N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupemphera M’dzina la Yesu?
NTHAWI zambiri Yesu ankaphunzitsa za kupemphera. M’masiku ake, atsogoleri achipembedzo achiyuda ankapemphera “m’mphambano za misewu ikuluikulu.” N’chifukwa chiyani ankachita zimenezi? Ankafuna kuti “anthu aziwaona.” Ndithudi, iwo ankafuna kudzionetsera kuti anali anthu opemphera kwambiri. Ambiri a iwo ankapemphera mapemphero aatali, obwerezabwereza, ngati kuti “mawu ambirimbiri” ndi amene amapangitsa mapemphero kumvedwa. (Mateyo 6:5-8) Yesu ananena poyera kuti khalidwe limeneli n’losafunika, chotero anaphunzitsa anthu oona mtima kuti apewe zimenezi popemphera. Komabe, sikuti anangowaphunzitsa zoti apewe popemphera basi.
Yesu anaphunzitsa kuti mapemphero athu ayenera kusonyeza kuti tikufunitsitsa kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe, Ufumu Wake ubwere ndiponso kuti chifuniro Chake chichitike. Iye anaphunzitsanso kuti n’kofunika kupempha Mulungu kuti atithandize pa zinthu zokhudza moyo wathu. (Mateyo 6:9-13; Luka 11:2-4) Yesu anagwiritsa ntchito fanizo posonyeza kuti popemphera tifunika kulimbikira, kukhala ndi chikhulupiriro ndiponso kudzichepetsa ngati tikufuna kuti mapemphero athu amvedwe. (Luka 11:5-13; 18:1-14) Ndipo Yesu popemphera anasonyeza bwino kwambiri zimene ankaphunzitsazo.—Mateyo 14:23; Maliko 1:35.
Sitikukayikira kuti malangizo amenewa anawathandiza ophunzira a Yesu kuti mapemphero awo akhale abwino. Komabe, Yesu anadikira mpaka usiku wake womaliza padziko lino lapansi kuti aphunzitse ophunzira ake zinthu zofunika kwambiri popemphera.
“Pamene Panasinthira Zinthu Pankhani ya Pemphero”
Yesu anathera nthawi yochuluka pa usiku wake womaliza padziko lino lapansi akulimbikitsa atumwi ake okhulupirika. Imeneyi inali nthawi yoyenera kuwauza kanthu kena katsopano. Yesu anati: “Ine ndine njira ndi choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” Kenako anawalonjeza zinthu zolimbikitsa izi: “Chilichonse chimene mudzapempha m’dzina langa, ndidzachita chimenecho, kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana wake. Ngati mupempha chilichonse m’dzina langa, ndidzachita chimenecho.” Atatsala pang’ono kumaliza kukambiranako, iye anati: “Kufikira nthawi ino simunapemphepo chilichonse m’dzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chisefukire.”—Yohane 14:6, 13, 14; 16:24.
Mawu amenewa anali ofunika kwambiri. Buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo limati “pamenepa m’pamene panasinthira zinthu pankhani ya pemphero.” Yesu sanatanthauze kuti anthu asiye kupemphera kwa Mulungu n’kumapemphera kwa iye. M’malo mwake, iye anali kuwasonyeza njira yatsopano yopempherera kwa Yehova Mulungu.
Kunena zoona Mulungu nthawi zonse amamvetsera mapemphero a atumiki ake okhulupirika. (1 Samueli 1:9-19; Salmo 65:2) Komabe, kuyambira nthawi imene Mulungu anachita pangano ndi Aisiraeli, anthu amene ankafuna kuti Mulungu amve mapemphero awo anayenera kuvomereza kuti Aisiraeli anali mtundu wosankhidwa ndi Mulungu. Kenako, kuyambira nthawi ya Solomo, anafunika kuvomereza kuti kachisi anali malo amene Mulungu anawasankha kuperekerako nsembe. (Deuteronomo 9:29; 2 Mbiri 6:32, 33) Komabe, kulambira mu njira imeneyi kunali kwa kanthawi. Malinga ndi kunena kwa mtumwi Paulo, Chilamulo chimene chinaperekedwa kwa Aisiraeli ndiponso nsembe zimene ankapereka pa kachisi zinali “mthunzi chabe wa zinthu zabwino zimene zikubwera, osati kuti [chinali] ndi zinthu zenizenizo.” (Aheberi 10:1, 2) Mthunziwu unafunika kulowedwa m’malo ndi zinthu zenizeni. (Akolose 2:17) Kuyambira mu 33 C.E., kuti munthu akhale paubwenzi ndi Yehova sizinadalirenso kutsatira Chilamulo cha Mose koma zimadalira kumvera Khristu Yesu, popeza Chilamulocho chinkatsogolera anthu kwa Khristu Yesu.—Yohane 15:14-16; Agalatiya 3:24, 25.
Dzina “Loposa Lina Lililonse”
Yesu anakhazikitsa njira yapadera kwambiri yopempherera kwa Yehova. Ndipo anazitchula kuti ndi bwenzi lamphamvu, limene limatsegula njira kuti Mulungu amve ndi kuyankha mapemphero athu. Kodi n’chiyani chimam’pangitsa Yesu kutichitira zimenezi?
Popeza tonsefe tinabadwa ochimwa, zimene timachita ndiponso nsembe zimene timapereka sizingachotse machimo amenewa kapena kutipangitsa kukhala paubwenzi ndi Mulungu wathu woyera, Yehova. (Aroma 3:20, 24; Aheberi 1:3, 4) Komatu, Yesu anapereka moyo wake wangwiro kuwombola anthu amene angafune kukhala paubwenzi ndi Mulungu. (Aroma 5:12, 18, 19) Choncho anthu onse amene akufuna kuti machimo awo akhululukidwe ali ndi mwayi wokhala paubwenzi wabwino ndi Yehova ndiponso kusangalala ndi ‘ufulu wa kulankhula’ ndi Mulungu. Koma izi n’zotheka pokhapokha ngati munthu amasonyeza chikhulupiriro mu nsembe ya Yesu ndiponso ngati amapemphera m’dzina lake.—Aefeso 3:11, 12.
Tikamapemphera m’dzina la Yesu timakhala tikusonyeza chikhulupiriro choti iye amakwaniritsa chifuniro cha Mulungu m’njira zitatu izi: (1) Iye ndi “Mwanawankhosa wa Mulungu,” amene nsembe yake imachititsa kuti machimo athu akhululukidwe. (2) Anaukitsidwa ndi Yehova ndipo tsopano ndi “mkulu wa ansembe” amene akutithandiza kuti tipindule ndi dipo. (3) Ndi iye yekha amene ali “njira” yofikira kwa Yehova m’pemphero.—Yohane 1:29; 14:6; Aheberi 4:14, 15.
Tikamapemphera m’dzina la Yesu timasonyeza kuti timamulemekeza. Iye ayeneradi kulemekezedwa popeza chifuniro cha Yehova n’chakuti “m’dzina la Yesu, onse apinde maondo awo, . . . aliyense avomereze poyera ndi lilime lake kuti Yesu Khristu ndiye Ambuye, polemekeza Mulungu Atate.” (Afilipi 2:10, 11) Komabe, chofunika kwambiri tikamapemphera m’dzina la Yesu n’chakuti timalemekeza Yehova, amene anapereka Mwana wake kuti zinthu zitiyendere bwino.—Yohane 3:16.
Pofuna kuti timvetse kukula kwa udindo wa Yesu, Baibulo limagwiritsa ntchito mawu osiyanasiyana omulemekezera. Zimenezi zimatithandiza kuzindikira madalitso ambiri amene timapeza chifukwa cha zimene Yesu anatichitira, akutichitira ndiponso adzatichitire. (Onani bokosi la mutu wakuti “ Udindo Wofunika wa Yesu”.) Ndithudi, Yesu anapatsidwa “dzina loposa lina lililonse.” a Ulamuliro wonse kumwamba ndi padziko lapansi unapatsidwa kwa iye.—Afilipi 2:9; Mateyo 28:18.
Usakhale Mwambo Chabe
Inde, tiyenera kupemphera m’dzina la Yesu ngati tikufuna kuti Yehova amve mapemphero athuwo. (Yohane 14:13, 14) Koma sitikufuna kuti tizibwereza mawu akuti “m’dzina la Yesu” chifukwa chakuti tinazolowera. Chifukwa chiyani?
Taonani chitsanzo ichi. Mukalandira kalata, kawirikawiri imatha ndi mawu akuti “nditha ine wanu.” Kodi mukuganiza kuti mawu amenewa amasonyeza maganizo a munthu wolemba kalatayo, kapena wangolemba chifukwa choti anthu anazolowera kulemba mawu amenewa? Zoonadi, tizigwiritsa ntchito dzina la Yesu popemphera mwatanthauzo osati ngati mawu akumapeto kwa kalata aja. Ngakhale kuti tifunika ‘kupemphera mosalekeza,’ tichite zimenezi ‘ndi mtima wathu wonse,’ osati mwamwambo chabe.—1 Atesalonika 5:17; Salmo 119:145.
Kodi inuyo mungapewe bwanji kugwiritsa ntchito mawu akuti “m’dzina la Yesu” mwamwambo chabe? Bwanji osaganizira kaye makhalidwe abwino a Yesu? Ganizirani zimene wakuchitirani kale ndi zimene akufuna kukuchitirani. Popemphera, thokozani Yehova ndi kum’tamanda chifukwa cha mmene wagwiritsira ntchito Mwana wake. Mukachita zimenezi, mudzaona kuti lonjezo la Yesu ili n’lodalirika kwambiri: “Ngati mupempha chilichonse kwa Atate m’dzina langa adzakupatsani.”—Yohane 16:23.
a Malinga ndi buku lina (Vine’s Expository Dictionary of New Testament Words), mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “dzina” angatanthauze “zimene dzinalo limaimira, udindo, makhalidwe apadera, ulamuliro, mphamvu, [ndi] ulemerero.”
Tizipemphera ndi mtima wathu wonse, osati mwamwambo chabe