NKHANI YOPHUNZIRA 46

Kodi Mukusamalira ‘Chishango Chanu Chachikulu Chachikhulupiriro’?

Kodi Mukusamalira ‘Chishango Chanu Chachikulu Chachikhulupiriro’?

“Nyamulani chishango chachikulu chachikhulupiriro.”​—AEF. 6:16.

NYIMBO NA. 119 Tiyenera Kukhala ndi Chikhulupiriro

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. (a) Malinga ndi Aefeso 6:16, kodi “chishango chachikulu chachikhulupiriro” chingatithandize bwanji? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

KODI inuyo muli ndi “chishango chachikulu chachikhulupiriro”? (Werengani Aefeso 6:16.) N’zosachita kufunsa kuti muli nacho. Kale chishango chinkateteza mbali yaikulu ya thupi la msilikali. Nachonso chikhulupiriro chimakutetezani kuti mupewe chiwerewere, chiwawa komanso zinthu zina zoipa zam’dzikoli.

2 Koma popeza tili ‘m’masiku otsiriza,’ tizikumana ndi zinthu zimene zingayese chikhulupiriro chathu. (2 Tim. 3:1) Ndiye kodi tingaonetsetse bwanji kuti chishango chathu chachikhulupiriro n’cholimba? Nanga tingatani kuti tichigwire mwamphamvu? Tiyeni tikambirane mayankho a mafunso amenewa.

MUZIONETSETSA KUTI CHISHANGO CHANU CHILI BWINO

Asilikali akabwera kuchokera kunkhondo ankakonza zishango zawo (Onani ndime 3)

3. Kodi asilikali ankasamalira bwanji zishango zawo, nanga n’chifukwa chiyani?

3 Asilikali akale ankakhala ndi zishango zimene ankazikutira ndi chikopa. Zishangozo ankazipaka mafuta n’cholinga choti chikopa chisawonongeke komanso zitsulo zake zisachite dzimbiri. Msilikali akaona kuti chishango chake chawonongeka ankaonetsetsa kuti chakonzedwa asanapitenso kunkhondo. Kodi mungatsatire bwanji chitsanzochi pa nkhani ya chikhulupiriro chanu?

4. N’chifukwa chiyani muyenera kuonetsetsa kuti chishango chanu chachikhulupiriro chili bwino, nanga mungachite bwanji zimenezi?

4 Mofanana ndi asilikali akale, muzionetsetsa kuti chikhulupiriro chanu ndi cholimba n’cholinga choti mukhale okonzeka kumenya nkhondo. Akhristufe tili pa nkhondo yauzimu ndipo adani athu ena ndi mizimu yoipa. (Aef. 6:10-12) Koma tiyenera kusamalira tokha chishango chathu chachikhulupiriro chifukwa palibe amene angatichitire zimenezi. Ndiye kodi mungatsimikizire bwanji kuti mwakonzeka kukumana ndi mayesero? Choyamba, muyenera kupempha Mulungu kuti azikuthandizani. Kenako muyenera kuwerenga Baibulo kuti muzidziona mmene Mulungu amakuonerani. (Aheb. 4:12) Paja Baibulo limati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu.” (Miy. 3:5, 6) Mogwirizana ndi mfundoyi, mungachite bwino kuganizira zimene mwasankha posachedwapa pa nkhani zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, kodi mwakumana ndi vuto lalikulu lazachuma? Kodi munakumbukira lonjezo la Yehova la pa Aheberi 13:5 lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono”? Nanga lonjezoli linakutsimikizirani kuti Yehova akuthandizani? Ngati zili choncho, ndiye kuti mukusamalira bwino chishango chanu chachikhulupiriro.

5. Kodi mukhoza kupeza zotani ngati mutafufuza mmene chikhulupiriro chanu chilili?

5 Mwina mungadabwe ndi zimene mungapeze pambuyo pofufuza mmene chikhulupiriro chanu chilili. Mukhoza kupeza mavuto ena omwe simunawadziwe. Mwachitsanzo, mungazindikire kuti nkhawa, mabodza kapena zinthu zina zokhumudwitsa zafooketsa chikhulupiriro chanu. Ngati zimenezi zakuchitikirani, kodi mungatani kuti muteteze chikhulupiriro chanu kuti chisapitirire kuwonongeka?

MUSASOKONEZEKE NDI NKHAWA, MABODZA NDI ZINTHU ZOKHUMUDWITSA

6. Perekani zitsanzo za nkhawa zoyenera.

6 Nkhawa zina ndi zoyenera. Mwachitsanzo, timakhala ndi nkhawa yoti tisakhumudwitse Yehova ndi Yesu. (1 Akor. 7:32) Ngati tachita tchimo lalikulu, timakhala ndi nkhawa yoti tikonze ubwenzi wathu ndi Mulungu. (Sal. 38:18) Timakhalanso ndi nkhawa yoti tisakhumudwitse mwamuna kapena mkazi wathu komanso kuti tizisamalira anthu a m’banja lathu ndi amumpingo.​—1 Akor. 7:33; 2 Akor. 11:28.

7. Malinga ndi Miyambo 29:25, n’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa anthu?

7 Komabe tikamada nkhawa mopitirira malire, tingawononge chikhulupiriro chathu. Mwachitsanzo, mwina tingamadere nkhawa kwambiri mmene tingapezere chakudya chokwanira komanso zovala. (Mat. 6:31, 32) Pofuna kuthana ndi nkhawa zimenezi, tingayambe kumangoganizira zopeza ndalama. Mwinanso tingayambe kukonda ndalamazo. Ngati titalola kuti zimenezi zichitike, chikhulupiriro chathu chingayambe kufooka ndipo tingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. (Maliko 4:19; 1 Tim. 6:10) Nkhawa ina yosayenera ndi kufunitsitsa kuti anthu azisangalala nafe. Tingayambe kuopa kwambiri kunyozedwa kapena kuzunzidwa ndi anthu kuposa mmene timaopera kukhumudwitsa Yehova. Kuti tipewe zimenezi, tiyenera kupempha Yehova kuti atithandize kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu komanso kukhala olimba mtima.​—Werengani Miyambo 29:25; Luka 17:5.

(Onani ndime 8) *

8. Kodi tiyenera kutani ngati munthu wina akufalitsa mabodza?

8 Satana, yemwe ndi “tate wake wa bodza,” amagwiritsa ntchito anthu ake kuti azifalitsa mabodza okhudza Yehova komanso abale ndi alongo athu. (Yoh. 8:44) Mwachitsanzo, anthu ampatuko amatha kugwiritsa ntchito zinthu monga intaneti kapena TV kuti afalitse mabodza kapena kupotoza mfundo zokhudza gulu la Yehova. Mabodza amenewa ali m’gulu la ‘mivi yoyaka moto’ ya Satana. (Aef. 6:16) Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati munthu wina akunena mabodza oterewa? Sitiyenera kumvetsera. Tikutero chifukwa choti timakhulupirira Yehova komanso abale athu. Choncho tiyenera kupeweratu ampatuko. Tisalole kuti munthu aliyense kapena chidwi chathu zitichititse kuyamba kukangana ndi ampatuko.

9. Kodi zinthu zokhumudwitsa zingatisokoneze bwanji?

9 Zinthu zokhumudwitsa zingafooketse chikhulupiriro chathu. N’zoona kuti nthawi zina timatha kukhumudwa chifukwa cha mavuto athu. Ndipotu si bwino kungonyalanyaza mavutowo. Koma tiyenera kupewa kumangoganizira za mavuto athuwo chifukwa zimenezi zikhoza kutiiwalitsa madalitso amene Yehova walonjeza. (Chiv. 21:3, 4) Ndiye tikhoza kukhumudwa kwambiri mpaka kufooka moti tingafike potaya mtima. (Miy. 24:10) Koma n’zotheka kupewa zimenezi.

10. Kodi tikuphunzira chiyani pa kalata imene mlongo wina analemba?

10 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina wa ku United States amene akusamalira mwamuna wake yemwe akudwala kwambiri. M’kalata imene analemba yopita kulikulu lathu ananena kuti: “N’zoona kuti vuto lathu limatidetsa nkhawa komanso kutikhumudwitsa nthawi zina, koma chiyembekezo chathu chidakali champhamvu. Ndimayamikira kwambiri zinthu zimene takhala tikulandira zomwe zikutilimbikitsa komanso kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Tinkafunikira kulangizidwa ndi kulimbikitsidwa m’njira imeneyi. Zimatithandiza kuti tizitumikirabe Mulungu n’kumapirira mayesero ochokera kwa Satana.” Chitsanzo cha mlongoyu chikusonyeza kuti tikhoza kupewa kukhumudwa kwambiri tikakumana ndi mavuto. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyenera kuona kuti mavuto athu ndi njira imene Satana akugwiritsa ntchito potiyesa. Tizikumbukiranso kuti Mulungu ndi amene angatitonthoze. Komanso tiziyamikira chakudya chauzimu chimene amatipatsa.

Kodi mumasamalira bwino ‘chishango chanu chachikulu chachikhulupiriro’? (Onani ndime 11) *

11. Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati kuti tidziwe ngati chikhulupiriro chathu chidakali cholimba?

11 Kodi pali zinthu zina zimene muyenera kukonza kuti chikhulupiriro chanu chikhale cholimba? Kodi pa miyezi yapitayi mwakwanitsa kupewa kuda nkhawa mopitirira malire? Kodi mwakhala mukupewa kumvetsera ampatuko kapena kukangana nawo pa mabodza amene amafalitsa? Nanga kodi mwakwanitsa kupirira mutakumana ndi zinthu zokhumudwitsa? Ngati ndi choncho, ndiye kuti chikhulupiriro chanu n’cholimba. Koma tiyenera kukhalabe maso chifukwa Satana angagwiritse ntchito zinthu zinanso pofuna kutisokoneza. Tiyeni tsopano tikambirane chinthu china chimene iye angagwiritse ntchito.

MUZIPEWA KUKONDA CHUMA

12. Kodi n’chiyani chingachitike ngati timakonda chuma?

12 Kukonda chuma kungatisokoneze komanso kufooketsa chikhulupiriro chathu. Mtumwi Paulo anati: “Msilikali amene ali pa nkhondo sachita nawo zamalonda zimene anthu wamba amachita, pofuna kukondweretsa amene anamulemba usilikali.” (2 Tim. 2:4) Asilikali achiroma sankaloledwa kuti azichita zamalonda ngakhale pang’ono. Kodi n’chiyani chikanachitikira msilikali ngati atanyalanyaza zimenezi?

13. N’chifukwa chiyani asilikali sankaloledwa kuchita zamalonda?

13 Tiyerekeze kuti gulu la asilikali lakhala likuphunzira kugwiritsa ntchito malupanga awo m’mawa wonse koma mmodzi palibe. Iye ali kumsika kukagulitsa zakudya. Madzulo, asilikaliwo akuonetsetsa kuti zovala zawo zili bwino komanso akunola malupanga awo. Koma wina uja akukonza zakudya zoti akagulitse mawa lake. Ndiyeno m’mawa wa tsiku lotsatira adani akuwaukira mwadzidzidzi. Kodi ndi msilikali uti amene angachite zinthu zoyenera komanso zosangalatsa mtsogoleri wawo? Nanga inuyo mungafune kukhala limodzi ndi msilikali uti, amene ankakonzekera nkhondo kapena amene ankasokonezedwa ndi kugulitsa zakudya?

14. Popeza ndife asilikali a Khristu, kodi chofunika kwambiri kwa ife n’chiyani?

14 Nafenso tisamalole kusokonezedwa ndi zinthu zina moti n’kulephera kusangalatsa Yehova ndi Khristu, amene ndi Atsogoleri athu. Tiyenera kuona kuti zimenezi n’zofunika kwambiri kuposa chilichonse chimene tingapeze m’dziko la Satanali. Choncho tizionetsetsa kuti tili ndi nthawi ndiponso mphamvu zokwanira kuti tizitumikira Yehova komanso kusamalira chishango chathu chachikhulupiriro ndi zida zina zauzimu.

15. Kodi Paulo anapereka chenjezo lotani, ndipo n’chifukwa chiyani?

15 Nthawi zonse tiyenera kukhala maso. Paja mtumwi Paulo anachenjeza kuti ‘anthu ofunitsitsa kulemera adzasocheretsedwa n’kusiya chikhulupiriro.’ (1 Tim. 6:9, 10) Mawu oti ‘kusocheretsedwa’ akusonyeza kuti tikhoza kusokonezedwa chifukwa choyesetsa kupeza zinthu zosafunika kwenikweni. Kenako tikhoza kuyamba ‘kulakalaka zinthu zopweteketsa komanso zopanda nzeru.’ Koma m’malo moyamba kuzilakalaka, tiyenera kuzindikira kuti zinthuzi ndi zida zomwe zingawononge chikhulupiriro chathu.

16. Kodi nkhani ya pa Maliko 10:17-22 ingatichititse kudzifunsa mafunso ati?

16 Tiyerekeze kuti tili ndi ndalama zokwanira moti tikhoza kugula zinthu zambiri. Kodi kungakhale kulakwa ngati titagula zinthu zimene timalakalaka koma zosafunika kwambiri? Osati kwenikweni, koma ndi bwino kudzifunsa mafunso awa: Ngakhale kuti tingakwanitse kugula chinthu chinachake, kodi tingakhaledi ndi nthawi komanso mphamvu zoti tizichigwiritsa ntchito ndiponso kuchisamalira? Nanga kodi tingayambe kukonda kwambiri zinthu zimene tagulazo? Kodi mwina tingafanane ndi mnyamata amene ankakonda zinthu zake mpaka kukana kuchita zambiri potumikira Mulungu atapemphedwa ndi Yesu? (Werengani Maliko 10:17-22.) Tingachite bwino kukhala moyo wosalira zambiri n’kumagwiritsa ntchito nthawi komanso mphamvu zathu potumikira Mulungu.

GWIRANI MWAMPHAMVU CHISHANGO CHANU CHACHIKHULUPIRIRO

17. Kodi sitiyenera kuiwala chiyani?

17 Tisaiwale kuti tili pankhondo ndipo tsiku lililonse tiyenera kukhala okonzeka kumenyana ndi adani athu. (Chiv. 12:17) Abale ndi alongo athu sangatinyamulire chishango chathu chachikhulupiriro. Koma aliyense ayenera kugwira mwamphamvu chishango chake.

18. N’chifukwa chiyani asilikali akale ankagwira mwamphamvu zishango zawo?

18 Kale, msilikali wolimba mtima kunkhondo ankalandira ulemu. Koma ankachita manyazi akabwera kunkhondo wopanda chishango chake. Wolemba mbiri yakale wa ku Rome dzina lake Tacitus, ananena kuti: “Msilikali akabwera kunkhondo wopanda chishango chake ankanyozeka kwambiri.” Ichi ndi chifukwa chimodzi chimene asilikali ankagwirira mwamphamvu zishango zawo.

Mlongo wagwira mwamphamvu chishango chachikulu chachikhulupiriro powerenga Mawu a Mulungu, kupezeka pamisonkhano nthawi zonse komanso kulalikira mwakhama (Onani ndime 19)

19. Kodi tingatani kuti tigwire mwamphamvu chishango chathu chachikhulupiriro?

19 Timagwira mwamphamvu chishango chathu chachikhulupiriro tikamapezeka pamisonkhano yathu nthawi zonse komanso kuuza ena za dzina la Yehova ndi Ufumu wake. (Aheb. 10:23-25) Tiyeneranso kuwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse n’kumapempha Yehova kuti atithandize kutsatira malangizo ake pa zonse zimene timachita. (2 Tim. 3:16, 17) Tikamatero, chida chilichonse chimene Satana angagwiritse ntchito sichidzativulaza mpaka kalekale. (Yes. 54:17) ‘Chishango chathu chachikulu chachikhulupiriro’ chidzatiteteza ndipo tidzakhala olimba mtima n’kumatumikira mogwirizana ndi abale ndi alongo athu. Tikamachita zimenezi, chikhulupiriro chathu chidzakhalabe cholimba ndipo tidzakhala ndi mwayi wokhala kumbali ya Yesu akadzapambana pa nkhondo yolimbana ndi Satana limodzi ndi gulu lake.​—Chiv. 17:14; 20:10.

NYIMBO NA. 118 “Tiwonjezereni Chikhulupiriro”

^ ndime 5 Asilikali akale ankadalira chishango kuti atetezeke. Chikhulupiriro chathu chimakhalanso ngati chishango. Ndipo mofanana ndi chishango, chikhulupiriro chathu chimafunika kuchisamalira. Munkhaniyi tiona zimene tingachite kuti tizisamalira ‘chishango chathu chachikulu chachikhulupiriro.’

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Banja la Mboni lathimitsa TV litangoona kuti ayamba kuonetsa ampatuko omwe amafalitsa mabodza okhudza Mboni za Yehova.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pa nthawi ya kulambira kwa pabanja, bambo akugwiritsa ntchito malemba ena kuti alimbitse chikhulupiriro cha banjalo.