NYIMBO 107

Tizitsanzira Chikondi cha Mulungu

Tizitsanzira Chikondi cha Mulungu

(1 Yohane 4:19)

  1. 1. Yehova M’lungu, n’chitsanzo chabwino

    Inde cha chikondi.

    Zochita zake, zimatithandiza

    Kuti tizimutsanzira.

    Anatipatsa, Mwana wake Yesu

    Kuti tikhululukidwe zolakwa.

    Monga umboni wa chikondi chake

    M’lungu wathu, ndiye chikondi.

  2. 2. Tikatsanzira M’lungu tisonyeza

    Chikondi choona,

    Abale onse, tidzawathandiza

    Mosasankha aliyense.

    Tikonde M’lungu komanso anzathu,

    Chimenechi ndi chikondi choona.

    Tizikwirira zolakwa za ena,

    Tidzasonyezadi chikondi.

  3. 3. Chikondi chathu chimatithandiza

    Kumagwirizana.

    Atate wathu akupempha kuti:

    ‘Dzalaweni mgwirizano.’

    Musangalale n’chikondi choona;

    Mawu a M’lungu amatiyengatu.

    Abale athu, amatikumbutsa,

    Za chikondi cha M’lungu wathu.