Zimene Mungachite Ngati Muli Nokhanokha

Zimene Mungachite Ngati Muli Nokhanokha

 Kodi muli nokhanokha ndiponso mukusungulumwa? Ngati ndi choncho, mwina mukumva ngati mmene wamasalimo ankamvera pamene anati: “Ndakhala ngati mbalame imene ili yokhayokha padenga.” (Salimo 102:7) M’Baibulo muli mfundo zomwe zingakuthandizeni kulimbana ndi mavuto omwe amabwera chifukwa choti muli nokhanokha.

 Yandikirani Mulungu

 Mukhoza kumakhala osangalala ngakhale pamene muli nokhanokha mukazindikira kuti mukufunikira kudziwa Mulungu kenako n’kuyamba kuphunzira za Iye. (Mateyu 5:3, 6) Zinthu zotsatirazi zingakuthandizeni kuchita zimenezi ndipo n’zaulere.

  •   Baibulo la paintaneti lolondola komanso losavuta kuwerenga

  •   Kuphunzira Baibulo paintaneti kuti mupeze ena mwa mayankho a mafunso ofunika kwambiri pamoyo wanu

  •   Mavidiyo aafupi ofotokoza zina mwa mfundo zofunika za m’Baibulo

  •   “Kuyankha Mafunso a m’Baibulo”—Mayankho achindunji a mafunso omwe anthu ambiri amafunsa kawirikawiri

  •   “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo”—Nkhani zosiyanasiyana zokuthandizani kuganizira zochitika pa moyo wa amuna ndi akazi okhulupirika otchulidwa m’Baibulo

  • “Kodi Zinangochitika Zokha?”—Nkhani zosiyanasiyana zofotokoza zinthu zokongola komanso zochititsa chidwi zomwe zili m’chilengedwechi.

  Werengani mavesi otonthoza m’Baibulo

Anthu ambiri atonthozedwa ndi malembawa. M’malo mowerenga mavesi ambiri nthawi imodzi, gwiritsani ntchito nthawi yomwe muli nokhanokhayo posinkhasinkha nkhani iliyonse payokha komanso popemphera.—Maliko 1:35.

 Dziwani chifukwa chake m’dzikoli mukuchitika zinthu zoipa

 Mungakwanitse kulimbana ndi vuto lililonse ngati mukudziwa chifukwa chake zinthu zoipa zimachitika komanso mmene Mulungu adzathetsere mavutowo.—Yesaya 65:17

  •   N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu azivutika?

  •   Kodi Baibulo limati chiyani za matenda komanso thanzi lathu?

  •   Kodi chizindikiro cha “masiku otsiriza” n’chiyani?

  •   Kodi anthu 4 okwera pamahatchi omwe anatchulidwa m’buku la Chivumbulutso akuimira chiyani?

  •   Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Chiyani?

 Musamangokhalira kuda nkhawa

 Nkhani zotsatirazi zingakuthandizeni kudziwa zimene mungachite kuti muchepetse nkhawa zomwe zimabwera chifukwa chokhala nokhanokha ndiponso zikuthandizani kuti ‘muleke kuda nkhawa.’—Mateyu 6:25.

  •   Zimene mungachite kuti muchepetse nkhawa

  •   Kuganizira zinthu zabwino ngakhale mukukumana ndi mavuto

  •   Kuda nkhawa chifukwa cha zinthu zoopsa

  •   Kuda nkhawa chifukwa cha kusowa kwa ndalama

  •   Nkhawa zimene achinyamata amakhala nazo

 Pezani anthu ocheza nawo

 Munthu akamacheza ndi ena amachepetsa nkhawa ndiponso amasangalala. Zimenezi n’zofunika kwambiri makamaka pamene simungathe kukumana ndi anzanuwo pamasom’pamaso. Ngati simungathe kuchoka panyumba, mukhoza kumacheza ndi anzanu kudzera pa vidiyokomfelensi kapena kuwaimbira foni kuti mulimbitse ubwenzi wanu komanso kupeza anzanu ena atsopano. Nkhani zotsatirazi zingakuthandizeni kuti mupeze komanso mukhale “bwenzi lenileni.”—Miyambo 17:17.

  •   Kodi mungatani kuti mukhale bwenzi labwino?

  •   Kodi ndiwonjezere anzanga?

  •   N’chifukwa chiyani ndilibe anzanga enieni?

  •   Limbitsani ubwenzi wanu pokhala wopatsa

  •   Limbitsani ubwenzi wanu pokhala woyamikira

 Muzichita masewera olimbitsa thupi

 Baibulo limavomereza kuti “kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.” (1 Timoteyo 4:8) Kumathandiza kuti muziganiza bwino komanso muzisangalala, makamaka pamene muli nokhanokha. Ngakhale pamene simukuchoka panyumba, pali zinthu zomwe mungachite kuti mulimbitse thupi lanu.

  •   Muzichita masewera olimbitsa thupi

  •   Kukhala wathanzi komanso wopirira