NYIMBO 105

“Mulungu Ndiye Chikondi”

“Mulungu Ndiye Chikondi”

(1 Yohane 4:7, 8)

  1. 1. Mulungu ndiye chikondi, wati:

    ‘Yendani nane.’

    Tikonde M’lungu ndi anthu,

    Tizichita zabwino.

    Tidzasangalala ndithu;

    Tidzapezanso moyo.

    Tizisonyeza chikondi;

    Ngati cha Yesu Khristu.

  2. 2. Tikakonda choonadi,

    Tidzachita zabwino.

    Tikalakwitsa n’kufo’ka;

    M’lungu amatidzutsa.

    Chikondi chilibe nsanje;

    Ndipo chimapirira.

    Choncho tizikonda ’nzathu;

    Tidzadalitsidwadi.

  3. 3. Musalole kuti mkwiyo;

    Ukutsogolereni.

    Khulupirirani M’lungu;

    Adzakuphunzitsani:

    Kukonda M’lungu ndi anthu,

    N’chikondi chenicheni.

    Tizisonyeza anzathu

    Chikondi cha Mulungu.