NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA September 2019
Yehova Amaona Kuti Atumiki Ake Odzichepetsa Ndi Amtengo Wapatali
Kudzichepetsa ndi khalidwe lofunika kwambiri. N’chifukwa chiyani tingavutike kukhala odzichepetsa zinthu zikasintha pa moyo wathu?
Uthenga Wokhudza Aramagedo Ndi Wosangalatsa
Kodi ndi zinthu zazikulu ziti zomwe zidzachitike Aramagedo isanayambe? Kodi tingatani kuti tikhalebe okhulupirika pamene mapeto akuyandikira?
Tizigonjera Yehova ndi Mtima Wonse
Akulu, abambo ndi amayi angaphunzire kugonjera kuchokera kwa Nehemiya, Mfumu Davide ndi Mariya, mayi ake a Yesu.
“Bwerani kwa Ine . . . Ndipo Ndidzakutsitsimutsani”
Kodi tingapite bwanji kwa Yesu? Tingapitirize kutsitsimulidwa ndi goli la Yesu ngati titachita zinthu zitatu.
“Ndinaona Khamu Lalikulu la Anthu”
M’masomphenya amene Yohane anaona, Yehova anathandiza anthu kudziwa khamu lalikulu, kukula kwake komanso kuti anthu ake ndi ochokera m’mitundu yosiyanasiyana. Khamuli lidzapulumuka chisautso chachikulu n’kukhala padziko lapansi mpaka kalekale.