenera chomwe chimatithandiza kuti tisamatengere nzeru za m’dzikoli pa nkhani ya makhalidwe abwino. *​—Werengani Aroma 1:24-27.

MAGANIZO A ANTHU ANASINTHA PA NKHANI YODZIKONDA

10-11. Kodi Baibulo linachenjeza kuti chidzachitike n’chiyani m’masiku otsiriza?

10 Baibulo linachenjezeratu kuti m’masiku otsiriza, anthu adzakhala “odzikonda.” (2 Tim. 3:1, 2) M’pake kuti masiku ano dzikoli limalimbikitsa anthu kuti azidziona kuti ndi ofunika kwambiri. Buku lina linanena kuti zaka za m’ma 1970, “mabuku opereka malangizo kwa anthu okhudza mmene angakhalire ndi moyo wabwino anachuluka kwambiri.” Mabuku ena “ankalimbikitsa anthu kuti ayenera kudzidziwa bwino ndipo ayenera kumasangalala ndi mmene alili basi.” Mwachitsanzo, m’buku lina analembamo kuti: “Uzidzikonda wekha chifukwa ngati pali munthu wooneka bwino, wofunika komanso wosangalatsa ndi iweyo basi.” Bukulo linkalimbikitsa anthu kuti “aziyendera mfundo zimene iwowo aona kuti ndi zabwino kapena zothandiza.”

11 Kodi munamvapo maganizo ngati amenewa? Satana analimbikitsa Hava kuchita zinthu ngati zimenezi. Iye anamuuza kuti ‘adzafanana ndi Mulungu ndipo adzadziwa zabwino ndi zoipa.’ (Gen. 3:5) Masiku ano, anthu ambiri ndi onyada kwambiri moti amaona kuti munthu wina, ngakhalenso Mulungu, sangawauze kuti izi n’zoyenera, izi n’zosayenera. Zimenezi zimaonekera kwambiri m’maganizo a anthu pa nkhani ya ukwati.

Mkhristu ayenera kuika zofuna za ena patsogolo, makamaka za mkazi kapena mwamuna wake (Onani ndime 12) *

12. Kodi dziko limalimbikitsa maganizo otani pa nkhani ya ukwati?

12 Baibulo limalangiza mwamuna ndi mkazi wake kuti azilemekezana komanso kukwaniritsa zimene analonjeza pa tsiku la ukwati wawo. Limalimbikitsa anthu okwatirana kuti apitirize kukhala okhulupirika m’banja mwawo. Paja Baibulo limanena kuti: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.” (Gen. 2:24) Koma mosiyana ndi zimenezi, anthu amene amayendera nzeru za m’dzikoli amaona kuti mwamuna kapena mkazi ayenera kumangoganizira zofuna zake. Buku lina lofotokoza zokhudza kuthetsa banja linanena kuti: “Anthu ambiri anasintha malumbiro a ukwati. M’malo molumbira kuti tikhala m’banja ‘pa nthawi yonse imene awirife tidzakhala ndi moyo,’ amangonena kuti tikhala m’banja ‘pa nthawi yonse imene awirife tidzakhala tikukondana.’” Maganizo olakwikawa achititsa kuti mabanja ambiri azitha ndipo zotsatira zake zimakhala zopweteka kwambiri. Apa n’zoonekeratu kuti maganizo osalemekeza ukwati amene anthu a m’dzikoli ali nawo ndi opusa kwambiri.

13. N’chifukwa chiyani Mulungu amanyansidwa ndi anthu onyada?

13 Baibulo limanena kuti: “Yehova amanyansidwa ndi munthu aliyense wa mtima wonyada.” (Miy. 16:5) N’chifukwa chiyani Yehova amanyansidwa ndi anthu onyada? Chifukwa chimodzi n’chakuti anthu onyada komanso odzikonda amafanana ndi Satana. Tangoganizani, Satana ankafuna kuti Yesu, amene Mulungu anamugwiritsira ntchito polenga zinthu zonse, agwade n’kumulambira. (Mat. 4:8, 9; Akol. 1:15, 16) Anthu amene amadziona kuti ndi ofunika kwambiri amapereka umboni wakuti nzeru za m’dzikoli ndi zopusa kwa Mulungu.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA PA NKHANI YODZIKONDA

14. Kodi lemba la Aroma 12:3 limatithandiza bwanji kuti tizidziona moyenera?

14 Baibulo limatithandiza kuti tizidziona m’njira yoyenera. Limavomereza kuti aliyense ayenera kudzikonda moyenera. Paja Yesu anati: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Mat. 19:19) Koma Baibulo siliphunzitsa kuti tiziganiza kuti ndife apamwamba kuposa anthu ena. M’malomwake, limanena kuti: “Musachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.”​—Afil. 2:3; werengani Aroma 12:3.

15. N’chifukwa chiyani mumaona kuti kutsatira malangizo a m’Baibulo ndi kothandiza?

15 Masiku ano, anthu ambiri omwe amaoneka kuti ndi anzeru amatsutsa malangizo a m’Baibulo pa nkhaniyi. Iwo amaganiza kuti kuona anthu ena kuti ndi okuposani kungachititse kuti anthuwo azikupezererani. Koma kodi zotsatira za maganizo a anthu odzikonda a m’dzikoli ndi zotani? Nanga inuyo mwaona zotani? Kodi anthu odzikonda amakhala osangalala? Nanga mabanja awo ndi osangalala? Kodi amakhala ndi anzawo enieni? Nanga amakhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu? Kodi mumaona kuti chothandiza n’chiyani pakati pa kutsatira nzeru za anthu a m’dzikoli ndi kutsatira nzeru za m’Mawu a Mulungu?

16-17. Kodi tiyenera kuyamikira chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

16 Anthu amene amatsatira malangizo a anthu omwe dzikoli limawaona kuti ndi anzeru sizingawayendere bwino. Amakhala ngati mlendo yemwe akufunsa mlendo mnzake njira, pomwe awiri onsewo asochera. Yesu ananena za anthu omwe ankaoneka kuti ndi anzeru pa nthawi yake kuti: “Iwo ndi atsogoleri akhungu. Chotero ngati munthu wakhungu akutsogolera wakhungu mnzake, onse awiri adzagwera m’dzenje.” (Mat. 15:14) Kunena zoona, nzeru za m’dzikoli ndi zopusa kwa Mulungu.

Atumiki a Mulungu akuona zithunzi zosonyeza zinthu zosangalatsa zimene akumana nazo potumikira Yehova(Onani ndime 17) *

17 Nthawi zonse malangizo anzeru a m’Baibulo amakhala “opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza m’chilungamo.” (2 Tim. 3:16) Timayamikira kwambiri kuti Yehova akugwiritsa ntchito gulu lake potiteteza kuti tisamatengere nzeru za m’dzikoli. (Aef. 4:14) Chakudya chauzimu chimene amapereka chimatipatsa mphamvu zoti tiziyendera mfundo za m’Mawu ake nthawi zonse. Ndi mwayi waukulu kwambiri kutsogoleredwa ndi nzeru zapamwamba zimene zimapezeka m’Baibulo.

NYIMBO NA. 54 “Njira Ndi Iyi”

^ ndime 5 Munkhaniyi tipeza umboni wotsimikizira kuti Yehova yekha ndi amene angatipatse malangizo abwino. Tionanso kuti kutsatira nzeru za m’dzikoli n’koopsa kwambiri koma kutsatira nzeru yochokera m’Mawu a Mulungu n’kothandiza.

^ ndime 9 Mwachitsanzo, onani buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba, mutu 24-26 ndi Buku Lachiwiri, mutu 4-5.

^ ndime 50 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Zithunzi zamunkhaniyi zikusonyeza zinthu zina zimene banja la Mboni lakhala likukumana nazo pa moyo wawo. M’bale ndi mlongo akulalikira chakumapeto kwa m’ma 1960.

^ ndime 52 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’ma 1980, mwamunayo akusamalira mkazi wake pamene wadwala ndipo mwana wawo akuyang’ana.

^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Masiku ano, banjali likuona zithunzi zosonyeza zinthu zosangalatsa zimene zachitika pa moyo wawo potumikira Yehova. Mwana wawo uja limodzi ndi banja lake akusangalala nawo.