“Mpaka pano sitinagwirizanebe ngati kuli koyenera kutchula dzina la Mulungu. Ndipo ngakhale titatero, dzina la Mulungulo lingakhale ndani?”—Pulofesa David Cunningham, Theological Studies.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Mulungu anati: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.” (Yesaya 42:8) Yehova ndi dzina lochokera ku Chiheberi ndipo limatanthauza kuti “Iye Amachititsa Kukhala.”—Onani Baibulo la Dziko Latsopano,Zakumapeto 1.
Yehova amafuna kuti tizitchula dzina lake. Baibulo limati: “Itanani pa dzina lake. Dziwitsani mitundu ya anthu zochita zake. Nenani kuti dzina lake n’lokwezeka.”—Yesaya 12:4.
Yesu ankatchula dzina la Mulungu. Iye anapemphera kwa Mulungu kuti: “Ine ndachititsa kuti iwo [ophunzira a Yesu] adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzinalo.” N’chifukwa chiyani Yesu anadziwitsa ophunzira ake dzina la Mulungu? Iye anapitiriza kunena kuti: “Kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, inenso ndikhale wogwirizana ndi iwo.”—Yohane 17:26.
CHIFUKWA CHAKE KUDZIWA DZINA LA MULUNGU N’KOFUNIKA
Katswiri wina wamaphunziro azachipembedzo, dzina lake Walter Lowrie, anati: “Munthu amene amaganiza kuti Mulungu ndi mphamvu chabe ndipo sadziwa dzina lake, ndiye kuti sadziwa Mulungu, ndipo munthu wotereyu sangamukonde Mulunguyo.”
Munthu wina, dzina lake Victor, ankapita kutchalitchi mlungu uliwonse koma sankadziwa kuti Mulungu ndi wotani kwenikweni. Iye anati: “Kenako ndinaphunzira kuti dzina la Mulungu ndi Yehova ndipo aka kanali koyamba kuti ndimudziwe. Zinali ngati ndakumana koyamba ndi munthu amene ndinkangomva zambiri za iye. Ndinayamba kuona kuti Mulungu ndi weniweni ndipo ndinakhala naye pa ubwenzi.”
Yehova nayenso amafuna kukhala pa ubwenzi ndi anthu amene amatchula dzina lake. Mulungu amalonjeza anthu amene ‘amaganizira za dzina lake’ kuti: “Ndidzawachitira chifundo monga mmene munthu amachitira chifundo mwana wake amene amamutumikira.” (Malaki 3:16, 17) Mulungu amadalitsanso anthu amene amaitanira pa dzina lake. Baibulo limati: “Aliyense amene adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”—Aroma 10:13.