KHALANI MASO

Katswiri wa za Umoyo Wachenjeza Kuti Achinyamata Angakumane Ndi Mavuto Pamalo Ochezera a pa Intaneti—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Katswiri wa za Umoyo Wachenjeza Kuti Achinyamata Angakumane Ndi Mavuto Pamalo Ochezera a pa Intaneti—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Pa 23 May 2023, katswiri wa za umoyo ku United States anachenjeza anthu za mavuto amene achinyamata ambiri akukumana nawo akamagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti.

  •   Magazini ina inati: “Ngakhale kuti ana komanso achinyamata ena akhoza kupeza zinthu zothandiza pamalo ochezera a pa intaneti, pali maumboni ambiri osonyeza kuti malowa angathe kuwononga maganizo komanso thanzi lawo.”​—Social Media and Youth Mental Health: The U.S. Surgeon General’s Advisory, 2023.

 Magaziniyi inatchula zinthu zosiyanasiyana zimene ochita kafukufuku anapeza zomwe zikuchititsa kuti pakhale nkhawa imeneyi.

  •   Achinyamata oyambira zaka 12 mpaka 15 “amene amakhala pamalo ochezera a pa intaneti kwa maola oposa atatu pa tsiku, amakhala pa chiopsezo chodwala matenda amaganizo kuwirikiza kawiri kuphatikizapo kusonyeza zizindikiro za matendawa.”

  •   Achinyamata azaka 14 “amene amagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, amalephera kugona, sasangalala ndi mmene amaonekera, amachitiridwa nkhanza za pa intaneti, amadzikayikira komanso amasonyeza zizindikiro zambiri za matenda amaganizo ndipo zimenezi zimachitikira kwambiri atsikana kuposa anyamata.”

 Ndiye makolo angateteze bwanji ana awo kuti asakumane ndi mavuto amenewa? Baibulo limapereka malangizo othandiza pa nkhaniyi.

Zomwe makolo angachite

 Muzichitapo kanthu. Makolo, ganizirani kuopsa kogwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti kenako mungasankhe kuti mwana wanu azigwiritsa ntchito malowa kapena ayi.

 Ngati mwana wanu munamulola kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, muzidziwa mavuto amene angakumane nawo komanso muzidziwa bwino zimene akuchita pa intaneti. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

 Muziteteza mwana wanu ku zinthu zoopsa zomwe zimapezeka pa intaneti. Muziphunzitsa mwana wanu kuzindikira komanso kupewa zinthu zoopsa zomwe zimapezeka pa intaneti.

 Muzimuikira malire. Mwachitsanzo, muzikhazikitsa malamulo okhudza kutalika kwa nthawi imene ayenera kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti.

  •   Mfundo ya m’Baibulo: “Samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru. Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu chifukwa masikuwa ndi oipa.”​—Aefeso 5:15, 16.

  •   Gwiritsani ntchito vidiyo yamakatuni yakuti Muzichita Zinthu Mosamala Mukamacheza ndi Anzanu pa Intaneti pothandiza mwana wanu kuti amvetse chifukwa chake mumafunika kumuikira malire.