BAIBULO LIMASINTHA ANTHU
Sindinkafuna Kufa
Yofotokozedwa ndi Yvonne Quarrie
-
CHAKA CHOBADWA: 1964
-
DZIKO: ENGLAND
-
POYAMBA: NDINAKHALA MAYI NDILI WAMNG’ONO
KALE LANGA
Ndinabadwira ku Paddington, mumzinda wa London ku England. M’derali munkakhala anthu ambiri. Ndinkakhala ndi mayi anga komanso azichemwali anga atatu. Bambo anga anali chidakwa ndipo nthawi zambiri sankapezeka pakhomo.
Ndili mwana, mayi anga anandiphunzitsa kuti ndizipemphera usiku uliwonse. Ndinali ndi Baibulo longokhala ndi buku la Masalimo lokha ndipo ndinkakonda kuimba mawu a m’masalimowo. Nthawi ina ndinawerenga mawu m’buku linalake omwe sindidzawaiwala akuti: “Padzakhala tsiku lina lomwe silidzakhala ndi mawa lake.” Mawuwa anandichititsa kuti ndizivutika kugona chifukwa choganizira kwambiri zam’tsogolo. Ndinkaona kuti moyo sunayenera kukhala chonchi. Ndinkakhulupirira kuti Mulungu anali ndi cholinga pondilenga ndipo sindinkafuna kufa.
Ndinayamba kuchita chidwi ndi zinthu zamatsenga. Ndinkayesa kulankhula ndi anthu akufa, ndinkapita kumanda osiyanasiyana ndi anzanga a kusukulu ndiponso tinkakonda kuonera mafilimu oopsa. Tinkaona kuti zimenezi ndi zosangalatsa ngakhale kuti zinali zochititsa mantha.
Ndinayamba kuchita zinthu zosokonekera ndili ndi zaka 10 zokha. Ndinayamba kusuta fodya kwambiri ndipo kenako ndinayambanso kusuta chamba. Mmene ndinkafika zaka 11 n’kuti nditayamba kumwa mowa. Ngakhale kuti sunkandikomera, kuledzera kunkandisangalatsa. Ndinkakondanso nyimbo komanso kuvina. Ndikakhala ndi mpata, ndinkapita kukamwa mowa kumabala komanso kumalo ena. Usiku ndinkakonda kuchoka kunyumba mozemba n’kubwera m’bandakucha. Zimenezi zinkachititsa kuti nthawi zambiri ndizijomba ku sukulu chifukwa chotopa. Koma ndikapitako ndinkakonda kumwa mowa pa buleki.
Chaka chomaliza ku sukulu sindinakhoze bwino mayeso. Mayi anga anakwiya ndi zimenezi chifukwa m’pamene anazindikira kuti ndinali nditalowerera kwambiri. Tinakangana kwambiri ndipo kenako ndinangochoka pakhomopo. Kwa kanthawi, ndinapita kukakhala ndi chibwenzi changa dzina lake Tony, yemwe anali Rasi. Iye anali wakuba komanso ankagulitsa mankhwala osokoneza bongo. Ankadziwikanso kuti anali wokonda ndewu. Pasanapite nthawi, ndinapezeka kuti ndili ndi mimba ndipo ndinabereka mwana wamwamuna ndili ndi zaka 16 zokha.
MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA
Anthu ena ogwira ntchito m’boma anandithandiza kupeza malo kunyumba yosungira atsikana osakwatiwa amene anali ndi ana. Kumeneko n’kumene ndinakumana koyamba ndi a Mboni za Yehova. Panali azimayi awiri a Mboni amene ankakonda kubwera kudzacheza ndi atsikana ena. Tsiku lina nanenso ndinacheza nawo. Ndinkafuna kuwasonyeza kuti zimene ankanena si zoona. Koma anayankha modekha komanso momveka bwino mafunso anga onse pogwiritsa ntchito Baibulo. Anandisangalatsa kwambiri chifukwa anali okoma mtima komanso ofatsa moti ndinavomera kuti azindiphunzitsa Baibulo.
Ndinaphunzira mfundo ina m’Baibulo yomwe inandikhudza kwambiri. Kuyambira ndili mwana, ndinkaopa kufa. Koma pa nthawiyi, ndinaphunzira zimene Yesu ananena zoti akufa adzauka. (Yohane 5:28, 29) Ndinaphunziranso kuti Mulungu amandikonda kwambiri. (1 Petulo 5:7) Mawu amene anandifika pamtima kwambiri ndi amene ali pa Yeremiya 29:11 omwe amati: “‘Maganizo anga kwa inu ndikuwadziwa bwino. Ndikuganizira zokupatsani mtendere osati masoka, kuti mukhale ndi chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino,’ watero Yehova.” Ndinayamba kukhulupirira kuti ndikhoza kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansili.—Salimo 37:29.
A Mboni za Yehova ankandikonda kwambiri. Nditapita koyamba kumisonkhano yawo, ndinaona kuti aliyense anali womasuka komanso wochezeka. (Yohane 13:34, 35) Zimenezi zinali zosiyana kwambiri ndi zomwe zinkachitika kutchalitchi komwe ndinapita nthawi ina. A Mboni za Yehova anandilandira bwino ngakhale kuti makhalidwe anga sanali abwino. Ankacheza nane ndiponso kundithandiza kwambiri moti ndinkaona kuti ndi abale anga enieni ndipo amandikonda kwambiri.
Nditayamba kuphunzira Baibulo, ndinazindikira kuti ndinkayenera kusintha makhalidwe anga kuti ndizisangalatsa Yehova. Koma sizinali zophweka kuti ndisiye kusuta fodya. Ndinaonanso kuti nyimbo zina zinkandipangitsa kukhala ndi chilakolako chosuta chamba, choncho ndinasiya kuzimvetsera. Ndinasiyanso kupita kumabala ndiponso kumalo azisangalalo n’cholinga choti ndisiye kuledzera. Ndinapezanso anzanga atsopano amene ankandithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino.—Miyambo 13:20.
Tony anali atayambanso kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Iye anaonanso kuti zimene ankaphunzira ndi zoona chifukwa ankamuyankha mafunso ake pogwiritsa ntchito Baibulo. Tony anasintha kwambiri khalidwe lake. Anasiya kuba, kusuta chamba komanso kucheza ndi anzake okonda ndewu. Kuti tisangalatse Yehova, tinaonanso kuti tiyenera kukwatirana mwadongosolo n’kumayesetsa kulera bwino mwana wathu. Choncho mu 1982, tinakwatirana.
“Panopa sindisowa tulo chifukwa choopa imfa kapena zimene zidzachitike m’tsogolo”
Ndimakumbukira kuti ndinkafufuza nkhani mu Nsanja ya Olonda komanso Galamukani! * za anthu amene anakwanitsa kusintha khalidwe lawo. Zimenezi zinandilimbikitsa kwambiri ndipo zinandipatsa mphamvu kuti ndiyesetse kusintha khalidwe langa. Ndinkapemphera kwa Yehova kuti asasiye kundithandiza. Ine ndi Tony tinabatizidwa mu July 1982 n’kukhala a Mboni za Yehova.
PHINDU LIMENE NDAPEZA
Kukhala pa ubwenzi ndi Yehova Mulungu kunapulumutsa moyo wanga. Ineyo ndi Tony taona Yehova akutithandiza kwambiri pa mavuto athu. Izi zatithandiza kumadalira kwambiri Yehova chifukwa taona kuti nthawi zonse amathandiza banja lathu.—Salimo 55:22.
Ndinkasangalala kwambiri ndikamaphunzitsa ana athu awiri za Yehova. Panopa ndimasangalala kuti nawonso akuthandiza ana awo kuphunzira za Mulungu.
Panopa sindisowa tulo chifukwa choopa imfa kapena zimene zidzachitike m’tsogolo. Mlungu uliwonse ine ndi Tony timayendera mipingo ya Mboni za Yehova kuti tizilimbikitsa Akhristu anzathu. Timagwira nawo limodzi ntchito yophunzitsa anthu ena kuti ngati atamakhulupirira Yesu, nawonso akhoza kudzapeza moyo wosatha.
^ ndime 19 Magaziniwa amafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi
ZOKHUDZA IFEYO
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo—Vidiyo Yathunthu
Baibulo likuthandiza anthu ambirimbiri padziko lonse lapansi kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri. Kodi inunso mungakonde?
KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO
Kodi Cholinga cha Moyo N’chiyani?
Kodi munayamba mwaganizirapo funso lakuti, ‘Kodi cholinga cha moyo n’chiyani?’ Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi.
KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO
Kodi Yehova Ndi Ndani?
Kodi iye ndi Mulungu wa mtundu umodzi wa anthu ngati Aisiraeli?
NSANJA YA OLONDA