NYIMBO 101

Tizigwira Ntchito Mogwirizana

Tizigwira Ntchito Mogwirizana

(Aefeso 4:3)

  1. 1. M’dziko logawikanali,

    Tili m’gulu la Mulungu.

    Timakhala mwamtendere,

    N’zosangalatsadi.

    Timaunyadira

    Mgwirizanowu.

    Palitu ntchito yambiri.

    Yesu akutsogolera.

    Ndiyetu tizimumvera,

    N’kumagwirizana.

  2. 2. Popempherera umodzi,

    Tizikondana kwambiri,

    Chikondicho chidzakula,

    Komanso mtendere.

    Mtendere n’ngwabwino,

    Utsitsimula.

    Pamene tikukondana,

    M’lungu adzatithandiza.

    Kukhala ogwirizana,

    Pomutumikira.