Anthu ambiri amapita kwa anthu amatsenga kuti akawathandize kudziwa zam’tsogolo. Ena amafunsira nzeru kwa okhulupirira nyenyezi ndipo nkhani zokhudza kukhulupirira nyenyezi zimapezeka m’magazini komanso m’manyuzipepala ambiri. Enanso amapita kukaombeza kwa asing’anga kapena anthu amene amanena kuti amatha kudziwa zam’tsogolo pogwiritsa ntchito makadi olosera, manambala kapena mizera ya m’manja mwa munthu.
Kale, anthu ena akafuna kudziwa zam’tsogolo ankakafunsira kwa ansembe aamuna kapena aakazi omwe ankati amanena zinthu zochokera kwa milungu yawo. Mwachitsanzo, ena amati Mfumu Kolosase ya ku Lidiya inatumiza mphatso zamtengo wapatali kwa wansembe wina wa ku Delphi ku Girisi, kuti amuuze zimene zingachitike ngati angakamenyane ndi gulu la nkhondo la Koresi wa ku Perisiya. Wansembeyo anena kuti “ufumu wamphamvu” udzagonjetsedwa ngati Kolosase angapite kukalimbana ndi Koresi. Ndi chidaliro chonse kuti akapambana, Kolosase anapitadi kukamenya nkhondoyo koma ufumu wamphamvu umene unagonjetsedwa unali wake.