NKHANI YOPHUNZIRA 32

Chikondi Chanu Chipitirire Kukula

Chikondi Chanu Chipitirire Kukula

“Ndikupitiriza kupemphera kuti chikondi chanu chipitirire kukula.”​—AFIL. 1:9.

NYIMBO NA. 106 Khalani Achikondi

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi ndi ndani amene anathandiza kukhazikitsa mpingo ku Filipi?

MTUMWI PAULO, Sila, Luka ndi Timoteyo atafika ku Filipi, anapeza anthu ambiri amene ankamvetsera uthenga wa Ufumu. Abale 4 akhamawa anathandiza kukhazikitsa mpingo ndipo abale ndi alongo amumpingo watsopanowu anayamba kusonkhana, mwina kunyumba ya wokhulupirira wina dzina lake Lidiya.​—Mac. 16:40.

2. Kodi abale ndi alongo amumpingowo anakumana ndi mavuto ati?

2 Koma kenako abale ndi alongowa anayamba kukumana ndi mavuto. Satana anachititsa kuti adani ena a choonadi ayambe kutsutsa kwambiri ntchito yolalikira ya Akhristu okhulupirikawa. Paulo ndi Sila anagwidwa, kumenyedwa ndi ndodo komanso kuikidwa m’ndende. Atamasulidwa, anapita kukaona ophunzira atsopanowo n’kuwalimbikitsa. Kenako Paulo, Sila ndi Timoteyo anachoka mumzindawu koma zikuoneka kuti Luka anatsala. Ndiye kodi abale ndi alongo atsopanowo anatani? Mzimu wa Yehova unawathandiza kuti apitirize kumutumikira mwakhama. (Afil. 2:12) Ndipo Paulo ayenera kuti ankawanyadira kwambiri.

3. Mogwirizana ndi Afilipi 1:9-11, kodi Paulo anatchula zinthu ziti m’pemphero?

3 Patapita zaka pafupifupi 10, Paulo analembera kalata Akhristu amumpingo wa ku Filipi. Mukamawerenga kalatayo mutha kuona kuti Paulo ankakonda kwambiri abalewo. Iye analemba kuti: “Ndikufunitsitsa nditakuonani ndi chikondi chachikulu ngati chimene Khristu Yesu ali nacho.” (Afil. 1:8) Paulo anawauza kuti ankawapempherera. Iye anapempha Yehova kuti awathandize kuti chikondi chawo chipitirire kukula, atsimikizire kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti, akhale opanda cholakwa, asakhumudwitse ena komanso kuti adzazidwe ndi zipatso zolungama. N’zosachita kufunsa kuti mawu ochokera mumtima a Paulowa angatithandizenso masiku ano. Choncho tiyeni tiwerenge zimene Paulo analembera Afilipi. (Werengani Afilipi 1:9-11.) Kenako tikambirana mfundo iliyonse imene anatchula n’kuona mmene tingaigwiritsire ntchito.

CHIKONDI CHATHU CHIZIKULA

4. (a) Malinga ndi 1 Yohane 4:9, 10, kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti amatikonda? (b) Kodi tiyenera kukonda bwanji Mulungu?

4 Yehova anasonyeza kuti amatikonda kwambiri pamene anatumiza Mwana wake kuti adzatifere chifukwa cha machimo athu. (Werengani 1 Yohane 4:9, 10.) Chikondi chachikulu chimene anatisonyezachi chimatilimbikitsa kuti nafenso tizimukonda. (Aroma 5:8) Koma kodi tiyenera kukonda bwanji Mulungu? Yesu anayankha funsoli pamene anauza Mfarisi wina kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” (Mat. 22:36, 37) Tiyenera kukonda Mulungu kuchokera pansi pa mtima ndipo chikondicho chiyenera kukula tsiku lililonse. Paulo anauza Akhristu a ku Filipi kuti chikondi chawo ‘chizipitirira kukula.’ Ndiye kodi tingatani kuti chikondi chathu chizikula?

5. Kodi tingatani kuti chikondi chathu chizikula?

5 Kuti tikonde Mulungu, choyamba tiyenera kumudziwa bwino. Paja Baibulo limanena kuti: “Munthu wopanda chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yoh. 4:8) Mtumwi Paulo ananenanso kuti chikondi chathu kwa Mulungu chimawonjezereka ‘tikamamudziwa molondola komanso kuzindikira bwino zinthu zokhudza iyeyo.’ (Afil. 1:9) Titangoyamba kuphunzira Baibulo, tinayamba kumukonda chifukwa chongodziwa pang’ono makhalidwe ake abwino. Koma titayamba kuphunzira zambiri m’pamene tinayambanso kumukonda kwambiri. N’chifukwa chake timaona kuti chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri pa moyo wathu ndi kuphunzira Baibulo komanso kuganizira mozama mfundo zake.​—Afil. 2:16.

6. Malinga ndi 1 Yohane 4:11, 20, 21, kodi tingatani kuti chikondi chathu chizikula?

6 Chikondi cha Mulungu chimatilimbikitsanso kuti tizikonda abale athu. (Werengani 1 Yohane 4:11, 20, 21.) Mwina tikhoza kuganiza kuti mwachibadwa tingathe kumakonda abale ndi alongo athu. Paja tonse timalambira Yehova n’kumayesetsa kutsanzira makhalidwe ake. Timatsanziranso Yesu, yemwe amatikonda kwambiri moti analolera kupereka moyo wake chifukwa cha ifeyo. Komatu nthawi zina zikhoza kutivuta kutsatira lamulo loti tizikondana. Chitsanzo ndi zimene zinachitika mumpingo wa ku Filipi.

7. Kodi tikuphunzira chiyani pa malangizo amene Paulo anapereka kwa Eodiya ndi Suntuke?

7 Eodiya ndi Suntuke anali alongo akhama omwe ‘ankayesetsa kutumikira Mulungu limodzi’ ndi mtumwi Paulo. Koma zikuoneka kuti anasemphana maganizo ndipo anasiya kugwirizana. M’kalata imene Paulo analembera mpingo wawo, iye anatchula Eodiya ndi Suntuke ndipo anawalangiza mosapita m’mbali kuti ayenera kukhala “amaganizo amodzi.” (Afil. 4:2, 3) Paulo anaona kuti ndi bwino kuuzanso mpingo wonse kuti: “Muzichita zinthu zonse popanda kung’ung’udza ndi kutsutsana.” (Afil. 2:14) N’zosakayikitsa kuti malangizo osapita m’mbali a Paulo anathandiza alongo okhulupirikawa komanso anthu onse mumpingo kuti azikondana kwambiri.

N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira makhalidwe abwino a abale athu? (Onani ndime 8) *

8. Kodi n’chiyani chingatilepheretse kukonda abale athu, nanga tingapewe bwanji?

8 Mofanana ndi alongo awiriwa, ifenso tikhoza kulephera kukonda kwambiri abale athu chifukwa choti timangoganizira zimene amalakwitsa. Koma tizikumbukira kuti aliyense amalakwitsa zinthu tsiku ndi tsiku. Choncho tikamangoganizira zimene ena amalakwitsa, tikhoza kusiya kuwakonda. Mwachitsanzo, tikhoza kukhumudwa ngati m’bale wina waiwala kuthandiza nawo poyeretsa Nyumba ya Ufumu. Ndiye tikayamba kuganizira zinthu zina zimene m’baleyo analakwitsanso mkwiyo wathu ukhoza kuwonjezeka ndipo tingasiye kumukonda. Zoterezi zikakuchitikirani, muzikumbukira mfundo iyi: Yehova amaona zimene ifeyo timalakwitsa komanso zimene m’bale wathuyo amalakwitsa. Ngakhale zili choncho, iye amatikonda tonse. Choncho ndi bwino kutsanzira chikondi cha Yehova n’kumaona zabwino zimene anzathu amachita. Tikamayesetsa kuti tizikonda abale athu tidzayamba kugwirizana nawo kwambiri.​—Afil. 2:1, 2.

“ZINTHU ZOFUNIKA KWAMBIRI”

9. Kodi zina mwa “zinthu zofunika kwambiri” zimene Paulo anatchula m’kalata yopita kwa Afilipi ndi ziti?

9 Motsogoleredwa ndi mzimu woyera, Paulo analangiza Akhristu a ku Filipi komanso tonsefe kuti: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.” (Afil. 1:10) Zina mwa zinthu zofunikazi ndi kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova, kukwaniritsidwa kwa zolinga zake komanso mtendere ndi mgwirizano mumpingo. (Mat. 6:9, 10; Yoh. 13:35) Tikamaona zinthu zimenezi kukhala zofunika kwambiri pa moyo wathu, timasonyeza kuti timakonda kwambiri Yehova.

10. Kodi tingatani kuti Yehova azitiona kuti ndife opanda cholakwa?

10 Paulo ananenanso kuti: “Mukhale opanda cholakwa.” Mawu amenewa sakutanthauza kuti tizikhala angwiro. N’zosatheka kuchita zinthu mosalakwitsa kalikonse ngati mmene Yehova Mulungu amachitira chifukwa iye ndi wangwiro. Koma Yehova akhoza kutiona kuti ndife opanda cholakwa ngati timayesetsa kukulitsa chikondi chathu komanso kutsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti. Njira imodzi imene tingasonyezere kuti ndife achikondi ndi kuyesetsa kuti tisamakhumudwitse ena.

11. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kukhumudwitsa ena?

11 Paulo anaperekanso chenjezo lakuti mukhale “osakhumudwitsa ena.” Kodi tingakhumudwitse bwanji anthu ena? Zimenezi zingachitike ngati sitinasankhe bwino zosangalatsa, zovala kapena ntchito. Zimene tingasankhezo mwina pazokha si zolakwika. Koma vuto limakhalapo ngati zimene tasankhazo zingavutitse chikumbumtima cha anthu ena mpaka kufika pokhumudwa nazo. Yesu ananena kuti aliyense wokhumudwitsa imodzi mwa nkhosa zake, zingamukhalire bwino kwambiri kumumangirira chimwala cholemera m’khosi mwake ndi kumumiza m’nyanja yaikulu.​—Mat. 18:6.

12. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha banja lina?

12 Taganizirani zimene banja lina la apainiya linachita potsatira zimene Yesu ananenazi. Mumpingo umene ankatumikira munali banja lina limene linali litangobatizidwa kumene ndipo onse m’banjali makolo awo ankawaletsa zinthu zambiri. Banjali linkaona kuti Akhristu sayenera kupita kumalo oonetsera mafilimu ngakhale mafilimuwo atakhala kuti ndi abwinobwino. Iwo anakhumudwa atadziwa kuti banja lomwe linkachita upainiya lija linapita kukaonera filimu. Zitatero apainiyawo anasiya kukaonera mafilimu mpaka pamene banja lija linaphunzira bwino n’kufika posiyanitsa zoyenera ndi zolakwika. (Aheb. 5:14) Zimene banjali linachita zinasonyeza kuti linkakonda m’bale ndi mlongo watsopanoyo mu zochita osati m’mawu okha.​—Aroma 14:19-21; 1 Yoh. 3:18.

13. Kodi tingachite bwanji zinthu zimene zingapangitse anthu ena kuchimwa?

13 Njira ina imene tingakhumudwitsire ena ndi kuchita zinthu zimene zingawapangitse kuti achimwe. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Taganizirani chitsanzo ichi. Tiyerekeze kuti munthu wina anali chidakwa ndiye pambuyo pophunzira Baibulo anayesetsa kwa nthawi yaitali kuti azidziletsa. Kenako anazindikira kuti ayenera kungosiyiratu mowa ndipo anasintha kwambiri mpaka kufika pobatizidwa. Ndiye tsiku lina waitanidwa kuti akacheze ndi abale ndi alongo ndipo amene wamuitanayo akumupatsa mowa n’kunena kuti: “Aaa imwani. Panotu ndinu Mkhristu ndipo mukutsogoleredwa ndi mzimu woyera. Paja khalidwe lina limene mzimu umatulutsa ndi kudziletsa. Ndipo ngati ndinu odziletsa sizingakuvuteni kudziwa malire omwera mowawu.” Kodi mukuganiza kuti chingachitike n’chiyani ngati m’bale watsopanoyu atatsatira malangizo olakwikawa?

14. Kodi misonkhano yathu imatithandiza bwanji kuti tizigwiritsa ntchito malangizo a pa Afilipi 1:10?

14 Misonkhano yathu imatithandizanso kutsatira malangizo a pa Afilipi 1:10 m’njira zosiyanasiyana. Choyamba, chakudya chauzimu chimene timalandira chimatithandiza kuti tizikumbukira zinthu zimene Yehova amaona kuti n’zofunika kwambiri. Chachiwiri, timamva mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zomwe timaphunzira n’cholinga choti tikhale opanda cholakwa. Ndipo chachitatu, timalimbikitsidwa “pa chikondi ndi ntchito zabwino.” (Aheb. 10:24, 25) Tikamalimbikitsidwa kwambiri ndi abale athu m’pamene timayambanso kukonda kwambiri Mulungu ndi Akhristu anzathu. Ndipo kukonda Mulungu ndi anzathu kuchokera mumtima kungatithandize kuti tiziyesetsa kuti tisakhumudwitse abale athu.

PITIRIZANI ‘KUDZAZIDWA NDI ZIPATSO ZOLUNGAMA’

15. Kodi tingadzazidwe bwanji ndi “zipatso zolungama”?

15 Paulo anapemphera kuti Akhristu a ku Filipi ‘adzazidwe ndi zipatso zolungama.’ (Afil. 1:11) N’zosakayikitsa kuti zina mwa ‘zipatso zolungamazi’ zinali kukonda Yehova komanso anthu ake. Zipatsozi zinkaphatikizanso kuuza anthu ena chifukwa chake ankakhulupirira Yesu komanso zinthu zabwino zimene ankayembekezera. Palemba la Afilipi 2:15 pali chitsanzo cha ‘kuwala monga zounikira m’dzikoli.’ Chitsanzochi ndi choyenera chifukwa Yesu ananena kuti ophunzira ake ndi “kuwala kwa dziko.” (Mat. 5:14-16) Iye analamulanso otsatira ake kuti ‘aziphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira ake.’ Ananenanso kuti akhale ‘mboni zake mpaka kumalekezero a dziko lapansi.’ (Mat. 28:18-20; Mac. 1:8) Timabala “zipatso zolungama” tikamagwira mwakhama ntchito yofunikayi.

Paulo ali pa ukaidi wosachoka panyumba ku Roma, analembera mpingo wa ku Filipi kalata ndipo ankalalikira anthu omulondera komanso ena amene anabwera kudzamuona (Onani ndime 16)

16. Kodi lemba la Afilipi 1:12-14 limasonyeza bwanji kuti tikhoza kuwalabe ngati zounikira ngakhale tikukumana ndi mavuto? (Onani chithunzi patsamba loyamba la magaziniyi.)

16 Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wathu, tonsefe tikhoza kuwala monga zounikira. Nthawi zina, zinthu zimene zingaoneke kuti zingatilepheretse kulalikira uthenga wabwino zikhoza kutipatsa mwayi woti tilalikire anthu ena. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anali pa ukaidi wosachoka panyumba ku Roma pa nthawi imene analembera kalata Akhristu a ku Filipi. Komabe iye ankakwanitsa kulalikira kwa anthu omulondera komanso amene ankabwera kudzamuona. Paulo ankalalikirabe mwakhama ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto amenewa ndipo zimenezi zinalimbikitsa abale kuti azilankhula “mawu a Mulungu mopanda mantha.”​—Werengani Afilipi 1:12-14; 4:22.

Nthawi zonse tiziyesetsa kupeza mpata wolalikira (Onani ndime 17) *

17. Perekani chitsanzo chamasiku ano cha anthu amene amabala zipatso ngakhale akukumana ndi mavuto.

17 Abale ndi alongo ambiri amakhala ndi mwayi woti azitsatira chitsanzo cha Paulo chokhala wolimba mtima. Tikutero chifukwa amakhala m’dziko limene mulibe ufulu wolalikira choncho amapeza njira zina zoti azilalikira. (Mat. 10:16-20) M’dziko lina, woyang’anira dera wina analimbikitsa wofalitsa aliyense kuti azilalikira anzake, achibale ake, anthu okhala nawo pafupi, anzake akusukulu komanso anzake akuntchito. Pasanathe zaka ziwiri, chiwerengero cha mipingo m’deralo chinawonjezereka kwambiri. Mwina m’dziko limene tikukhala muli ufulu wolalikira, koma tikhoza kutsatirabe chitsanzo cha abale ndi alongowa. Tingachite zimenezi poyesetsa nthawi zonse kupeza mpata wolalikira. Komanso tisamakayikire kuti Yehova adzatipatsa mphamvu yochitira zimenezi ngakhale tikukumana ndi mavuto.​—Afil. 2:13.

18. Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani?

18 M’masiku otsirizawa, tiyeni tiziyesetsa kutsatira malangizo amene Mulungu anauzira Paulo kuti alembere Afilipi. Tizitsimikizira kuti zinthu zofunika ndi ziti, tizikhala opanda cholakwa, tizipewa kukhumudwitsa ena komanso tizibala zipatso zolungama. Tikatero chikondi chathu chidzapitiriza kukula komanso tizilemekeza Yehova yemwe ndi Atate wathu wachikondi.

NYIMBO NA. 17 “Ndikufuna”

^ ndime 5 Masiku ano, tiyenera kukonda kwambiri abale athu kusiyana ndi m’mbuyo monsemu. Kalata imene Paulo analembera Afilipi ingatithandize kudziwa zimene tingachite kuti chikondi chathu chizikula ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto.

^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Abale akuyeretsa Nyumba ya Ufumu ndipo m’bale wina dzina lake Joe wasiya kaye kuti alankhule ndi m’bale wina ndi mwana wake. Zimene wachitazi zakwiyitsa Mike yemwe akuyeretsanso nawo. Iye akuganiza kuti, ‘Koma zoona Joe akucheza m’malo mogwira ntchito?’ Koma pa nthawi ina, Mike akuona Joe akuthandiza mokoma mtima mlongo wina wachikulire. Zimenezi zakumbutsa Mike kuti ayenera kuyesetsa kuganizira makhalidwe abwino a Joe.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: M’dziko limene mulibe ufulu wolalikira, m’bale wina akulalikira mnzake mosamala. Pa nthawi ina, m’baleyo akulalikiranso mnzake wakuntchito pa nthawi yopuma.