NKHANI YOPHUNZIRA 33

“Anthu Okumvera” Adzapulumuka

“Anthu Okumvera” Adzapulumuka

“Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa. Pitiriza kuchita zimenezi, chifukwa ukatero udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvera.”​—1 TIM. 4:16.

NYIMBO NA. 67 “Lalikira Mawu”

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi tonse timafuna kuti achibale athu achite chiyani?

MLONGO wina dzina lake Pauline * ananena kuti: “Kuyambira pamene ndinaphunzira choonadi ndakhala ndikufuna kuti achibale anga onse adzakhale nane mu Paradaiso. Makamaka ndinkafuna ndizitumikira Yehova limodzi ndi mwamuna wanga dzina lake Wayne komanso mwana wanga.” Kodi nanunso muli ndi achibale amene sanayambe kutumikira Yehova? Ngati zili choncho, muyenera kuti mumamva mofanana ndi Pauline.

2. Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?

2 Sitingakakamize achibale athu kuti azimvetsera uthenga wabwino. Koma tikhoza kuwathandiza kuti akhale ndi mtima wofuna kumvetsera uthengawu. (2 Tim. 3:14, 15) N’chifukwa chiyani tiyenera kuthandiza achibale athu? Ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kuwamvetsa? Kodi tingatani kuti tiwathandize kukonda Yehova ngati mmene ifeyo timachitira? Nanga kodi onse mumpingo angathandize bwanji pa nkhaniyi?

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUTHANDIZA ACHIBALE ATHU?

3. Mogwirizana ndi 2 Petulo 3:9, n’chifukwa chiyani tiyenera kuthandiza achibale athu?

3 Posachedwapa, Yehova adzawononga dziko loipali. Anthu amene adzapulumuke ndi okhawo ‘amene ali ndi maganizo abwino owathandiza kudzapeza moyo wosatha.’ (Mac. 13:48) Akhristufe timagwiritsa ntchito nthawi yambiri ndi mphamvu zathu polalikira kwa anthu omwe sitiwadziwa. Choncho m’pomveka kuti timafuna kuti achibale athu nawonso azitumikira Yehova. Atate wathu, yemwe ndi wachikondi, “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.”​—Werengani 2 Petulo 3:9.

4. Kodi tikhoza kulakwitsa chiyani polalikira achibale athu?

4 Tiyenera kukumbukira kuti pali njira yoyenera ndi njira yolakwika yolalikirira uthenga wabwino. Nthawi zambiri timalankhula mokoma mtima tikamalalikira anthu omwe sitiwadziwa n’komwe. Koma mwina tikhoza kulankhula mosasamala tikamalalikira achibale athu.

5. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani tisanayambe kulalikira achibale athu?

5 Ambirife mwina timaona kuti sitinachite zinthu mokoma mtima pa nthawi yoyamba imene tinalalikira achibale athu ndipo mwina timanong’oneza bondo. Mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti: “Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, okoma ngati kuti mwawathira mchere, kuti mudziwe mmene mungayankhire wina aliyense.” (Akol. 4:5, 6) Ndi bwino kukumbukira malangizo amenewa tikamathandiza achibale athu. Tikapanda kusamala, tikhoza kuwakhumudwitsa m’malo mowathandiza kuti amvetsere uthenga wathu.

KODI TINGATHANDIZE BWANJI ACHIBALE ATHU?

6-7. Perekani chitsanzo chosonyeza kufunika komvetsa mwamuna kapena mkazi yemwe si wa Mboni.

6 Tiziwamvetsa. Pauline amene tamutchula kale uja anati: “Poyamba, ndikakhala ndi mwamuna wanga ndinkangofuna kuti ndizilankhula za Mulungu zokhazokha. Sitinkacheza bwinobwino.” Koma Wayne sankadziwa zambiri zokhudza Baibulo ndipo sankamvetsa zimene mkazi wakeyo ankakonda kunena. Anafika poona kuti mkazi wake amangoganiza za chipembedzo chake basi. Iye ankaopa kuti mwina walowa gulu loopsa lomwe likumusokoneza.

Mukhoza kuthandiza kwambiri anthu ngati mumawamvetsa komanso kukhala ndi khalidwe labwino (Onani ndime 6-8) *

7 Pauline anavomereza kuti nthawi zambiri madzulo komanso Loweruka ndi Lamlungu ankakhala ndi abale ndi alongo kumisonkhano, polalikira komanso kocheza. Iye anati: “Nthawi zina Wayne akafika kunyumba ankapeza kulibe munthu ndipo ankasowa wocheza naye.” N’zosachita kufunsa kuti Wayne ankasowa mkazi wake ndi mwana wake. Iye sankadziwa anthu amene mkazi wakeyo ankakhala nawo ndipo ankaganiza kuti mkaziyo amaona kuti anzakewo ndi ofunika kwambiri kuposa iyeyo. Zitatero, Wayne anamuopseza kuti athetsa banja. Kodi Pauline akanasonyeza bwanji kuti amamumvetsa mwamuna wake?

8. Malinga ndi 1 Petulo 3:1, 2, kodi n’chiyani chingathandize kwambiri achibale athu?

8 Muzikhala ndi khalidwe labwino. Nthawi zambiri, zochita zathu n’zimene zimathandiza kwambiri achibale athu kuposa zolankhula zathu. (Werengani 1 Petulo 3:1, 2.) Patapita nthawi, Pauline anazindikira mfundo imeneyi. Iye anati: “Ndinkadziwa kuti Wayne ankatikonda ndipo sankafuna kuthetsa banja. Koma zimene ananenazi zinandichititsa kuganiza zoyamba kutsatira malangizo a Yehova pa nkhani ya banja. Ndinaona kuti m’malo mongolankhula, ndiyenera kukhala ndi khalidwe labwino.” Pauline anasiya kukakamiza Wayne kuti azikambirana naye nkhani zokhudza Baibulo ndipo anayamba kumacheza naye nkhani zina. Wayne anaona kuti mkazi wake wayamba kuchita zinthu zambiri mwamtendere ndipo mwana wake wayamba kukhala womvera kwambiri. (Miy. 31:18, 27, 28) Wayne ataona kuti mfundo za m’Baibulo zikuthandiza banja lake anayamba kumvetsera uthenga wa m’Mawu a Mulungu.​—1 Akor. 7:12-14, 16.

9. N’chifukwa chiyani sitiyenera kusiya kuthandiza achibale athu?

9 Musagwe ulesi pothandiza achibale anu. Yehova wapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Iye amapereka mpata kwa anthu “mobwerezabwereza” kuti amvetsere uthenga wabwino n’cholinga choti adzapulumuke. (2 Mbiri 36:15) Nayenso mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti asasiye kuthandiza anthu ena. Ananena kuti akamachita zimenezi adzadzipulumutsa yekha komanso anthu amene angamumvere. (1 Tim. 4:16) Timakonda achibale athu choncho timafuna kuti adziwe choonadi. Zolankhula ndiponso zochita za Pauline zinathandiza banja lake. Panopa amatumikira Yehova limodzi ndi mwamuna wake. Onse awiri ndi apainiya ndipo Wayne ndi mkulu.

10. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala oleza mtima?

10 Muzikhala oleza mtima. Tikayamba kutsatira mfundo za Mulungu, achibale athu angavutike kumvetsa zimene timakhulupirira komanso kuchita. Nthawi zambiri, chinthu choyamba chimene amaona n’chakuti tasiya kuchita nawo zandale komanso zikondwerero zachipembedzo. Poyamba, achibale ena angatikwiyire. (Mat. 10:35, 36) Koma sitiyenera kusiya kuwathandiza kuti amvetse zimene timakhulupirira. Tikasiya zingakhale ngati tawaweruza kuti ndi osayenera kudzapeza moyo wosatha. Koma Yehova wapereka udindo woweruzawu kwa Yesu osati ifeyo. (Yoh. 5:22) Tikakhala oleza mtima achibale athu akhoza kuyamba kumvetsera uthenga wathu.​—Onani bokosi lakuti “ Tizigwiritsa Ntchito Webusaiti Yathu Pophunzitsa.”

11-13. Kodi mukuphunzira chiyani pa zimene Alice anachita ndi makolo ake?

11 Muzichita zinthu molimba mtima koma mwaulemu. (Miy. 15:2) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Alice. Iye anaphunzira za Yehova akukhala kutali ndi makolo ake omwe sankakhulupirira zoti kuli Mulungu komanso ankachita zandale. Alice anazindikira kuti ayenera kuwauza msanga zinthu zabwino zimene ankaphunzira. Iye anati: “Mukachedwa kuuza achibale anu zimene mwayamba kukhulupirira komanso kuchita, zingawavute kwambiri kuzivomereza.” Choncho iye analembera makalata makolo ake kuti awafunse maganizo awo pa mfundo zina za m’Baibulo. Anasankha mfundo zimene ankaona kuti akhoza kuchita nazo chidwi monga zokhudza chikondi. (1 Akor. 13:1-13) Alice anathokoza makolo ake chifukwa chomulera komanso kumusamalira ndipo anawatumizira mphatso. Akapita kukaona makolo ake ankathandiza kwambiri mayi ake ntchito zapakhomo. Poyamba, makolo a Alice sanasangalale atamva zimene mwana wawo wayamba kukhulupirira.

12 Koma Alice ali kwa makolo ake, sanasiye kuwerenga Baibulo tsiku lililonse. Iye anati, “Zimenezi zinathandiza mayi anga kuzindikira kuti Baibulo ndi lofunika kwambiri kwa ineyo.” Koma bambo ake anasankha zoti aphunzire Baibulo kuti amvetse zimene mwana wawo amakhulupirira komanso kuti alipezere zifukwa. Alice ananena kuti, “Ndinawapatsa Baibulo ndipo ndinalembamo mawu enaake.” Kodi n’chiyani chinachitika? M’malo mopeza zifukwa, bambo ake anakhudzidwa kwambiri ndi zimene anawerenga m’Baibulolo.

13 Tiyenera kuchita zinthu molimba mtima koma mwaulemu ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto. (1 Akor. 4:12b) Mwachitsanzo, Alice ankatsutsidwa kwambiri ndi mayi ake. Iye anati, “Nditabatizidwa, mayi ananena kuti ndine mwana woipa.” Kodi Alice anatani? Iye anati: “M’malo mongonyalanyaza nkhaniyo, ndinawafotokozera kuti ndasankha kuti ndikhale wa Mboni za Yehova ndipo sindidzasintha. Koma ndinawatsimikizira kuti ndimawakonda kwambiri. Tonse tinalira ndipo ndinawaphikira chakudya chabwino. Kuyambira nthawi imeneyo, mayi anayamba kuvomereza kuti Baibulo likundithandiza kukhala munthu wabwino.”

14. N’chifukwa chiyani sitiyenera kulola kuti achibale asinthe maganizo athu pa nkhani yotumikira Yehova?

14 Mwina zingawatengere nthawi achibale athu kuti amvetse mmene timaonera nkhani yotumikira Yehova. Mwachitsanzo, Alice atasankha kuti achite upainiya m’malo mogwira ntchito imene makolo ake ankafuna, mayi ake analiranso. Koma Alice sanasinthe maganizo ake. Iye anati: “Munthu akasintha zimene wasankha, achibale ake sangasiye kumuvutitsa. Koma akamachita zinthu mwaulemu ndiponso molimba mtima ena mwa iwo angayambe kumvetsera uthenga wathu.” Izi n’zimene zinachitikira Alice. Panopa makolo ake onse ndi apainiya ndipo bambo ake ndi mkulu.

KODI ONSE MUMPINGO ANGATHANDIZE BWANJI?

Kodi mpingo ungathandize bwanji achibale athu omwe si Mboni? (Onani ndime 15-16) *

15. Mogwirizana ndi Mateyu 5:14-16 komanso 1 Petulo 2:12, kodi ‘ntchito zabwino’ zingathandize bwanji achibale athu?

15 ‘Ntchito zabwino’ zimene mpingo umachita zimathandiza kuti anthu akokeredwe m’gulu la Yehova. (Werengani Mateyu 5:14-16; 1 Petulo 2:12.) Ngati mwamuna kapena mkazi wanu si wa Mboni, kodi anayamba wakumanapo ndi abale ndi alongo amumpingo wanu? Pauline, yemwe tamutchula kale uja, ankaitanira abale ndi alongo kunyumba kwake n’cholinga choti mwamuna wake adziwane nawo. Mwamuna wakeyo amakumbukira mmene m’bale wina anamuthandizira kumvetsa zinthu zina zokhudza a Mboni ndipo ananena kuti: “Tsiku lina m’baleyo anatenga tchuthi kuti tidzaonere mpira kunyumba kwathu. Zimenezi zinandithandiza kuona kuti nayenso ndi munthu ngati ine ndemwe.”

16. N’chifukwa chiyani tiyenera kuitanira achibale athu kumisonkhano?

16 Njira ina yabwino yothandizira achibale athu ndi kuwaitana kuti apite nafe kumisonkhano. (1 Akor. 14:24, 25) Wayne anapezeka koyamba pa Chikumbutso chifukwa chinachitika ataweruka kuntchito komanso msonkhano wake unali waufupi. Iye ananena kuti: “Sindinamvetse kwenikweni mfundo zamunkhani yake. Zomwe ndimakumbukira ndi zimene anthu anachita. Iwo anandilandira bwino n’kundipatsa moni wapadzanja. Ndinatha kuona kuti akuchita zimenezi mochokera pansi pa mtima.” Banja lina linkathandiza kwambiri Pauline kusamalira mwana wake kumisonkhano ndiponso mu utumiki. Patapita nthawi, Wayne anaganiza kuti amvetse zimene mkazi wake amakhulupirira choncho anapempha kuti aziphunzira Baibulo ndi m’bale wa m’banjalo.

17. (a) Kodi sitiyenera kudziimba mlandu pa nkhani iti? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kugwa ulesi pothandiza achibale athu?

17 Timafuna kuti achibale athu nawonso ayambe kutumikira Yehova. Koma mwina sangayambe ngakhale titayesetsa kuwathandiza. Ngati zimenezi zitachitika, sitiyenera kudziimba mlandu. Tikutero chifukwa sitingakakamize munthu kuti azikhulupirira zomwe timakhulupirira. Koma ngakhale zili choncho, dziwani kuti zimene mumachita potumikira Yehova mosangalala zingawathandize kwambiri. Choncho muziwapempherera, kukambirana nawo mwaulemu ndipo musagwe ulesi. (Mac. 20:20) Musakayikire kuti Yehova adzakudalitsani chifukwa cha khama lanu. Ndipo ngati achibale anuwo angakumvereni, adzapulumuka.

NYIMBO NA. 57 Tizilalikira kwa Anthu a Mitundu Yonse

^ ndime 5 Tonse timafuna kuti achibale athu azitumikira Yehova koma iwo ayenera kusankha okha ngati akufuna kapena ayi. Munkhaniyi, tikambirana zimene tingachite pothandiza achibale athu kuti azimvetsera uthenga wathu.

^ ndime 1 Mayina ena asinthidwa. Munkhaniyi tizigwiritsa ntchito mawu oti “achibale” ponena za achibale athu amene sanayambe kutumikira Yehova.

^ ndime 53 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: M’bale wachinyamata akuthandiza bambo ake omwe si Mboni kukonza galimoto. Pa nthawi yoyenera akuwasonyeza vidiyo pa jw.org®.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mlongo akumvetsera pamene mwamuna wake yemwe si Mboni akufotokoza mmene tsiku lake layendera. Kenako akusewera ndi banja lake.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mlongo waitanira abale ndi alongo kunyumba kwake. Abale ndi alongowo akuyesetsa kuti amudziwe bwino mwamuna wake. Kenako mwamunayo wapita ku Chikumbutso limodzi ndi mkazi wake.