NKHANI YOPHUNZIRA 49

Pali Nthawi Yogwira Ntchito ndi Nthawi Yopuma

Pali Nthawi Yogwira Ntchito ndi Nthawi Yopuma

“Tipite kwatokha kopanda anthu kuti mupumule pang’ono.”—MALIKO 6:31.

NYIMBO NA. 143 Pitirizani Kugwira Ntchito, Kukhala Maso ndi Kudikira

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi anthu ambiri ali ndi maganizo otani pa nkhani ya ntchito?

KODI maganizo a anthu pa nkhani ya ntchito ndi otani kumene mumakhala? M’mayiko ena anthu akulimbikira kwambiri ntchito ndipo akumagwira nthawi yaitali kuposa m’mbuyomu. Anthu oterewa sakhala ndi nthawi yopuma, yocheza ndi mabanja awo kapena yophunzira za Mulungu. (Mlal. 2:23) Koma anthu ena safuna kugwira ntchito ngakhale pang’ono ndipo amapeza zifukwa zodzikhululukira.​—Miy. 26:13, 14.

2-3. Kodi Yehova ndi Yesu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani ya ntchito?

2 Koma maganizo a Yehova ndi Yesu pa nkhani ya ntchito ndi osiyana kwambiri ndi a anthu ambiri m’dzikoli. N’zosachita kufunsa kuti Yehova amagwira ntchito. Paja Yesu ananena kuti: “Atate wanga akugwirabe ntchito mpaka pano, inenso ndikugwirabe ntchito.” (Yoh. 5:17) Taganizirani ntchito yaikulu imene Mulungu anagwira polenga kumwamba komanso angelo osawerengeka. Yehova anagwiranso ntchito polenga zinthu zambiri zokongola zomwe zili padziko lapansili. M’pake kuti wolemba masalimo anati: “Ntchito zanu ndi zochuluka, inu Yehova! Zonsezo munazipanga mwanzeru zanu. Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga.”​—Sal. 104:24.

3 Yesu ankatsanzira Atate ake. Iye anathandiza Mulungu pamene ‘ankakonza kumwamba.’ Ndiponso anali “mmisiri waluso” pogwira ntchito ndi Yehova. (Miy. 8:27-31) Yesu ali padzikoli, ankagwiranso ntchito mwakhama. Iye ananena kuti ntchito yakeyo inali ngati chakudya ndipo zimene ankachita zinkatsimikizira kuti anatumidwa ndi Mulungu.​—Yoh. 4:34; 5:36; 14:10.

4. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Yehova ndi Yesu pa nkhani yopuma?

4 Kodi khama la Yehova ndi Yesu pogwira ntchito likusonyeza kuti kupuma si kofunika? Ayi. Yehova satopa, choncho safunika kupuma. Komabe Baibulo limanena kuti Yehova atalenga kumwamba ndi dziko lapansi, “anapuma pa ntchito yake.” (Eks. 31:17) Apa zikuoneka kuti Yehova anaima kaye n’kumasangalala ndi ntchito imene anagwira. Nayenso Yesu ankagwira ntchito mwakhama ali padzikoli koma ankakhala ndi nthawi yopuma komanso kudya ndi anzake.​—Mat. 14:13; Luka 7:34.

5. Kodi anthu ambiri amakumana ndi vuto lotani?

5 Baibulo limalimbikitsa anthu a Mulungu kuti azikonda kugwira ntchito. Atumiki a Mulungu amafunika kukhala akhama osati aulesi. (Miy. 15:19) Mwina mumagwira ntchito kuti muzisamalira banja lanu. Ndipo ophunzira onse a Khristu ali ndi udindo wogwira ntchito yolalikira uthenga wabwino. Koma muyeneranso kupuma mokwanira. Kodi zimakuvutani kugawa bwino nthawi kuti muzitha kugwira ntchito, kulalikira komanso kupuma? Kodi mungatani kuti muzigwira bwino ntchito komanso kupuma mokwanira?

KHALANI NDI MAGANIZO OYENERA

6. Kodi lemba la Maliko 6:30-34 likusonyeza bwanji kuti Yesu anali ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito ndiponso kupuma?

6 Tizikhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito. Mfumu Solomo analemba kuti: “Chilichonse chili ndi nthawi yake.” Iye anatchula za nthawi yobzala, yomanga, yolira, yoseka, yovina komanso ya zinthu zina. (Mlal. 3:1-8) Apa n’zoonekeratu kuti kugwira ntchito komanso kupuma ndi zinthu zofunika kwambiri pa moyo. Yesu anali ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito komanso kupuma. Pa nthawi ina, atumwi anabwera kuchokera kokalalikira. Iwo anatanganidwa kwambiri moti “analibe nthawi yopuma, ngakhale yoti adye chakudya.” Atabwerako, Yesu anawauza kuti: “Inuyo bwerani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mupumule pang’ono.” (Werengani Maliko 6:30-34.) Ngakhale kuti nthawi zina Yesu ndi ophunzira ake sankapeza nthawi yokwanira yoti apume, iye ankadziwa kuti onsewo ankafunika kupuma.

7. Kodi kukambirana za Sabata kungatithandize bwanji?

7 Anthufe nthawi zina timafunika kupuma kapena kusintha zochita. Umboni wake ndi lamulo lokhudza Sabata limene Mulungu anapatsa Aisiraeli. N’zoona kuti sitiyendera Chilamulo cha Mose. Koma zimene Mulungu ananena pa nkhani ya Sabata zingatithandize kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito ndi kupuma.

SABATA INALI NTHAWI YOPUMA KOMANSO YOLAMBIRA

8. Malinga ndi Ekisodo 31:12-15, kodi anthu ankachita chiyani pa Sabata?

8 Mawu a Mulungu amasonyeza kuti pambuyo polenga zinthu kwa ‘masiku 6,’ Mulungu anapuma pa ntchito yake yolenga zinthu padzikoli. (Gen. 2:2) Koma Yehova amakonda kugwira ntchito ndipo “akugwirabe ntchito” zina mpaka pano. (Yoh. 5:17) Iye anagwira ntchito kwa ‘masiku 6’ n’kupuma la 7 ndipo anauza Aisiraeli kuti azipumanso pa tsiku la 7. Mulungu ananena kuti Sabata linali chizindikiro pakati pa iye ndi Aisiraeliwo. Linali tsiku “lopuma pa ntchito zonse . . . lopatulika kwa Yehova.” (Werengani Ekisodo 31:12-15.) Aliyense sankayenera kugwira ntchito, kaya ndi mwana, kapolo kapena ziweto. (Eks. 20:10) Tsikuli linkathandiza kuti anthu azichita zinthu zokhudza kulambira Mulungu.

9. Kodi anthu anali ndi maganizo olakwika ati okhudza Sabata mu nthawi ya Yesu?

9 Tsiku la Sabata linali lothandiza kwambiri kwa anthu a Mulungu. Koma atsogoleri achipembedzo a nthawi ya Yesu anaika malamulo okhwima okhudza tsikuli. Ankanena kuti n’kulakwa ngakhale kungobudula ngala za mbewu pa tsikuli kapena kuchiritsa munthu amene akudwala. (Maliko 2:23-27; 3:2-5) Zimenezi zinali zosiyana kwambiri ndi maganizo a Yehova ndipo Yesu anathandiza anthu kuzindikira mfundoyi.

Anthu a m’banja la Yesu ankachita zinthu zokhudza kulambira pa tsiku la Sabata (Onani ndime 10) *

10. Malinga ndi Mateyu 12:9-12, kodi maganizo a Yesu pa nkhani ya Sabata anali otani?

10 Yesu ndi otsatira ake achiyuda ankasunga Sabata chifukwa choti ankatsatira Chilamulo cha Mose. * Koma zolankhula ndi zochita za Yesu zinasonyeza maganizo oyenera pa nkhani ya Sabata. Iye anasonyeza kuti kuchita zinthu zothandiza anthu ena patsikuli n’kololeka. Yesu ananena momveka bwino kuti: ‘N’kololeka kuchita chinthu chabwino pa tsiku la sabata.’ (Werengani Mateyu 12:9-12.) Iye ankaona kuti kukomera anthu mtima komanso kuwathandiza pa tsikuli si kuphwanya malamulo. Zimene Yesu ankachita pa Sabata zinasonyeza chinthu chofunika chokhudza tsikuli. Popeza anthu a Mulungu ankapuma pa ntchito zawo, ankakhala ndi mwayi wochita zinthu zokhudza kulambira. Yesu anakulira m’banja limene liyenera kuti linkachita zinthu zokhudza kulambira pa tsiku la Sabata. Umboni wake ndi zimene Baibulo limanena pofotokoza za Yesu ali kwawo ku Nazareti. Limanena kuti: “Malinga ndi chizolowezi chake pa tsiku la sabata, [Yesu] analowa m’sunagoge, ndi kuimirira kuti awerenge Malemba.”​—Luka 4:15-19.

KODI MAGANIZO ANU NDI OTANI PA NKHANI YA NTCHITO?

11. Kodi ndi ndani anapereka chitsanzo chabwino kwa Yesu pa nkhani ya ntchito?

11 N’zosakayikitsa kuti Yosefe ankaphunzitsa Yesu ukalipentala komanso maganizo a Mulungu pa nkhani ya ntchito. (Mat. 13:55, 56) Yesu ayenera kuti ankaona Yosefe akugwira ntchito mwakhama kuti azisamalira banja lake lomwe linali lalikulu. N’zochititsa chidwi kuti Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Wantchito ayenera kulandira malipiro ake.” (Luka 10:7) Choncho tingati iye ankadziwa kugwira ntchito mwakhama.

12. Kodi ndi malemba ati omwe amasonyeza zimene Baibulo limanena pa nkhani yogwira ntchito mwakhama?

12 N’chimodzimodzinso ndi mtumwi Paulo. Ntchito yake yaikulu inali youza anthu za Yesu komanso zimene ankaphunzitsa. Komabe Paulo ankagwira ntchito zina kuti azipeza zofunika pa moyo. Akhristu a ku Tesalonika ankadziwa kuti iye ‘ankagwira ntchito mwakhama’ “usiku ndi usana” pofuna kuti ‘aliyense asamulipirire kanthu kalikonse’ pomuthandiza. (2 Ates. 3:8; Mac. 20:34, 35) N’kutheka kuti Paulo ankanena za ntchito yake yopanga matenti. Ali ku Korinto, iye ankakhala ndi Akula ndi Purisikila ndipo “ankagwira ntchito pamodzi pakuti onse anali amisiri opanga mahema.” Koma mawu oti Paulo ankagwira ntchito “usiku ndi usana” sakutanthauza kuti ankagwira ntchito popanda kupuma. Iye ankapuma masiku ena monga pa Sabata. Pa tsikulo ankakhala ndi mwayi wolalikira Ayuda omwe sankagwiranso ntchito pa Sabata.​—Mac. 13:14-16, 42-44; 16:13; 18:1-4.

13. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Paulo?

13 Mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Iye ankafunika kugwira ntchito zina koma ankagwirabe ntchito yopatulika “yolengeza uthenga wabwino wa Mulungu.” (Aroma 15:16; 2 Akor. 11:23) Paulo ankalimbikitsa anthu ena kuti azichitanso zimenezi. Ndipo Akula ndi Purisika anali ‘antchito anzake mwa Khristu Yesu.’ (Aroma 12:11; 16:3) Paulo ankalimbikitsa Akhristu a ku Korinto kuti azikhala ndi “zochita zambiri nthawi zonse mu ntchito ya Ambuye.” (1 Akor. 15:58; 2 Akor. 9:8) Yehova anauzira Paulo kulemba kuti: “Ngati wina sakufuna kugwira ntchito, asadye.”​—2 Ates. 3:10.

14. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena mawu a pa Yohane 14:12?

14 M’masiku otsirizawa, ntchito yofunika kwambiri ndi yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. Yesu ananeneratu kuti ophunzira ake adzachita ntchito zazikulu kuposa zake. (Werengani Yohane 14:12.) Sankatanthauza kuti tidzachita zozizwitsa ngati mmene iye ankachitira. Koma ankatanthauza kuti ophunzira ake adzalalikira komanso kuphunzitsa anthu ambiri, m’dera lalikulu komanso kwa nthawi yaitali kuposa iye.

15. Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati? Perekani chifukwa.

15 Ngati mumagwira ntchito, dzifunseni mafunso awa: ‘Kodi kuntchito kwathu anthu amaona kuti ndimagwira ntchito mwakhama? Kodi ndimagwira bwino ntchito komanso kuimaliza pa nthawi yake?’ Ngati mungayankhe kuti inde pa mafunsowa, abwana anu angaone kuti ndinu wodalirika. Zingathandizenso kuti anthu amene amakuonani azichita chidwi ndi uthenga wa Ufumu. Pa nkhani ya ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa, mungadzifunse kuti: ‘Kodi anthu amaona kuti ndine wakhama mu utumiki? Nanga ndimakonzekera bwino kulalikira? Kodi ndimabwerera msanga kwa anthu amene anachita chidwi? Nanga ndimagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zolalikirira?’ Ngati mungayankhe kuti inde pa mafunsowa, ndiye kuti muzigwira ntchitoyi mosangalala.

KODI MAGANIZO ANU NDI OTANI PA NKHANI YOPUMA?

16. Kodi maganizo a Yesu ndi atumwi ake pa nkhani yopuma ndi osiyana bwanji ndi anthu ambiri masiku ano?

16 Yesu ankadziwa kuti nthawi zina iye ndi atumwi ankafunika kupuma. Komabe anthu ambiri pa nthawiyo komanso masiku ano ali ngati munthu wachuma wamufanizo la Yesu. Munthuyo anadziuza kuti: “Ungoti phee tsopano, ndipo udye, umwe ndi kusangalala.” (Luka 12:19; 2 Tim. 3:4) Iye ankaona kuti chofunika kwambiri ndi kupuma komanso kusangalala. Koma Yesu ndi atumwi ake sankaona kuti kuchita zofuna zawo n’kumene kunali kofunika kwambiri.

Kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito ndi kupuma kumathandiza kuti tizichita zinthu zabwino n’kumasangalala (Onani ndime 17) *

17. Kodi tiyenera kugwiritsa ntchito bwanji nthawi yathu yopuma?

17 Tiyenera kutsanzira Yesu pogwiritsa ntchito nthawi yathu yopuma kuti tichitenso zinthu zabwino monga kulalikira ndi kupezeka pamisonkhano. Tiziona kuti kuphunzitsa anthu komanso kupezeka pamisonkhano ndi kofunika kwambiri ndipo tiziyesetsa kuti tisamalephere kuchita zinthuzi. (Aheb. 10:24, 25) Ngakhale titapita kutchuthi, tiziyesetsabe kusonkhana komanso kulalikira anthu amene tingakumane nawo.​—2 Tim. 4:2.

18. Kodi Mfumu yathu Khristu Yesu amafuna kuti tizichita chiyani?

18 Timayamikira kwambiri kuti Mfumu yathu Khristu Yesu ali ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito ndi kupuma ndipo amatithandiza kuti tizichita zomwezo. (Aheb. 4:15) Iye amafuna kuti tizipuma mokwanira. Amafunanso kuti tizigwira ntchito mwakhama kuti tipeze zofunika pa moyo komanso tiziphunzitsa anthu. Munkhani yotsatira, tidzakambirana za udindo wa Yesu potithandiza kuti timasuke ku ukapolo woipa kwambiri.

NYIMBO NA. 38 Mulungu Adzakulimbitsa

^ ndime 5 Malemba amatithandiza kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito komanso kupuma. Nkhaniyi itithandiza kudzifufuza kuti tidziwe mmene timaonera zinthu zimenezi. Ndipo tikambirana pogwiritsa ntchito zimene Aisiraeli ankachita pa Sabata.

^ ndime 10 Ophunzira a Yesu ankalemekeza kwambiri lamulo la Sabata moti anasiya kupanga zonunkhiritsa zoti akonzere thupi la Yesu mpaka tsiku la Sabata litadutsa.​—Luka 23:55, 56.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Yosefe akupita kusunagoge ndi banja lake pa tsiku la Sabata.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Bambo amene amagwira ntchito akuchita zinthu zokhudza kulambira ngakhale pamene ali kutchuthi ndi banja lake.