NKHANI YA PACHIKUTO | BAIBULO​—BUKU LOMWE LINAPULUMUKA M’ZAMBIRI

Kodi Kudziwa Mmene Baibulo Linapulumukira N’kothandiza?

Kodi Kudziwa Mmene Baibulo Linapulumukira N’kothandiza?

Palibe buku lina lililonse la chipembedzo lomwe lingapose Baibulo, chifukwa lakhala likuthandiza anthu kuti azikhulupirira zinthu zolondola. Komanso ndi buku lokhalo limene anthu alifufuza kwambiri ndiponso kulipezera zifukwa.

Akatswiri ena amakaikira ngati uthenga wa m’Mabaibulo a masiku ano ulidi wofanana ndi womwe unali m’mipukutu yoyambirira. Mwachitsanzo, pulofesa wina wamaphunziro azachipembedzo ananena kuti: “Sitinganene motsimikiza kuti tinakoperadi uthenga wa m’Baibulo molondola chifukwa Mabaibulo ambiri ali ndi zinthu zolakwika zokhazokha. Komanso analembedwa patadutsa zaka zambiri kuchokera pamene mipukutu yoyambirira inalembedwa, choncho uthenga wake ndi wosiyana kwambiri ndi womwe unali m’mipukutuyi.”

Anthu enanso amakhulupirira kuti uthenga wa m’Baibulo unasinthidwa chifukwa ndi zomwe anaphunzitsidwa kuzipembedzo zawo. Mwachitsanzo Faizal, anauzidwa ndi anthu a m’banja lake omwe si Akhristu, kuti Baibulo ndi buku lopatulika koma linasinthidwa. Iye anati: “Chifukwa cha zimenezi, anthu akamandifotokozera zokhudza Baibulo ndinkakayikira kwambiri uthenga wake. Ndinkaona kuti si lolondola chifukwa linasinthidwa.”

Kodi kudziwa ngati Baibulo linasinthidwa kapena ayi kuli ndi phindu lililonse? Kuti mupeze yankho la funsoli, taganizirani mafunso awa: Kodi zikanakhala kuti zinthu zabwino zimene Baibulo limalonjeza sizinalembedwe m’mipukutu yoyambirira, mukanazikhulupirira? (Aroma 15:4) Zikanakhala kuti mfundo zonse za m’Mabaibulo a masiku ano ndi zolakwika, kodi mukanazigwiritsa ntchito posankha zochita pa nkhani zokhudza ntchito, banja kapena kupembedza Mulungu?

Ngakhale kuti mipukutu yoyambirira ya Baibulo sikupezeka, pali zolemba zina zakale komanso mipukutu ina yambiri ya Baibulo imene imatithandiza. Kodi zinatheka bwanji kuti mipukutuyi izipezekabe masiku ano? Funsoli ndi lofunika chifukwa anthu ena ankafuna kuithetseratu, kusintha uthenga wake komanso ikanatha kuwola. Kodi kupezeka kwa mipukutuyi kungakuthandizeni bwanji kukhulupirira kuti uthenga wa m’Baibulo ndi wolondola? Kuti mudziwe mayankho a mafunsowa, werengani nkhani zokhudza mmene Baibulo linapulumukira ku zinthu zonsezi.