BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinapeza Mayankho Ogwira Mtima a Mafunso Anga

Ndinapeza Mayankho Ogwira Mtima a Mafunso Anga
  • CHAKA CHOBADWA: 1948

  • DZIKO: HUNGARY

  • POYAMBA: NDINKAFUNITSITSA KUPEZA MAYANKHO A MAFUNSO ANGA

KALE LANGA:

Ndinabadwira mumzinda wa Székesfehérvár m’dziko la Hungary. Mzindawu uli ndi mbiri yochititsa chidwi ya zinthu zomwe zakhala zikuchitika kuyambira chisanafike chaka cha 1014. Komabe ndimamva chisoni ndikakumbukira zinthu zoopsa zomwe zinachitika pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse.

Ndili mwana, ndinkakhala ndi agogo anga akuchikazi. Anali anthu abwino kwambiri moti ndimakumbukirabe zimene ankachita, makamaka agogo aakazi omwe dzina lawo anali a Elisabeth. Agogo aakaziwa anandiphunzitsa kuti ndizikhulupirira Mulungu. Kuyambira ndili ndi zaka zitatu, madzulo alionse ine ndi iwowo tinkapemphera pemphero la Ambuye. Koma pa nthawiyi sindinkamvetsa tanthauzo la pempheroli.

Ndinkakhala ndi agogo chifukwa choti makolo anga ankagwira ntchito masana ndi usiku womwe. Ankachita zimenezi n’cholinga chofuna kupeza ndalama zogulira nyumba yabwino. Komabe pakatha milungu iwiri iliyonse tinkakumana Loweruka ndipo tinkadyera limodzi chakudya. Nthawi imeneyi inkakhala yosangalatsa kwambiri.

Mu 1958, makolo anga anaguladi nyumba imene ankafuna ija. Zitatere, ndinasamuka kwa agogo n’kuyamba kukhala ndi makolo anga. Apa ndinasangalala kwambiri. Koma chisangalalochi sichinakhalitse chifukwa patangotha miyezi 6, bambo anamwalira ndi khansa.

Ndinakhumudwa kwambiri ndi zimenezi. Ndinapemphera kwa Mulungu kuti: “Ndinakupemphani kuti muwathandize bambo anga kuti asamwalire. Ndikuwafuna kwambiri kuti ndizikhala nawo. N’chifukwa chiyani simunayankhe pemphero langa?” Ndinkafunitsitsa nditadziwa kumene bambo anga apita. Ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi apita kumwamba? Kodi zateremu ndiye kuti sindidzawaonanso?’ Ndinkasirira ndikaona ana omwe ali ndi bambo awo.

Pafupifupi tsiku lililonse, ndinkapita kumanda komwe bambo anaikidwa. Ndinkagwada pamanda awo n’kupemphera kuti: “Chonde Mulungu ndithandizeni kudziwa komwe kuli bambo anga.” Ndinkapemphanso Mulungu kuti andithandize kudziwa chifukwa chimene analengera anthufe.

Ndili ndi zaka 13, ndinayamba kuphunzira Chijeremani. Ndinkaganiza kuti popeza pali mabuku ambiri achijeremani, ndingathe kupezamo mayankho a mafunso anga. Mu 1967, ndinapita ku Germany ndipo ndinayamba kuphunzira mumzinda wa Jena, womwe pa nthawiyo unali mbali ya East Germany. Ndinkakonda kuwerenga mabuku a akatswiri a ku Germany a nzeru za anthu, makamaka ofotokoza zokhudza moyo wa anthu. Ngakhale kuti ndinkapezamo mfundo zosiyanasiyana, sindinapeze mayankho ogwira mtima a mafunso anga. Choncho ndinapitirizabe kupempha Mulungu kuti andithandize.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Mu 1970, ndinabwereranso ku Hungary. Ndili kumeneko, ndinakumana ndi mtsikana wina, dzina lake Rose, ndipo kenako tinakwatirana. Pa nthawiyi, n’kuti dziko la Hungary lili pansi pa ulamuliro wachikomyunizimu. Pasanathe nthawi yaitali, ine ndi Rose tinasamukira ku Austria. Tinkafuna kuti tidzapite mumzinda wa Sydney m’dziko la Australia, komwe kunkakhala amalume anga.

Tili ku Austria, ndinapeza ntchito. Tsiku lina mnzanga wakuntchito anandiuza kuti Baibulo lingayankhe mafunso anga onse. Anandipatsa mabuku angapo othandiza kuphunzira Baibulo omwe amafalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Nthawi yomweyo ndinawerenga mabuku onsewo n’kuwamaliza. Komabe ndinkafuna kudziwa zambiri. Choncho ndinalembera a Mboni kuti anditumizire ena.

Pa tsiku lomwe tinkakumbukira kuti tatha chaka tili m’banja, kunyumba kwathu kunabwera mnyamata wina wa Mboni za Yehova. Anandibweretsera mabuku aja n’kundipempha kuti azindiphunzitsa Baibulo ndipo ndinavomera. Chifukwa choti ndinkafuna kudziwa zambiri, ndinkaphunzira kawiri pa mlungu kwa maola 4.

Ndinasangalala kwambiri ndi mfundo za m’Baibulo zomwe a Mboni ankandiphunzitsa. Atandionetsa dzina la Mulungu lakuti Yehova m’Baibulo langa lachihangare, ndinadabwa kwambiri. Kwa zaka 27 zomwe ndinkapita kutchalitchi kwathu, ndinali ndisanamvepo kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Zinandidabwitsa kuona kuti, kuchokera m’Baibulo ndinapeza mayankho ogwira mtima komanso omveka bwino a mafunso anga aja. Mwachitsanzo, ndinaphunzira kuti akufa sadziwa chilichonse ndipo ali ngati akugona tulo tofa nato. (Mlaliki 9:5, 10; Yohane 11:11-15) Ndinaphunziranso za lonjezo la m’Baibulo lonena za dziko latsopano, limene simudzakhalanso imfa. (Chivumbulutso 21:3, 4) Ndikuyembekezera kudzaonananso ndi bambo anga pa nthawiyi chifukwa “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”​—Machitidwe 24:15.

Nayenso Rose anayamba kuphunzira Baibulo ndipo tinkaphunzirira limodzi. Ankasangalalanso kwambiri ndi zomwe ankaphunzira moti patangotha miyezi iwiri, tinamaliza buku lomwe linkaphunzira. Tinkapitanso kukasonkhana ndi a Mboni za Yehova ku Nyumba ya Ufumu. Tinachita chidwi kwambiri kuona kuti a Mboni amakondana, amathandizana komanso ndi ogwirizana kwambiri.​—Yohane 13:34, 35.

Mu 1976 ine ndi mkazi wanga tinasamukira ku Australia. Titangofika kumeneko tinafufuza a Mboni za Yehova n’kuwapeza. Anatilandira bwino ndipo mu 1978 tinabatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Ndinapeza mayankho a mafunso omwe kwa nthawi yaitali ankandizunguza mutu. Kuphunzira za Yehova kwandithandiza kuti ndiyambe kumukonda kwambiri komanso kumuona kuti ndi Atate wanga wachikondi. (Yakobo 4:8) Komanso ndimasangalala kwambiri chifukwa chodziwa kuti m’dziko latsopano ndidzawaonanso bambo anga.​—Yohane 5:28, 29.

Mu 1989 tinabwereranso ku Hungary kuti tikauze achibale, anzathu komanso anthu ena za zinthu zomwe taphunzira m’Baibulo. Tathandiza anthu 70 kudziwa zomwe Baibulo limaphunzitsa n’kuyamba kutumikira Yehova. Mmodzi wa anthuwa ndi mayi anga.

Kwa zaka 17 ndinkapemphera kuti ndipeze mayankho a mafunso anga. Tsopano patha zaka 39 Yehova atayankha pemphero langali. Panopa ndimapempherabe ndipo ndimathokoza Yehova chifukwa choyankha zomwe ndinkamupempha kuyambira ndili mwana.