KHALANI MASO

Nkhondo ya ku Ukraine Ikulowa Chaka Chachiwiri—Kodi Baibulo Limapereka Chiyembekezo Chotani?

Nkhondo ya ku Ukraine Ikulowa Chaka Chachiwiri—Kodi Baibulo Limapereka Chiyembekezo Chotani?

 Pofika Lachisanu pa 24 February 2023, pakhala patatha chaka chimodzi kuchokera pamene nkhondo ya ku Ukraine inayamba. Malipoti ena akusonyeza kuti asilikali pafupifupi 300,000 a ku Ukraine ndi Russia aphedwa kapena kuvulazidwa ndipo anthu wamba pafupifupi 30,000 aphedwa pankhondoyi. Komabe, ziwerengerozi zikhoza kukhala zochulukirapo.

 N’zachisoni kuti nkhondoyi ikupitirirabe ndipo sipakuoneka chiyembekezo kuti ikhoza kutha posachedwapa.

  •   “Kungochokera pamene asilikali a ku Russia analowa m’dziko la Ukraine, palibe chizindikiro chilichonse chakuti nkhondoyi ikhoza kutha posachedwapa. Palibe mbali imene ikuonekeratu kuti ikhoza kuwina nkhondoyi ndipo n’zokayikitsa ngati mbali zonse ziwiri zingagwirizane njira yothetsera kusamvanaku.”​—(National Public Radio, NPR), February 19, 2023.

 N’zomveka kuti anthu ambiri akuda nkhawa chifukwa cha mavuto amene nkhondoyi komanso nkhondo zina zikubweretsa kwa anthu osalakwa padziko lapansili. Kodi Baibulo limapereka chiyembekezo chotani? Kodi nkhondo zidzathadi?

Nkhondo yomwe idzathetse nkhondo zonse

 Baibulo limanena kuti pali nkhondo imene idzapulumutse mitundu yonse ya anthu osati kuiwononga. Nkhondoyi imatchedwa Aramagedo ndipo imafotokozedwa kuti ndi ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.’ (Chivumbulutso 16:14, 16) Mulungu adzagwiritsa ntchito nkhondoyi kuthetsa maulamuliro onse a anthu omwe akuchititsa nkhondo zambiri padzikoli. Kuti mudziwe mmene Aramagedo idzabweretsere mtendere wosatha, werengani nkhani zotsatirazi: