Mfundo za M’Baibulo Sizikalamba

Mfundo za M’Baibulo Sizikalamba

TAYEREKEZERANI IZI: Mwapita kukaona malo kumalo osungirako zinthu zakale. Zipilala zambiri zimene mwaona kumaloko ndi zoswekasweka komanso zogumuka. Zina ndi zoti zinangotsala mbali imodzi, kwina kunachoka. Koma kenako mukuona chipilala china choti sichinawonongeke paliponse. Podabwa ndi zimenezi, mukufunsa munthu amene akukutsogoleraniyo kuti: “Kodi ichi si chakale kwambiri ngati zinazi?” Koma akuyankha kuti: “Ayi. Ndipotu chimenechi ndiye chakale kwambiri kuposa zipilala zambiri zimene mwaonazi komanso chiyambire sichinakonzedwepo.” Inu mukufunsanso kuti: “Kapena m’mbuyo monsemu chinkasungidwa muchinachake?” Wokutsogoleraniyo akuyankha kuti: “Ayi. Chipilala chimenechi chakhala chikuvumbidwa ndi mvula komanso kuwombedwa ndi mphepo yamphamvu. Komanso akuba akhala akufuna kuchiwononga.” Mwina mungayambe kudzifunsa kuti, ‘Kodi chipilala cholimba chonchichi chinapangidwa ndi chiyani?’

Baibulo lili ngati chipilala chimenechi. Linalembedwa kalekale kuposa mabuku ambiri amene alipo masiku ano. N’zoona kuti pali mabuku ena akale, koma mofanana ndi zipilala zambiri zakale, mabuku amenewa anawonongeka n’kupita kwa nthawi. Mwachitsanzo, mabuku ambiri akalewa anangotsala zidutswa zokhazokha, mbali zina zinasowa kapena kuwonongeka. Komanso zimene mabukuwa amanena zokhudza sayansi, patapita nthawi zinaoneka kuti si zoona chifukwa cha zimene asayansi anatulukira. Ndipotu malangizo a zaumoyo amene ali m’mabukuwa ndi oti akhoza kutipweteketsa.

Koma Baibulo ndi losiyana kwambiri ndi mabuku amenewa. Linayamba kulembedwa zaka zoposa 3,500 zapitazo koma lidakali lonse ndipo uthenga wake sunasinthe. Izi zili choncho ngakhale kuti kwa zaka zambiri anthu akhala akuwotcha Baibulo, kuletsa kuti lisamafalitsidwe komanso kunyoza zimene limanena. Ndipo zimene anthu akhala akuzitulukira sizitsutsana ndi zimene Baibulo linanena kalekale. Pali zinthu zambiri zimene zimasonyeza kuti Baibulo linanena zinthu molondola anthu ambiri asanazitulukire.​—Onani bokosi lakuti, “Kodi Ndi Lachikale Kapena Limanena Zinthu Zoti Ena Sanazitulukire?

MFUNDO ZOTHANDIZA MASIKU ANO

Koma mwina mungafunse kuti, ‘Kodi zimene Baibulo limanena n’zothandizadi masiku ano?’ Kuti mupeze yankho, dzifunseni kuti, ‘Kodi mavuto aakulu amene anthu akukumana nawo masiku ano ndi ati? Nanga kodi anthu ambiri amadera nkhawa za chiyani?’ Mwina mungaganize za nkhondo, kuwononga chilengedwe, uchigawenga kapena katangale. Tiyeni tikambirane mfundo za m’Baibulo zimene zingathandize pa nkhani zimenezi. Tikamakambirana muzidzifunsa kuti, ‘Kodi zinthu zikanakhala bwanji padzikoli akanakhala kuti anthu amatsatira mfundo zimenezi?’

KUKONDA MTENDERE

“Odala ndi anthu amene amabweretsa mtendere, chifukwa adzatchedwa ‘ana a Mulungu.’” (Mateyu 5:9) “Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.”​—Aroma 12:18.

CHIFUNDO NDIPONSO KUKHULULUKA

“Odala ndi anthu achifundo, chifukwa adzachitiridwa chifundo.” (Mateyu 5:7) “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova * anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.”​—Akolose 3:13.

KUGWIRIZANA NDI ANTHU AMITUNDU INA

“Kuchokera mwa munthu mmodzi [Mulungu] anapanga mtundu wonse wa anthu, kuti akhale padziko lonse lapansi.” (Machitidwe 17:26) “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”​—Machitidwe 10:34, 35.

KUWONONGA ZINTHU ZACHILENGEDWE

“Yehova Mulungu anatenga munthu uja n’kumuika m’munda wa Edeni kuti aziulima ndi kuusamalira.” (Genesis 2:15) Mulungu adzawononga “amene akuwononga dziko lapansi.”​—Chivumbulutso 11:18.

KUDANA NDI DYERA KOMANSO CHIWEREWERE

“Chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse, chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) “Dama ndi chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo zisatchulidwe n’komwe pakati panu, monga mmene anthu oyera amayenera kuchitira.”​—Aefeso 5:3.

KUCHITA ZINTHU MWACHILUNGAMO NDIPONSO KUGWIRA NTCHITO MOLIMBIKA

“Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.” (Aheberi 13:18) “Wakubayo asabenso, koma agwire ntchito molimbikira.”​—Aefeso 4:28.

UBWINO WOTHANDIZA ANTHU OVUTIKA

“Lankhulani molimbikitsa kwa amtima wachisoni, thandizani ofooka, khalani oleza mtima kwa onse.” (1 Atesalonika 5:14) ‘Muzisamalira ana amasiye ndi akazi amasiye m’masautso awo.’​—Yakobo 1:27.

Sikuti Baibulo limangotchula mfundo zimenezi. Limatiphunzitsanso zimene tingachite kuti tizitsatira mfundozi pa moyo wathu. Zikanakhala kuti anthu ambiri amatsatira zimene Baibulo limaphunzitsazi, si bwenzi padzikoli pali mavuto ambiri chonchi. Mfundo za m’Baibulo ndi zofunika komanso ndi zothandiza kwambiri masiku ano. Koma kodi mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni bwanji inuyo?

KODI MFUNDO ZA M’BAIBULO ZINGAKUTHANDIZENI BWANJI PANOPA?

Munthu wanzeru kwambiri kuposa onse anati: “Nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha zotsatira zake.” (Luka 7:35) Mwina inunso mukuona kuti zimenezi ndi zoona. Mfundo imadziwika kuti ndi yanzeru kapena ayi ukaigwiritsa ntchito n’kuona zotsatira zake. Ndiye mwina mungaganize kuti: ‘Ngati Baibulo lilidi lothandiza ndiye kuti likhoza kusintha moyo wanga. Nanga kodi lingandithandize bwanji pa mavuto amene ndikukumana nawo panopa?’ Kuti tiyankhe mafunso amenewa, taganizirani chitsanzo ichi:

Mayi wina dzina lake Delphine, * ankaona kuti zinthu zikumuyendera bwino kwambiri pa moyo wake. Koma mwadzidzidzi zinthu zinasintha kwambiri. Mwana wake wamkazi anamwalira, banja lake linatha komanso anakumana ndi mavuto azachuma. Delphine anati: “Ndinasoweratu mtengo wogwira chifukwa ndinalibenso mwana, mwamuna komanso pokhala. Ndinkadziona kuti si inenso munthu ndipo ndilibe tsogolo lililonse.”

Pa nthawiyi ndi pamene Delphine anazindikira kuti mawu a m’Baibulo awa ndi oona, akuti: “Masiku a moyo wathu amangokwana zaka 70, ndipo ngati tili ndi mphamvu yapadera amakwana zaka 80. Koma ngakhale zili choncho, amangodzaza ndi mavuto ndi zopweteka. Pakuti masiku amene timakhala ndi moyo amatha mwamsanga ndipo timachoka mofulumira.”​—Salimo 90:10.

Delphine anaona kuti Baibulo linamuthandiza kwambiri pa nthawi yovutayi. Monga mmene nkhani zitatu zotsatira zikusonyezera, palinso anthu ambiri amene Baibulo linawathandiza pamene ankakumana ndi mavuto. Anthuwa anaona kuti Baibulo lili ngati chipilala chimene chafotokozedwa kumayambiriro kwa nkhaniyi. Baibulo silili ngati mabuku ambiri amene malangizo ake amasiya kugwira ntchito pakapita nthawi. Kodi n’chifukwa chiyani zili chonchi? Kodi n’kutheka kuti ndi chifukwa choti uthenga wake ndi wochokera kwa Mulungu osati kwa anthu?​—1 Atesalonika 2:13.

Mwina inunso mumaona kuti moyo ndi waufupi komanso wodzadza ndi mavuto okhaokha. Koma kodi mukakumana ndi mavuto, mumafufuza kuti thandizo komanso malangizo?

Tiyeni tikambirane njira zitatu zosonyeza kuti Baibulo ndi lothandiza kwambiri pa moyo wathu. Njira zake ndi izi:

  1. Lingakuthandizeni kupewa mavuto.

  2. Kuthetsa mavuto.

  3. Kudziwa zoyenera kuchita pa mavuto amene simungathe kuwathetsa.

Munkhani zotsatira tikambirana mfundo zimenezi.

^ ndime 10 Yehova ndi dzina la Mulungu ndipo limapezeka m’Baibulo.​—Salimo 83:18.

^ ndime 24 Mayina ena asinthidwa munkhaniyi komanso munkhani zitatu zotsatira.