NKHANI YA PACHIKUTO | MABODZA OMWE AMALEPHERETSA ANTHU KUKONDA MULUNGU

Bodza Lachitatu: Mulungu ndi Wankhanza

Bodza Lachitatu: Mulungu ndi Wankhanza

ZIMENE ANTHU AMBIRI AMAKHULUPIRIRA

Buku lina limanena kuti: “Munthu wochimwa akafa, nthawi yomweyo mzimu wake umakawotchedwa kumoto komwe umakazunzidwa kwamuyaya.” (Catechism of the Catholic Church) Atsogoleri ena azipembedzo amanena kuti Mulungu amaona kuti anthu amene amakawotchedwa kumoto ndi osafunika.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limanena kuti: “Moyo umene ukuchimwawo ndi umene udzafe.” (Ezekieli 18:4) Ndipo limanenanso kuti: “Akufa sadziwa chilichonse.” (Mlaliki 9:5) Ndiye ngati moyo umafa ndipo akufa sadziwa chilichonse, zingatheke bwanji kuti akufa azizunzidwa kumoto kwamuyaya n’kumamva kupweteka mpaka kalekale?

N’zoona kuti Baibulo limanena za “nyanja yamoto ndi sulufule.” (Chivumbulutso 20:10) Komabe Baibulo limatithandizanso kudziwa tanthauzo la mawu amenewa. Chifukwa limati: “Nyanja yamoto imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.” (Chivumbulutso 20:14; 21:8) Choncho, zimenezi zikutanthauza kuti nyanjayo si yeniyeni komanso motowo si weniweni. Mawu akuti ‘kuzunzidwa kwamuyaya’ m’nyanja yamoto, akutanthauza “imfa yachiwiri” imene palibe chiyembekezo choti munthuyo adzaukitsidwa.

CHIFUKWA CHAKE KUDZIWA ZIMENEZI N’KOFUNIKA

Nkhanza sizingatipangitse kukonda Mulungu koma zingapangitse kuti tizichita naye mantha. Mayi wina, dzina lake ndi Rocío amene amakhala ku Mexico, anati: “Kungoyambira ndili mwana, ndinkaphunzitsidwa zakuti anthu amakawotchedwa kumoto. Ndinkachita mantha kwambiri ndipo ndinkaona kuti Mulungu si wabwino ngakhale pang’ono. Ndinkamuonanso kuti ndi waukali komanso wovuta.”

Koma Rocío ataphunzira m’Baibulo zoti Mulungu sawotcha anthu kumoto komanso amaweruza mwachilungamo anasinthiratu mmene ankaonera Mulungu. Iye anati: “Ndinayamba kuona kuti ndamasuka tsopano. Ndinayamba kuona kuti Mulungu amatifunira zabwino, amatikonda, komanso kuti tikhoza kumukonda. Iye ali ngati bambo yemwe wagwira dzanja mwana wake chifukwa chakuti amamukonda.”—Yesaya 41:13.

Anthu ambiri amakakamizika kukonda Mulungu chifukwa choopa kuti adzawotchedwa kumoto. Koma Mulungu safuna kuti tizimutumikira chifukwa cha mantha. Yesu anati: “Uzikonda Yehova Mulungu wako.” (Maliko 12:29, 30) Komanso, kudziwa kuti Mulungu amachita zinthu mwachilungamo masiku ano, kungatithandize kukhala ndi chikhulupiriro chakuti kutsogoloku adzaweruzanso mwachilungamo. Izi n’zogwirizana ndi zimene Elihu, bwenzi la Yobu, ananena. Iye anati: “Mulungu woona sangachite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuyonse sangachite zinthu zopanda chilungamo ngakhale pang’ono.”—Yobu 34:10.