NKHANI YOPHUNZIRA 28

Tizilambirabe Yehova Ngakhale Boma Litatiletsa

Tizilambirabe Yehova Ngakhale Boma Litatiletsa

“Sitingaleke kulankhula zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.”​MAC. 4:19, 20.

NYIMBO NA. 122 Khalani Olimba Komanso Osasunthika

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. (a) N’chifukwa chiyani sitidabwa ngati boma latiletsa kulambira Yehova? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

MU 2018, ofalitsa oposa 223,000 ankakhala m’mayiko amene ntchito yathu inkaletsedwa kapena kutsutsidwa kwambiri. Zimenezi n’zosadabwitsa. Malinga ndi zimene tinakambirana munkhani yapita ija, Akhristu oona amayembekezera kuzunzidwa. (2 Tim. 3:12) Kaya tikukhala m’dziko liti, boma likhoza kuletsa mosayembekezereka ntchito yathu yotumikira Yehova, yemwe ndi Mulungu wachikondi.

2 Ngati boma litaletsa kulambira Yehova tikhoza kudzifunsa kuti: ‘Kodi kuzunzidwa kumatanthauza kuti Mulungu wasiya kutidalitsa? Kodi bomalo lingatilepheretse kulambira Yehova? Kodi ndisamukire kudziko lina kuti ndizikalambira Mulungu mwaufulu?’ Munkhaniyi tikambirana mafunso amenewa. Tikambirananso zimene tingachite kuti tizilambirabe Mulungu pa nthawi imene boma latiletsa komanso misampha imene tiyenera kupewa.

KODI KUZUNZIDWA KUMATANTHAUZA KUTI MULUNGU WASIYA KUTIDALITSA?

3. Malinga ndi 2 Akorinto 11:23-27, kodi mtumwi Paulo anazunzidwa bwanji, nanga tikuphunzira chiyani pa chitsanzo chake?

3 Ngati boma laletsa ntchito yathu, tikhoza kuganiza kuti Mulungu wasiya kutidalitsa. Koma tiyenera kukumbukira kuti kuzunzidwa sikutanthauza kuti Yehova sakusangalala nafe. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mtumwi Paulo. Mulungu ankasangalala naye kwambiri. Paja anali ndi mwayi wolemba makalata 14 omwe ali m’Malemba Achigiriki ndipo anasankhidwa kukhala mtumwi wothandiza anthu amitundu ina. Ngakhale zinali choncho, nthawi zina ankazunzidwa koopsa. (Werengani 2 Akorinto 11:23-27.) Nkhani ya Pauloyi ikusonyeza kuti Yehova amatha kulola kuti atumiki ake okhulupirika azizunzidwa.

4. N’chifukwa chiyani anthu am’dzikoli amadana nafe?

4 Yesu anafotokoza chifukwa chake tiyenera kuyembekezera kuzunzidwa. Iye ananena kuti tidzadedwa chifukwa chakuti sitili mbali ya dziko. (Yoh. 15:18, 19) Choncho kuzunzidwa si umboni wakuti Yehova sakutidalitsa. Koma kumasonyeza kuti tikuchita zinthu zoyenera.

KODI MABOMA ANGATILEPHERETSE KULAMBIRA YEHOVA?

5. Kodi anthu angatilepheretse kulambira Yehova? Fotokozani.

5 Anthu alibe mphamvu zotilepheretseratu kulambira Yehova, yemwe ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Ambiri ayesapo kuchita zimenezi koma alephera. Chitsanzo ndi zimene zinachitika pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Pa nthawi imeneyi, maboma ambiri ankazunza koopsa anthu a Mulungu. Mwachitsanzo, ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa m’mayiko olamulidwa ndi Germany komanso ku Australia, ku Canada ndi m’mayiko enanso. Koma kodi mukudziwa zomwe zinachitika? Pamene nkhondoyi inkayamba mu 1939, padziko lonse panali ofalitsa okwana 72,475. Koma malipoti akusonyeza kuti pamene nkhondoyi inkatha mu 1945, Yehova anali atadalitsa anthu ake moti chiwerengero chinawonjezeka kwambiri kufika 156,299.

6. Kodi chingachitike n’chiyani anthu a Yehovafe tikamatsutsidwa? Perekani chitsanzo.

6 Anthu a Yehovafe tikamatsutsidwa sitichita mantha, koma tikhoza kulimbikitsidwa kuti tizitumikira Yehova ndi mtima wonse. Chitsanzo ndi banja lina limene linali ndi mwana mmodzi, ndipo linkakhala m’dziko limene linaletsa ntchito yathu. M’malo mobwerera m’mbuyo chifukwa cha mantha, banjali linayamba upainiya wokhazikika. Mkazi wa m’banjali anafika posiya ntchito yake yabwino n’cholinga choti azichita upainiyawo. Mwamuna wake ananena kuti zimene boma linachitazi zinachititsa kuti anthu akhale ndi mafunso ambiri okhudza Mboni za Yehova. Izi zinathandiza kuti aziyambitsa mosavuta maphunziro a Baibulo. Kuletsa ntchito yathu kunathandizanso anthu ena. Mkulu wam’dziko lomweli ananena kuti anthu ambiri amene anasiya kutumikira Yehova anayamba kufika kumisonkhano ndiponso kulalikira.

7. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa lemba la Levitiko 26:36, 37? (b) Kodi inuyo mudzatani ngati boma litatiletsa kulambira Yehova?

7 Adani athu akamatiletsa kulambira Yehova amaganiza kuti tichita mantha n’kusiyadi. Iwo akhozanso kufalitsa mabodza okhudza ifeyo, kutumiza apolisi kuti afufuze zinthu m’nyumba zathu, kutitengera kukhoti kapenanso kutsekera ena kundende. Iwo amaganiza kuti tikhoza kuchita mantha kwambiri chifukwa choti anzathu ochepa ali kundende. Koma tikangoyamba kuchita mantha, tikhoza kubwerera m’mbuyo n’kukhala ngati tadzipatsa tokha bani pa kulambira kwathu. Si bwino kukhala ngati anthu ofotokozedwa pa Levitiko 26:36, 37. (Werengani.) Sitingalole kuchita mantha mpaka kufika pochepetsa kapena kusiyiratu zimene timachita polambira Yehova. Timadalira Yehova ndi mtima wonse ndipo sitida nkhawa kwambiri. (Yes. 28:16) Timamupempha kuti azititsogolera. Ndipo timadziwa kuti ngati ali kumbali yathu, ngakhale boma lamphamvu kwambiri silingatilepheretse kumulambira mokhulupirika.​—Aheb. 13:6.

KODI NDISAMUKIRE KUDZIKO LINA?

8-9. (a) Kodi aliyense ayenera kusankha yekha zochita pa nkhani iti? (b) N’chiyani chingathandize munthu kuti asankhe zochita mwanzeru?

8 Ngati boma laletsa ntchito yathu, mukhoza kuganiza kuti, Kodi ndisamukire kudziko lina kuti ndizikalambira Yehova mwaufulu? Palibe munthu amene ayenera kusankhira anzake zochita pa nkhaniyi. Anthu ena angathandizidwe kusankha zochita akaganizira zimene Akhristu oyambirira anachita atayamba kuzunzidwa. Sitefano ataphedwa, Akhristu a ku Yerusalemu anasamukira kumadera ena a ku Yudeya komanso ku Samariya ndipo anapita ngakhale ku Foinike, ku Kupuro ndi ku Antiokeya. (Mat. 10:23; Mac. 8:1; 11:19) Koma ena angakumbukire zimene mtumwi Paulo anachita Akhristu atayambiranso kuzunzidwa nthawi ina. Iye anasankha zoti asasamuke kumadera amene anthu ankadana ndi ntchito yolalikira. Anachita izi n’cholinga choti apitirize kulalikira uthenga wabwino ndiponso kulimbikitsa abale amene ankazunzidwa kwambiri.​—Mac. 14:19-23.

9 Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani zimenezi? Aliyense amene ndi mutu wa banja ayenera kusankha yekha zochita pa nkhani ya kusamuka. Asanasankhe zochita ayenera kupemphera komanso kuganizira kwambiri mmene zilili ndi banja lake komanso ubwino ndi kuipa kwa kusamuka. Pa nkhani imeneyi, Mkhristu aliyense ayenera “kunyamula katundu wake.” (Agal. 6:5) Ndipo sitiyenera kuweruza ena chifukwa cha zimene asankha pa nkhaniyi.

KODI TINGALAMBIRE BWANJI YEHOVA NGATI BOMA LATILETSA?

10. Kodi ofesi ya nthambi komanso akulu azidzapereka malangizo otani?

10 Kodi mungatani kuti muzilambirabe Yehova ngakhale boma litatiletsa? Ofesi ya nthambi izidzapatsa akulu malangizo okhudza mmene angapezere chakudya chauzimu, kusonkhana komanso kulalikira uthenga wabwino. Ngati ofesi ya nthambi singathe kulankhula ndi akulu, akuluwo ndi amene azidzathandiza aliyense mumpingo kuti azilambirabe Yehova. Iwo azidzapereka malangizo ochokera m’Baibulo komanso m’mabuku athu.​—Mat. 28:19, 20; Mac. 5:29; Aheb. 10:24, 25.

11. Kodi tikudziwa bwanji kuti sitidzasowa chakudya chauzimu, nanga mungatani kuti muteteze chakudya chanu chauzimu?

11 Yehova walonjeza kuti nthawi zonse atumiki ake azikhala ndi chakudya chauzimu chokwanira. (Yes. 65:13, 14; Luka 12:42-44) Choncho simuyenera kukayikira kuti gulu lake lizidzakupatsani zonse zimene lingathe kuti muzilimbikitsidwa mokwanira. Koma kodi inuyo muyenera kuchita chiyani? Boma likaletsa kulambira Yehova, muyenera kupeza malo abwino oti mubise Baibulo lanu komanso mabuku ena, kaya mabuku enieni kapena apazipangizo. Muzipewa kusiya zinthu zamtengo wapatali ngati zimenezi pamalo amene anthu angazipeze mosavuta. Aliyense wa ife ayenera kuchita zonse zimene angathe kuti akhalebe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.

Yehova akhoza kutithandiza kuti tilimbe mtima n’kumasonkhanabe kuti timulambire (Onani patsamba 12) *

12. Kodi akulu angakonze bwanji misonkhano m’njira yoti adani athu asamazindikire?

12 Kodi zizidzatheka kukhala ndi misonkhano mlungu uliwonse? Akulu adzakonza zoti muzisonkhana m’njira yoti adani athu asamazindikire. Mwina angakuuzeni kuti muzisonkhana m’timagulu ndipo akhoza kumasinthasintha nthawi komanso malo oti musonkhane. Kuti muthandize kuteteza anthu amene asonkhana, muyenera kupewa kulankhula mokweza pofika kapena pochoka kumisonkhanoyo. Mwina mudzayenera kuvala ngati simukupita kumisonkhano n’cholinga choti anthu asamakayikire zimene mukuchita.

Sitidzasiya kulalikira ngakhale boma litatiletsa (Onani patsamba 13) *

13. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha abale athu amene ankakhala ku Soviet Union?

13 Ntchito yolalikira ikhoza kugwiridwa mosiyanasiyana malinga ndi kumene mumakhala. Koma popeza tonsefe timakonda Yehova ndipo timakonda kuuza anthu za Ufumu wake, tidzapeza njira yoti tizilalikirabe. (Luka 8:1; Mac. 4:29) Wolemba mbiri yakale dzina lake Emily B. Baran anafotokoza zimene a Mboni za Yehova ankachita ku Soviet Union kuti azilalikirabe. Iye anati: “Boma litauza a Mboni kuti asiye kulalikira, ankalalikira pocheza ndi anthu amene ankakhala nawo pafupi, anzawo akuntchito komanso anzawo ena. Zimenezi zinachititsa kuti atsekeredwe m’ndende koma a Mboniwo ankalalikirabe kwa akaidi anzawo.” Abale athu a ku Soviet Union sanasiye kulalikira ngakhale ntchito yathu italetsedwa. Ngati ntchito yolalikira yaletsedwa kumene mumakhala, muziyesetsa kutsatira chitsanzo cha abalewa.

MISAMPHA IMENE TIYENERA KUPEWA

Tizidziwa nthawi yoyenera kukhala chete (Onani patsamba 14) *

14. Kodi lemba la Salimo 39:1 lingatithandize kupewa chiyani?

14 Tizisamala ndi zimene timauza ena. Pamene ntchito yathu yaletsedwa, tiyenera kuzindikira nthawi yoti ‘tikhale chete.’ (Mlal. 3:7) Sitiyenera kuulula zinthu zachinsinsi monga mayina a abale ndi alongo athu, malo amene timasonkhana, mmene timalalikirira ndiponso njira zolandirira chakudya chauzimu. Sitiyenera kuuza akuluakulu a boma zinthu ngati zimenezi kapena kuuza anzathu komanso achibale athu, kaya a m’dziko lathu kapena m’mayiko ena. Zili choncho chifukwa tikawauza tikhoza kuika moyo wa abale athu pa ngozi.​—Werengani Salimo 39:1.

15. Kodi Satana amayesetsa kutani, nanga tingapewe bwanji msampha wakewu?

15 Tizipewa kukwiyirana pa nkhani zing’onozing’ono. Satana amadziwa kuti nyumba yogawanika singakhale. (Maliko 3:24, 25) Choncho angamayesetse kuti atigawanitse. Iye amafuna kuti tizilimbana tokhatokha m’malo molimbana ndi iyeyo.

16. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Mlongo Gertrud Poetzinger anachita?

16 Ngakhale Akhristu olimba mwauzimu ayenera kusamala. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Mlongo Gertrud Poetzinger ndi Mlongo Elfriede Löhr. Alongo awiriwa anali odzozedwa ndipo anamangidwa limodzi ndi alongo ena m’ndende ya chipani cha Nazi. Gertrud anayamba kuchitira nsanje Elfriede chifukwa choti ankakamba nkhani zolimbikitsa kwambiri kwa alongo kundendeko. Koma kenako Gertrud anachita manyazi n’kupempha Yehova kuti amuthandize. Iye analemba kuti: “Tiziphunzira kuvomereza ngati anzathu ali ndi luso lotiposa kapena ngati amaoneka kuti amachita bwino zinthu kuposa ifeyo.” N’chiyani chinamuthandiza kuti asiye kuchita nsanje? Gertrud anayamba kuganizira kwambiri makhalidwe abwino amene Elfriede anali nawo. Izi zinathandiza kuti ayambenso kugwirizana naye. Alongo onsewa anapirira mpaka pamene anatulutsidwa kundende ndipo anatumikira Yehova mokhulupirika mpaka pamene anamaliza utumiki wawo padziko lapansi. Tikamayesetsa kuthetsa mavuto mwamsanga sitidzalola kuti chilichonse chitisiyanitse ndi abale athu.​—Akol. 3:13, 14.

17. N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera malangizo nthawi zonse?

17 Tizitsatira malangizo nthawi zonse. Tikhoza kupewa mavuto ambiri tikamamvera malangizo amene abale audindo odalirika atipatsa. (1 Pet. 5:5) Mwachitsanzo, boma litaletsa ntchito yathu m’dziko lina, abale audindo anapereka malangizo akuti tisamagawire mabuku kapena magazini mu utumiki. Koma m’bale wina amene ankachita upainiya sanamvere ndipo ankagawira zinthu zimenezi. Kodi mukudziwa zimene zinachitika? M’baleyu ndi anzake atangomaliza kulalikira mwamwayi, apolisi anafika n’kuyamba kuwafunsa mafunso. Zikuoneka kuti apolisiwo ankawatsatira pamene ankachita zimenezi ndipo analanda mabuku amene anagawirawo. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Ndi bwino kutsatira malangizo ngakhale amene tikuganiza kuti si abwino. Nthawi zonse Yehova amatidalitsa tikamatsatira malangizo ochokera kwa abale amene wawasankha kuti azititsogolera.​—Aheb. 13:7, 17.

18. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kupanga malamulo osafunika?

18 Tisamapange malamulo osafunika. Akulu akamapanga malamulo osafunika amavutitsa abale awo. Chitsanzo ndi zimene zinachitika pa nthawi ya bani kudziko limene linkadziwika kuti Czechoslovakia. M’bale Juraj Kaminský ananena kuti: “Akulu ambiri atamangidwa, ena amene anatsala m’mipingo komanso m’madera anayamba kupanga malamulo awoawo. Ankauza ofalitsa zoyenera kuchita ndi zosayenera kuchita.” Komatu Yehova sanatipatse udindo wosankhira anzathu zochita. Munthu amene amapanga malamulo ake kuti abale azitsatira amakhala akulamulira chikhulupiriro chawo, osati kuwateteza.​—2 Akor. 1:24.

MUSASIYE KULAMBIRA YEHOVA ZIVUTE ZITANI

19. Ngakhale kuti Satana amayesetsa kutichititsa mantha, kodi lemba la 2 Mbiri 32:7, 8 limatilimbikitsa bwanji?

19 Mdani wathu Satana Mdyerekezi sadzasiya kuzunza atumiki a Yehova okhulupirika. (1 Pet. 5:8; Chiv. 2:10) Iye limodzi ndi aliyense amene ali kumbali yake adzayesetsa kutiletsa kulambira Yehova. Koma palibe chifukwa chochitira mantha mpaka kufika pobwerera m’mbuyo. (Deut. 7:21) Tizikumbukira kuti Yehova ali kumbali yathu ndipo adzapitiriza kutithandiza ngakhale pamene boma laletsa ntchito yathu.​—Werengani 2 Mbiri 32:7, 8.

20. Kodi inuyo simudzasiya kuchita chiyani?

20 Tiyeni tikhale ndi mtima ngati umene Akhristu oyambirira anali nawo. Paja iwo anauza olamulira kuti: “Weruzani nokha, ngati n’koyenera pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu. Koma ife sitingaleke kulankhula zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.”​—Mac. 4:19, 20.

NYIMBO NA. 73 Tithandizeni Kukhala Olimba Mtima

^ ndime 5 Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati boma latiletsa kulambira Yehova? Munkhaniyi tikambirana zinthu zimene tiyenera kuchita komanso zimene tiyenera kupewa kuti tisasiye kulambira Mulungu.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Zithunzi zonse zikusonyeza zimene a Mboni akuchita m’dziko limene boma laletsa ntchito yathu. Pachithunzichi anthu ochepa akuchita misonkhano m’chipinda chosungira katundu cha m’bale wina.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mlongo (amene ali kumanzere) akucheza ndi munthu ndipo akufuna kupeza mpata woti akambirane naye nkhani zokhudza Yehova.

^ ndime 63 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: M’bale akufunsidwa mafunso ndi apolisi ndipo sakuulula zinthu zokhudza mpingo wake.