NYIMBO 102

“Muthandize Ofookawo”

“Muthandize Ofookawo”

(Machitidwe 20:35)

  1. 1. Tonse timavutika,

    Timafo’kanso.

    Koma Mulungu wathu

    Amatikonda.

    Iye n’ngwachifundo;

    Ndi wachikondinso.

    Nafe tikonde ena,

    Tiwathandize.

  2. 2. Atumiki a M’lungu,

    Angafooke.

    Tiziwalimbikitsa,

    Ndi mawu athu.

    Ndi anthu a M’lungu;

    Amawalimbitsa.

    Tiziwadera nkhawa,

    Tiwatonthoze.

  3. 3. M’malo mowaweruza,

    Tikumbukire

    Kuti kukoma mtima

    N’kolimbikitsa.

    Tizichita khama,

    Powalimbikitsa.

    Tikamawathandiza,

    Atonthozedwa.