KHALANI MASO

Mmene a Mboni za Yehova Amaonera Nkhani ya Kuphedwa kwa Ayuda Ambirimbiri mu Ulamuliro wa Chipani Cha Nazi​—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Mmene a Mboni za Yehova Amaonera Nkhani ya Kuphedwa kwa Ayuda Ambirimbiri mu Ulamuliro wa Chipani Cha Nazi​—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Pa 27 January 2023, anthu ambiri padziko lonse adzachita mwambo wokumbukira kuphedwa kwa Ayuda ambirimbiri mu ulamuliro wa nkhanza wa chipani cha Nazi (International Holocaust Remembrance Day). Tsopano patha zaka zoposa 75 chichitikireni zinthu zoopsazi. Koma mwina mungafunse kuti, n’chifukwa chiyani Mulungu analola kuti zimenezi zichitike?

 Anthu a mtundu wa Chiyuda ndi amene anavutika kwambiri chifukwa cha nkhanza zimenezi ndipo anthu mamiliyoni anaphedwa mwadala. Nkhanzazi sizinakhudze Ayuda okha. Magulu enanso a anthu anazunzidwa komanso kuphedwa. Ena mwa anthuwa anali a Mboni za Yehova omwe anazunzidwa chifukwa cha zimene amakhulupirira m’Baibulo.

“Chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino”

 Anthu ambiri amaopa kuti zinthu zoopsazi zikhoza kudzachitikanso. Komabe chosangalatsa n’chakuti Baibulo limatilonjeza kuti m’tsogolomu zinthu zoopsa ngati zimenezi sizidzachitikanso.

  •   “‘Maganizo anga kwa inu ndikuwadziwa bwino. Ndikuganizira zokupatsani mtendere osati masoka, kuti mukhale ndi chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino,’ watero Yehova.”​—Yeremiya 29:11. a

 Chiyembekezochi chidzakwaniritsidwa pamene Yehova Mulungu adzathetse kuipa konse ndi kubwezeretsa zinthu zonse zomwe zinawonongeka. Posachedwapa, Iye:

  •   Adzachotsa anthu oipa omwe amachitira nkhanza anzawo.​—Miyambo 2:22.

  •   Adzathandiza anthu amene anakhudzidwa ndi zinthu za nkhanza.​—Chivumbulutso 21:4.

  •   Adzaukitsa anthu omwe anamwalira kuti akhalenso ndi moyo padziko lapansili.​—Yohane 5:28, 29.

 Mukhoza kukhulupirira uthenga wotonthozawu wochokera m’Baibulo. Kuti mudziwe chifukwa chake, tikukulimbikitsani kuti muyambe kuphunzira Baibulo mwaulele mothandizidwa ndi munthu wina.

a Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu.​—Salimo 83:18.